Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Hoseya 2:14-20

14 “Koma tsopano ndidzamukopa mkaziyo;
    ndidzapita naye ku chipululu
    ndipo ndidzamuyankhula mwachikondi.
15 Kumeneko ndidzamubwezera minda yake ya mpesa,
    ndipo ndidzasandutsa Chigwa cha Akori kukhala khomo la chiyembekezo.
Kumeneko iye adzayimba nyimbo monga mʼmasiku a ubwana wake,
    monga tsiku limene anatuluka ku Igupto.

16 “Tsiku limeneli,” Yehova akuti,
    “udzandiyitana kuti, ‘Amuna anga;’
    sudzandiyitananso kuti, ‘Mbuye wanga.’
17 Ndidzachotsa mayina a Abaala pakamwa pake;
    sadzatchulanso mayina awo popemphera.
18 Tsiku limenelo ndidzachita pangano
    ndi zirombo zakuthengo ndi mbalame zamumlengalenga
    ndiponso zolengedwa zokwawa pansi kuti ziyanjane ndi anthu anga.
Ndidzachotsa mʼdzikomo uta,
    lupanga ndi zida zonse zankhondo,
    kuti onse apumule mwamtendere.
19 Ndidzakutomera kuti ukhale mkazi wanga mpaka muyaya;
    ndidzakutomera mwachilungamo, mwaungwiro,
    mwachikondi ndi mwachifundo.
20 Ndidzakutomera mokhulupirika
    ndipo udzadziwa Yehova.

Masalimo 103:1-13

Salimo la Davide.

103 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga;
    ndi zonse zamʼkati mwanga zitamande dzina lake loyera.
Tamanda Yehova, iwe moyo wanga,
    ndipo usayiwale zabwino zake zonse.
Amene amakhululuka machimo ako onse
    ndi kuchiritsa nthenda zako zonse,
amene awombola moyo wako ku dzenje
    ndi kukuveka chikondi ndi chifundo chake ngati chipewa chaufumu,
amene akwaniritsa zokhumba zako ndi zinthu zabwino,
    kotero kuti umakhala wamphamvu zatsopano ngati mphungu.

Yehova amachita chilungamo
    ndipo amaweruza molungama onse opsinjika.

Iye anadziwitsa Mose njira zake,
    ntchito zake kwa Aisraeli.
Yehova ndi wachifundo ndi wokoma mtima,
    wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka.
Iye sadzatsutsa nthawi zonse,
    kapena kusunga mkwiyo wake kwamuyaya;
10 satichitira molingana ndi machimo athu,
    kapena kutibwezera molingana ndi mphulupulu zathu.
11 Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi,
    koteronso chikondi chake nʼchachikulu kwa iwo amene amamuopa;
12 monga kummawa kutalikirana ndi kumadzulo,
    koteronso Iye watichotsera mphulupulu zathu kuti zikhale kutali nafe.
13 Monga bambo amachitira chifundo ana ake,
    choncho Yehova ali ndi chifundo ndi iwo amene amamuopa;

Masalimo 103:22

22 Tamandani Yehova, ntchito yake yonse
    kulikonse mu ulamuliro wake.

Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.

2 Akorinto 3:1-6

Akhristu ndi Kalata Yochokera kwa Khristu

Kodi tayambanso kudzichitira umboni tokha? Kapena kodi ifenso tikufuna makalata otivomereza kwa inu, kapena ochokera kwa inu monga anthu ena? Inu ndinu kalata yathu, yolembedwa pa mitima yathu, yodziwika ndi yowerengedwa ndi aliyense. Inu mukuonetsa kuti ndinu kalata yochokera kwa Khristu, zotsatira za utumiki wathu, osati yolembedwa ndi inki koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo, osati pa miyala yosemedwa koma mʼmitima ya anthu.

Kulimba mtima kumeneku tili nako pamaso pa Mulungu kudzera mwa Khristu. Sikuti mwa ife muli kanthu kotiganizitsa kuti tingathe kugwira ntchitoyi patokha, koma kulimba mtima kwathu kumachokera kwa Mulungu. Iye watipatsa kulimba mtima kuti tikhale atumiki a pangano latsopano, osati malamulo olembedwa koma a Mzimu; pakuti malamulo olembedwa amapha koma Mzimu amapereka moyo.

Marko 2:13-22

Kuyitanidwa kwa Levi

13 Yesu anatulukanso napita kumbali ya nyanja. Gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Iye, ndipo anayamba kuliphunzitsa. 14 Pamene ankayendabe, anaona Levi mwana wa Alufeyo atakhala mʼnyumba ya msonkho. Yesu anamuwuza kuti, “Tsate Ine.” Ndipo Levi anayimirira namutsata Iye.

15 Yesu atakalandira chakudya ku nyumba kwa Levi, amisonkho ambiri ndi “ochimwa” ankadya naye pamodzi ndi ophunzira ake, pakuti anali ambiri amene anamutsatira. 16 Pamene aphunzitsi amalamulo a Afarisi anamuona akudya ndi “ochimwa” ndi amisonkho, anafunsa ophunzira ake kuti, “Chifukwa chiyani amadya ndi olandira msonkho ndi ochimwa?”

17 Yesu atamva zimenezi, anawawuza kuti, “Anthu amene ali bwino safuna singʼanga koma odwala. Ine sindinabwere kudzayitana olungama, koma ochimwa.”

Za Kusala Kudya

18 Ndipo ophunzira a Yohane ndi a Afarisi amasala kudya. Anthu ena anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Zitheka bwanji kuti ophunzira a Yohane ndi ophunzira a Afarisi amasala kudya, koma anu satero?”

19 Yesu anayankha nati, “Kodi alendo a mkwati angasale kudya bwanji pamene iye ali nawo pamodzi? Iwo sangatero, pamene iye ali nawo pamodzi. 20 Koma nthawi idzafika pamene mkwati adzachotsedwa pakati pawo, ndipo pa tsiku limenelo adzasala kudya.

21 “Palibe amene amasokerera chigamba chatsopano pa chovala chakale. Ngati atatero, chigamba chatsopanocho chidzazomola chovala chakalecho, kukulitsa chibowocho. 22 Ndipo palibe amene amathira vinyo watsopano mʼmatumba akale a vinyo. Ngati atatero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa matumba a vinyo ndipo vinyoyo pamodzi ndi matumbawo zidzawonongeka. Ayi, satero, amathira vinyo watsopano mʼmatumba atsopanonso.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.