Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yeremiya 6-8

Kuzingidwa kwa Yerusalemu

“Thawani, inu anthu a ku Benjamini!
    Tulukani mu Yerusalemu!
Lizani lipenga ku Tekowa!
    Kwezani mbendera ku Beti-Hakeremu!
Pakuti tsoka lalikulu likubwera kuchokera kumpoto,
    ndipo chiwonongekocho nʼchachikulu.
Kodi mzinda wa Ziyoni suli ngati msipu wokongola kwambiri,
    kumene abusa amafikako ndi ziweto zawo?
Abusa ndi nkhosa zawo adzabwera kudzalimbana nawo;
    adzamanga matenti awo mowuzinga,
    ndipo aliyense adzakhazika anthu ake pamalo pake.”

Adzanena kuti, “Konzekani kuwuthira nkhondo mzindawo!
    Nyamukani, kuti tiwuthire nkhondo mzindawu masana ano.
Koma tili ndi tsoka, dzuwa lapendeka,
    ndipo zithunzithunzi za kumadzulo zikunka zitalika.
Tsono nyamukani kuti tiwuthire nkhondo mzindawu usiku uno
    ndi kuwononga malinga ake!”

Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Dulani mitengo
    ndipo mumange mitumbira yankhondo kulimbana ndi Yerusalemu.
Mzinda umenewu uyenera kulangidwa;
    wadzaza ndi kuponderezana.
Monga momwe chitsime chimatulutsira madzi
    ndi mmenenso Yerusalemu amatulutsira zoyipa zake.
Chiwawa ndi chiwonongeko ndi zomwe zimamveka mu mzindamo;
    nthenda yake ndi mabala ake ndimaziona nthawi zonse.
Iwe Yerusalemu, tengapo phunziro,
    kuopa kuti chikondi changa pa iwe chingakuchokere
ndi kusandutsa dziko lako kukhala bwinja
    mopanda munthu wokhalamo.”

Yehova Wamphamvuzonse anandiwuza kuti,

“Adani adzawakunkha ndithu anthu otsala a Israeli,
    monga momwe amachitira populula mphesa.
Tsono iwe yesetsa kupulumutsa amene ungathe
    monga mmene amachitira munthu wokolola mphesa.”

10 Kodi ndiyankhule ndi yani ndi kumuchenjeza?
    Ndinene mawu ochenjeza kwa yani kuti amve?
Makutu awo ndi otsekeka
    kotero kuti sangathe kumva.
Mawu a Yehova ndi onyansa kwa iwo;
    sasangalatsidwa nawo.
11 Koma ine ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Yehova,
    ndipo ndatopa ndi kusunga mkwiyo wa Yehova.

Yehova anandiwuza kuti, “Tsono ndidzawutulutsira mkwiyo umenewu pa ana oyenda mʼmisewu
    ndi pa achinyamata amene asonkhana pamodzi;
pakutinso mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa,
    pamodzi ndi okalamba amene ali ndi zaka zochuluka.
12 Nyumba zawo adzazipereka kwa ena,
    pamodzi ndi minda yawo ndi akazi awo.
Ndidzatambasula dzanja langa kukantha
    anthu okhala mʼdzikomo,”
            akutero Yehova.
13 “Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,
    onse ali ndi dyera lofuna kupeza phindu mwa kuba;
aneneri pamodzi ndi ansembe omwe,
    onse amachita zachinyengo.
14 Amapoletsa zilonda za anthu anga
    pamwamba pokha.
Iwo amanena kuti, ‘Mtendere, mtendere,’
    pamene palibe mtendere.
15 Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazo?
    Ayi, sachita manyazi ndi pangʼono pomwe;
    sadziwa ndi kugwetsa nkhope komwe.
Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale;
    adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalange,”
            akutero Yehova.

16 Yehova akuti,

“Imani pa mphambano ndipo mupenye;
    kumeneko ndiye kuli njira zakale,
funsani kumene kuli njira yabwino. Yendani mʼmenemo,
    ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.
    Koma inu munati, ‘Ife sitidzayenda njira imeneyo.’
17 Ine ndinakupatsani alonda oti akuyangʼanireni
    ndipo ndinati, ‘Imvani kulira kwa lipenga!’
    koma inu munati, ‘Sitidzamvera.’
18 Nʼchifukwa chake imvani, inu anthu a mitundu ina;
    yangʼanitsitsani, inu amene mwasonkhana pano,
    chimene chidzawachitikire anthuwo.
19 Imvani, inu anthu okhala pa dziko lapansi,
ndikubweretsa masautso pa anthu awa.
    Zimenezi ndi mphotho ya ntchito zawo.
Iwowa sanamvere mawu anga
    ndipo anakana lamulo langa.
20 Kodi pali phindu lanji ngakhale mubwere ndi lubani kuchokera ku Seba,
    kapena zonunkhira zina kuchokera ku dziko lakutali?
Nsembe zanu zopsereza Ine sindidzalandira;
    nsembe zanu sizindikondweretsa.”

21 Choncho Yehova akuti,

“Ndidzayika zokhumudwitsa pamaso pa anthu awa.
    Abambo ndi ana awo aamuna onse adzapunthwa ndi kugwa;
    anansi awo ndi abwenzi awo adzawonongeka.”

22 Yehova akunena kuti,

“Taonani, gulu lankhondo likubwera
    kuchokera kumpoto;
mtundu wa anthu amphamvu wanyamuka
    kuchokera kumathero a dziko lapansi.
23 Atenga mauta ndi mikondo;
    ndi anthu ankhanza ndi opanda chifundo.
Phokoso lawo lili ngati mkokomo wa nyanja.
    Akwera pa akavalo awo
ndipo akonzekera ngati anthu ankhondo,
    kudzakuthirani nkhondo anthu a ku Ziyoni.”

24 A ku Ziyoni akuti “Ife tamva mbiri yawo,
    ndipo manja anthu alefukiratu.
Nkhawa yatigwira,
    ndipo tikumva ululu ngati mayi pa nthawi yake yochira.
25 Musapite ku minda
    kapena kuyenda mʼmisewu,
pakuti mdani ali ndi lupanga,
    ndipo ponseponse anthu akuchita mantha.
26 Inu anthu anga, valani ziguduli
    ndipo gubudukani pa phulusa;
lirani mwamphamvu
    ngati munthu wolirira mwana wake mmodzi yekha,
pakuti mwadzidzidzi wowonongayo
    adzabwera kudzatipha.

27 “Iwe Yeremiya, ndakuyika kuti ukhale choyesera zitsulo.
    Uwayese anthu anga
monga ungayesere chitsulo
    kuti uwone makhalidwe awo.
28 Onsewo ali ndi khalidwe lokanika ndi lowukira
    ndipo akunka nanena zamiseche.
Iwo ndi olimba ngati mkuwa ndi chitsulo.
    Onse amangochita zoyipa zokhazokha.
29 Moto mu mvukuto ukuyaka kwambiri;
    mtovu watha kusungunuka ndi moto.
Koma ntchito yosungunulayo sikupindula
    chifukwa zoyipa sizikuchokapo.
30 Iwo ali ngati siliva wotayidwa,
    chifukwa Yehova wawakana.”

Chipembedzo Chabodza Nʼchopanda Phindu

Mawu amene Yehova anayankhula kwa Yeremiya ndi awa, “Ima pa chipata cha Nyumba ya Yehova ndipo kumeneko ukalalikire uthenga uwu:

“ ‘Imvani mawu a Yehova, inu nonse anthu a ku Yuda amene mumalowa pa chipata ichi kudzapembedza Yehova. Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Konzani makhalidwe anu ndi zochita zanu, ndipo ndidzakulolani kukhala pa malo ano. Musamakhulupirire mawu anu achinyengo onena kuti, ‘Ino ndi Nyumba ya Yehova, Nyumba ya Yehova, Nyumba ya Yehova!’ Ngati mutasinthadi makhalidwe anu ndi zochita zanu, ndi kumachitirana zolungama, ngati mutaleka kuzunza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye ndi kuleka kupha anthu osalakwa pa malo ano, ndipo ngati muleka kutsatira milungu ina, kuti ingakuwonongeni, Ine ndidzakulolani kukhala pa malo ano, mʼdziko limene ndinapatsa makolo anu mpaka muyaya. Koma onani, inu mukudalira mawu abodza amene alibe phindu.

“Kodi inu muziba ndi kupha, kuchita chigololo ndi kulumbira monama, kufukiza lubani kwa Baala ndi kutsatira milungu ina imene simunayidziwe, 10 ndipo kenaka nʼkubwera kudzayima pamaso panga mʼNyumba ino, Nyumba imene imadziwika ndi Dzina langa, inu nʼkumati, ‘Tapulumuka.’ Mwapulumuka kuti muzichitabe zonyansazi? 11 Kodi Nyumba ino imene imadziwika ndi Dzina langa, yasanduka phanga la anthu olanda zinthu anzawo mwachifwamba inu mukuona? Komatu ndakhala ndi kuziona zonsezi! akutero Yehova.”

12 “ ‘Pitani tsopano ku malo anga ku Silo, malo amene poyamba ankadziwika ndi Dzina langa, ndipo mukaone zimene ndinachita kumeneko chifukwa cha kuyipa kwa anthu anga Aisraeli. 13 Tsono popeza munkachita zonsezi, ngakhale Ine kukuyankhulani koma inu osamvera, kukuyitanani koma inu osayankha, 14 choncho ndidzachita pa Nyumba imene imadziwika ndi Dzina langayi, Nyumba ya Yehova imene mumayidalira, malo amene ndinapereka kwa inu ndi makolo anu, zomwe ndinachita ku Silo. 15 Ndidzakuthamangitsani pamaso panga, ngati momwe ndinachitira abale anu onse, anthu a Efereimu.’ ”

16 “Choncho iwe Yeremiya usawapempherere anthu awa ngakhale kuwapepesera kapenanso kuwapembedzera; usandidandaulire, chifukwa Ine sindidzakumvera. 17 Kodi sukuona zimene akuchita mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya ku Yerusalemu? 18 Ana akutorera nkhuni, abambo akusonkha moto, ndipo amayi akukanda ufa kuti aphike makeke oti akapereke nsembe kwa mfumukazi yazakumwamba. Iwo amathira nsembe ya zakumwa kwa milungu ina kuti andipsetse mtima. 19 Koma kodi akuvutitsa Ine? Kodi sakungodzivuta okha, ndi kudzichititsa manyazi? akutero Yehova.”

20 “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti: Ndidzatsanulira mkwiyo wanga pa Nyumba yangayi, anthu, nyama, mitengo ndi zipatso zomwe. Mkwiyowo udzakhala ngati moto wosazimitsika.

21 “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Wonjezerani nsembe zanu zopsereza pa nsembe zanu zinazo ndipo mudye nyama yakeyo! 22 Pakuti pamene ndinatulutsa makolo anu ku Igupto ndi kuyankhula nawo, sindinawalamulire kuti azipereka nsembe zopsereza kapena nsembe zinazo, 23 koma ndinawalamula kuti: Mverani Ine, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu ndipo inu mudzakhala anthu anga. Muzitsata zonse zimene ndakulamulirani, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino. 24 Koma anthuwo sanamvere kapena kulabadira; mʼmalo mwake anapitirira kusamvera ndi mitima yawo yoyipa. Iwo anabwerera mʼmbuyo mʼmalo mopita patsogolo. 25 Kuyambira tsiku limene makolo awo anachoka ku Igupto mpaka lero lino, ndakhala ndikuwatumizira atumiki anga, aneneri. 26 Koma anthuwo sanandimvere kapena kusamalira. Anawumitsa mitima yawo ndi kuchita zoyipa kuposa makolo awo.

27 “Ngakhale iwe uwawuze zonsezi koma sadzakumvera. Ngakhale uwayitane koma sadzakuyankha. 28 Nʼchifukwa chake udzawawuze kuti, ‘Uwu ndi mtundu wa anthu umene sunamvere Yehova Mulungu wake, wosalola kulangizidwa. Choonadi chatha; chazimirira pa milomo yawo.’

29 “Tsono meta tsitsi lako ndi kulitaya. Ulire kwambiri pa zitunda zopanda zomera, pakuti Yehova waukana ndi kuwusiya mʼbado umene wamukwiyitsawu.”

Chigwa cha Imfa

30 “Anthu a ku Yuda achita zoyipa pamaso panga, akutero Yehova. Ayimika mafano awo onyansa mʼnyumba imene imadziwika ndi Dzina langa ndipo ayipitsa. 31 Amanga nsanja yopembedzera Tofeti mʼChigwa cha Hinomu kuti apserezereko ana awo aamuna ndi aakazi. Zimenezi Ine sindinawalamulire ngakhale kuziganizira nʼkomwe. 32 Nʼchifukwa chake masiku akubwera, akutero Yehova, pamene anthu sadzawatchulanso malowo Tofeti kapena Chigwa cha Hinomu, koma adzawatchula Chigwa cha Imfa, chifukwa adzakwirira anthu akufa ku Tofeti mpaka osapezekanso malo owayika. 33 Ndipo mitembo ya anthu amenewa idzakhala chakudya cha mbalame zamlengalenga ndi zirombo zakuthengo, ndipo palibe wina amene adzazipirikitse. 34 Ndidzathetsa nyimbo zonse zachisangalalo ndi zachikondwerero mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya ku Yerusalemu. Sikudzamvekanso mawu a chikondwerero a mkwatibwi ndi mkwati pakuti dzikolo lidzasanduka chipululu.”

Yehova akuti, “ ‘Pa nthawi imeneyo, mafupa a mafumu ndi a akuluakulu a ku Yuda, mafupa a ansembe ndi a aneneri, ndiponso mafupa a anthu a ku Yerusalemu adzafukulidwa. Adzawamwaza pa nthaka kuyangʼana dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zonse zamlengalenga, zimene ankazikonda, kuzitumikira ndi kuzitsatira, kupemphako nzeru ndiponso kuzilambira. Mafupawo sadzawasonkhanitsa kapena kuwakwirira, koma adzakhala ngati ndowe pamwamba pa nthaka. Otsala onse a mtundu woyipawu adzafuna imfa kopambana moyo kulikonse kumene ndidzawapirikitsirako, akutero Yehova Wamphamvuzonse.’ ”

Tchimo ndi Chilango Chake

“Tsono awuze anthuwa, ‘Yehova akuti:

“ ‘Kodi anthu akagwa sangadzukenso?
    Munthu akasochera kodi sangathe kubwereranso?
Chifukwa chiyani nanga anthu awa akupitirirabe kuchimwa, osabwerera?
    Chifukwa chiyani Yerusalemu akubwerera mʼmbuyo?
Iwo akangamira chinyengo;
    akukana kubwerera.
Ine ndinatchera khutu kumvetsera
    koma iwo sanayankhulepo zoona.
Palibe woyipa amene analapapo zoyipa zake,
    nʼkumati, ‘Ine ndachita chiyani?’
Aliyense akutsatira njira yake
    ngati kavalo wothamangira nkhondo.
Mbalame yotchedwa kakowa ija imadziwa
    nthawi yake mlengalenga.
Koma nkhunda, namzeze ndi chingalu
    zimadziwa nthawi yonyamukira ulendo,
koma anthu anga sadziwa
    malamulo a Yehova.

“ ‘Inu mukunena bwanji kuti,
    ‘Ndife anzeru ndipo timasunga malamulo a Yehova?’
Koma ndi alembi anu
    amene akulemba zabodza.
Anthu anzeru achita manyazi;
    athedwa nzeru ndipo agwidwa.
Iwo anakana mawu a Yehova.
    Nanga tsono nzeru zawo ziwapinduliranji?
10 Nʼchifukwa chake akazi awo ndidzawapereka kwa amuna ena
    ndipo minda yawo ndidzayipereka kwa amene adzawagonjetse.
Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,
    onse ali ndi khalidwe lofuna kupeza chuma mwakuba.
Aneneri pamodzi ndi ansembe omwe,
    onse amachita zachinyengo.
11 Iwo amapoletsa zilonda za anthu anga
    pamwamba chabe
nʼkumati, ‘Mtendere, mtendere,’
    pamene palibe mtendere.
12 Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazi?
    Ayi, alibe manyazi ndi pangʼono pomwe;
    iwo sadziwa nʼkugwetsa nkhope komwe.
Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale;
    adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalanga,
            akutero Yehova.

13 “ ‘Ndidzatenga zokolola zawo,
    Sipadzakhalanso mphesa pa mpesa
kapena nkhuyu pa mkuyu,
    ndipo masamba ake adzawuma.
Zinthu zimene ndinawapatsa
    ndidzawachotsera.’ ”

14 Koma amati, “Tikukhala pano chifukwa chiyani?
    Tiyeni tonse pamodzi
tithawire ku mizinda yotetezedwa
    ndi kukafera kumeneko.
Pakuti Yehova Mulungu wathu watsimikiza kuti tiyenera kufa.
    Watipatsa madzi aululu kuti timwe,
    chifukwa tamuchimwira.
15 Tinkayembekezera mtendere
    koma palibe chabwino chomwe chinachitika,
tinkayembekezera kuchira
    koma tinakumana ndi zoopsa zokhazokha.
16 Kulira kwa ngʼombe zazimuna za mdani
    kukumveka kuchokera ku Dani;
dziko lonse likunjenjemera
    chifukwa cha kulira kwa akavalowo.
Akubwera kudzawononga dziko
    ndi zonse zimene zili mʼmenemo.
    Adzawononga mzinda ndi onse okhalamo.”

17 Yehova akuti, “Onani, ndikukutumizirani njoka zaululu,
    mphiri zimene munthu sangathe kuzilodza,
    ndipo zidzakulumani,”

18 Ndadzazidwa ndi chisoni kwambiri,
    mtima wanga walefukiratu.
19 Imvani kulira kwa anthu anga
    kuchokera ku dziko lakutali:
akuti, “Kodi Yehova sali ku Ziyoni?
    Kodi mfumu yake sili kumeneko?”

“Chifukwa chiyani akundiputa ndi mafano awo osema,
    ndi milungu yawo yachilendo?”

20 “Nthawi yokolola yapita,
    chilimwe chapita,
    koma sitinapulumuke.”

21 Chifukwa cha mavuto a anthu anga, ine ndikumva kuwawa;
    ndikungolira ndipo mantha aakulu andigwira.
22 Kodi ku Giliyadi kulibe mankhwala ochiritsa?
    Kodi kumeneko kulibe singʼanga?
Nanga chifukwa chiyani mabala
    a anthu anga sanapole?

1 Timoteyo 5

Malangizo kwa Amayi Amasiye, Akulu Ampingo ndi Akapolo

Usadzudzule munthu wachikulire mokalipa, koma umuchenjeze ngati abambo ako. Achinyamata uwatenge ngati abale ako. Amayi achikulire uwatenge ngati amayi ako ndipo amayi achitsikana uwatenge ngati alongo ako, nʼkuyera mtima konse.

Uziwachitira ulemu akazi amasiye amene ali okhaokha. Koma ngati mkazi wamasiye ali ndi ana ndi zidzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wawo pa banja lawo moopa Mulungu, potero akubweza zabwino kwa makolo awo ndi agogo awo. Pakuti zimenezi ndiye zimakondweretsa Mulungu. Mkazi wamasiye amene ali yekha ndi wopanda womuthandiza, ameneyo wayika chiyembekezo chake pa Mulungu, ndipo amapemphera kosalekeza usana ndi usiku kuti Mulungu azimuthandiza. Koma mkazi wamasiye amene amangokhalira kuchita zosangalatsa moyo wake, wafa kale ngakhale akanali ndi moyo. Pereka malangizo amenewa kwa anthu kuti akhale opanda zolakwa. Ngati wina sasamalira abale ake, makamaka a mʼbanja mwake mwenimweni, ameneyo wakana chikhulupiriro ndipo ndi woyipa kuposa wosakhulupirira.

Mayi wamasiye aliyense amene sanakwanitse zaka 60 zakubadwa, asakhale mʼgulu la akazi amasiye. Akhale woti anakwatiwapo ndi mwamuna wake mmodzi yekha. 10 Akhale mayi woti amadziwika bwino pa ntchito zake zabwino monga kulera ana, kusamalira alendo, kusambitsa mapazi a anthu a Mulungu, kuthandiza amene ali pa mavuto ndi kudzipereka pa ntchito zonse zabwino.

11 Akazi amasiye achitsikana, usawayike mʼgulu limeneli. Pakuti zilakolako zawo zikayamba kuwavutitsa nʼkuwalekanitsa ndi Khristu, amafuna kukwatiwanso. 12 Zikatero amadziweruza okha chifukwa aphwanya lonjezo lawo loyamba. 13 Komanso amakhala ndi chizolowezi cha ulesi ndi kumangoyenda khomo ndi khomo. Ndipo sikungokhala aulesi kokha komanso kuchita miseche, kududukira za eni ake, kumangokamba zinthu zosayenera kukamba. 14 Kotero, ndikulangiza akazi amasiye achitsikana kuti akwatiwe, akhale ndi ana, asamalire makomo awo ndipo asamupatse mdani mpata wonyoza 15 Akazi amasiye ena apatuka kale nʼkumatsatira Satana.

16 Ngati mayi aliyense wokhulupirira ali ndi akazi amasiye amene akuwasamalira, apitirizebe kuwasamalira ndipo asalemetse mpingo, kuti mpingo uthandize akazi amasiye amene ali okhaokha.

17 Akulu ampingo amene amayangʼanira bwino zochitika za mu mpingo, ndi oyenera ulemu wowirikiza, makamaka amene ntchito yawo ndi kulalikira ndi kuphunzitsa. 18 Pakuti Mawu a Mulungu amati, “Musamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha tirigu,” ndi “Wantchito ngoyenera kulandira malipiro ake.” 19 Usamamvere mawu oneneza akulu ampingo pokhapokha patakhala mboni ziwiri kapena zitatu. 20 Akulu ampingo amene akuchimwa, uwadzudzule poyera kuti ena aphunzirepo.

21 Ndikukulamulira pamaso pa Mulungu, pamaso pa Yesu Khristu ndi pamaso pa angelo osankhika, kuti usunge malangizowa mosachotsera ndipo usachite kalikonse mokondera.

22 Usafulumire kusanjika manja munthu, ndipo usavomerezane ndi anthu ena pa machimo. Usunge bwino kuyera mtima kwako.

23 Uleke kumangomwa madzi okha, koma uzimwako vinyo pangʼono chifukwa cha vuto lako la mʼmimba ndi kudwala kwako kwa pafupipafupi.

24 Anthu ena machimo awo amaonekeratu poyera, amakafika pa mpando wachiweruzo eni akewo asanakafike. Machimo a anthu ena amabwera mʼmbuyo mwawo. 25 Momwemonso, ntchito zabwino zimaonekera poyera, ndipo ngakhale zipande kutero, sizingatheke kubisika.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.