Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 110

Salimo la Davide.

110 Yehova akuwuza Mbuye wanga kuti,
    “Khala ku dzanja langa lamanja
mpaka nditasandutsa adani ako
    kukhala chopondapo mapazi ako.”

Yehova adzakuza ndodo yamphamvu ya ufumu wako kuchokera mʼZiyoni;
    udzalamulira pakati pa adani ako.
Ankhondo ako adzakhala odzipereka
    pa tsiku lako la nkhondo.
Atavala chiyero chaulemerero,
    kuchokera mʼmimba ya mʼbandakucha,
    udzalandira mame a unyamata wako.

Yehova walumbira
    ndipo sadzasintha maganizo ake:
“Ndiwe wansembe mpaka muyaya
    monga mwa unsembe wa Melikizedeki.”

Ambuye ali kudzanja lako lamanja;
    Iye adzaponda mafumu pa tsiku la ukali wake.
Adzaweruza anthu a mitundu ina,
    adzadzaza dziko lapansi ndi mitembo ndipo adzaphwanya olamulira a pa dziko lonse lapansi.
Iye adzamwa mu mtsinje wa mʼmbali mwa njira;
    choncho adzaweramutsa mutu wake.

Eksodo 1:22-2:10

22 Pamenepo Farao analamulira anthu ake onse kuti, “Mwana wamwamuna aliyense akabadwa, mukamuponye mu mtsinje wa Nailo, koma wamkazi mulekeni akhale ndi moyo.”

Kubadwa kwa Mose

Ndipo munthu wina wa fuko la Levi anakwatira mkazi wa fuko lomwelo. Mkaziyo anatenga pathupi ndipo anabereka mwana wamwamuna. Ataona kuti mwanayo anali wokongola, anamubisa kwa miyezi itatu. Koma mwanayo atafika pa msinkhu woti sakanathanso kubisidwa, amayi ake anatenga kadengu kopangidwa ndi bango nakamata phula. Kenaka anayika mwanayo mʼmenemo ndi kukamuyika pa mabango mu mtsinje wa Nailo. Mlongo wake wa mwanayo anayima pataliko kuti aone chimene chidzamuchitikira mwanayo.

Mwana wamkazi wa Farao anapita ku mtsinje wa Nailo kukasamba ndipo adzakazi ake ankayenda mʼmbali mwa mtsinjewo. Tsono mwana wa Farao uja anaona kadenguko pakati pa mabango ndipo anatuma mdzakazi wake kuti akakatenge. Iye atavundukula anaona mwana wamwamuna akungolira. Iye anamva naye chisoni mwana uja, nati, “Ameneyu ndi mmodzi mwa ana a Chihebri.”

Kenaka mlongo wake wa mwanayo anafunsa mwana wa Farao kuti, “Ndingapite kukakupezerani mmodzi mwa amayi a Chihebri kuti azikakulererani mwanayu?”

Iye anayankha kuti, “Inde, pita.” Ndipo mtsikanayo anapita nakayitana amayi a mwanayo. Mwana wa Farao anati, “Tengani mwanayu mukandilerere, ndidzakulipirani.” Mayiyo anatenga mwanayo kukamulera. 10 Mwanayo atakula anakamupereka kwa mwana wa Farao ndipo anakhala mwana wake. Iye anamutcha dzina lake Mose, popeza anati, “Ndinamuvuwula mʼmadzi.”

Ahebri 11:23-26

23 Ndi chikhulupiriro Mose atabadwa makolo ake anamubisa miyezi itatu, chifukwa iwo anaona kuti mwanayo anali wokongola ndipo sanaope konse lamulo la mfumu.

24 Ndi chikhulupiriro Mose atakula, anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao. 25 Iye anasankha kuzunzika nawo limodzi anthu a Mulungu kuposa kusangalala ndi zokondweretsa za uchimo kwa nthawi yochepa. 26 Anaona kuti kuzunzika chifukwa cha Khristu kunali kwa mtengowapatali kuposa chuma cha ku Igupto, chifukwa amaona mphotho ya mʼtsogolo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.