Old/New Testament
Chiweruzo kwa Mafumu Oyipa
22 Yehova anandiwuza kuti, “Pita ku nyumba ya mfumu ya ku Yuda ndipo ukayiwuze kuti, 2 ‘Imva mawu a Yehova, iwe mfumu ya ku Yuda, amene umakhala pa mpando waufumu wa Davide; iwe, nduna zako pamodzi ndi anthu ako amene amalowera pa zipata izi. 3 Yehova akuti, uziweruza molungama ndi mosakondera. Uzipulumutsa munthu amene walandidwa katundu mʼdzanja la womuzunza. Usazunze kapena kupondereza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye. Usaphe munthu wosalakwa pa malo pano. 4 Pakuti ngati udzamvera malamulo awa, ndiye kuti mafumu onse okhala pa mpando waufumu wa Davide azidzalowabe pa zipata za nyumba yaufumu ino, atakwera magaleta ndi akavalo, iwowo pamodzi ndi nduna zawo ndi anthu awo. 5 Koma ngati sumvera malamulo awa, akutero Yehova, ndikulumbira pali Ine ndemwe kuti nyumba ino yaufumu idzasanduka bwinja.’ ”
6 Pakuti zimene Yehova akunena za nyumba yaufumu ya mfumu ya ku Yuda ndi izi:
“Ngakhale iwe uli ngati Giliyadi kwa Ine,
ngati msonga ya phiri la Lebanoni,
komabe ndidzakusandutsa chipululu,
ngati mizinda yopanda anthu.
7 Ndidzatuma anthu oti adzakuwononge,
munthu aliyense ali ndi zida zake,
ndipo adzadula mikungudza yako yokongola
nadzayiponya pa moto.
8 “Pamene anthu a mitundu ina adzadutsa pa mzinda umenewu adzafunsana kuti, ‘Chifukwa chiyani Yehova wachita chinthu chotere pa mzinda waukuluwu?’ 9 Ndipo yankho lake lidzakhala lakuti, ‘Chifukwa anasiya pangano limene anapangana ndi Yehova Mulungu wawo ndipo anapembedza ndi kutumikira milungu ina.’ ”
10 Musayilire mfumu Yosiya, musamuyimbire nyimbo womwalirayo;
mʼmalo mwake, mulire kwambiri chifukwa cha Yehowahazi amene wapita ku ukapolo,
chifukwa sadzabwereranso
kapena kuonanso dziko lake lobadwira.
11 Pakuti zimene Yehova akunena za Yehowahazi mwana wa Yosiya, amene anatenga mpando waufumu wa Yuda mʼmalo mwa abambo ake koma nʼkuwusiya ndi izi: “Iye sadzabwereranso. 12 Iyeyo adzafera ku ukapoloko. Sadzalionanso dziko lino.”
13 “Tsoka kwa munthu womanga nyumba yake mopanda chilungamo,
womanga zipinda zake zosanja monyenga,
pogwiritsa ntchito abale ake mwathangata,
osawapatsa malipiro a ntchito yawo.
14 Munthuyo amati, ‘Ndidzadzimangira nyumba yayikulu
ya zipinda zikuluzikulu zamʼmwamba.’
Kotero ndidzapanga mazenera akuluakulu,
ndi kukhomamo matabwa a mkungudza
ndi kukongoletsa ndi makaka ofiira.
15 “Kodi kukhala ndi nyumba ya mkungudza wambiri
zingachititse iwe kukhala mfumu?
Ganiza za abambo ako. Suja anali ndi zonse zakudya ndi zakumwa.
Abambo ako ankaweruza molungama ndi mosakondera,
ndipo zonse zinkawayendera bwino.
16 Iye ankateteza anthu osauka ndi osowa,
ndipo zonse zinkamuyendera bwino.
Kodi zimenezi sindiye tanthauzo la kudziwa Ine?”
akutero Yehova.
17 “Koma maso ako ndi mtima sizili penanso,
koma zili pa phindu lachinyengo,
pa zopha anthu osalakwa
ndi pa kuzunza ndi pakulamulira mwankhanza.”
18 Nʼchifukwa chake Yehova ponena za Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda akuti,
“Anthu sadzamulira maliro kapena kunena kuti,
‘Kalanga ine, mʼbale wanga! Kalanga ine mlongo wanga!
Anthu ake sadzamulira maliro kuti,
Kalanga ine, mbuye wathu! Taonani ulemerero wake wapita!’
19 Adzayikidwa ngati bulu,
kuchita kumuguguza ndi kukamutaya
kunja kwa zipata za Yerusalemu.”
20 “Tsono inu anthu a ku Yerusalemu, pitani ku mapiri a Lebanoni kuti mukalire mofuwula kumeneko,
mawu anu akamveke mpaka ku Basani.
Mulire mofuwula muli ku Abarimu
chifukwa abwenzi ako onse awonongeka.
21 Ndinakuchenjezani pamene munali pa mtendere.
Koma inu munati, ‘Sindidzamvera.’
Umu ndi mmene mwakhala mukuchitira kuyambira mukali aangʼono.
Simunandimvere Ine.
22 Mphepo idzakuchotserani abusa anu onse,
ndipo abwenzi anu adzatengedwa ku ukapolo.
Pamenepo mudzachita manyazi ndi kunyozedwa
chifukwa cha zoyipa zanu zonse.
23 Inu amene mumakhala mʼnyumba ya ku Lebanoni,
amene munamanga nyumba zanu pakati pa mikungudza,
mudzabuwula kwambiri pamene zowawa zidzakugwerani,
zonga za mkazi pa nthawi yake yochira!
24 “Pali Ine wamoyo, akutero Yehova, ngakhale iwe, Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, ukanakhala ngati mphete ya ku dzanja langa lamanja, ndikanakuvula nʼkukutaya. 25 Ndidzakupereka kwa amene akufuna kukupha, amene iwe umawaopa. Ndidzakupereka kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni ndi anthu ake. 26 Iwe pamodzi ndi amayi ako amene anakubereka ndidzakupititsani ku dziko lachilendo. Ngakhale inu simunabadwire kumeneko, komabe mudzafera komweko. 27 Simudzabwereranso ku dziko limene mudzafuna kubwerera.”
28 Kodi Yehoyakini wakhala ngati mbiya yonyozeka,
yosweka imene anthu sakuyifunanso?
Kodi nʼchifukwa chake iye pamodzi ndi ana ake,
achotsedwa nʼkutayidwa ku dziko limene iwo sakulidziwa?
29 Iwe dziko, dziko, dziko,
Imva mawu a Yehova!
30 Yehova akuti,
“Munthu ameneyu mumutenge ngati wopanda ana,
munthu amene sadzakhala wochita bwino pamoyo wake wonse,
pakuti palibe ndi mmodzi yemwe mwa zidzukulu zake zomwe zidzachita bwino.
Palibe amene adzathe kukhala pa mpando waufumu wa Davide
ndi kulamulira Yuda.”
Nthambi Yolungama
23 “Tsoka kwa abusa amene akuwononga ndi kubalalitsa nkhosa za pabusa panga!” akutero Yehova. 2 Nʼchifukwa chake Yehova, Mulungu wa Israeli, ponena za abusa amene akuweta anthu anga akuti, “Mwabalalitsa ndi kumwaza nkhosa zanga. Komanso simunazisamale bwino. Choncho ndidzakulangani chifukwa cha machimo anu,” akutero Yehova. 3 “Pambuyo pake Ine mwini wakene ndidzasonkhanitsa nkhosa zanga zotsala, kuzichotsa ku mayiko onse kumene ndinazibalalitsira ndi kuzibweretsanso ku msipu wawo. Kumeneko zidzaswana ndi kuchulukana. 4 Ndidzazipatsa abusa amene adzaziweta, ndipo sizidzaopanso kapena kuchita mantha, ndipo palibe imene idzasochera,” akutero Yehova.
5 Yehova akuti, “Masiku akubwera,
pamene ndidzaphukitsira Davide Nthambi yowongoka.
Imeneyi ndiye mfumu imene idzalamulira mwanzeru, mwachilungamo ndi mosakondera mʼdziko.
6 Pa masiku a ulamuliro wake Yuda adzapulumuka
ndipo Israeli adzakhala pamtendere.
Dzina limene adzamutcha ndi ili:
Yehova ndiye Chilungamo Chathu.
7 Choncho, masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene anthu sadzanenanso polumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli ku Igupto,’ 8 koma adzanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa zidzukulu za Israeli ku dziko lakumpoto ndi ku mayiko konse kumene anawabalalitsira.’ Ndipo iwo adzawabweretsa ku dziko lawolawo.”
Aneneri Onyenga
9 Kunena za aneneri awa:
Mtima wanga wasweka;
mʼnkhongono mwati zii.
Ndakhala ngati munthu woledzera,
ngati munthu amene wasokonezeka ndi vinyo,
chifukwa cha Yehova
ndi mawu ake opatulika.
10 Dziko ladzaza ndi anthu achigololo;
lili pansi pa matemberero.
Dziko lasanduka chipululu ndipo msipu wawuma.
Aneneri akuchita zoyipa
ndipo akugwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika.
11 “Mneneri ngakhale wansembe onse sapembedza Yehova.
Amachita zoyipa ngakhale mʼnyumba yanga,”
akutero Yehova.
12 “Nʼchifukwa chake njira zawo zidzakhala zoterera;
adzawapirikitsira ku mdima
ndipo adzagwera kumeneko.
Adzaona zosaona
mʼnthawi ya chilango chawo,”
akutero Yehova.
13 “Pakati pa aneneri a ku Samariya
ndinaona chonyansa ichi:
Ankanenera mʼdzina la Baala
ndipo anasocheretsa anthu anga, Aisraeli.
14 Ndipo pakati pa aneneri a ku Yerusalemu
ndaonapo chinthu choopsa kwambiri:
amachita chigololo, amanena bodza
ndipo amalimbitsa mtima anthu ochita zoyipa.
Choncho palibe amene amasiya zoyipa zake.
Kwa Ine anthu onsewa
ali ngati a ku Sodomu ndi Gomora.”
15 Choncho ponena za aneneriwa Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Ndidzawadyetsa zakudya zowawa
ndi kuwamwetsa madzi a ndulu,
chifukwa uchimo umene wafalikira mʼdziko lonse
ndi wochokera kwa aneneri a ku Yerusalemuwa.”
16 Koma Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Musamvere zimene aneneri amenewa akulosera kwa inu;
zomwe aloserazo nʼzachabechabe.
Iwo akungoyankhula za masomphenya a mʼmitima mwawo basi,
osati zochokera kwa Yehova.
17 Iwo amapita ndi kumakawuza amene amandinyoza Ine kuti,
‘zinthu zidzakuyenderani bwino.’
Kwa iwo amene amawumirira kutsata zofuna za mitima yawo amakawawuza kuti,
‘palibe choyipa chimene chidzakugwereni.’ ”
18 Ine ndikuti, “Koma ndani wa iwo amene anakhalapo mu msonkhano wa Yehova?
Ndani anaonapo kapena kumvapo mawu ake?
Ndani mwa iwo analabadirako za mawu ake ndi kuwamvera?
19 Taonani ukali wa Yehova
uli ngati chimphepo chamkuntho,
inde ngati namondwe.
Ndipo adzakantha mitu ya anthu oyipa.
20 Mkwiyo wa Yehova sudzaleka
mpaka atachita zonse zimene
anatsimikiza mu mtima mwake.
Mudzazizindikira bwino zimenezi
masiku akubwerawa.”
21 Yehova anati, “Ine sindinatume aneneri amenewa,
komabe iwo athamanga uku ndi uku kulalikira uthenga wawo;
Ine sindinawayankhule,
komabe iwo ananenera.
22 Iwo akanakhala pa msonkhano wanga
ndiye kuti akanamayankhula mawu anga kwa anthu anga.
Komanso bwenzi atawachotsa anthu anga mʼnjira zawo zoyipa
kuti aleke machimo awo.”
23 Yehova akuti, “Kodi ndimakhala Mulungu pokhapokha ndikakhala pafupi,
ndiye sindine Mulungu?
24 Kodi wina angathe kubisala
Ine osamuona?”
“Kodi Ine sindili ponseponse kumwamba ndi dziko lapansi?”
Akutero Yehova.
25 “Ndamva zimene aneneri akuyankhula. Iwo amalosera zabodza mʼdzina langa nʼkumati, ‘Ndalota! Ndalota!’ 26 Kodi zabodzazi zidzakhalabe mʼmitima ya aneneriwa mpaka liti? Iwotu amalosera zonyenga za mʼmitima yawo. 27 Aneneriwa amakhulupirira kuti anthu anga adzayiwala mawu anga akamamva za maloto awo amene amayankhulana ngati mmene anachitira makolo awo popembedza Baala. 28 Mneneri amene ali ndi maloto afotokoze malotowo. Koma iye amene ali ndi mawu anga alalikire mawuwo mokhulupirika. Kodi phesi lingafanane ndi chimanga? 29 Kodi suja mawu anga amatentha ngati moto? Suja mawu anga amaphwanya monga ichitira nyundo kuphwanya miyala?” Akutero Yehova.
30 Yehova akuti, “Nʼchifukwa chake, Ine ndikudana nawo aneneri amene amaberana okhaokha mawu nʼkumati mawuwo ndi a Yehova.” 31 Yehova akuti, “Inde, Ine ndikudana ndi aneneri amene amakonda kuyankhula zabodza nʼkumanena kuti, ‘Amenewa ndi mawu a Yehova.’ ” 32 Yehova akuti, “Ndithudi, Ine ndikudana ndi aneneri a maloto abodzawa. Iwo amafotokoza malotowo nʼkumasocheretsa anthu anga ndi bodza lawo losachita nalo manyazilo, chonsecho Ine sindinawatume kapena kuwalamula. Iwo sathandiza anthuwa ndi pangʼono pomwe,” akutero Yehova.
Uthenga Wabodza ndi Aneneri Abodza
33 Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Anthu awa, kapena mneneri, kapenanso wansembe, akakufunsa kuti, ‘Kodi uthenga wolemetsa wa Yehova ukuti chiyani?’ uwawuze kuti, ‘Inuyo ndinu katundu wolemetsa Yehova, ndipo adzakutayani.’ 34 Ngati mneneri kapena wansembe kapenanso munthu wina aliyense anena kuti, ‘Uthenga wolemetsa wa Yehova ndi uwu,’ Ine ndidzalanga munthu ameneyo pamodzi ndi banja lake. 35 Koma chimene aliyense wa inu azifunsa kwa mnzake kapena mʼbale wake ndi ichi: ‘Kodi Yehova wayankha chiyani?’ kapena ‘Yehova wayankhula chiyani?’ 36 Koma musanenenso kuti ‘nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ chifukwa mawu a munthu aliyense ndiwo uthenga wa iye mwini, kotero kuti inu mumakhotetsa mawu a Mulungu wamoyo, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wathu. 37 Tsono iwe Yeremiya udzamufunse mneneri kuti, ‘Kodi Yehova wakuyankha chiyani?’ kapena, ‘Kodi Yehova wayankhula chiyani?’ 38 Ngati mudzanena kuti, ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ ndiye tsono Yehova akuti, ‘Popeza mwagwiritsa ntchito mawu akuti: Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova, mawu amene ndinakuletsani kuti musawatchule, 39 ndiye kuti Ine ndidzakunyamulani ngati katundu nʼkukuponyani kutali. Ndidzakuchotsani pamaso panga, inuyo pamodzi ndi mzinda umene ndinakupatsani inu ndi makolo anu. 40 Ndidzakunyozani mpaka muyaya. Ndidzakuchititsani manyazi osayiwalika.’ ”
1 Ndine Paulo, mtumiki wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Ndinatumidwa kuti nditsogolere amene Mulungu anawasankha ku chikhulupiriro ndi ku chidziwitso cha choonadi chimene chimawafikitsa ku moyo wolemekeza Mulungu 2 ndi kuwapatsa chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu amene sanama, analonjeza nthawi isanayambe. 3 Pa nthawi yake Mulungu, Mpulumutsi wathu anawulula poyera mawu ake ndipo analamula kuti ndipatsidwe udindo wolalikira uthengawu.
4 Kwa Tito, mwana wanga weniweni mʼchikhulupiriro cha ife tonse:
Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu.
Ntchito ya Tito ku Krete
5 Ndinakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene ndinazisiya zisanathe ndiponso usankhe akulu ampingo mʼmizinda yonse, monga momwe ndinakulamulira. 6 Mkulu wampingo akhale munthu wopanda cholakwa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, munthu amene ana ake ndi okhulupirira, osati amakhalidwe oyipa ndi osamvera. 7 Popeza mkulu wa mpingo amayendetsa ntchito za banja la Mulungu, ayenera kukhala wopanda cholakwa, asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena womwa zoledzeretsa, kapena wandewu, kapena wopeza phindu mwachinyengo. 8 Koma akhale wosamala bwino alendo, wokonda zabwino, wodziretsa, wolungama, woyera mtima ndi wosunga mwambo. 9 Iye ayenera kugwiritsa mawu okhulupirika monga tinaphunzitsira, kuti athe kulimbikitsa ena ndi chiphunzitso choona ndiponso kugonjetsa amene atsutsana nacho.
Kudzudzula Olephera Kuchita Bwino
10 Paja pali anthu ambiri osaweruzika, makamaka mʼgulu la anthu a mdulidwe, oyankhula nkhani zopanda pake ndi kusocheretsa anzawo. 11 Ayenera kuletsedwa kuyankhula chifukwa akusokoneza mabanja athunthu pophunzitsa zinthu zomwe sayenera kuwaphunzitsa. Iwo amachita izi kuti apeze ndalama mwachinyengo. 12 Mneneri wina, mmodzi wa iwo omwewo anati, “Akrete nthawi zonse ndi amabodza, akhalidwe loyipitsitsa ndiponso alesi adyera.” 13 Mawu amenewa ndi woona. Nʼchifukwa chake, uwadzudzule mwamphamvu, kuti akhale ndi chikhulupiriro choona, 14 kuti asasamalenso nthano za Chiyuda, ndi malamulo a anthu amene akukana choonadi. 15 Kwa oyera mtima, zinthu zonse ndi zoyera, koma kwa amene ndi odetsedwa ndi osakhulupirira, palibe kanthu koyera. Kunena zoona, mitima yawo ndi chikumbumtima chawo, zonse nʼzodetsedwa. 16 Iwo amati amadziwa Mulungu, pamene ndi zochita zawo amamukana. Ndi anthu onyansa ndi osamvera, ndi osayenera kuchita kalikonse kabwino.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.