Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 146

146 Tamandani Yehova.

Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
    Ndidzatamanda Yehova ndi moyo wanga wonse;
    ndidzayimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.

Musamadalire mafumu,
    anthu osakhalitsa, amene sangathe kupulumutsa.
Pamene mizimu yawo yachoka, iwo amabwerera ku dothi;
    zimene ankafuna kuchita zimatha tsiku lomwelo.

Wodala ndi amene thandizo lake ndi
    Mulungu wa Yakobo.
Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi,
    nyanja ndi zonse zili mʼmenemo;
    Yehova, amene ndi wokhulupirika kwamuyaya.
Iye amachitira chilungamo anthu oponderezedwa
    ndipo amapereka chakudya kwa anthu anjala.
Yehova amamasula amʼndende,
    Yehova amatsekula maso anthu osaona,
Yehova amadzutsa onse amene awerama pansi,
    Yehova amakonda anthu olungama.
Yehova amasamalira alendo
    ndipo amathandiza ana ndi akazi amasiye,
    koma amasokoneza njira za anthu oyipa.

10 Yehova ndiye Mfumu mpaka muyaya,
    Mulungu wako iwe Ziyoni, pa mibado yonse.

Tamandani Yehova.

Numeri 15:17-26

17 Yehova anawuza Mose kuti, 18 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo unene kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukutengeraniko 19 ndipo mukakadya chakudya cha mʼdzikolo, mukapereke gawo lina kwa Yehova monga chopereka. 20 Pa buledi wanu woyamba, mukapereke mmodzi monga nsembe, ngati chopereka chochokera ku malo wopunthira tirigu. 21 Pa mibado yanu yonse muzidzapereka chopereka ichi kwa Yehova kuchokera ku zakudya zanu zoyamba za mʼnthaka.

Chopereka Chopepesera Machimo Ochita Mosadziwa

22 “ ‘Ndipo ngati muchimwa mosadziwa posasunga ena mwa malamulo awa amene Yehova wapereka kwa Mose, 23 lina lililonse mwa malamulo a Yehova amene wapereka kwa inu kudzera mwa Mose, kuyambira tsiku limene Yehova anawapereka mpaka mibado ya mʼtsogolo, 24 ndipo ngati zimenezi zachitika osati mwadala ndipo gulu lonse silinadziwe, zikatero gulu lonselo lipereke mwana wangʼombe wamwamuna monga nsembe yopsereza kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova pamodzinso ndi chopereka chachakudya ndi chopereka cha chakumwa ndi mbuzi yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo potsata zimene zinalamulidwa. 25 Wansembe apereke nsembe yopepesera machimo a gulu lonse la Aisraeli, ndipo adzakhululukidwa, pakuti linali tchimo lochita mosadziwa. Ndipo chifukwa cha tchimo lawolo, abweretse kwa Yehova nsembe yotentha pa moto ndi nsembe yopepesera machimo. 26 Gulu lonse la Aisraeli ndi alendo okhala pakati pawo adzakhululukidwa chifukwa anthu onsewo anachimwa mosadziwa.

Machitidwe a Atumwi 26:1-11

Mawu a Paulo Pamaso pa Mfumu Agripa

26 Ndipo Agripa anawuza Paulo kuti, “Takulola kuti unene mawu ako.” Paulo anatambasula dzanja lake nayamba kudziteteza kuti, “Mfumu Agripa ine ndikudziyesa wa mwayi kuyima pamaso panu lero lino ndi kudziteteza, kutsutsa zonse zimene Ayuda andinenera, ndipo makamaka chifukwa inu mukudziwa bwino miyambo yonse ya Chiyuda ndiponso zonse zimene amatsutsana. Nʼchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundimvetsere moleza mtima.

“Ayuda onse akudziwa za moyo wanga mmene ndakhalira kuyambira ndili mwana, kuchokera pachiyambi cha moyo wanga mʼdziko lathu ndiponso mu Yerusalemu. Iwo akundidziwa kuyambira kalekale ndipo angathe kuchitira umboni kuti ndakhala ndili Mfarisi moyo wanga wonse, mmodzi wa gulu limene limasamala chipembedzo chathu koposa. Ndipo tsopano ndikuyimbidwa mlandu lero chifukwa cha chiyembekezo changa pa zimene Mulungu analonjeza makolo athu. Ili ndi lonjezo limene mafuko athu khumi ndi awiri akuyembekezera kuti likwaniritsidwe pamene akupembedza Mulungu molimbika usana ndi usiku. Wolemekezeka Mfumu, nʼchifukwa cha chiyembekezo chimenechi Ayuda kuti akundiyimba mlandu. Nʼchifukwa chiyani ena a inu mukuganiza kuti nʼkosatheka kuti Mulungu aukitse akufa?

“Inenso ndimaganiza kuti ndimayenera kuchita zinthu zambiri pofuna kuthana ndi dzina la Yesu wa ku Nazareti. 10 Ndipo izi ndi zimene ndinazichita ku Yerusalemu. Ndi ulamuliro wa akulu a ansembe, ine ndinayika mʼndende oyera mtima ambiri, ndipo pamene amaphedwa, ine ndimavomereza. 11 Nthawi zambiri ndinkapita mʼsunagoge iliyonse kuti alangidwe, ndipo ndinayesera kuwakakamiza kuti achitire chipongwe Mulungu. Mu mkwiyo wangawo, ndimapita ngakhale ku mizinda yachilendo kuti ndikawazunze.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.