Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide.
103 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga;
ndi zonse zamʼkati mwanga zitamande dzina lake loyera.
2 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga,
ndipo usayiwale zabwino zake zonse.
3 Amene amakhululuka machimo ako onse
ndi kuchiritsa nthenda zako zonse,
4 amene awombola moyo wako ku dzenje
ndi kukuveka chikondi ndi chifundo chake ngati chipewa chaufumu,
5 amene akwaniritsa zokhumba zako ndi zinthu zabwino,
kotero kuti umakhala wamphamvu zatsopano ngati mphungu.
6 Yehova amachita chilungamo
ndipo amaweruza molungama onse opsinjika.
7 Iye anadziwitsa Mose njira zake,
ntchito zake kwa Aisraeli.
8 Yehova ndi wachifundo ndi wokoma mtima,
wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka.
9 Iye sadzatsutsa nthawi zonse,
kapena kusunga mkwiyo wake kwamuyaya;
10 satichitira molingana ndi machimo athu,
kapena kutibwezera molingana ndi mphulupulu zathu.
11 Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi,
koteronso chikondi chake nʼchachikulu kwa iwo amene amamuopa;
12 monga kummawa kutalikirana ndi kumadzulo,
koteronso Iye watichotsera mphulupulu zathu kuti zikhale kutali nafe.
13 Monga bambo amachitira chifundo ana ake,
choncho Yehova ali ndi chifundo ndi iwo amene amamuopa;
22 Tamandani Yehova, ntchito yake yonse
kulikonse mu ulamuliro wake.
Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
53 “ ‘Koma, ndidzadalitsanso Sodomu ndi ana ake aakazi. Ndidzadalitsanso Samariya ndi ana ake aakazi. Pa nthawi yomweyo ndidzakudalitsanso iwe Yerusalemu. 54 Ndidzatero kuti uchite manyazi ndi kunyozeka chifukwa cha zonse zimene unachita powatonthoza anthuwa. 55 Motero mʼbale wako Sodomu ndi ana ake akadzakhala monga mmene analili poyamba paja, ndiponso mʼbale wako Samariya akadzakhalanso monga mmene anali poyamba paja, ndiye kuti iwenso ndi ana ako mudzakhala monga mmene munalili payamba paja. 56 Kale lija pamene unkanyada, suja unkanyogodola mʼbale wako Sodomu 57 kuyipa kwako kusanadziwike? Koma tsopano wafanana naye. Wasandukano chinthu chonyozeka kwa anthu a ku Edomu ndi kwa onse owazungulira ndiponso kwa Afilisti. Ndithu onse amene akuzungulira amakunyoza. 58 Choncho udzalangidwa chifukwa cha zigololo zako ndi machitidwe anu onyansa, akutero Yehova.
59 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzakulanga molingana ndi zimene unachita. Iwe unanyoza lumbiro lako pophwanya pangano langa. 60 Komabe, Ine ndidzakumbukira pangano limene ndinachita nawe mʼmasiku a unyamata wako, ndipo ndidzakhazikitsa pangano losatha ndi iwe. 61 Tsono udzakumbukira njira zako zakale. Udzachita manyazi polandiranso abale ako, wamkulu ndi wamngʼono yemwe. Ndidzawaperekanso kwa iwe kuti akhale ngati ana ako ngakhale kuti sali a mʼpangano langa ndi iwe. 62 Kotero ndidzakhazikitsa pangano langa ndi iwe, ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 63 Ndikadzakukhululukira zoyipa zako zonse zimene unachita, udzazikumbukira ndipo udzachita manyazi kwambiri, kotero kuti sudzatha nʼkuyankhula komwe, akutero Ambuye Yehova.’ ”
[Mipukutu yoyambirira ndi maumboni akale mulibe 7:53 mpaka 8:11]
Za Mkazi Wachigololo
53 Kenaka onse anachoka, napita kwawo. 8 1 Koma Yesu anapita ku phiri la Olivi. 2 Mmamawa Iye anaonekeranso ku Nyumba ya Mulungu kumene anthu onse anamuzungulira ndipo Iye anakhala pansi nawaphunzitsa. 3 Aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi anabweretsa mkazi amene anagwidwa akuchita chigololo. Iwo anamuyimiritsa patsogolo pa anthu ndipo 4 anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, mkazi uyu tinamugwira akuchita chigololo. 5 Mʼmalamulo a Mose anatilamulira kuti akazi otere tiwagende ndi miyala. Tsopano Inu mukuti chiyani?” 6 Iwo anagwiritsa ntchito funsoli ngati msampha, ndi cholinga choti apeze chifukwa cha kumuneneza Iye.
Koma Yesu anawerama pansi ndi kuyamba kulemba pa dothi ndi chala chake. 7 Pamene iwo anapitirira kumufunsa, Iye anaweramuka ndipo anawawuza kuti, “Ngati wina wa inu alipo wopanda tchimo, ayambe iyeyo kumugenda ndi miyala mkaziyu.” 8 Iye anaweramanso pansi ndi kulemba pa dothi.
9 Iwo atamva izi anayamba kuchoka mmodzimmodzi, akuluakulu poyamba, mpaka Yesu anatsala yekha ndi mkaziyo atayimirira pomwepo. 10 Yesu anaweramuka ndipo anamufunsa iye kuti, “Akuluakulu aja ali kuti? Kodi palibe amene wakutsutsa?”
11 Iye anati, “Ambuye, palibe ndi mmodzi yemwe.”
“Inenso sindikukutsutsa iwe. Pita kuyambira tsopano usakachimwenso.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.