Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
6 Mpando wanu waufumu, Inu Mulungu, udzakhala ku nthawi za nthawi;
ndodo yaufumu yachilungamo idzakhala ndodo yaufumu ya ufumu wanu.
7 Inu mumakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa;
choncho Mulungu, Mulungu wanu, wakukhazikani pamwamba pa anzanu
pokudzozani ndi mafuta a chimwemwe.
8 Mikanjo yanu yonse ndi yonunkhira ndi mure ndi aloe ndi kasiya;
kuchokera ku nyumba zaufumu zokongoletsedwa ndi mnyanga wanjovu
nyimbo za zoyimbira zazingwe zimakusangalatsani.
9 Ana aakazi a mafumu ali pakati pa akazi anu olemekezeka;
ku dzanja lanu lamanja kuli mkwatibwi waufumu ali mu golide wa ku Ofiri.
10 Tamvera, iwe mwana wa mkazi ganizira ndipo tchera khutu;
iwala anthu ako ndi nyumba ya abambo ako.
11 Mfumu yathedwa nzeru chifukwa cha kukongola kwako;
mulemekeze pakuti iyeyo ndiye mbuye wako.
12 Mwana wa mkazi wa ku Turo adzabwera ndi mphatso,
amuna a chuma adzafunafuna kukoma mtima kwako.
13 Wokongola kwambiri ndi mwana wa mfumu ali mʼchipinda mwake,
chovala chake ndi cholukidwa ndi thonje ndi golide.
14 Atavala zovala zamaluwamaluwa akupita naye kwa mfumu;
anamwali okhala naye akumutsatira
ndipo abweretsedwa kwa inu.
15 Iwo akuwaperekeza ndi chimwemwe ndi chisangalalo;
akulowa mʼnyumba yaufumu.
16 Ana ako aamuna adzatenga malo a makolo ako;
udzachititsa kuti akhale ana a mfumu mʼdziko lonse.
17 Ndidzabukitsa mbiri yako mʼmibado yonse;
choncho mitundu yonse idzakutamanda ku nthawi za nthawi.
Kulapa Kubweretsa Madalitso
14 Iwe Israeli bwerera kwa Yehova Mulungu wako.
Machimo anu ndi amene akugwetsani!
2 Bweretsani zopempha zanu
ndipo bwererani kwa Yehova.
Munene kwa Iye kuti,
“Tikhululukireni machimo athu onse
ndi kutilandira mokoma mtima,
kuti tithe kukuyamikani ndi mawu a pakamwa pathu.
3 Asiriya sangatipulumutse;
ife sitidzakwera pa akavalo ankhondo,
sitidzanenanso kuti, ‘Milungu yathu’
kwa zimene manja athu omwe anazipanga,
pakuti ndinu amene mumachitira chifundo ana amasiye.”
4 Ine ndidzachiza kusakhulupirika kwawo
ndipo ndidzawakonda mwaufulu
pakuti ndaleka kuwakwiyira.
5 Ndidzakhala ngati mame kwa Israeli
Ndipo iye adzachita maluwa ngati kakombo.
Adzazika mizu yake pansi
ngati mkungudza wa ku Lebanoni;
6 mphukira zake zidzakula.
Kukongola kwake kudzakhala ngati mtengo wa olivi,
kununkhira kwake ngati mkungudza wa ku Lebanoni.
7 Anthu adzakhalanso mu mthunzi wake.
Iye adzakula bwino ngati tirigu.
Adzachita maluwa ngati mphesa
ndipo kutchuka kwake kudzakhala ngati vinyo wochokera ku Lebanoni.
8 Efereimu adzati, “Ndidzachita nawonso chiyani mafano?
Ine ndidzamuyankha ndi kumusamalira.
Ine ndili ngati mtengo wa payini wobiriwira;
zipatso zako zimachokera kwa Ine.”
9 Ndani ali ndi nzeru? Adzazindikire zinthu izi.
Ndani amene amamvetsa zinthu? Adzamvetse izi.
Njira za Yehova ndi zolungama;
anthu olungama amayenda mʼmenemo,
koma anthu owukira amapunthwamo.
Paulo ndi Atumwi Onyenga
11 Ndikukhulupirira kuti mupirira nako pangʼono kupusa kwanga. Chonde tandipirirani! 2 Nsanje imene ndimakuchitirani ndi yofanana ndi ya Mulungu. Ndinakulonjezani mwamuna mmodzi yekha, mwamunayo ndiye Khristu, kuti ndidzakuperekeni inuyo kwa Iyeyo monga namwali wangwiro. 3 Koma ndikuopa kuti monga Hava ananyengedwa ndi kuchenjera kwa njoka, mitima yanunso ingasocheretsedwe kuleka nʼkudzipereka moona mtima ndi modzipereka kwenikweni kwa Khristu. 4 Pakuti ngati wina abwera kwa inu nalalikira Yesu wina wosiyana ndi Yesu amene tinamulalikira, kapena ngati mulandira mzimu wina wosiyana ndi Mzimu amene munalandira, kapena uthenga wabwino wina wosiyana ndi umene munawuvomereza, inuyo mumangolandira mosavuta.
5 Komatu sindikuganiza kuti ndine wotsika kwambiri kwa “atumwi apamwamba.” 6 Mwina ndikhoza kukhala wosaphunzitsidwa kayankhulidwe, koma ndili ndi chidziwitso. Izi tinakufotokozerani momveka bwinobwino. 7 Kodi linali tchimo kwa ine kudzichepetsa nʼcholinga chakuti ndikukwezeni pamene ndinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu mwaulere? 8 Ndinkalanda mipingo ina pomalandira thandizo kwa iwo kuti ndikutumikireni. 9 Ndipo pamene ndinali pakati panu, nditasowa kanthu, sindinalemetse munthu aliyense, pakuti abale ena amene anachokera ku Makedoniya anandipatsa zonse zimene ndinkazisowa. Ndayesetsa kuti ndisakhale cholemetsa kwa inu mʼnjira ina iliyonse, ndipo ndidzapitiriza kutero. 10 Kunena moona mtima molingana ndi chilungamo cha Khristu chimene chili mwa ine, palibe amene angandiletse kudzitamandira mʼzigawo za ku Akaya. 11 Nʼchifukwa chiyani ndikutero? Kodi nʼchifukwa choti sindikukondani? Mulungu akudziwa kuti ndimakukondani!
12 Ndipo ndipitiriza kuchita zomwe ndikuchitazi nʼcholinga chakuti ndisapereke mpata kwa amene akufuna kupezera mwayi woti afanane nafe pa zinthu zimene iwowo amadzitamandira. 13 Pakuti anthu oterewa ndi atumwi onama, antchito achinyengo, odzizimbayitsa ngati atumwi a Khristu. 14 Sizododometsa zimenezi, pakuti Satana mwini amadzizimbayitsa kuoneka ngati mngelo wowunikira anthu. 15 Nʼzosadabwitsa tsono ngati atumiki ake akudzizimbayitsa ngati otumikira chilungamo. Matsiriziro awo adzalandira zoyenerana ndi ntchito zawo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.