Old/New Testament
Tchimo, Kuvomereza ndi Chipulumutso
59 Taonani, mkono wa Yehova si waufupi kuti sungathe kupulumutsa,
kapena khutu lake kuti ndilogontha kuti sangamve.
2 Koma zoyipa zanu zakulekanitsani
ndi Mulungu wanu;
ndipo wakufulatirani chifukwa cha machimo anu,
kotero Iye sadzamva.
3 Pakuti manja anu ali psuu ndi magazi.
Munayipitsa zala zanu ndi zamphulupulu.
Pakamwa panu payankhula zabodza,
ndipo lilime lanu lanena zinthu zoyipa.
4 Palibe amene akuyimba mnzake mlandu molungama,
palibe amene akupita ku mlandu moona mtima.
Iwo amadalira mawu opanda pake ndipo amayankhula mabodza;
amalingalira za mphulupulu ndipo amachita zoyipa.
5 Iwo amayikira mazira a mamba
ndipo amaluka ukonde wakangawude.
Aliyense amene adzadya mazira awo adzafa,
ndipo ngati dzira limodzi lasweka limatulutsa mphiri.
6 Ukonde wawo wa kangawude sangawuvale ngati chovala;
ndipo chimene apangacho sangachifunde.
Ntchito zawo ndi zoyipa,
ndipo amakonda kuchita zandewu ndi manja awo.
7 Amathamangira kukachita zoyipa;
sachedwa kupha anthu osalakwa.
Maganizo awo ndi maganizo oyipa;
kulikonse kumene amapita amasiyako bwinja ndi chiwonongeko.
8 Iwo sadziwa kuchita za mtendere;
zonse zimene amachita nʼzopanda chilungamo.
Njira zawo zonse nʼzokhotakhota;
aliyense oyenda mʼnjira zimenezo sadzapeza mtendere.
9 Anthu akuti, “Chifukwa cha zimenezi chilungamo chatitalikira;
ndipo chipulumutso sichitifikira.
Timafunafuna kuwala koma timangopeza mdima okhaokha;
tinayembekezera kuyera koma timayenda mu mdima wandiweyani.
10 Timapapasapapasa khoma ngati munthu wosaona,
kuyangʼanayangʼana njira ngati anthu opanda maso.
Timapunthwa dzuwa lili paliwombo ngati kuti ndi usiku;
timakhala pansi mu mdima ngati anthu akufa.
11 Tonse timabangula ngati zimbalangondo:
Timalira modandaula ngati nkhunda.
Tinayembekezera kuweruza kolungama; koma sitikupeza.
Timayembekezera chipulumutso koma chimakhala nafe kutali.”
12 Pakuti zolakwa zathu nʼzochuluka pamaso panu,
ndipo machimo athu akutsutsana nafe.
Zolakwa zathu zili ndi ife nthawi zonse
ndipo tikuvomereza machimo athu:
13 Tawukira ndi kumukana Yehova.
Tafulatira Mulungu wathu,
pa kupondereza anzathu ndi kupandukira Yehova,
ndi pa kuyankhula mabodza amene tawaganiza mʼmitima mwathu.
14 Motero kuweruza kolungama kwalekeka
ndipo choonadi chili kutali ndi ife;
kukhulupirika sikukupezekanso mʼmabwalo a milandu,
ndipo kuona mtima sikukupezekanso mʼmenemo.
15 Choonadi sichikupezeka kumeneko,
ndipo wina akakana kuchita nawo zoyipa amapeza mavuto.
Yehova anaziona zimenezi ndipo zinamunyansa
kuti panalibe chiweruzo cholungama.
16 Yehova anaona kuti panalibe ndi mmodzi yemwe,
Iye anadabwa kuti panalibe ndi mmodzi yemwe woti nʼkupembedzera;
Choncho mphamvu zake zomwe zinamuthandiza,
ndipo anadzilimbitsa ndi kulungama kwake;
17 Iye anavala chilungamo ngati chovala chachitsulo chapachifuwa,
ndipo kumutu kwake amavala chipewa chachipulumutso;
anavala kulipsira ngati chovala
ndipo anadzikuta ndi mkwiyo ngati chofunda.
18 Iye adzawabwezera chilango adani a anthu ake
molingana ndi zimene anachita,
adzaonetsa ukali kwa adani ake
ndi kubwezera chilango odana naye.
Adzalanga ngakhale okhala mayiko akutali.
19 Choncho akadzabwera ngati madzi
oyendetsedwa ndi mphepo yamphamvu yamkuntho.
Anthu onse kuyambira kumadzulo mpaka kummawa
adzaopa dzina la Yehova ndi ulemerero wake.
20 “Mpulumutsi adzabwera ku Ziyoni
kudzapulumutsa anthu a fuko la Yakobo amene analapa machimo awo,”
akutero Yehova.
21 Yehova akuti, “Kunena za pangano lake ndi iwo, Mzimu wanga umene uli pa inu, ndiponso mawu anga amene ndayika mʼkamwa mwanu sadzachoka mʼkamwa mwanu, kapena kuchoka mʼkamwa mwa ana anu, kapena mʼkamwa mwa zidzukulu zawo kuyambira tsopano mpaka kalekale,”
akutero Yehova.
Ulemerero wa Ziyoni
60 “Dzuka, wala, pakuti kuwala kwako kwafika,
ndipo ulemerero wa Yehova wakuwalira.
2 Taona, mdima waphimba dziko lapansi
ndipo mdima wandiweyani wagwa pa anthu a mitundu ina,
koma Yehova adzakuwalira iwe,
ndipo ulemerero wake udzaoneka pa iwe.
3 Mitundu ya anthu idzatsata kuwunika kwako
ndipo mafumu adzalondola kunyezimira kwa mʼbandakucha wako.
4 “Tukula maso ako, yangʼanayangʼana ndipo ona zimene zikuchitika.
Onse akusonkhana ndipo akubwera kwa iwe;
ana ako a amuna akubwera kuchokera kutali
ndipo ana ako aakazi anyamulidwa mʼmanja.
5 Ukadzaona zimenezi udzasangalala kwambiri,
mtima wako udzalumpha ndi kudzaza ndi chimwemwe;
chuma chakunyanja chidzabwera kwa iwe
chuma cha mitundu ya anthu chidzabwera kwa iwe.
6 Gulu la ngamira lidzaphimba dziko lako,
ngamira zingʼonozingʼono zidzachokera ku Midiyani ndi ku Efai.
Ndipo onse a ku Seba adzabwera
atanyamula golide ndi lubani
uku akutamanda Yehova.
7 Ziweto zonse za ku Kedara adzazisonkhanitsa kwa inu,
nkhosa zazimuna za ku Nabayoti zidzakutumikirani;
zidzalandiridwa monga chopereka pa guwa langa la nsembe,
ndipo ndidzakongoletsa Nyumba yanga.
8 “Kodi ndi zayani izo zikuwuluka ngati mitambo,
ngati kapena nkhunda zobwerera ku zisa zawo?
9 Ndithu, izi ndi sitima za pa madzi zochokera ku mayiko akutali;
patsogolo pali sitima zapamadzi za ku Tarisisi,
zikubweretsa ana ako ochokera kutali,
pamodzi ndi siliva wawo ndi golide wawo,
kudzalemekeza Yehova Mulungu wako,
Woyerayo wa Israeli,
pakuti Iye wakuvekani inu ulemerero.
10 “Alendo adzamanganso malinga ako,
ndipo mafumu awo adzakutumikira.
Ngakhale ndinakukantha ndili wokwiya,
koma tsopano ndidzakukomera mtima ndikukuchitira chifundo.
11 Zipata zako zidzakhala zotsekula nthawi zonse,
sadzazitseka nthawi zonse, usana ndi usiku,
kotero anthu adzabwera kwa iwe ndi chuma chawo,
akuyenda pa mdipiti mafumu awo ali patsogolo.
12 Pakuti mtundu wa anthu ndi mafumu amene sakutumikira iwe;
adzawonongeka kotheratu.
13 “Adzabwera nayo kwa iwe mitengo ya payini,
mkuyu ndi naphini imene ili mʼnkhalango ya Lebanoni
kuti adzakongoletsere malo a nyumba yanga yopatulika;
ndipo ndidzalemekeza malo amene Ine ndimapondapo.
14 Ana aja amene anakuzunzani adzabwera ndipo adzakugwadirani;
onse amene anakunyozani adzagwada pansi pa mapazi anu.
Ndipo adzakutchani kuti Mzinda wa Yehova;
Ziyoni mzinda wa Woyerayo wa Israeli.
15 “Ngakhale anthu anakusiya nadana nawe,
koma Ine ndidzakukuza mpaka muyaya,
ndipo udzakhala malo a chimwemwe
cha anthu amibado yonse.
16 Udzamwa mkaka wa mitundu ya anthu
ndi kuleredwa pa maere aufumu,
motero udzadziwa kuti Ine Yehova, ndine Mpulumutsi wako,
Momboli wako ndiye Wamphamvu wa Yakobo.
17 Ndidzakupatsa golide mʼmalo mwa mkuwa,
ndi siliva mʼmalo mwa chitsulo.
Ndidzakupatsa mkuwa mʼmalo mwa thabwa
ndi chitsulo mʼmalo mwa miyala.
Olamulira ako adzakhala a mtendere.
Ndidzasandutsa okulamulira kuti akhale achilungamo.
18 Ziwawa sizidzamvekanso mʼdziko lako,
bwinja kapena chiwonongeko sizidzapezeka mʼdziko lako,
ndidzakhala malinga ako okuteteza
ndipo udzanditamanda.
19 Sipadzakhala dzuwa kuti likuwunikire,
kapena mwezi kuti uwunikire usiku,
pakuti Yehova ndiye adzakhale kuwunika kwako kwa muyaya,
ndipo Mulungu wako adzakhala ulemerero wako.
20 Dzuwa lako silidzalowanso,
ndipo mwezi wako sudzazimiriranso;
Yehova adzakhala kuwunika kwako kwamuyaya,
ndipo masiku a mavuto ako adzatha.
21 Ndipo anthu ako onse adzakhala olungama
ndipo dzikolo lidzakhala lawo mpaka muyaya.
Iwo ndi mphukira imene Ine ndayidzala,
ntchito ya manja anga,
kuti aonetse ulemerero wanga.
22 Kabanja kakangʼono kadzasanduka fuko,
kafuko kakangʼono kudzasanduka mtundu wamphamvu.
Ine ndine Yehova,
nthawi yake ikafika ndidzazichita zimenezi mofulumira.”
Uthenga Wabwino wa Yehova
61 Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine,
chifukwa Yehova wandidzoza
kuti ndilalikire uthenga wabwino kwa anthu osauka.
Wandituma kuti ndikatonthoze anthu osweka mtima,
ndikalengeze kwa akapolo kuti alandire ufulu
ndiponso kuti ndikamasule a mʼndende.
2 Wandituma kuti ndikalengeze nthawi imene Yehova adzapulumutsa anthu ake;
za tsiku limene Yehova adzalanga adani a anthu ake.
Wandituma kuti ndikatonthoze olira.
3 Wandituma kuti ndiwakonzere olira a ku Ziyoni,
nkhata ya maluwa yokongola
mʼmalo mwa phulusa,
ndiwapatse mafuta achikondwerero
mʼmalo mwa kulira.
Ndiwapatse chovala cha matamando
mʼmalo mwa mtima wopsinjika.
Ndipo iwo adzatchedwa mitengo ya thundu yamphamvu yachilungamo,
yoyidzala Yehova
kuti Iye mwini apezemo ulemerero wake.
4 Adzamanganso mabwinja akale a mzinda
ndipo malo amene anawonongeka kalekale aja adzakonzanso.
Adzakonzanso mizinda imene inapasuka,
imene yakhala yowonongeka kwa nthawi yayitali kwambiri.
5 Anthu achilendo adzakutumikirani; adzazidyetsa ziweto zanu;
iwo adzagwira ntchito mʼminda yanu ya mpesa.
6 Ndipo inu mudzatchedwa ansembe a Yehova,
adzakutchulani kuti ndinu atumiki a Mulungu wathu.
Mudzadyerera chuma cha mitundu ya anthu,
ndipo mudzanyadira ulemu umene mwalandira.
7 Chifukwa manyazi awo anali owirikiza;
ndi kuti munalandira
chitonzo ndi kutukwana,
adzakondwera ndi cholowa chawo,
tsono adzalandira cholowa chawo cha chigawo cha dziko mowirikiza,
ndipo chimwemwe chamuyaya chidzakhala chawo.
8 “Pakuti Ine Yehova, ndimakonda chilungamo;
ndimadana ndi zakuba ndi zoyipa.
Anthu anga ndidzawapatsa mphotho mokhulupirika
ndikupangana nawo pangano losatha.
9 Ana awo adzakhala odziwika pakati pa mitundu ya anthu
ndipo adzukulu awo adzakhala otchuka pakati pa anthu a mitundu ina.
Aliyense wowaona adzazindikira
kuti ndi anthu amene Yehova wawadalitsa.”
10 Ine ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Yehova;
moyo wanga ukukondwera chifukwa cha Mulungu wanga.
Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso,
ndipo wandiveka mkanjo wachilungamo.
Zili ngati mkwati wovala nkhata ya maluwa mʼkhosi mwake,
ndiponso ngati mkwatibwi wovala mikanda yamtengowapatali.
11 Monga momwe nthaka imameretsa mbewu
ndiponso monga munda umakulitsa mbewu zimene anadzala,
momwemonso Ambuye Yehova adzaonetsa chilungamo ndi matamando
pamaso pa mitundu yonse ya anthu.
Tipempherereni
3 Potsiriza, abale, mutipempherere kuti uthenga wa Ambuye ufalikire msanga ndi kulemekezedwa monga momwe munachitira inu. 2 Ndipo pempherani kuti tilanditsidwe mʼmanja mwa anthu ovuta ndi oyipa, pakuti si onse amene ali nacho chikhulupiriro. 3 Koma Ambuye ndi wokhulupirika, ndipo adzakulimbikitsani ndi kukutetezani kwa woyipayo. 4 Tili ndi chikhulupiriro mwa Ambuye kuti mukuchita zonse ndipo mudzapitirira kuchita zimene tinakulamulirani. 5 Ambuye atsogolere mitima yanu kuti mudziwe chikondi cha Mulungu ndiponso kupirira kumene Khristu amapereka.
Awachenjeza za Kusagwira Ntchito
6 Abale, tikukulamulani mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, kuti mupewe mʼbale aliyense amene ndi waulesi ndi wachisokonezo, wosafuna kutsata zimene tinakuphunzitsani. 7 Pakuti inu mukudziwa zimene muyenera kuchita pofuna kutitsatira. Ife sitinali alesi pamene tinali nanu 8 ndipo sitinadye chakudya cha aliyense osalipira. Komatu tinkagwira ntchito mwamphamvu usiku ndi usana kuti tisakhale cholemetsa kwa aliyense. 9 Sitinachite zimenezi chifukwa choti tinalibe mphamvu zolamula kuti mutithandize koma kuti tikhale chitsanzo choti mutsatire. 10 Pakuti ngakhale pamene tinali nanu, tinakupatsani lamulo lakuti, “Munthu wosafuna kugwira ntchito, asadye.”
11 Ife tikumva kuti pakati panu pali ena amene ndi alesi. Iwo safuna kugwira ntchito, koma amangolowerera pa za eni. 12 Mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, tikuwalamula ndi kuwakakamiza kuti azigwira ntchito mwabata ndi kumadya chakudya chodzigwirira ntchito okha. 13 Koma inu abale, musatope nʼkuchita zabwino.
14 Ngati wina aliyense akana kumvera malangizo athu a mʼkalatayi, mumuonetsetse ameneyo ndipo musayanjane naye kuti achite manyazi. 15 Komatu musamutenge kukhala mdani, koma muchenjezeni ngati mʼbale.
Malonje Otsiriza
16 Tsopano Ambuye mwini mtendere akupatseni mtendere nthawi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse.
17 Ine Paulo, ndikulemba malonje awa ndi dzanja langa, chimene ndi chizindikiro chodziwika mʼmakalata anga onse. Umo ndi mmene ndimalembera.
18 Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.