Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yeremiya 9-11

Aa, ndikanakonda kuti mutu wanga ukanakhala chitsime cha madzi,
    ndi maso anga ngati kasupe wa misozi!
Ndikanalira usana ndi usiku
    kulirira anthu anga amene aphedwa.
Ndani adzandipatsa malo
    ogona mʼchipululu
kuti ndiwasiye anthu anga
    ndi kuwachokera kupita kutali;
pakuti onse ndi achigololo,
    ndiponso gulu la anthu onyenga.

“Amapinda lilime lawo ngati uta.
    Mʼdzikomo mwadzaza
ndi mabodza okhaokha
    osati zoonadi.
Amapitirirabe kuchita zoyipa;
    ndipo sandidziwa Ine.”
            Akutero Yehova.
“Aliyense achenjere ndi abwenzi ake;
    asadalire ngakhale abale ake.
Aliyense amafuna kumudyera mʼbale wake masuku pa mutu.
    Choncho aliyense amachitira bwenzi lake ugogodi.
Aliyense amamunamiza mʼbale wake
    ndipo palibe amene amayankhula choonadi.
Anapazoloweza pakamwa pawo kunena zabodza;
    amalimbika kuchita machimo.
Iwe wakhalira mʼchinyengo
    ndipo ukukana kundidziwa Ine,”
            akutero Yehova.

Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Taonani, Ine ndidzawasungunula ngati chitsulo ndi kuwayesa.
    Kodi ndingachite nawonso
    bwanji chifukwa cha machimo awo?
Lilime lawo lili ngati muvi wakuthwa;
    limayankhula zachinyengo.
Aliyense ndi pakamwa pake amayankhula mawu achikondi kwa mnansi wake,
    koma mu mtima mwake amakonzekera zomuchita chiwembu.
Kodi ndilekerenji kuwalanga chifukwa cha zimenezi?
    akutero Yehova.
‘Kodi ndisawulipsire
    mtundu wotere wa anthu?’ ”

10 Ndidzakhetsa misozi ndi kulira kwamphamvu chifukwa cha mapiri
    ndipo ndidzadandaula chifukwa cha msipu wa ku chipululu.
Malo onsewo awonongeka ndipo palibe amene amapitako,
    ndipo sikumveka kulira kwa ngʼombe.
Mbalame zamlengalenga zathawa
    ndipo nyama zakuthengo zachokako.

11 Ndipo Yehova anati, “Ndidzasandutsa Yerusalemu kukhala bwinja,
    malo okhalamo ankhandwe;
ndipo ndidzawononga mizinda ya Yuda
    kotero kuti palibe munthu amene adzakhalemo.”

12 Ine ndinati, “Kodi munthu wanzeru ndani woti nʼkumvetsa zimenezi? Kodi ndani amene Yehova anayankhula naye zimenezi kuti akafotokozere ena? Nʼchifukwa chiyani dziko lawonongeka ndi kusanduka chipululu, mʼmene anthu sadutsamo?”

13 Yehova anati, “Nʼchifukwa chakuti anthuwa analeka kutsata malamulo anga amene ndinawapatsa; sanandimvere kapena kuwasamala. 14 Mʼmalo mwake, anatsatira zolakwa za mʼmitima yawo; anapembedza Abaala ngati momwe makolo awo anawaphunzitsira.” 15 Tsono chimene Ine Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli ndidzachite ndi anthu amenewa ndi ichi: “Ndidzawadyetsa chakudya cha ziphe ndi kuwamwetsa madzi a ndulu. 16 Ndidzawabalalitsa pakati pa mitundu ya anthu imene iwowo kapena makolo awo sanayidziwe, ndipo ndidzawalondola ndi ankhondo mpaka nditawawononga.”

17 Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Tsopano ganizirani! Muyitane akazi olira mwachisoni kuti abwere;
    itanani akazi odziwa kulira bwino.”
18 Anthu akuti, “Abwere mofulumira
    kuti adzatilire
mpaka mʼmaso mwathu mutatuluka misozi
    ndi kuti msidze zathu zinyowe ndi madzi.
19 Kulira mwachisoni kukumveka kuchokera mu Ziyoni akuti,
    ‘Aa! Ife tawonongeka!
    Tachita manyazi kwambiri!
Tiyenera kuchoka mʼdziko lathu
    chifukwa atipirikitsa mʼnyumba zathu.’ ”

20 Tsono inu amayi, imvani mawu a Yehova;
    tcherani makutu anu kuti mumve mawu a Yehova.
Phunzitsani ana anu aakazi kulira mwachisoni;
    aliyense aphunzitse mnzake nyimbo ya maliro.
21 Imfa yatifikira kudzera mʼmazenera athu
    ndipo yalowa mʼnyumba zathu zotetezedwa;
yapha ana athu mʼmisewu,
    ndi achinyamata athu mʼmabwalo.

22 Yehova anandiwuza kuti ndinene izi kuti,

“ ‘Mitembo ya anthu
    idzakhala ili lambalamba ngati ndowe mʼminda,
ngati mapesi mʼmbuyo mwa wokolola,
    popanda munthu woyitola.’ ”

23 Yehova akuti,

“Munthu wanzeru asanyadire nzeru zake,
    kapena munthu wamphamvu kunyadira nyonga zake,
    kapena munthu wolemera kunyadira chuma chake,
24 koma ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire chinthu ichi:
    kuti iye amamvetsa za Ine ndipo amandidziwa,
kuti ndine Yehova, amene ndimakonda chifundo,
    chilungamo ndiponso ungwiro pa dziko lapansi.
    Zimenezi ndizo ndimakondwera nazo,”
            akutero Yehova.

25 “Nthawi ikubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzalanga onse amene anachita mdulidwe koma mu mtima sasamala nʼkomwe. 26 Ndidzalanga anthu a ku Igupto, Yuda, Edomu, Amoni, Mowabu, ndiponso onse amene amakhala kutali ku chipululu. Mitundu ina yonseyi ndi yosachita mdulidwe, ngakhalenso Aisraeli nawonso sanachite mdulidwe wa mu mtima.”

Mulungu ndi Mafano

10 Inu Aisraeli, imvani zimene Yehova akunena. Yehova akuti,

“Musatsatire makhalidwe a anthu a mitundu ina
    kapena kuchita mantha ndi zizindikiro zamlengalenga,
    ngakhale anthu a mitundu ina amachita nazo mantha.
Pakuti miyambo ya mitundu inayo ndiyachabechabe.
    Iwo amakadula mtengo ku nkhalango
    ndipo mmisiri amawusema ndi sompho.
Amakongoletsa chosemacho ndi siliva ndi golide;
    kenaka amachikhomerera ndi misomali
    kuti chisagwedezeke.
Mafano awo ali ngati mtengo wakanjedza woopsezera mbalame mʼmunda wa minkhaka.
    Mafanowo sangathe nʼkuyankhula komwe
ndipo ayenera kunyamulidwa
    popeza sangathe nʼkuyenda komwe.
Musachite nawo mantha
    popeza sangathe kukuchitani choyipa
    ndiponso alibe mphamvu yochitira chabwino chilichonse.”

Palibe wofanana nanu, Inu Yehova;
    Inu ndinu wamkulu,
    ndipo dzina lanu lili ndi mphamvu yayikulu.
Ndani amene angaleke kukuopani,
    inu Mfumu ya mitundu ya anthu?
    Chimenechi ndicho chokuyenerani.
Pakati pa anthu anzeru onse komanso mafumu onse
    a mitundu ya anthu,
    palibe wina wofanana nanu.
Onsewo ndi opusa ndi opanda nzeru;
    malangizo awo amawatenga kuchokera kwa mafano achabechabe opanga ndi mitengo.
Siliva wosula amabwera naye kuchokera ku Tarisisi
    ndipo golide amachokera naye ku Ufazi.
Mafanowo ndi ntchito ya anthu aluso ndi odziwa kuzokota golide.
    Tsono mafanowo amawaveka zovala za mtundu wamtambo ndi pepo.
    Yonseyo ndi ntchito ya anthu a luso.
10 Koma Yehova ndiye Mulungu woona;
    Iyeyo ndiye Mulungu wamoyo, Mfumu yamuyaya.
Akakwiya, dziko limagwedezeka;
    anthu a mitundu ina sangathe kupirira ukali wakewo.

11 “Awuze anthu awa kuti, ‘Milungu iyi, imene sinalenge dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, idzawonongeka pa dziko lapansi ndi pansi pa thambo.’ ”

12 Koma Mulungu analenga dziko lapansi ndi mphamvu zake;
    Iye anapanga dziko lonse ndi nzeru zake
    ndipo anayala thambo mwaluso lake.
13 Iye akayankhula, kumamveka mkokomo wamadzi akumwamba;
    Iyeyo amabweretsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.
Amabweretsa mphenzi pamodzi ndi mvula
    ndi kutulutsa mphepo yamkuntho kumalo kumene osungirako.

14 Anthu onse ndi opusa ndiponso opanda nzeru;
    mmisiri aliyense wosula golide akuchita manyazi ndi mafano ake.
Mafano akewo ndi abodza;
    alibe moyo mʼkati mwawo.
15 Mafanowo ndi achabechabe, zinthu zosekedwa nazo.
    Pamene anthuwo azidzaweruzidwa, mafanowo adzawonongedwa.
16 Koma Yehova amene ndi Cholowa cha Yakobo sali ngati mafanowo.
    Iyeyu ndi Mlengi wa zinthu zonse
kuphatikizapo Israeli, mtundu umene anawusankha kuti ukhale anthu ake.
    Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.

Chiwonongeko Chikubwera

17 Sonkhanitsani katundu wanu,
    inu amene mukukhala mʼlinga la ankhondo.
18 Pakuti Yehova akuti,
    “Tsopano Ine ndidzachotsa anthu onse
    amene akukhala mʼdziko lino;
adzakhala pa mavuto
    mpaka adzamvetsa.”

19 Aliyense ankangoti, “Mayo ine, chifukwa cha kupweteka kwanga!
    Chilonda changa nʼchachikulu!”
Koma ine ndinkaganiza kuti, “Ndithu, ili ndi vuto langa basi,
    choncho ndingolipirira.”
20 Tenti yanga yawonongeka,
    zingwe zake zonse zaduka.
Ana anga andisiya ndipo kulibenso.
    Palibenso amene adzandimangire tenti,
    kapena kufunyulula nsalu yake.
21 Abusa ndi opusa
    ndipo sanapemphe nzeru kwa Yehova;
choncho palibe chimene anapindula
    ndipo nkhosa zawo zonse zabalalika.
22 Tamvani! kukubwera mphekesera,
    phokoso lalikulu la gulu la a ankhondo likumveka kuchokera kumpoto!
Lidzasandutsa bwinja mizinda ya ku Yuda,
    malo okhala nkhandwe.

Pemphero la Yeremiya

23 Inu Yehova, ndikudziwa kuti moyo umene munthu ali nawo si wake;
    munthuyo sangathe kuwongolera mayendedwe ake.
24 Inu Yehova, langizeni, komatu mwachilungamo,
    osati ndi mkwiyo wanu,
    mungandiwononge kotheratu.
25 Tsanulirani ukali wanu pa mitundu ya anthu amene sakudziwani,
    ndiye kuti mitundu ya anthu amene satama pa dzina lanu mopemba.
Iwo aja anasakaza Yakobo;
    amusakaza kotheratu
    ndipo awononga dziko lake.

Pangano Liphwanyidwa

11 Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, “Imvani mawu a pangano ili, ndipo uwawuze anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. Awuze kuti Yehova, Mulungu wa Israeli akuti ‘adzakhala wotembereredwa munthu amene samvera mawu a pangano ili. Awa anali mawu amene ndinalamulira makolo anu nditawatulutsa mu Igupto, kuchoka mʼngʼanjo yamoto.’ Ine ndinati, ‘Mverani Ine ndi kuchita chilichonse chimene ndakulamulirani. Mukatero mudzakhala anthu anga ndi Ine ndidzakhala Mulungu wanu. Tsono Ine ndidzakwaniritsa lumbiro lomwe ndinalumbira kwa makolo anu kuti ndidzawapatsa dziko loyenda mkaka ndi uchi,’ dziko lomwe inu lero mukukhalamo.”

Tsono Ine ndinayankha kuti, “Ameni, Yehova.”

Yehova anandiwuza kuti, “Lengeza mawu onsewa mʼmizinda yonse ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu: ‘Mverani mawu a pangano ili ndi kuzitsatira. Kuyambira nthawi imene ndinatulutsa makolo anu ku Igupto mpaka lero, ndakhala ndi kuwachenjeza kawirikawiri kuti, ‘Mverani Ine.’ Koma sanamvere kapena kulabadirako. Aliyense anawumirira kuchita zoyipa za mʼmitima yawo. Ngakhale ndinawalamulira kuti asunge pangano langa koma iwo sanasunge. Choncho ndinawalanga monga ndinaneneramo.’ ”

Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu andiwukira. 10 Abwereranso ku machimo a makolo awo, amene anakana kumvera mawu anga. Akutsata milungu ina ndi kumayitumikira. Aisraeli ndi Ayuda aphwanya pangano limene ndinachita ndi makolo awo. 11 Choncho Yehova akuti, ‘Ndidzawagwetsera mavuto amene sadzatha kuwalewa. Ngakhale adzandilirire, sindidzawamvera. 12 Anthu a mʼmizinda ya Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu adzapita ndi kukalirira milungu imene ankayifukizira lubani, koma milunguyo sidzawathandiza ndi pangʼono pomwe mavuto akadzafika. 13 Iwe Yuda, uli ndi milungu yochuluka ngati chiwerengero cha mizinda yako; chiwerengero cha maguwa ansembe amene umafukizirapo lubani kwa Baala chili ngati misewu ya mu Yerusalemu.’

14 “Tsono iwe Yeremiya usawapempherere anthu amenewa ngakhale kuwadandaulira kapena kuwapepesera, chifukwa sindidzawamvera akadzandiyitana pa nthawi ya mavuto awo.

15 “Kodi anthu anga okondedwa akudzachita chiyani mʼNyumba yanga?
    Kodi suja iwowa amachita zoyipa zambiri?
    Kodi mungathe kupulumuka,
tsoka osakugwerani
    chifukwa cha nsembe zanuzo?”

16 Kale Yehova ankakutchani mtengo wa olivi wa masamba obiriwira,
    wokhala ndi zipatso zokongola.
Koma tsopano adzawutentha
    ndi mkuntho wamkokomo
    ndipo nthambi zake zidzapserera.

17 Yehova Wamphamvuzonse, amene anakudzalani, walamula kuti mavuto akugwereni. Inu a banja la Yuda ndi a banja la Israeli munachitira Yehova zoyipa ndi kumukwiyitsa pamene munkapereka nsembe zanu kwa Baala.

Amuchitira Chiwembu Yeremiya

18 Yehova anandiwululira ndipo ndinadziwa. Iye anatsekula maso anga kuti ndione chiwembu chawocho. 19 Ndinali ngati mwana wankhosa wofatsa amene akupita naye kukamupha; sindinkadziwa kuti chiwembu chimene ankakonzekeracho chinkaloza ine. Iwo amati:

“Tiyeni timuphe
    munthu ameneyu
    kuti dzina lake lisadzakumbukiridwenso.”
20 Koma, Inu Yehova Wamphamvuzonse, Inu amene mumaweruza molungama
    ndi kuyesa mitima ndi maganizo,
lolani kuti ine ndione kuti mwawalipsira,
    pakuti mlandu wanga ndawupereka mʼmanja mwanu.

21 “Nʼchifukwa chake Yehova akunena za anthu a ku Anatoti amene akufuna kuwononga moyo wako namanena kuti, ‘Usanenere mʼdzina la Yehova, ukatero ife tidzakupha ndi manja athu,’ 22 koma Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ine ndidzawalanga. Achinyamata awo adzaphedwa ndi lupanga, ana awo aamuna ndi aakazi adzafa ndi njala. 23 Sipadzakhala otsala ndi mmodzi yemwe, chifukwa ndidzalanga anthu a ku Anatoti chikadzafika chaka chawo cha chilango.’ ”

1 Timoteyo 6

Onse amene ali mu ukapolo ayenera kuona ambuye awo ngati oyenera kuwachitira ulemu, kuti anthu anganyoze dzina la Mulungu ndi chiphunzitso chathu. Amene ambuye awo ndi okhulupirira, asawapeputse chifukwa ambuye ndi abale mʼchikhulupiriro. Mʼmalo mwake akuyenera kuwatumikira bwino chifukwa ambuye wawo ndi okondedwa monga okhulupirira ndiponso ndi odzipereka kusamalira akapolo awo.

Aphunzitsi Onyenga ndi Kukonda Ndalama

Zinthu izi ukuyenera kuziphunzitsa ndi kuwalamula anthu. Ngati wina aphunzitsa zosiyana ndi zimenezi, wosagwirizana ndi malangizo woona a Ambuye athu Yesu Khristu ndi chiphunzitso cholemekeza Mulungu, ameneyo ndi wodzitukumula ndipo sakudziwa chilichonse. Iyeyo ali ndi maganizo oyipa, wokonda kusemphana mawu ndi kutsutsana. Zimenezi zimabweretsa nsanje, mikangano, mʼnyozo, kuganizirana zoyipa, ndi kulimbana kosatha pakati pa anthu amitima yopotoka amene alandidwa choonadi ndipo amaganiza kuti kulemekeza Mulungu ndi njira yopezera chuma.

Koma kulemekeza Mulungu kuli ndi phindu lalikulu. Pakuti sitinabweretse kanthu mʼdziko lapansi, ndipo sitingatengenso kanthu pochoka mʼdziko lapansi. Koma ngati tili ndi chakudya ndi zovala, zimenezi zitikwanire. Anthu amene amafuna kulemera amagwa mʼmayesero ndi mu msampha ndi mʼzilakolako zambiri zopusa ndi zoopsa zimene zimagwetsera anthu mʼchitayiko ndi mʼchiwonongeko. 10 Pakuti kukonda ndalama ndiye muzu wa zoyipa za mitundu yonse. Anthu ena ofunitsitsa ndalama, asochera ndipo asiya njira yachikhulupiriro ndipo adzitengera zowawitsa zambiri.

Malangizo Otsiriza kwa Timoteyo

11 Koma iwe, munthu wa Mulungu, thawa zinthu zonsezi. Tsatira chilungamo, moyo wolemekeza Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, kupirira ndi kufatsa. 12 Menya nkhondo yabwino yachikhulupiriro. Gwiritsitsa moyo wosatha umene anakuyitanira pamene unavomereza bwino lomwe pamaso pa mboni zambiri. 13 Ndikukulamula pamaso pa Mulungu amene amapatsa moyo zinthu zonse, ndiponso pamaso pa Khristu Yesu amene pochitira umboni pamaso pa Pontiyo Pilato, ananena zoona zenizeni. 14 Usunge lamuloli mopanda banga ndi cholakwa kufikira Ambuye athu Yesu Khristu ataonekera. 15 Pa nthawi yake Mulungu adzamubweretsa kwa ife. Mulungu ndi wodalitsika ndipo Iye yekha ndiye Wolamulira, Mfumu ya mafumu, Mbuye wa ambuye. 16 Ndiye yekha wosafa ndipo amakhala mʼkuwala koopsa. Mulungu amene munthu aliyense sanamuone. Kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu mpaka muyaya. Ameni.

Za Kudalira Chuma

17 Anthu onse amene ali ndi chuma uwalamule kuti asanyade kapena kuyika mitima yawo pa chuma chimene nʼchosadalirika. Koma chiyembekezo chawo chikhale mwa Mulungu amene amatipatsa mowolowamanja zonse zotisangalatsa. 18 Uwalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, owolowamanja ndi okonda kugawana zinthu zawo ndi anzawo. 19 Potero adzadziwunjikira chuma chokhalitsa ngati maziko okhazikika a nthawi zakutsogolo, kuti akalandire moyo, umene ndi moyo weniweni.

Mawu Otsiriza

20 Timoteyo, samalitsa zimene unapatsidwa. Upewe nkhani zopanda pake zosalemekeza Mulungu ndiponso maganizo otsutsana amene amaganizidwa molakwika kuti ndi nzeru. 21 Anthu ena chifukwa chovomereza nzeru zotere, asochera nʼkutaya chikhulupiriro chawo.

Chisomo chikhale nawe.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.