Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Nyimbo ya Mariya
46 Ndipo Mariya anati:
“Moyo wanga ulemekeza Ambuye.
47 Ndipo mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,
48 pakuti wakumbukira
kudzichepetsa kwa mtumiki wake.
Kuyambira tsopano mibado yonse idzanditcha wodala,
49 pakuti Wamkuluyo wandichitira ine zinthu zazikulu,
dzina lake ndi loyera.
50 Chifundo chake chifikira kwa iwo amene amuopa Iye
kufikira mibadomibado.
51 Iye wachita zamphamvu ndi dzanja lake;
Iye anabalalitsa iwo amene ali onyada mʼmaganizo awo.
52 Iye anachotsa olamulira pa mipando yawo yaufumu,
koma wakweza odzichepetsa.
53 Iye wakhutitsa a njala ndi zinthu zabwino
koma anachotsa olemera wopanda kanthu.
54 Iye anathandiza mtumiki wake Israeli,
pokumbukira chifundo chake.
55 Kwa Abrahamu ndi zidzukulu zake ku nthawi zonse
monga ananena kwa makolo athu.”
19 Elikana ndi banja lake anadzuka mmawa mwake nakapemphera pamaso pa Yehova. Pambuyo pake anabwerera kwawo ku Rama. Elikana anakhala pamodzi ndi mkazi wake, ndipo Yehova anamukumbuka Hanayo. 20 Motero Hana anakhala ndi pakati ndipo anabereka mwana wamwamuna. Anamutcha dzina lake Samueli, popeza anati, “Ndinachita kumupempha kwa Yehova.”
Hana Apereka Samueli kwa Yehova
21 Elikana ndi banja lake lonse anapita kukapereka nsembe ya pa chaka kwa Yehova ndi kukakwaniritsa malonjezo ake. 22 Koma Hana sanapite nawo popeza anawuza mwamuna wake kuti, “Mwanayu akadzaleka kuyamwa, ndidzapita naye ndi kukamupereka pamaso pa Yehova ndipo adzakhala kumeneko moyo wake wonse.”
23 Elikana mwamuna wake anamuwuza kuti, “Chita chimene chakukomera. Tsala kuno mpaka utamusiyitsa kuyamwa, Yehova yekha akwaniritse mawu ake.” Choncho mkaziyo anatsala ku nyumba ndi kusamalira mwana wake mpaka atamuletsa kuyamwa.
24 Atamuletsa kuyamwa, Hana anatenga mwanayo ali wachichepere, ndikupita naye ku nyumba ya Yehova ku Silo. Anatenga ngʼombe yamphongo ya zaka zitatu, ufa wa makilogalamu khumi, ndi thumba lachikopa la vinyo. 25 Tsono anapha ngʼombe yamphongo ija ndi kupereka mwana uja kwa Eli. 26 Ndipo Hana anati kwa Eli, “Mbuye wanga, ine ndikunenetsadi pamaso panu kuti ndine mkazi uja amene anayima pamaso panu ndi kumapemphera kwa Yehova. 27 Ndinapempha mwana uyu, ndipo Yehova wandipatsa chimene ndinamupempha. 28 Ndiye tsopano ine ndikumupereka kwa Yehova. Pa moyo wake wonse adzakhala wa Yehova.” Ndipo onse anapembedza Yehova kumeneko.
Mkulu wa Ansembe wa Pangano Latsopano
8 Fundo yayikulu pa zimene tikunenazi ndi iyi: Tili naye ife Mkulu wa ansembe, amene anakhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu Waulemerero kumwamba. 2 Ndipo akutumikira mʼmalo opatulika, mu Tenti yeniyeni yoyikidwa ndi Ambuye, osati ndi munthu.
3 Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa kuti azipereka mphatso ndi nsembe kwa Mulungu, ndipo kunali koyenera kuti wansembe wathunso akhale nʼkanthu kopereka. 4 Ngati iye akanakhala pa dziko lapansi, sakanakhala wansembe pakuti alipo kale anthu amene amapereka mphatso zolembedwa mʼMalamulo. 5 Iwo amatumikira pamalo opatulika amene ndi chithunzi ndi chifanizo cha zimene zili kumwamba. Ichi ndi chifukwa chake Mose anachenjezedwa pamene anali pafupi kumanga Tenti: “Uwonetsetse kuti wapanga zonse monga momwe ndikukuonetsera pa phiri pano.” 6 Koma Yesu analandira utumiki wopambana kuposa wawo monga Iyenso ali Nkhoswe ya pangano lopambana kuposa lakale lija, chifukwa pangano latsopano lakhazikika pa malonjezano opambana kwambiri.
7 Ngati pangano loyamba lija likanakhala langwiro, sipakanafunikanso lina mʼmalo mwake. 8 Koma Mulungu anapeza zolakwika pakati pa anthu ndipo anati,
“Masiku akubwera,” akutero Yehova,
“pamene ndidzachita pangano latsopano
ndi Aisraeli
ndiponso nyumba ya Yuda.
9 Silidzakhala ngati pangano
limene ndinachita ndi makolo awo,
pamene ndinawagwira padzanja
nʼkuwatulutsa ku Igupto
chifukwa iwo sanasunge pangano langa lija
ndipo Ine sindinawasamalire,
akutero Ambuye.
10 Tsono ili ndi pangano ndidzapangane ndi nyumba ya Israeli:
Atapita masiku amenewa, akutero Ambuye,
Ine ndidzayika malamulo anga mʼmaganizo mwawo,
ndi kulemba mʼmitima mwawo.
Ine ndidzakhala Mulungu wawo,
ndipo iwo adzakhala anthu anga.
11 Sipadzafunikanso wina kuti aphunzitse mnzake,
kapena munthu kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, udziwe Ambuye
chifukwa onse adzandidziwa,
kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu.
12 Pakuti Ine ndidzawakhululukira zoyipa zawo,
ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”
13 Ponena kuti, pangano “latsopano” Mulungu wapanga pangano loyamba lija kukhala lotha ntchito, ndipo chilichonse chimene chayamba kutha ntchito ndi kukalamba, chili pafupi kuchokeratu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.