Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 103:1-13

Salimo la Davide.

103 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga;
    ndi zonse zamʼkati mwanga zitamande dzina lake loyera.
Tamanda Yehova, iwe moyo wanga,
    ndipo usayiwale zabwino zake zonse.
Amene amakhululuka machimo ako onse
    ndi kuchiritsa nthenda zako zonse,
amene awombola moyo wako ku dzenje
    ndi kukuveka chikondi ndi chifundo chake ngati chipewa chaufumu,
amene akwaniritsa zokhumba zako ndi zinthu zabwino,
    kotero kuti umakhala wamphamvu zatsopano ngati mphungu.

Yehova amachita chilungamo
    ndipo amaweruza molungama onse opsinjika.

Iye anadziwitsa Mose njira zake,
    ntchito zake kwa Aisraeli.
Yehova ndi wachifundo ndi wokoma mtima,
    wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka.
Iye sadzatsutsa nthawi zonse,
    kapena kusunga mkwiyo wake kwamuyaya;
10 satichitira molingana ndi machimo athu,
    kapena kutibwezera molingana ndi mphulupulu zathu.
11 Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi,
    koteronso chikondi chake nʼchachikulu kwa iwo amene amamuopa;
12 monga kummawa kutalikirana ndi kumadzulo,
    koteronso Iye watichotsera mphulupulu zathu kuti zikhale kutali nafe.
13 Monga bambo amachitira chifundo ana ake,
    choncho Yehova ali ndi chifundo ndi iwo amene amamuopa;

Masalimo 103:22

22 Tamandani Yehova, ntchito yake yonse
    kulikonse mu ulamuliro wake.

Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.

Ezekieli 16:44-52

44 “ ‘Taona, onse onena miyambi adzakuphera mwambi wakuti, ‘Make mbuu, mwana mbuu.’ 45 Ndiwedi mwana weniweni wamkazi wa mayi wako, amene amanyoza mwamuna wake ndi ana ake. Ndiwe mʼbale weniweni wa abale ako, amene amanyoza amuna awo ndi ana awo. Amayi ako anali Mhiti ndipo abambo ako anali Mwamori. 46 Mkulu wako anali Samariya, ndipo iye pamodzi ndi ana ake aakazi ankakhala cha kumpoto kwako. Mngʼono wako, Sodomu ankakhala cha kummwera kwako pamodzi ndi ana ake aakazi. 47 Iwe sunangotsatira kokha njira zawo zoyipa ndi kuchita zonyansa zawo, koma patangopita nthawi pangʼono machitidwe ako oyipa anaposa awo. 48 Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, ngakhale mʼbale wako Sodomu ndi ana ake aakazi sanachitepo zimene iwe ndi ana ako aakazi munachita.

49 “ ‘Tsono tchimo la mʼbale wako Sodomu linali ili: Iye ndi ana ake aakazi ankanyadira kuchuluka kwa chakudya ndi chuma chawo. Koma sanalabadireko kuthandiza osauka ndi aumphawi. 50 Anali odzitukumula ndipo ankachita zonyansa pamaso panga. Nʼchifukwa chake ndinawachotsa monga mmene waoneramu. 51 Samariya sanachite ngakhale theka la machimo amene unachita. Iwe wachita zinthu zonyansa zambiri kuposa iwo, motero kuti abale ako awiriwo amaoneka ngati olungama kuyerekeza ndi iye. 52 Tsono iwenso uyenera kuchita manyazi popeza waonetsa abale ako ngati osachimwa. Popeza kuti machimo ako ndi onyansa kwambiri kupambana awo, tsonotu iwowo akuoneka olungama kupambana iweyo. Choncho iwenso uchite manyazi ndi kunyozedwa popeza unaonetsa abale ako ngati olungama.

2 Petro 1:1-11

Ndine Simoni Petro, mtumiki ndi mtumwi wa Yesu Khristu.

Kwa anthu amene analandira chikhulupiriro cha mtengowapatali chomwe ifenso tinalandira chifukwa cha chilungamo cha Mulungu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.

Chisomo ndi mtendere zochuluka zikhale nanu pomudziwa Mulungu ndi Yesu Ambuye athu.

Kudziwa za Mayitanidwe ndi za Kusankhidwa Kwathu

Mulungu mwa mphamvu zake anatipatsa zonse zofunika kukhala moyo opembedza, potidziwitsa za Iyeyo amene anatiyitana ku ulemerero wake ndi ubwino wake. Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo, anatipatsa malonjezo opambana kwambiri ndi a mtengowapatali. Amenewa ndi malonjezo amene amakuthandizani kulandira nawo moyo wa Mulungu, titapulumuka ku chiwonongeko chimene chili mʼdziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoyipa.

Choncho, chitani khama kuwonjezera moyo wabwino pa chikhulupiriro chanu, ndipo pa moyo wabwino muwonjezerepo nzeru. Pa nzeru muwonjezerepo kudziretsa, pa kudziretsa muwonjezerepo chipiriro, ndipo pa chipiriro muwonjezerepo khalidwe lolemekeza Mulungu. Pa khalidwe lolemekeza Mulungu muwonjezerepo chifundo cha ubale, pa chifundo cha ubale muwonjezerepo chikondi. Ngati zonsezi zikhala mwa inu nʼkumachuluka, zidzakuthandizani kuti musakhale aulesi ndi osapindula ndi chidziwitso chanu cha Ambuye athu Yesu Khristu. Koma ngati wina alibe zimenezi, ndi wakhungu sangathe kuona patali, ndipo wayiwala kuti anayeretsedwa machimo ake akale.

10 Nʼchifukwa chake abale anga, funitsitsani kuti mayitanidwe ndi masankhidwe anu akhale otsimikizika. Pakuti ngati muchita zinthu izi, simudzagwa konse. 11 Mudzalandiridwa bwino kwambiri mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.