Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yeremiya 12-14

Madandawulo a Yeremiya

12 Yehova, Inu mumakhala wokhoza nthawi zonse
    ndikati nditsutsane nanu.
Komabe ndikufuna kuyankhula nanu za mlandu wanga.
    Chifukwa chiyani anthu oyipa zinthu zimawayendera bwino?
    Chifukwa chiyani anthu achinyengo amakhala pabwino?
Inu munawadzala ndipo anamera mizu;
    amakula ndi kubereka zipatso.
Dzina lanu limakhala pakamwa pawo nthawi zonse,
    koma mitima yawo imakhala kutali ndi Inu.
Koma Inu Yehova, ine mumandidziwa;
    mumandiona ndipo mumayesa zolingalira zanga.
Akokeni anthu oyipawo ngati nkhosa zokaphedwa!
    Ayikeni padera mpaka tsiku loti akaphedwe!
Kodi dziko lidzakhala likulirabe mpaka liti
    ndipo udzu mʼmunda uliwonse udzakhalabe ofota mpaka liti?
Nyama ndi mbalame kulibiretu
    chifukwa anthu amene amakhalamo ndi oyipa.
Iwo amati:
    “Yehova sangathe kuona ntchito zathu.”

Yankho la Mulungu

Yehova anayankha kuti, “Ngati kukutopetsa kuthamanga pamodzi ndi anthu
    nanga ungapikisane bwanji ndi akavalo?
    Ngati ukupunthwa ndi kugwa pa malo abwino,
udzatha bwanji kuthamanga mʼnkhalango
    za ku Yorodani?
Ngakhale abale ako
    ndi anansi akuwukira,
    onsewo amvana zokuyimba mlandu.
Usawakhulupirire,
    ngakhale ayankhule zabwino ndi iwe.

“Ine ndawasiya anthu anga;
    anthu amene ndinawasankha ndawataya.
Ndapereka okondedwa anga
    mʼmanja mwa adani awo.
Anthu amene ndinawasankha
    asanduka ngati mkango wa mʼnkhalango.
Akundibangulira mwaukali;
    nʼchifukwa chake Ine ndikudana nawo.
Anthu anga amene ndinawasankha
    asanduka ngati mbalame yolusa yamawangamawanga
    imene akabawi ayizinga.
Pitani, kasonkhanitseni nyama zakuthengo.
    Mubwere nazo kuti zidzadye mbalameyo.
10 Abusa ambiri anawononga munda wanga wa mpesa,
    anapondereza munda wanga;
munda wanga wabwino uja
    anawusandutsa chipululu.
11 Unawusandutsadi chipululu.
    Ukanali wokhawokha chomwecho ukundilirira Ine.
Dziko lonse lasanduka chipululu
    chifukwa palibe wolisamalira.
12 Anthu onse owononga abalalikira
    ku zitunda zonse za mʼchipululu.
Yehova watuma ankhondo ake
    kudzawatha kuyambira kumalire ena a dziko mpaka ku malire enanso a dziko,
    ndipo palibe amene adzakhale pa mtendere.
13 Anthu anafesa tirigu koma anatuta minga;
    anadzitopetsa kugwira ntchito koma osapeza phindu lililonse.
Choncho mudzachita manyazi ndi zokolola zanu
    chifukwa cha mkwiyo wa Yehova.”

14 “Anthu oyipa oyandikana ndi anthu anga Aisraeli, akuwalanda Aisraeliwo dziko, cholowa chimene ndinawapatsa. Nʼchifukwa chake ndidzawachotsa mʼdziko limenelo, ndipo ndidzachotsa banja la Yuda pakati pawo. 15 Komabe nditawachotsa, ndidzawachitiranso chifundo, ndipo ndidzabwezera aliyense cholowa chake ndi dziko lake. 16 Ndipo ngati iwo adzaphunzira bwino njira za anthu anga ndi kulumbira mʼdzina langa, namanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo,’ monga iwo anaphunzitsira anthu anga kulumbira mʼdzina la Baala, Ine ndidzawakhazikitsa pakati pa anthu anga. 17 Koma ngati mtundu wina uliwonse sudzamvera, Ine ndidzawuchotsa ndi kuwuwonongeratu,” akutero Yehova.

Lamba Womanga Mʼchiwuno

13 Yehova anandiwuza kuti, “Pita kagule lamba wansalu yosalala ndipo ukavale mʼchiwuno mwako, koma usakamuviyike mʼmadzi.” Choncho ndinakagula lambayo, monga momwe anandiwuzira Yehova, ndipo ndinamanga mʼchiwuno mwanga.

Kenaka Yehova anandiyankhulanso kachiwiri kuti, “Tenga lamba amene unagula ndi kuvala mʼchiwuno mwako uja. Tsono pita ku mtsinje wa Yufurate ndipo ukamubise lambayo mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe.” Ndipo ndinapitadi ndi kukabisa lambayo ku Yufurate, monga anenera Yehova.

Patapita masiku ambiri Yehova anandiwuzanso kuti, “Pitanso ku Yufurate ndipo ukatenge lamba amene ndinakuwuza kuti ukamubise kumeneko.” Choncho ndinapita ku Yufurate kukafukula lambayo ndi kumuchotsa pamalo pamene ndinamubisa, koma nthawi imeneyi nʼkuti lambayo atawonongeka kotheratu ndipo analibenso ntchito.

Pamenepo Yehova anandiwuza kuti, “Izi ndi zimene ine ndikunena: ‘Umu ndi mmene ndidzawonongere zimene akunyadira kwambiri a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. 10 Anthuwa ndi oyipa. Iwo akana kumvera mawu anga. Mʼmalo mwake amawumirira kutsata milungu ina, kuyitumikira ndi kuyipembedza. Anthu amenewa adzakhala ngati lamba wopanda ntchitoyu. 11 Monga momwe lamba amakanirira mʼchiwuno cha munthu, momwemonso ndinakonza kuti nyumba yonse ya Israeli ndi nyumba yonse ya Yuda indikangamire Ine kuti akhale anthu anga, kuti azitamanda dzina langa ndi kulemekeza Ine. Koma iwo sanamvere,’ akutero Yehova.

Zikopa Zothiramo Vinyo

12 “Awuze anthuwo kuti, ‘Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Mtsuko uliwonse adzawudzaza ndi vinyo.’ Ndipo ngati iwo anena kwa iwe kuti, ‘Kodi ngati ife sitikudziwa kuti mtsuko uliwonse udzadzazidwa ndi vinyo?’ 13 Tsono iwe uwawuze kuti, Yehova akuti ‘Ine ndidzaledzeretsa anthu onse okhala mʼdziko muno, kuyambira mafumu amene amakhala pa mpando waufumu wa Davide, ansembe, aneneri, pamodzi ndi anthu onse amene akukhala mu Yerusalemu. 14 Ndidzawagundanitsa mitu kuti aphwanyane okhaokha ngati mitsuko, makolo ndi ana awo, akutero Yehova. Sindidzawamvera chisoni kapena kuwachitira chifundo kapena kukhudzidwa nawo kuti ndileke kuwawononga.’ ”

Yuda Adzapita ku Ukapolo

15 Imvani inu Aisraeli ndipo tcherani khutu,
    musadzitukumule,
    pakuti ndi Yehova amene akuyankhula.
16 Lemekezani Yehova Mulungu wanu
    asanagwetse mdima,
mapazi anu asanayambe kupunthwa
    mʼchisisira chamʼmapiri.
Asanasandutse kuwala
    mukuyembekezerako kukhala
    mdima wandiweyani.
17 Koma ngati simumvera,
    ndidzalira kwambiri
    chifukwa cha kunyada kwanu.
Mʼmaso mwanga
    mwadzaza ndi misozi yowawa
    chifukwa nkhosa za Yehova zatengedwa ukapolo.

18 Uza mfumu pamodzi ndi amayi ake kuti,
    “Tsikani pa mipando yaufumuyo,
pakuti zipewa zanu zaufumu zokongolazo
    zagwa pansi.”
19 Mizinda ya ku Negevi yatsekedwa
    ndipo palibe wina woti nʼkuyitsekula.
Yuda yense watengedwa kupita ku ukapolo,
    watengedwa yense ukapolo.

20 Tukula maso ako kuti uwone
    amene akubwera kuchokera kumpoto.
Kodi nkhosa zimene anakusungitsa zili kuti,
    nkhosa zanu zokongola zija?
21 Kodi udzanena chiyani pamene [Yehova] adzakuyikira
    anthu amene unkanena kuti ndi abale ako akukugonjetsa ndi kukulamulira?
Kodi sudzamva zowawa
    ngati za mayi pa nthawi yake yochira?
22 Ndipo ngati udzadzifunsa kuti,
    “Kodi zimenezi zandichitikira chifukwa chiyani?”
Ndi chifukwa cha machimo anu ambiri
    kuti zovala zanu zingʼambike
    ndiponso kuti akuchitireni nkhanza.
23 Kodi wa dziko la Kusi nʼkusintha khungu lake,
    kapena kambuku kusintha mawanga ake?
Inunso amene munazolowera kuchita
    zoyipa simungathe kusintha.

24 “Ine ndidzakumwazani ngati mankhusu
    amene amawuluka ndi mphepo ya ku chipululu.
25 Limeneli ndiye gawo lanu,
    chilango chimene ndakukonzerani
chifukwa chondiyiwala Ine
    ndi kutumikira milungu yabodza,
            akutero Yehova.
26 Ine ndidzakwinya zovala zanu mpaka ku maso
    kuti umaliseche wanu uwonekere.
27 Ndaona zonyansa zanu: zigololo zanu, kutchetcherera kwanu
    ndi ziwerewere zanu,
zochitika pa mapiri ndi mʼminda.
    Tsoka iwe Yerusalemu!
Udzakhala wosayeretsedwa
    pa zachipembedzo mpaka liti?”

Chilala, Njala, Lupanga

14 Awa ndi mawu amene Yehova anamuwuza Yeremiya onena za chilala:

“Yuda akulira,
    mizinda yake ikuvutika;
anthu ake adzigwetsa pansi mwachisoni,
    kulira kwa Yerusalemu kwakula.
Anthu awo wolemekezeka akutuma antchito awo kuti akatunge madzi.
    Apita ku zitsime
    osapezako madzi.
Choncho amabwerera ndi mitsuko yopanda madzi.
    Amanyazi ndi othedwa nzeru
    adziphimba kumaso.
Popeza pansi pawumiratu
    chifukwa kulibe madzi,
alimi ali ndi manyazi
    ndipo amphimba nkhope zawo.
Ngakhale mbawala yayikazi
    ikusiya mwana wake wakhanda ku thengo
    chifukwa kulibe msipu.
Mbidzi zikuyima pa zitunda zopanda kanthu
    nʼkumapuma wefuwefu ngati nkhandwe;
maso awo achita chidima
    chifukwa chosowa msipu.”

Anthu akuti, “Ngakhale machimo athu akutitsutsa,
    koma Inu Yehova chitanipo kanthu chifukwa cha dzina lanu.
Pakuti kusakhulupirika kwathu nʼkwakukulu;
    ife takuchimwirani.
Inu Yehova amene Aisraeli amakukhulupirirani
    ndi amene mumawapulumutsa pa nthawi ya masautso,
chifukwa chiyani mukukhala ngati mlendo mʼdziko muno?
    Chifukwa chiyani muli ngati wapaulendo amene akungogona tsiku limodzi?
Chifukwa chiyani muli ngati munthu amene wadzidzimutsidwa,
    kapena ngati wankhondo amene alibe mphamvu yopulumutsa?
Komabe Inu Yehova, muli pakati pathu,
    ndipo tikudziwika ndi dzina lanu;
    musatitaye ife!”

10 Zimene Yehova akunena za anthuwa ndi izi:

“Iwo amakonda kuyendayenda kwambiri;
    samatha kudziretsa.
Nʼchifukwa chake Ine Yehova sindingawalandire,
    ndipo tsopano ndidzakumbukira zoyipa zawo
    ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo.”

11 Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Usawapempherere anthu awa kuti zinthu ziwayendere bwino. 12 Ngakhale asale zakudya, Ine sindidzamva kulira kwawo; ngakhale apereke nsembe zopsereza ndi chopereka cha chakudya, sindidzazilandira. Mʼmalo mwake, ndidzawapha ndi lupanga, njala ndi mliri.”

13 Koma ine ndinati, “Aa, Ambuye Yehova, aneneri amawawuza anthuwo kuti, sadzaphedwa ndi lupanga kapena kuvutika ndi njala. Koma kuti Inu mudzawapatsa mtendere wokhawokha pamalo pano.”

14 Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Ndi zabodza kuti aneneriwa akunenera mʼdzina langa. Ine sindinawatume kapena kuwasankha kapenanso kuyankhula nawo. Iwo amakuwuzani zinthu zabodza zomwe amati anaziona mʼmasomphenya, kapena pogwiritsa ntchito mawula achabechabe. Zimene amayankhula ndi zongopeka mʼmutu mwawo. 15 Nʼchifukwa chake Ine Yehova ndikuti aneneri amenewa akulosera mʼdzina langa pamene Ine sindinawatume. Iwo amati simudzafa pa nkhondo kapena ndi njala mʼdziko muno. Koma tsono ndi iwowo, aneneriwa amene adzafe pa nkhondo kapena ndi njala. 16 Ndipo anthu amene anawaloserawo adzaponyedwa mʼmisewu ya mu Yerusalemu atafa ndi njala ndi lupanga. Sipadzapezeka wowayika mʼmanda popeza iwowo, akazi awo, ana awo aamuna, onse adzakhala atafa. Ine ndidzawagwetsera chilango chowayenera.

17 “Awuze mawu awa:

“ ‘Maso anga akugwetsa misozi kosalekeza
    usana ndi usiku;
chifukwa anthu anga okondedwa
    apwetekeka kwambiri,
    akanthidwa kwambiri.
18 Ndikapita kuthengo,
    ndikuona amene aphedwa ndi lupanga;
ndikapita mu mzinda,
    ndikuona amene asakazidwa ndi njala.
Ngakhale aneneri pamodzi
    ndi ansembe onse atengedwa.’ ”

19 Kodi anthu a ku Yuda mwawakana kwathunthu?
    Kodi mtima wanu wanyansidwa nawo anthu a ku Ziyoni?
Chifukwa chiyani mwatikantha chotere
    kuti sitingathenso kuchira?
Ife tinayembekezera mtendere
    koma palibe chabwino chomwe chabwera,
tinayembekezera kuchira
    koma panali kuopsezedwa kokhakokha.
20 Inu Yehova, ife tikuvomereza kuyipa kwathu
    ndiponso kulakwa kwa makolo athu;
    ndithu ife tinakuchimwiranidi.
21 Musatikane kuopa kuti dzina lanu linganyozedwe;
    musanyoze mpando wanu waufumu waulemerero.
Kumbukirani pangano lanu ndi ife
    ndipo musachiphwanye.
22 Mwa milungu yachabechabe ya anthu a mitundu ina,
    kodi pali mulungu amene angagwetse mvula?
Ife chikhulupiriro chathu chili pa Inu,
    popeza Inu nokha ndinu Yehova Mulungu wathu
    amene mukhoza kuchita zimenezi.

2 Timoteyo 1

Paulo mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu. Anandituma kuti ndilalike za lonjezo la moyo umene uli mwa Khristu Yesu.

Kwa Timoteyo, mwana wanga wokondedwa:

Chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye athu Yesu Khristu.

Chilimbikitso Pokhala Wokhulupirika

Ndikuyamika Mulungu amene ndimamutumikira ndi chikumbumtima chosatsutsika, monga momwe ankachitira makolo anga. Usiku ndi usana ndimakukumbukira mosalekeza mʼmapemphero anga. Ndikamakumbukira misozi yako, ndimalakalaka nditakuona kuti ndidzazidwe ndi chimwemwe. Ndakumbukira za chikhulupiriro chako choona chimene chinayamba mwa agogo ako a Loisi ndi mwa amayi ako Yunike ndipo ndikutsimikiza mtima kuti chilinso mwa iwe.

Kumvera Paulo ndi Uthenga Wabwino

Nʼchifukwa chake ndikukukumbutsa kuti upemerere monga amachitira moto, mphatso imene Mulungu anakupatsa nditakusanjika manja. Pakuti Mzimu amene Mulungu anatipatsa, si Mzimu wotipatsa manyazi, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzisunga.

Choncho usachite manyazi kuchitira umboni Ambuye athu, kapena kuchita manyazi chifukwa cha ine wamʼndende. Koma umve nane zowawa chifukwa cha Uthenga Wabwino, mothandizidwa ndi mphamvu za Mulungu. Iye anatipulumutsa ndipo anatiyitanira ku moyo oyera mtima, osati chifukwa cha chilichonse chimene tinachita, koma chifukwa cha chikonzero ndi chisomo chake. Chisomo chimenechi anatipatsa ife mwa Khristu Yesu nthawi isanayambe. 10 Koma tsopano Mulungu watiwululira kudzera mʼkuoneka kwa Mpulumutsi wathu, Khristu Yesu, amene anathetsa mphamvu za imfa ndipo mwa Uthenga Wabwino anaonetsa poyera moyo umene sungafe. 11 Ine ndinasankhidwa kukhala wamthenga, ndi mtumwi ndi mphunzitsi wa Uthenga Wabwinowu. 12 Nʼchifukwa chake ndikuvutika monga ndililimu. Komabe zimenezi sizikundichititsa manyazi, popeza ndikumudziwa amene ndamukhulupirira ndipo ndikutsimikiza mtima kuti akhoza kusamalira chimene ndinamusungitsa mpaka tsiku lijalo.

13 Zimene unamva kwa ine, uzisunge kuti zikhale chitsanzo cha chiphunzitso choona, mwa chikhulupiriro ndi chikondi mwa Khristu Yesu. 14 Samalira bwino zokoma zimene anakusungitsa. Uzisamalire mothandizidwa ndi Mzimu Woyera amene amakhala mwa ife.

Zitsanzo za Kusakhulupirika ndi Kukhulupirika

15 Iwe udziwa kuti onse a mʼchigawo cha Asiya anandithawa, kuphatikizapo Fugelo ndi Herimogene omwe.

16 Mulungu achitire chifundo banja lonse la Onesiforo chifukwa ankandisangalatsa kawirikawiri ndipo sankachita nane manyazi ngakhale ndinali womangidwa ndi maunyolo. 17 Mʼmalo mwake, atangofika ku Roma, anandifunafuna ndipo anandipeza. 18 Ambuye amulole kuti adzalandire chifundo kwa Ambuye pa tsiku lijalo! Ukudziwa bwino momwe iye anandithandizira mʼnjira zosiyanasiyana ku Efeso.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.