Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 62-64

Dzina Latsopano la Ziyoni

62 Chifukwa chokonda Ziyoni sindidzakhala chete,
    chifukwa chokonda Yerusalemu sindidzakhala chete,
mpaka chilungamo chake chitaoneka poyera ngati kuwala,
    ndi chipulumutso chake chitaoneka ngati sakali yoyaka.
Mitundu ya anthu idzaona iwe utapambana pa nkhondo
    ndipo mafumu onse adzaona ulemerero wako.
Adzakuyitanira dzina latsopano
    limene adzakupatse ndi Yehova.
Udzakhala ngati chipewa chaulemerero mʼdzanja la Yehova,
    ndi ngati nduwira yaufumu mʼdzanja la Mulungu wako.
Sadzakutchanso “Wosiyidwa,”
    ndipo dziko lako silidzatchedwanso “Chipululu.”
Koma dzina lako latsopano lidzakhala “Ndakondwera naye.”
    Ndipo dziko lako lidzatchedwa “Wokwatiwa.”
Chifukwa Yehova akukondwera nawe,
    ndipo adzakhala ngati mwamuna wa dziko lako.
Monga mnyamata amakwatira namwali,
    momwenso mmisiri wodzakumanga adzakukwatira;
monga mkwati amakondwera ndi mkwatibwi,
    chonchonso Mulungu adzakondwera nawe.

Iwe Yerusalemu, pa malinga ako ndayikapo alonda;
    sadzakhala chete usana kapena usiku.
Inu amene mumakumbutsa Yehova za malonjezo ake
    musapumule.
Musamupatse mpata wopuma mpaka atakhazikitsa Yerusalemu
    kukhala mzinda umene dziko lapansi lidzawutamande.

Yehova analumbira atakweza dzanja lake.
    Anati,
“Sindidzaperekanso tirigu wako
    kuti akhale chakudya cha adani ako,
ndipo alendo sadzamwanso vinyo wako watsopano
    pakuti unamuvutikira.
Koma amene amakakolola ndiwo amene adzadye buledi
    ndi kutamanda Yehova,
ndipo amene amasonkhanitsa pamodzi mphesa ndiwo amene adzamwe vinyo
    mʼmabwalo a Nyumba yanga.”

10 Tulukani, dutsani pa zipata!
    Konzerani anthu njira.
Lambulani, lambulani msewu waukulu!
    Chotsani miyala.
Kwezani mbendera kuti mitundu ya anthu izione.

11 Yehova walengeza
    ku dziko lonse lapansi kuti,
Awuzeni anthu a ku Yerusalemu kuti,
    “Taonani, chipulumutso chanu chikubwera;
Yehova akubwera ndi mphotho yake
    akubwera nazo zokuyenerani.”
12 Iwo adzatchedwa Anthu Opatulika,
    owomboledwa a Yehova;
ndipo adzakutchani “Okondwa a Yehova”
    “Mzinda umene Yehova sanawusiye.”

Yehova Agonjetsa Anthu a Mitundu Ina

63 Kodi ndani uyo akubwera kuchokera ku Edomu,
    atavala zovala za ku Bozira za madontho ofiira?
Kodi uyu ndani, amene wavala zovala zokongola,
    akuyenda mwa mphamvu zake?

“Ndi Ineyo, woyankhula zachilungamo
    ndiponso wamphamvu zopulumutsa.”

Nanga bwanji zovala zanu zili psuu,
    ngati za munthu wofinya mphesa?

“Ndapondereza ndekha anthu a mitundu ina ngati mphesa,
    palibe ndi mmodzi yemwe anali nane.
Ndinawapondereza ndili wokwiya
    ndipo ndinawapondereza ndili ndi ukali;
magazi awo anadothera pa zovala zanga,
    ndipo zovala zanga zonse zinathimbirira.
Pakuti ndinatsimikiza mu mtima mwanga kuti lafika tsiku lolipsira anthu anga;
    ndipo chaka cha kuwomboledwa kwanga chafika.
Ndinayangʼana ndipo panalibe munthu wondithandiza.
    Ndinadabwa kwambiri kuti panalibe wondichirikiza;
choncho ndinapambana ndi mphamvu zanga,
    ndipo mkwiyo wanga unandilimbitsa.
Ndinapondereza mitundu ya anthu ndili wokwiya;
    ndipo ndinawasakaza
    ndipo ndinathira magazi awo pansi.”

Matamando ndi Pemphero

Ndidzafotokoza za kukoma mtima kwa Yehova,
    ntchito zimene Iye ayenera kutamandidwa.
    Ndidzatamanda Yehova chifukwa cha zonse zimene watichitira.
Inde, mwa chifundo ndi kukoma mtima kwake
    Yehova wachitira nyumba ya Israeli
    zinthu zabwino zambiri.
Yehova anati, “Ndithu awa ndi anthu anga,
    ana anga amene sadzandinyenga Ine.”
    Choncho anawapulumutsa.
Iyenso anasautsidwa mʼmasautso awo onse,
    ndipo mngelo wochokera kwa Iye anawapulumutsa.
Mwa chikondi ndi chifundo chake iye anawapulumutsa,
    anawanyamula ndikuwatenga
    kuyambira kale lomwe.
10 Komabe iwo anawukira
    ndi kumvetsa chisoni Mzimu Woyera.
Motero Yehova anatembenuka nakhala mdani wawo
    ndipo Iye mwini anamenyana nawo.

11 Pamenepo anthu ake anakumbukira masiku amakedzana,
    masiku a Mose mtumiki wake;
ndipo anafunsa kuti, “Ali kuti Yehova amene anawawolotsa pa nyanja,
    pamodzi ndi Mose mʼbusa wawo?
Ali kuti Iye amene anayika
    Mzimu Woyera pakati pawo?
12 Ali kuti amene anachita zinthu zodabwitsa
    ndi mphamvu zake zazikulu kudzera mwa Mose?
Ali kuti amene anagawa madzi pa nyanja anthu ake akuona,
    kuti dzina lake limveke mpaka muyaya,
13 amene anawayendetsa pa nyanja yozama?
Monga kavalo woyendayenda mʼchipululu,
    iwo sanapunthwe;
14 Mzimu Woyera unawapumulitsa
    ngati mmene ngʼombe zimapumulira.
Umu ndi mmene Inu munatsogolera anthu anu
    kuti dzina lanu lilemekezeke.”

15 Inu Yehova amene muli kumwambako, pa mpando wanu wolemekezeka,
    wopatulika ndi waulemerero, tiyangʼaneni ife.
Kodi changu chanu ndi mphamvu zanu zili kuti?
    Simukutionetsanso kukoma mtima kwanu ndi chifundo chanu.
16 Koma Inu ndinu Atate athu,
    ngakhale Abrahamu satidziwa
    kapena Israeli kutivomereza ife;
Inu Yehova, ndinu Atate athu,
    kuyambira kale dzina lanu ndinu Mpulumutsi wathu.
17 Chifukwa chiyani, Inu Yehova, mukutisocheretsa pa njira zanu?
    Bwanji mukutilola kuti tikhale owuma mitima kotero kuti sitikukuopaninso?
Bwererani chifukwa cha atumiki anu;
    mafuko a anthu amene ali cholowa chanu.
18 Anthu anu atangokhala pa malo anu opatulika pa kanthawi kochepa,
    adani athu anasakaza malo anu opatulika.
19 Ife tili ngati anthu amene
    simunawalamulirepo
    ngati iwo amene sanakhalepo anthu anu.
64 Inu Yehova, bwanji mukanangongʼamba mlengalenga ndi kutsika pansi,
    kuti mapiri agwedezeke pamaso panu!
Monga momwe moto umatenthera tchire
    ndiponso kuwiritsa madzi,
tsikani kuti adani anu adziwe dzina lanu,
    ndiponso kuti mitundu ya anthu injenjemere pamaso panu.
Pakuti nthawi ina pamene munatsika munachita zinthu zoopsa zimene sitinaziyembekezere,
    ndipo mapiri anagwedezeka pamaso panu.
Chikhalire palibe ndi mmodzi yemwe anamvapo
    kapena kuona
Mulungu wina wonga Inu,
    amene amachitira zinthu zotere amene amadikira pa Iye.
Inu mumabwera kudzathandiza onse amene amakondwera pochita zolungama,
    amene amakumbukira njira zanu.
Koma Inu munakwiya,
    ife tinapitiriza kuchimwa.
    Kodi nanga tingapulumutsidwe bwanji?
Tonsefe takhala ngati anthu amene ndi odetsedwa,
    ndipo ntchito zathu zili ngati sanza za msambo;
tonse tafota ngati tsamba,
    ndipo machimo athu akutiwuluzira kutali ngati mphepo.
Palibe amene amapemphera kwa Inu
    kutekeseka kuti apemphe chithandizo kwa Inu;
pakuti mwatifulatira
    ndi kutisiya chifukwa cha machimo athu.

Komabe, Inu Yehova ndinu Atate athu.
    Ife ndife chowumba, Inu ndinu wowumba;
    ife tonse ndi ntchito ya manja anu.
Inu Yehova, musatikwiyire kopitirira muyeso
    musakumbukire machimo athu mpaka muyaya.
Chonde, mutiganizire, ife tikupempha,
    pakuti tonsefe ndi anthu anu.
10 Mizinda yanu yopatulika yasanduka chipululu;
    ngakhaletu Ziyoni wasanduka chipululu, Yerusalemu ndi wamasiye.
11 Nyumba yanu yopatulika ndi yaulemu, kumene makolo athu ankakutamandani,
    yatenthedwa ndi moto
    ndipo malo onse amene tinkawakonda asanduka bwinja.
12 Inu Yehova, zonse zachitikazi, kodi mungokhala osatithandiza?
    Kodi mudzapitirizabe kukhala chete ndi kutilangabe mopitirira muyeso?

1 Timoteyo 1

Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa lamulo la Mulungu, Mpulumutsi wathu ndiponso Khristu Yesu chiyembekezo chathu.

Kwa Timoteyo mwana wanga weniweni mʼchikhulupiriro.

Chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye athu zikhale ndi iwe.

Kutsutsa Aphunzitsi Onyenga

Monga ndinakupempha pamene ndinkapita ku Makedoniya, khala ku Efeso komweko kuti uletse anthu ena kuphunzitsa ziphunzitso zonyenga, kapena kumangoyika mitima pa nthano zopeka ndi kufufuza za mayina a makolo awo. Zinthu zotere zimapititsa mʼtsogolo mikangano mʼmalo mwa ntchito ya Mulungu yomwe ndi ya chikhulupiriro. Cholinga cha lamuloli ndi chikondi, chomwe chimachokera mu mtima woyera, chikumbumtima chabwino ndi chikhulupiriro choona. Anthu ena anapatuka pa zimenezi ndipo anatsata nkhani zopanda tanthauzo. Iwo amafuna kukhala aphunzitsi amalamulo, koma sadziwa zimene akunena, kapena zimene akufuna kutsimikiza.

Tikudziwa kuti Malamulo ndi abwino ngati munthu awagwiritsa ntchito bwino. Tikudziwanso kuti Malamulo sakhazikitsidwa chifukwa cha anthu olungama, koma ophwanya lamulo ndi owukira, osaopa Mulungu ndi ochimwa, wopanda chiyero ndi osapembedza; amene amapha abambo awo ndi amayi awo, kapena anthu ena. 10 Malamulo amayikidwa chifukwa cha anthu achigololo ndi ochita zadama ndi amuna anzawo, anthu ogulitsa akapolo, abodza ndi olumbira zabodza, ndi ochita chilichonse chotsutsana ndi chiphunzitso choona. 11 Chiphunzitso chimene chimagwirizana ndi Uthenga Wabwino wonena za ulemerero wa Mulungu wodala, umene Iye mwini anandisungitsa.

Chisomo cha Ambuye kwa Paulo

12 Ndikuthokoza Khristu Yesu Ambuye athu, amene anandipatsa mphamvu pa ntchitoyi. Iye ananditenga kukhala wokhulupirira, nandipatsa ntchito mu utumiki wake. 13 Ngakhale kuti kale ndinali wachipongwe, wozunza ndi wankhanza, anandichitira chifundo chifukwa ndinkachita mwaumbuli ndi mopanda chikhulupiriro. 14 Chisomo cha Ambuye athu chinatsanulidwa pa ine mochuluka, pamodzi ndi chikhulupiriro ndi chikondi zimene zili mwa Khristu Yesu.

15 Mawu odalirika ndi woyenera kuwavomereza kwathunthu ndi awa: Yesu Khristu anabwera pa dziko lapansi kudzapulumutsa ochimwa, ndipo mwa iwowo ine ndiye wochimwitsitsa. 16 Ndipo pa chifukwa chimenechi, Mulungu anandichitira chifundo, kuti mwa ine, wochimwitsitsa, Khristu Yesu aonetse kuleza mtima kwake konse kuti ndikhale chitsanzo cha omwe angathe kumukhulupirira ndi kulandira moyo wosatha. 17 Tsopano kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Ameni.

Ntchito ya Timoteyo

18 Mwana wanga Timoteyo, ndikukupatsa langizo ili molingana ndi maulosi amene aneneri ananena za iwe. Pamene ukumbukira mawu amenewa udzatha kumenya bwino nkhondo 19 utagwiritsitsa chikhulupiriro ndi chikumbumtima chabwino. Ena anazikana zimenezi motero chikhulupiriro chawo chinawonongeka. 20 Ena mwa amenewa ndi Humenayo ndi Alekisandro, amene ndinawapereka kwa Satana kuti aphunzire kusachita chipongwe Mulungu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.