Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yeremiya 3-5

“Ngati munthu asudzula mkazi wake
    ndipo mkaziyo nʼkuchoka nakakwatiwa ndi mwamuna wina,
kodi mwamuna woyambayo angathe kumutenganso mkaziyo?
    Kodi atatero sindiye kuti dzikolo layipitsidwa kwambiri?
Koma iwe Israeli wachita zadama ndi zibwenzi zambiri.
    Komabe bwerera kwa ine,”
            akutero Yehova.
“Tayangʼana ku zitunda zowuma.
    Kodi aliponso malo ena amene iwe sunachitepo zadama?
Iwe unkakhala mʼmbali mwa njira kumadikira zibwenzi zako,
    ngati Mluya wobisalira anthu mʼchipululu.
Inu mwayipitsa dziko ndi zadama zanu
    ndi ntchito zanu zoyipa.
Nʼchifukwa chake Yehova wayimitsa mvula,
    ndipo mvula ya nthawi ya masika sinagwe.
Komabe uli ndi maonekedwe a mkazi wachiwerewere;
    ndipo sukuchita manyazi ndi pangʼono pomwe.
Kodi iwe siposachedwa pomwepa pamene wanena
    kuti, ‘Abambo anga, Inu bwenzi langa la unyamata wanga,
kodi mudzandikwiyira nthawi zonse?
    Kodi ukali wanu udzakhalabe mpaka muyaya?’
Umu ndimo mmene umayankhulira,
    koma umapitirizabe kuchita zoyipa monga momwe umathera.”

Kusakhulupirika kwa Israeli

Pa nthawi ya Mfumu Yosiya Yehova anandiwuza kuti, “Kodi waona zomwe Israeli wosakhulupirika uja wachita? Anakwera pa phiri lililonse lalitali ndi kupita pa tsinde pa mtengo uliwonse wogudira kukapembedza. Choncho anachita za chiwerewere kumeneko. Ndinaganiza kuti atachita zonsezi, adzabwerera kwa Ine, koma sanabwerere, ndipo mlongo wake wosakhulupirika uja, Yuda, anaziona zimenezi. Anaona kuti ndinasudzula Israeli wosakhulupirikayo ndi kumupirikitsa chifukwa cha zigololo zake. Komabe Yuda mʼbale wake wosakhulupirika uja sanaope, nayenso anapita kukachita chigololo. Chiwerewere cha Israeli chinali chochititsa manyazi kotero kuti chinayipitsa dziko lonse. Anachita chigololo popembedza mafano a miyala ndi mitengo. 10 Israeli atachita zonsezi, Yuda mʼbale wake wosakhulupirika uja sanabwerere kwa Ine ndi mtima wake wonse, koma mwachiphamaso chabe,” akutero Yehova.

11 Yehova anandiwuza kuti, “Kusakhulupirika kwa Israeli nʼkochepa kuyerekeza ndi kusakhulupirika kwa Yuda. 12 Pita ukalalikire kumpoto uthenga wakuti,

“ ‘Israeli wosakhulupirikawe, bwerera,’ akutero Yehova.
    ‘Sindidzakukalipira mpaka kalekale,
pakuti ndine wachifundo,’ akutero Yehova.
    ‘Sindidzakukwiyira mpaka kalekale.
13 Ungovomera kulakwa kwako
    kuti unawukira Yehova Mulungu wako.
Vomera kuti unayendayenda kukapembedza milungu yachilendo
    pansi pa mtengo uliwonse wogudira,
    ndiponso kuti sunandimvere,’ ”
            akutero Yehova.

14 “Bwererani, ana osakhulupirika, pakuti ndine mbuye wanu,” akutero Yehova. “Ndinakusankhani, mmodzimmodzi kuchokera ku mudzi uliwonse ndiponso awiriawiri kuchokera ku banja lililonse. 15 Ndipo ndidzakupatsani abusa a pamtima panga amene adzakutsogolerani mwanzeru ndi mwaluntha. 16 Masiku amenewo mukadzachulukana kwambiri mʼdzikomo, anthu sadzanenanso za ‘Bokosi la Chipangano la Yehova’ kapena kuliganizira. Sadzalikumbukiranso kapena kulifuna, ndipo sadzapanganso lina,”

            akutero Yehova.

17 Nthawi imeneyo adzatcha Yerusalemu Mpando Waufumu wa Yehova, ndipo mitundu yonse ya anthu idzasonkhana mu Yerusalemu pamaso pa Yehova. Sadzawumiriranso kutsata mitima yawo yoyipa. 18 Masiku amenewo fuko la Yuda lidzaphatikizana ndi fuko la Israeli, onse pamodzi adzachokera ku dziko la kumpoto kupita ku dziko limene ndinapatsa makolo awo, kuti likhale cholowa.

19 “Ine mwini ndinati,

“ ‘Ndikanakonda bwanji kukukhazikani pakati pa ana anga
    ndikukupatsani dziko labwino kwambiri,
    cholowa chokongola kwambiri kuposa cha mitundu ina ya anthu.’
Ndinaganiza kuti mudzanditcha Ine ‘Atate’
    ndi kuti simudzaleka kunditsata.
20 Koma monga mkazi wosakhulupirika amasiya mwamuna wake,
    momwemonso inu mwakhala osakhulupirika kwa Ine, inu fuko la Israeli,”
            akutero Yehova.

21 Mawu akumveka pa magomo,
    Aisraeli akulira ndi kupempha chifundo
chifukwa anatsata njira zoyipa
    ndi kuyiwala Yehova Mulungu wawo.

22 Inu mukuti, “Bwererani, anthu osakhulupirika;
    ndidzachiritsa kubwerera mʼmbuyo kwanu.”

“Inde, tidzabwerera kwa Inu
    pakuti ndinu Yehova Mulungu wathu.
23 Ndithu kupembedza pa magomo
    komanso kuchita maphwando pa mapiri zilibe phindu.
Zoonadi chipulumutso cha Israeli
    chili mwa Yehova Mulungu wathu basi.
24 Kuyambira pa ubwana wathu milungu yochititsa manyazi ija yakhala ikutiwonongetsa phindu
    la ntchito za makolo athu,
nkhosa ndi ngʼombe zawo,
    ana awo aamuna ndi aakazi.
25 Tilekeni tigone pansi mwa manyazi,
    ndipo kunyozeka kwathu kutiphimbe.
Paja tachimwira Yehova Mulungu wathu,
    ife pamodzi ndi makolo athu
kuyambira nthawi ya ubwana wathu mpaka lero lino
    sitinamvere Yehova Mulungu wathu.”
“Ngati mukufuna kubwerera, inu Aisraeli,
    bwererani kwa Ine,”
            akutero Yehova.
“Chotsani mafano anu onyansa pamaso panga
    ndipo musasocherenso.
Muzilumbira mokhulupirika ndiponso mwa chilungamo
    kuti, ‘Pali Yehova wamoyo.’
Mukatero anthu a mitundu ina yonse adzandipempha kuti ndiwadalitse
    ndipo adzanditamanda.”

Zimene Yehova akunena kwa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu ndi izi:

“Limani masala anu
    musadzale pakati pa minga.
Dziperekeni nokha kwa Ine
    kuti munditumikire ndi mtima wanu wonse,
    inu anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu.
Muzichita zimenezi kuopa kuti mkwiyo wanga ungabuke ngati moto ndi kukutenthani,
    chifukwa cha ntchito zanu zoyipazo
    popanda wina wowuzimitsa.

Adani Ochokera Kumpoto kwa Yuda

“Lengeza ku Yuda ndi kulalikira mu Yerusalemu kuti,
    ‘Lizani lipenga mʼdziko lonse!’
Ndipo fuwulani kuti,
    ‘Sonkhanani!
    Tiyeni tithawire ku mizinda yotetezedwa!’
Kwezani mbendera kuyangʼana ku Ziyoni!
    Musachedwe, thawani kuti mupulumuke!
Pakuti Ine ndikubweretsa chilango kuchokera kumpoto,
    kudzakhala chiwonongeko choopsa.”

Monga mkango umatulukira mʼngaka yake
    momwemonso wowononga mayiko
wanyamuka ndi kutuluka ku mbuto yake.
    Watero kuti awononge dziko lanu.
Mizinda yanu idzakhala mabwinja
    popanda wokhalamo.
Choncho valani ziguduli,
    lirani ndi kubuwula,
pakuti mkwiyo waukulu wa Yehova
    sunatichokere.

“Pa tsiku limenelo, mfumu ndi nduna zake adzataya mtima,
    ansembe adzachita mantha kwambiri,
ndipo aneneri adzathedwa nzeru,”
    akutero Yehova.

10 Ndipo ine ndinati, “Haa, Ambuye Yehova, ndithu munawanyenga anthu awa pamodzi ndi Yerusalemu pamene munanena kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’ chonsecho lupanga lili pakhosi pathu.”

11 Nthawi imeneyo anthu awa ndi Yerusalemu adzawawuza kuti, “Mphepo yotentha yochokera ku magomo a mʼchipululu ikuwomba pa anthu anga, osati mphepo yopeta kapena yoyeretsa; 12 koma mphepo yamphamvu kwambiri yochokera kwa Ine. Tsono ndi Ineyo amene ndikuwaweruza.”

13 Taonani, adani akubwera ngati mitambo,
    magaleta awo akubwera ngati kamvuluvulu,
akavalo awo ndi aliwiro kupambana chiwombankhanga.
    Tsoka ilo! Tawonongeka!
14 Iwe Yerusalemu, tsuka mtima wako kuchotsa zoyipa kuti upulumuke.
    Kodi maganizo ako oyipawo udzakhala nawo mpaka liti?
15 Pakuti amithenga akulalika mawu mʼdziko la Dani;
    akulengeza za masautso kuchokera ku mapiri a Efereimu.
16 Iwo akuti, “Fotokozani zimenezi kwa anthu a mitundu ina,
    lengezani zimenezi mu Yerusalemu kuti,
‘Ankhondo akubwera kuchokera ku dziko lakutali,
    akufuwula ndi kudzazinga mizinda ya Yuda.
17 Azinga Yerusalemu ngati anthu olondera munda,
    chifukwa Yerusalemu wandiwukira,’ ”
            akutero Yehova.
18 “Makhalidwe anu ndi zochita zanu
    zakubweretserani zimenezi.
Chimenechi ndiye chilango chanu.
    Nʼchowawa kwambiri!
    Nʼcholasa mpaka mu mtima!”

19 Mayo, mayo,
    ndikumva kupweteka!
Aa, mtima wanga ukupweteka,
    ukugunda kuti thi, thi, thi.
    Sindingathe kukhala chete.
Pakuti ndamva kulira kwa lipenga;
    ndamva mfuwu wankhondo.
20 Tsoka limatsata tsoka linzake;
    dziko lonse lasanduka bwinja.
Mwadzidzidzi matenti athu awonongedwa,
    mwa kanthawi kochepa nsalu zake zotchinga zagwetsedwa.
21 Kodi ndikhale ndikuona mbendera ya nkhondo,
    ndi kumva kulira kwa lipenga mpaka liti?

22 Yehova akuti, “Anthu anga ndi zitsiru;
    iwo sandidziwa.
Iwo ndi ana opanda nzeru;
    samvetsa chilichonse.
Ali ndi luso lochita zoyipa,
    koma sadziwa kuchita zabwino.”

23 Ndinayangʼana dziko lapansi,
    ndipo linali lopanda anthu ndi lopanda kanthu;
ndinayangʼana thambo,
    koma linalibe kuwala kulikonse.
24 Ndinayangʼana mapiri,
    ndipo ankagwedezeka;
    magomo onse ankangosunthira uku ndi uku.
25 Ndinayangʼana, ndipo sindinaone anthu;
    mbalame iliyonse ya mlengalenga inali itathawa.
26 Ndinayangʼana, dziko lachonde linali litasanduka chipululu;
    mizinda yake yonse inali itasanduka bwinja
    pamaso pa Yehova, chifukwa cha mkwiyo wake.

27 Yehova akuti,

“Dziko lonse lidzasanduka chipululu
    komabe sindidzaliwononga kotheratu.
28 Chifukwa chake dziko lapansi lidzalira
    ndipo thambo lidzachita mdima,
pakuti ndayankhula ndipo sindidzafewa mtima,
    ndatsimikiza ndipo sindidzabwerera mʼmbuyo.”

29 Pakumva phokoso la okwera pa akavalo ndi la anthu oponya mivi,
    anthu a mʼmizinda adzathawa.
Ena adzabisala ku nkhalango;
    ena adzakwera mʼmatanthwe
mizinda yonse nʼkuyisiya;
    popanda munthu wokhalamo.

30 Iwe Yerusalemu, ndiwe bwinja!
    Ukutanthauza chiyani kuvala zovala zofiira
    ndi kuvalanso zokometsera zagolide?
Ngakhale udzikonze maso ako powapaka zokometsera,
    ukungodzivuta chabe.
Zibwenzi zako zikukunyoza;
    zikufuna kuchotsa moyo wako.

31 Ndikumva kulira ngati kwa mayi pa nthawi yake yobereka,
    kubuwula ngati kwa mayi amene akubereka mwana wake woyamba.
Kuliraku ndi kwa anthu a mu Ziyoni, wefuwefu.
    Atambalitsa manja awo nʼkumati,
“Kalanga ife! Tikukomoka.
    Moyo wathu waperekedwa kwa anthu otipha.”

Palibe Munthu Wolungama

“Pitani uku ndi uku mʼmisewu ya Yerusalemu,
    mudzionere nokha,
    funafunani mʼmabwalo ake.
Ngati mungapeze munthu mmodzi
    amene amachita zachilungamo ndi kufunafuna choonadi,
    ndipo ndidzakhululukira mzinda uno.
Ngakhale anthu akulumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo,’
    komabe akungolumbira mwachinyengo.”

Inu Yehova, kodi suja mumafuna anthu onena zoona?
    Inu munawakantha anthuwo, koma sanamve kupweteka;
    munawaphwanya anthuwo, koma sanatengepo phunziro.
Anawumitsa mitima yawo ngati mwala
    ndipo anakaniratu kulapa.
Ndiye ndinati, “Awa ndi amphawi chabe;
    anthu ochita zopusa.
Sadziwa njira ya Yehova,
    sazindikira zimene Mulungu wawo amafuna.
Tsono ndidzapita kwa atsogoleri
    ndi kukayankhula nawo;
ndithu iwo amadziwa njira ya Yehova,
    amadziwa zomwe Mulungu wawo amafuna.”
Koma ayi, iwonso anathyola goli la Yehova
    ndipo anadula msinga zawo.
Choncho mkango wochokera ku nkhalango udzawapha,
    mmbulu wochokera ku thengo udzawawononga,
kambuku adzawabisalira pafupi ndi mizinda yawo
    kuti akhadzule aliyense amene adzayesera kutuluka mʼmizindamo
pakuti kuwukira kwawo ndi kwakukulu
    ndipo abwerera mʼmbuyo kwambiri.

Yehova akuti, “Kodi ndingakukhululukireni bwanji ndi zimene mwachita?
    Ana anu andisiya Ine
    ndipo amapembedza milungu imene si milungu konse.
Ine ndinawapatsa zonse zimene ankasowa,
    komabe iwo anachita chigololo
    namasonkhana ku nyumba za akazi achiwerewere.
Monga amachitira akavalo onenepa akamamemesa,
    aliyense wa iwo ankathamangira mkazi wa mnzake.
Tsono ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi?”
    akutero Yehova.
“Kodi nʼkuleka kuwulipsira
    mtundu woterewu?

10 “Pitani ku minda yake ya mipesa ndi kukayiwononga,
    koma musakayiwononge kotheratu.
Sadzani nthambi zake
    pakuti anthu amenewa si a Yehova.
11 Nyumba ya Israeli ndi nyumba ya Yuda
    onse akhala osakhulupirika kotheratu kwa Ine.”

12 Iwowa ankanama ponena za Yehova kuti,
    “Yehova sangachite zimenezi!
Choyipa sichidzatigwera;
    sitidzaona nkhondo kapena njala.
13 Mawu a aneneri azidzangopita ngati mphepo;
    ndipo mwa iwo mulibe uthenga wa Yehova.
    Choncho zimene amanena zidzawachitikira okha.”

14 Chifukwa chake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse akuti,

“Popeza kuti anthu awa ayankhula mawu amenewa,
    tsono mawu anga ndidzawasandutsa moto mʼkamwa mwako
    ndipo anthu awa ndidzawasandutsa nkhuni zimene moto udzapserezeretu.
15 Inu Aisraeli,” Yehova akuti,
    “Ndikukubweretserani mtundu wa anthu ochokera kutali,
ndi mtundu umene sunagonjetsedwepo,
    mtundu wakalekale umene chiyankhulo chawo inu simuchidziwa,
    zimene akunena inu simungazimvetse.
16 Zida zawo za nkhondo zapha anthu ambirimbiri;
    onsewo ndi ankhondo amphamvu okhaokha.
17 Adzakudyerani zokolola zanu ndi chakudya chanu,
    adzapha ana anu aamuna ndi aakazi;
adzakupherani nkhosa zanu ndi ngʼombe zanu,
    adzawononga mpesa wanu ndi mikuyu yanu.
Ndi malupanga awo adzagwetsa
    mizinda yanu yotetezedwa imene mumayidalira.

18 “Komabe pa masiku amenewo sindidzakuwonongani kotheratu,” akutero Yehova. 19 Ndipo pamene anthu adzafunsa Yehova kuti, “Chifukwa chiyani Yehova Mulungu wathu wachita zimenezi?” Iwe udzawawuze kuti, “Monga momwe mwasiyira Ine ndi kutumikira milungu yachilendo mʼdziko mwanu, momwemonso mudzatumikira anthu a mʼdzikonso lachilendo.”

20 “Lengeza izi kwa ana a Yakobo
    ndipo mulalikire kwa anthu a ku Yuda kuti,
21 Imvani izi, inu anthu opusa ndi opanda nzeru,
    inu amene maso muli nawo koma simupenya,
    amene makutu muli nawo koma simumva.
22 Kodi simuyenera kuchita nane mantha?”
            Akutero Yehova.
    “Kodi simuyenera kunjenjemera pamaso panga?
Ine ndinayika mchenga kuti ukhale malire a nyanja,
    malire a muyaya amene nyanjayo singadutsepo.
Mafunde angawombe motani, koma sangathe kupitirira malirewo;
    mafunde angakokome motani, koma sangadutse malirewo.
23 Koma anthu awa ndi nkhutukumve ndiponso a mitima yowukira;
    andifulatira ndipo andisiyiratu.
24 Sananenepo mʼmitima mwawo kuti,
    ‘Tiyeni tizipembedza Yehova Mulungu wathu.
Kodi suja amatipatsa pa nthawi yake mvula yachizimalupsa ndi yamasika.
    Iye salephera konse kutipatsa nyengo ya kholola.’
25 Koma zolakwa zanu zalepheretsa zonsezi;
    ndipo machimo anu akumanitsani zabwino.

26 “Pakati pa anthu anga pali anthu ena oyipa
    amene amabisalira anzawo monga amachitira mlenje mbalame
    ndiponso ngati amene amatchera misampha kuti akole anthu anzawo.
27 Nyumba zawo zadzaza ndi chuma chochipeza mwa chinyengo
    ngati zikwere zodzaza ndi mbalame.
Nʼchifukwa chake asanduka otchuka ndi olemera.
28     Ndipo ananenepa ndi kukhala ndi matupi osalala.
Ntchito zawo zoyipa nʼzopanda malire;
    saweruza mwachilungamo nkhani ya ana amasiye kuti iyende bwino,
    sateteza ufulu wa anthu osauka.
29 Kodi Ine ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi?
    Kodi ndisawulipsire
mtundu woterewu?
            Akutero Yehova.

30 “Chinthu chothetsa nzeru ndi choopsa kwambiri
    chachitika mʼdzikomo:
31 Aneneri akunenera zabodza,
    ndipo ansembe akuvomerezana nawo,
ndipo anthu anga akukonda zimenezi.
    Koma mudzatani potsiriza?

1 Timoteyo 4

Malangizo kwa Timoteyo

Mzimu akunena momveka bwino kuti mʼmasiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chawo ndi kutsatira mizimu yonyenga ndi zinthu zophunzitsidwa ndi ziwanda. Ziphunzitso zimenezi zimachokera ku chinyengo cha anthu onama, amene chikumbumtima chawo chinamatidwa ndi chitsulo cha moto. Iwo amaletsa anthu ukwati ndi kuwalamula kuti asamadye zakudya zina, zimene Mulungu analenga kuti amene anakhulupirira ndi kudziwa choonadi, azidye moyamika. Pakuti chilichonse chimene Mulungu analenga ndi chabwino, ndipo chilichonse chisasalidwe, akamachilandira moyamika, pakuti chimayeretsedwa ndi mawu a Mulungu ndi pemphero.

Ngati abale uwalangiza zimenezi, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa mʼchoonadi cha chikhulupiriro ndi mʼchiphunzitso chabwino chimene wakhala ukutsata. Koma upewe nkhani zachabe ndi nthano za amayi okalamba; mʼmalo mwake udziphunzitse kukhala moyo wolemekeza Mulungu. Pakuti kulimbitsa thupi kumapindulitsapo pangʼono, koma moyo woopa Mulungu umapindulitsa pa zonse. Umatilonjeza moyo pa moyo uno ndiponso pa moyo umene ukubwerawo.

Amenewa ndi mawu odalirika ndi oyenera kuwalandira kwathunthu. 10 Nʼchifukwa chake timagwira ntchito molimbika ndi kuyesetsa, chifukwa tayika chiyembekezo chathu mwa Mulungu wamoyo, amene ndi Mpulumutsi wa anthu onse, koma makamaka wa amene amakhulupirira.

11 Lamulira ndi kuphunzitsa zinthu zimenezi. 12 Usalole kuti wina akupeputse chifukwa ndiwe wachinyamata, koma khala chitsanzo kwa okhulupirira pa mayankhulidwe, pa makhalidwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima. 13 Mpaka nditabwera, udzipereke powerenga mawu a Mulungu kwa anthu, kulalikira ndi kuphunzitsa. 14 Usanyozere mphatso yako yomwe inapatsidwa kwa iwe kudzera mʼmawu auneneri pamene gulu la akulu ampingo linakusanjika manja.

15 Uzichita zimenezi mosamalitsa ndi modzipereka kwathunthu, kuti aliyense aone kuti ukupita mʼtsogolo. 16 Samala kwambiri moyo wako ndi ziphunzitso zako. Uzichitabe zimenezi chifukwa ukatero, udzadzipulumutsa ndiponso udzapulumutsa okumvetsera.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.