Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
6 Mpando wanu waufumu, Inu Mulungu, udzakhala ku nthawi za nthawi;
ndodo yaufumu yachilungamo idzakhala ndodo yaufumu ya ufumu wanu.
7 Inu mumakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa;
choncho Mulungu, Mulungu wanu, wakukhazikani pamwamba pa anzanu
pokudzozani ndi mafuta a chimwemwe.
8 Mikanjo yanu yonse ndi yonunkhira ndi mure ndi aloe ndi kasiya;
kuchokera ku nyumba zaufumu zokongoletsedwa ndi mnyanga wanjovu
nyimbo za zoyimbira zazingwe zimakusangalatsani.
9 Ana aakazi a mafumu ali pakati pa akazi anu olemekezeka;
ku dzanja lanu lamanja kuli mkwatibwi waufumu ali mu golide wa ku Ofiri.
10 Tamvera, iwe mwana wa mkazi ganizira ndipo tchera khutu;
iwala anthu ako ndi nyumba ya abambo ako.
11 Mfumu yathedwa nzeru chifukwa cha kukongola kwako;
mulemekeze pakuti iyeyo ndiye mbuye wako.
12 Mwana wa mkazi wa ku Turo adzabwera ndi mphatso,
amuna a chuma adzafunafuna kukoma mtima kwako.
13 Wokongola kwambiri ndi mwana wa mfumu ali mʼchipinda mwake,
chovala chake ndi cholukidwa ndi thonje ndi golide.
14 Atavala zovala zamaluwamaluwa akupita naye kwa mfumu;
anamwali okhala naye akumutsatira
ndipo abweretsedwa kwa inu.
15 Iwo akuwaperekeza ndi chimwemwe ndi chisangalalo;
akulowa mʼnyumba yaufumu.
16 Ana ako aamuna adzatenga malo a makolo ako;
udzachititsa kuti akhale ana a mfumu mʼdziko lonse.
17 Ndidzabukitsa mbiri yako mʼmibado yonse;
choncho mitundu yonse idzakutamanda ku nthawi za nthawi.
Dzina Latsopano la Ziyoni
62 Chifukwa chokonda Ziyoni sindidzakhala chete,
chifukwa chokonda Yerusalemu sindidzakhala chete,
mpaka chilungamo chake chitaoneka poyera ngati kuwala,
ndi chipulumutso chake chitaoneka ngati sakali yoyaka.
2 Mitundu ya anthu idzaona iwe utapambana pa nkhondo
ndipo mafumu onse adzaona ulemerero wako.
Adzakuyitanira dzina latsopano
limene adzakupatse ndi Yehova.
3 Udzakhala ngati chipewa chaulemerero mʼdzanja la Yehova,
ndi ngati nduwira yaufumu mʼdzanja la Mulungu wako.
4 Sadzakutchanso “Wosiyidwa,”
ndipo dziko lako silidzatchedwanso “Chipululu.”
Koma dzina lako latsopano lidzakhala “Ndakondwera naye.”
Ndipo dziko lako lidzatchedwa “Wokwatiwa.”
Chifukwa Yehova akukondwera nawe,
ndipo adzakhala ngati mwamuna wa dziko lako.
5 Monga mnyamata amakwatira namwali,
momwenso mmisiri wodzakumanga adzakukwatira;
monga mkwati amakondwera ndi mkwatibwi,
chonchonso Mulungu adzakondwera nawe.
Yohane Mʼbatizi Achita Umboni za Yesu
22 Zitatha izi, Yesu ndi ophunzira ake anapita mʼmadera a ku midzi ya ku Yudeya, kumene Iye anakhala kanthawi akubatiza. 23 Ndipo Yohane amabatizanso ku Ainoni kufupi ndi Salimu, chifukwa kumeneko kunali madzi ambiri ndipo anthu amabwererabwererabe kudzabatizidwa. 24 (Apa nʼkuti Yohane asanatsekeredwe mʼndende). 25 Mkangano unabuka pakati pa ophunzira ena a Yohane ndi Ayuda ena pa zamwambo wodziyeretsa wa Ayuda. 26 Iwo anabwera kwa Yohane anati, “Rabi, munthu uja munali naye mbali inayo ya mu mtsinje wa Yorodani, amene munamuchitira umboni, taonani naye akubatizanso, ndipo aliyense akupita kwa Iye.”
27 Atamva zimenezi, Yohane anayankha kuti, “Munthu amalandira chokhacho chapatsidwa kwa iye kuchokera kumwamba. 28 Inuyo ndinu mboni zanga kuti ine ndinati, ‘Ine sindine Khristu koma ndatumidwa patsogolo pa Iye.’ 29 Mwini wake wa mkwatibwi ndi mkwati. Ndipo bwenzi lamkwati limadikira ndi kumvetsera iye, ndipo amakondwa akamva mawu a mkwatiyo. Ine changa ndi chimwemwe ndipo ndine wosangalala kwambiri. 30 Nʼkoyenera kuti Iyeyo akule, ine ndichepe.
31 “Iye wochokera kumwamba ndi wapamwamba pa onse: iye wochokera mʼdziko lapansi ndi wa dziko lapansi, ndipo amayankhula monga mmodzi wa adziko lapansi. Iye wochokera kumwamba ndi wopambana onse. 32 Iye achita umboni pa zimene waziona ndi kuzimva, koma palibe avomereza umboni wake. 33 Munthu amene amawulandira akutsimikizira kuti Mulungu ndi woona. 34 Pakuti amene Mulungu wamutuma amayankhula mawu a Mulungu; Mulungu wamupatsa Mzimu Woyera mopanda malire. 35 Atate amakonda Mwana ndipo apereka zonse mʼmanja mwake. 36 Aliyense wokhulupirira Mwanayo ali ndi moyo wosatha, koma iye amene samvera Mwanayo sadzawuona moyo, pakuti mkwiyo wa Mulungu umakhala pa iye.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.