Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 6:9-22

Nowa ndi Chigumula

Mbiri ya Nowa inali yotere:

Nowa anali munthu wolungama ndi wopanda tchimo pakati pa anthu a mʼbado wake. Ndipo anayenda ndi Mulungu. 10 Nowa anabereka ana aamuna atatu: Semu, Hamu ndi Yafeti.

11 Chiwawa chinadzaza pa dziko lapansi kotero kuti dziko linakhala lowonongeka pamaso pa Mulungu. 12 Mulungu atayangʼana, anaona kuti dziko layipadi chifukwa cha makhalidwe oyipa a anthu onse pa dziko lapansi. 13 Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, “Ndatsimikiza mtima kuti ndiwononge anthu onse, pakuti dziko lapansi ladzaza ndi ntchito zawo zoyipa. Ndithudi ndiwawononga pamodzi ndi zonse za pa dziko. 14 Tsono udzipangire chombo cha matabwa a mtengo wanjale; mʼkati mwake upange zipinda ndipo upake phula mʼkati ndi kunja. 15 Uchipange motere: Chombo chikhale mamita 140 mulitali, mamita 23 mulifupi ndi mamita 13 mu msinkhu wake. 16 Uchipangire denga ndi kuchimaliza ndi zenera la masentimita makumi asanu. Uyike khomo mʼmbali mwa chombocho ndi kupanga zipinda zosanjikana; chapansi, chapakati ndi chapamwamba. 17 Ndidzagwetsa mvula ya chigumula pa dziko lapansi kuti ndiwononge zamoyo zonse za pansi pa thambo ndipo chilichonse cha pa dziko lapansi chidzafa. 18 Koma ndidzachita pangano langa ndi iwe. Iwe, ana ako aamuna, mkazi wako ndi akazi a ana ako nonse mudzalowa mʼchombocho. 19 Iwe udzalowa mʼchombocho ndi zolengedwa zamoyo zonse ziwiriziwiri, chachimuna ndi chachikazi, kuti zisungike ndi moyo pamodzi ndi iwe. 20 Udzatenga ziwiriziwiri za mitundu yonse ya mbalame, mitundu yonse ya nyama, ndi mitundu yonse ya zokwawa kuti zikhale ndi moyo. 21 Udzatengenso chakudya cha mtundu uliwonse ndi kuchisunga kuti inu ndi nyamazo muzidzadya.”

22 Nowa anachita zonse monga Mulungu anamulamulira.

Genesis 7:24

24 Madziwo anadzaza dziko lonse lapansi kwa masiku 150.

Genesis 8:14-19

14 Pokwana tsiku la 27 la mwezi wachiwiri dziko lapansi linawumiratu.

15 Tsono Mulungu anawuza Nowa kuti, 16 “Iwe, mkazi wako, ana ako pamodzi ndi akazi awo tulukani mʼchombomo. 17 Tulutsa zamoyo zonse zili ndi iwe, mbalame, nyama ndi zokwawa zonse kuti ziswane ndi kuchulukana pa dziko lapansi.”

18 Nowa anatuluka pamodzi ndi ana ake aamuna, mkazi wake ndi akazi a ana ake. 19 Nyama zonse, zokwawa zonse, mbalame zonse, chilichonse choyenda pa dziko lapansi, zinatuluka mʼchombo motsogozana monga mwa mitundu yawo.

Masalimo 46

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora. Nyimbo ya anamwali.

46 Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu,
    thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.
Nʼchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisunthike,
    ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja,
ngakhale madzi ake atakokoma ndi kuchita thovu,
    ngakhale mapiri agwedezeke ndi kukokoma kwake.

Kuli mtsinje umene njira zake za madzi zimasangalatsa mzinda wa Mulungu,
    malo oyera kumene Wammwambamwamba amakhalako.
Mulungu ali mʼkati mwake, iwo sudzagwa;
    Mulungu adzawuthandiza mmawa.
Mitundu ikupokosera, mafumu akugwa;
    Iye wakweza mawu ake, dziko lapansi likusungunuka.

Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife,
    Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.

Bwerani kuti mudzaone ntchito za Yehova,
    chiwonongeko chimene wachibweretsa pa dziko lapansi.
Iye amathetsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi;
    Iye amathyola uta ndi kupindapinda mkondo;
    amatentha zishango ndi moto.
10 Iye akuti, “Khala chete, ndipo dziwa kuti ndine Mulungu;
    ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu;
    ine ndidzakwezedwa mʼdziko lapansi.”

11 Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife,
    Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.

Aroma 1:16-17

16 Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino chifukwa ndiwo mphamvu za Mulungu zopulumutsa aliyense amene akhulupirira, poyamba Myuda, kenaka Mhelene. 17 Pakuti mu Uthenga Wabwino anawulula kuti chilungamo chimachokera kwa Mulungu. Kuyambira pachiyambi mpaka potsiriza ndi chilungamo chobwera mwachikhulupiriro, monga kwalembedwera kuti, “Wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.”

Aroma 3:22-28

22 Timakhala olungama pamaso pa Mulungu pamene takhulupirira Yesu Khristu. Mulungu amachitira zimenezi anthu onse amene akhulupirira Khristu. Palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina, 23 pakuti onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu 24 ndipo onse alungamitsidwa mwaulere mwa chisomo chake chifukwa cha Khristu Yesu amene anawawombola. 25 Mulungu anamupereka Iyeyu kuti pokhetsa magazi ake, akhale nsembe yokhululukira machimo. Mulungu anachita zimenezi kufuna kuonetsa chilungamo chake. Chifukwa cha kuleza mtima kwake, sanalange anthu chifukwa cha machimo amene anachita kale. 26 Iye anachita izi kuti aonetse chilungamo chake lero lino. Anthu azindikire kuti Iye ndi wolungama ndipo amalungamitsa aliyense amene akhulupirira Yesu.

27 Nanga tsono pamenepa munthu anganyadenso? Kunyadatu kwachotsedwa. Chifukwa cha Malamulo? Kodi Malamulo samafuna ntchito za munthu? Ayi, koma mwachikhulupiriro. 28 Ife tikunenabe kuti munthu amalungamitsidwa mwachikhulupiriro osati mwakusunga Malamulo.

Aroma 3:29-31

29 Kodi Mulungu ndi Mulungu wa Ayuda okha? Kodi si Mulungu wa a mitundu inanso? Inde wa a mitundu inanso, 30 popeza ndi Mulungu mmodzi yemweyo amene adzalungamitsa mwachikhulupiriro ochita mdulidwe ndi osachita mdulidwe kudzera mʼchikhulupiriro chomwecho. 31 Kodi tsono ife, tikutaya Malamulo pamene tikunena kuti pafunika chikhulupiriro? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Komatu ife tikukwaniritsadi Malamulo.

Mateyu 7:21-29

Ophunzira Owona ndi Onyenga

21 “Si munthu aliyense amene amanena kwa Ine, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowe mu ufumu wakumwamba, koma ndi yekhayo amene amachita chifuniro cha Atate anga amene ali kumwamba. 22 Ambiri adzati kwa Ine pa tsikulo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi sitinkanenera mʼdzina lanu ndi mʼdzina lanunso tinkatulutsa ziwanda ndi kuchita zodabwitsa zambiri?’ 23 Pamenepo ndidzawawuza momveka bwino kuti, ‘Sindinakudziweni inu. Chokani kwa Ine, inu ochita zoyipa!’

Womanga Nyumba Wanzeru ndi Wopusa

24 “Nʼchifukwa chake aliyense amene amva mawu anga ndi kuwachita akufanana ndi munthu wanzeru amene anamanga nyumba yake pa thanthwe. 25 Mvula inagwa, mitsinje inadzaza, ndi mphepo zinawomba pa nyumbayo; koma sinagwe, chifukwa maziko ake anali pa thanthwe. 26 Koma aliyense amene amva mawu angawa ndi kusawachita ali ngati munthu wopusa amene anamanga nyumba yake pa mchenga. 27 Mvula inagwa, mitsinje inadzaza, ndi mphepo zinawomba pa nyumbayo, ndipo inagwa ndipo kugwa kwake kunali kwakukulu.”

28 Yesu atamaliza kunena zonsezi, magulu a anthu anadabwa ndi chiphunzitso chake, 29 chifukwa anaphunzitsa ngati amene anali ndi ulamuliro osati ngati aphunzitsi amalamulo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.