Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 30

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba popereka Nyumba ya Mulungu.

30 Ndidzakukwezani Yehova,
    chifukwa mwanditulutsa kwakuya,
    ndipo simunalole kuti adani anga akondwere pa ine.
Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo
    ndipo Inu munandichiritsa.
Inu Yehova, munanditulutsa ku manda,
    munandisunga kuti ndisatsalire mʼdzenje.

Imbirani Yehova inu anthu ake okhulupirika;
    tamandani dzina lake loyera.
Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi
    koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse;
utha kuchezera kulira usiku wonse,
    koma chimwemwe chimabwera mmawa.

Pamene ndinaona kuti ndili otetezedwa ndinati,
    “Sindidzagwedezekanso.”
Inu Yehova, pamene munandikomera mtima,
    munachititsa phiri langa kuyima chilili;
koma pamene munabisa nkhope yanu,
    ndinataya mtima.

Kwa Inu Yehova ndinayitana;
    kwa Ambuye ndinapempha chifundo;
“Kodi pali phindu lanji powonongeka kwanga
    ngati nditsikira ku dzenje?
Kodi fumbi lidzakutamandani Inu?
    Kodi lidzalengeza za kukhulupirika kwanu?
10 Imvani Yehova ndipo mundichitire chifundo;
    Yehova mukhale thandizo langa.”

11 Inu munasandutsa kulira kwanga kukhala kuvina;
    munachotsa chiguduli changa ndi kundiveka ndi chimwemwe,
12 kuti mtima wanga uthe kuyimbira Inu usakhale chete.
    Yehova Mulungu wanga, ndidzapereka kwa Inu mayamiko kwamuyaya.

Levitiko 13:1-17

Malamulo a Nthenda za pa Khungu Zopatsirana

13 Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti, “Munthu akakhala ndi chithupsa, kapena mʼbuko, kapena chikanga pa thupi lake chimene chitha kusanduka nthenda ya khate, abwere naye munthuyo kwa Aaroni wansembe kapena kwa mmodzi mwa ana ake amene ndi ansembe. Tsono wansembe ayangʼanitsitse nthendayo pa khungupo, ndipo ngati ubweya wa pamalo pamene pali nthendapo wasanduka woyera, komanso kuti nthendayo yazama mʼkati kupitirira khungu, ndiye kuti nthendayo ndi khate. Wansembe akamuonetsetsa alengeze kuti ndi wodetsedwa. Ngati chikanga cha pa khungulo chikuoneka choyera, ndipo kuya kwake sikukuonekera kuti kwapitirira khungu ndi ubweya wake pamalopo sunasanduke woyera, wansembe amuyike wodwalayo padera kwa masiku asanu ndi awiri. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe amuonenso bwino wodwalayo. Ndipo ngati waona kuti nthendayo sinasinthe ndipo sinafalikire pa khungu, amuyikenso wodwalayo padera kwa masiku ena asanu ndi awiri. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembeyo amuonenso bwino munthuyo, ndipo ngati nthendayo yazima ndi kusafalikira pa khungu, wansembe amutchule munthuyo kuti ndi woyera. Umenewo unali mʼbuko chabe. Choncho munthuyo achape zovala zake ndipo adzakhala woyera. Koma ngati mʼbukowo ufalikira pakhungu atakadzionetsa kale kwa wansembe ndipo wansembeyo nʼkulengeza kuti munthuyo ndi woyeretsedwa, ndiye kuti apitenso kukadzionetsa kwa wansembeyo. Wansembe amuonetsetsenso munthuyo, ndipo ngati mʼbukowo wafalikira pa khungu, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa ndi kuti nthendayo ndi khate.

“Ngati munthu aliyense ali ndi nthenda ya pakhungu yoyipitsa thupi, wodwalayo abwere naye kwa wansembe. 10 Wansembe amuonetsetse munthuyo, ndipo ngati ali ndi chithupsa chamaonekedwe woyera pa khungupo chimene chasandutsa ubweya wa pamalopo kukhala woyera, ndipo ngati pali zilonda pa chotupacho, 11 limenelo ndi khate lachikhalire la pa khungu, ndipo wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Asamutsekere munthu woteroyo pakuti ndi wodetsedwa kale.

12 “Ndipo ngati, mʼkuona kwa wansembe, khate lija lafalikira pa khungu lonse moti lamugwira thupi lonse kuyambira kumutu mpaka kumapazi, 13 wansembe amuonetsetse munthuyo, ndipo ngati khatero lagwira thupi lake lonse, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyera. Popeza kuti thupi lonse lasanduka loyera, munthuyo ndi woyeretsedwa. 14 Koma pa tsiku limene zilonda zidzaoneka pa iye, munthuyo adzakhala wodetsedwa. 15 Wansembe aonetsetse zilondazo ndipo alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Zilondazo ndi zodetsedwa ndipo ili ndi khate. 16 Koma zilondazo zikasinthika ndi kusanduka zoyera, munthuyo ayenera kupita kwa wansembe. 17 Wansembe amuonetsetse ndipo ngati zilondazo zasanduka zoyera, wansembe amutchule wodwalayo kuti ndi woyera ndipo adzakhala woyera ndithu.

Ahebri 12:7-13

Pamene mukupirira masautso monga chilango, Mulungu achitira inu monga ana ake. Kodi ndi mwana wotani amene abambo ake samulanga? Ngati inu simulangidwa, komatu aliyense amalangidwa, ndiye kuti sindinu ana enieni koma amʼchigololo. Komanso, tonsefe tinali ndi abambo athu otibala amene amatilanga ndipo timawapatsa ulemu. Nanga kodi sitidzagonjera Atate a mizimu yathu kuti tikhale ndi moyo? 10 Abambo athu ankatilanga kwa kanthawi kochepa monga amaonera kufunika kwake, koma Mulungu amatilanga kuti tipindule, kuti tikhale oyera mtima. 11 Palibe chilango chimene chimaoneka kuti ndi chabwino pa nthawiyo, komatu chowawa. Koma pambuyo pake, chimabweretsa chipatso chachilungamo ndi mtendere kwa iwo amene aleredwa mwa njira imeneyi.

12 Nʼchifukwa chake limbitsani manja anu otopa ndi mawondo anu ogowoka. 13 Muziyenda mʼnjira zowongoka, kuti iwo amene akukutsatirani ngakhale ndi olumala ndi ofowoka asapunthwe ndi kugwa koma adzilimbikitsidwa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.