Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 47-49

Kugwa kwa Babuloni

47 “Tsika, ndi kukhala pa fumbi,
    iwe namwali, Babuloni;
khala pansi wopanda mpando waufumu,
    iwe namwali, Kaldeya
pakuti sadzakutchulanso wanthete kapena woyenera
    kumugwira mosamala.
Tenga mphero ndipo upere ufa;
    chotsa nsalu yako yophimba nkhope
kwinya chovala chako mpaka ntchafu
    ndipo woloka mitsinje.
Maliseche ako adzakhala poyera
    ndipo udzachita manyazi.
Ndidzabwezera chilango
    ndipo palibe amene adzandiletse.”

Woyerayo wa Israeli ndiye Mpulumutsi wathu,
    dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.

“Khala chete, ndipo lowa mu mdima,
    iwe namwali, Kaldeya;
chifukwa sadzakutchulanso
    mfumukazi ya maufumu.
Ndinawakwiyira anthu anga,
    osawasamalanso.
Ndinawapereka manja mwako,
    ndipo iwe sunawachitire chifundo.
Iwe unachitira nkhanza
    ngakhale nkhalamba.
Iwe unati, ‘Ine ndidzakhalapo nthawi zonse
    ngati mfumukazi.’
Koma sunaganizire zinthu izi
    kapena kusinkhasinkha za mmene ziti zidzathere.

“Ndipo tsopano, tamvera, iwe wongokonda zokondweretsawe,
    amene ukukhala mosatekesekawe,
umaganiza mu mtima mwako kuti,
    ‘Ine ndi Ine, ndipo kupatula ine palibenso wina.
Sindidzakhala konse mkazi wamasiye,
    ndipo ana anga sadzamwalira.’
Koma mʼkamphindi, ndiponso tsiku limodzi,
    zinthu ziwiri izi zidzakuchitikira:
    ana ako kukufera komanso kukhala mkazi wamasiye.
Zimenezi zidzakuchitikira kwathunthu
    ngakhale ali ndi amatsenga ambiri
    ndi mawula amphamvu.
10 Iwe unkadalira kuyipa kwako
    ndipo unati, ‘Palibe amene akundiona.’
Kuchenjera ndi nzeru zako zidzakusokoneza,
    choncho ukuganiza mu mtima mwako kuti,
    ‘Ine ndine basi, ndipo kupatula ine palibenso wina.’
11 Ngozi yayikulu idzakugwera
    ndipo sudzadziwa momwe ungayipewere ndi matsenga ako.
Mavuto adzakugwera
    ndipo sudzatha kuwachotsa;
chipasupasu chimene iwe sukuchidziwa
    chidzakugwera mwadzidzidzi.

12 “Pitiriza tsono kukhala ndi matsenga ako,
    pamodzi ndi nyanga zako zochulukazo,
    wakhala ukuzigwiritsa ntchito kuyambira ubwana wako.
Mwina udzatha kupambana
    kapena kuopsezera nazo adani ako.
13 Malangizo onse amene unalandira angokutopetsa basi!
    Abwere patsogolopa anthu amene amatanthauzira za kumwamba kuti adzakupulumutseni.
Abwere amene amayangʼana nyenyezi, ndi kumalosera mwezi ndi mwezi
    zimene ziti zidzakuchitikire.
14 Ndithudi, anthuwo ali ngati phesi;
    adzapsa ndi moto.
Sangathe kudzipulumutsa okha
    ku mphamvu ya malawi a moto.
Awa si makala a moto woti wina nʼkuwotha;
    kapena moto woti wina nʼkuwukhalira pafupi.
15 Umu ndi mmene adzachitire amatsenga,
    anthu amene wakhala ukugwira nawo ntchito
    ndi kuchita nawo malonda chiyambire cha ubwana wako.
Onse adzamwazika ndi mantha,
    sipadzakhala ndi mmodzi yemwe wokupulumutsa.”

Israeli ndi Nkhutukumve

48 “Mverani izi, inu nyumba ya Yakobo,
    inu amene amakutchani dzina lanu Israeli,
    ndinu a fuko la Yuda,
inu mumalumbira mʼdzina la Yehova,
    ndi kupemphera kwa Mulungu wa Israeli,
    ngakhale osati mʼchoonadi kapena mʼchilungamo.
Komabe inu mumadzitcha nzika za mzinda wopatulika
    ndipo mumadalira Mulungu wa Israeli,
    amene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse:
Zimene zinachitika poyamba ndinalosera kalekale,
    zinatuluka mʼkamwa mwanga ndipo ndinazilengeza;
    tsono mwadzidzidzi ndinachitapo kanthu ndipo zinachitikadi.
Pakuti Ine ndinadziwa kuti iwe ndiwe nkhutukumve
    wa nkhongo gwaa,
    wa mutu wowuma.
Ine ndinakuwuziratu zinthu izi kalekale lomwe;
    zisanachitike ndinazilengezeratu kwa iwe
kuti unganene kuti,
    ‘Fano langa ndilo lachita zimenezi,
    kapena kuti fano langa losema ndi kamulungu kanga kachitsulo ndiwo analamula kuti zimenezi zichitike.’
Inu munamva zinthu zimenezi.
    Kodi inu simungazivomereze?

“Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo ndidzakuwuzani zinthu zatsopano
    zinthu zobisika zimene simunazidziwe konse.
Zinthu zimenezi zikulengedwa tsopano lino, osati kalekale;
    munali musanazimve mpaka lero lino.
Choncho inu simunganene kuti,
    ‘Zimenezi ndiye ayi, ndinazidziwa kale.’
Inu simunazimvepo kapena kuzidziwa;
    makutu anu sanali otsekuka.
Tsono Ine ndinadziwa bwino kuti ndinu anthu achiwembu ndi kuti
    chiyambire ubwana wanu munatchedwa owukira.
Ine ndikuchedwetsa mkwiyo wanga chifukwa cha dzina langa.
    Ndikukulezerani ukali wanga kuti anthu andilemekeze.
    Sindidzakuwonongani kotheratu.
10 Taonani, ndinakuyeretsani ngati siliva;
    ndinakuyesani mʼngʼanjo yamasautso.
11 Chifukwa cha ulemu wanga, chifukwa cha ulemu wanga Ine ndikuchita zimenezi.
    Ndingalole bwanji kuti ndinyozeke?
    Ulemerero wanga sindidzawupereka kwa wina.

Kumasulidwa kwa Israeli

12 “Tamvera Ine, iwe Yakobo,
    Israeli, amene ndinakuyitana:
Mulungu uja Woyamba
    ndi Wotsiriza ndine.
13 Inde dzanja langa linamanga maziko a dziko lapansi,
    dzanja langa lamanja linafunyulula mlengalenga.
Ndi mawu anga ndinalenga kumwamba
    ndi dziko lapansi.

14 “Sonkhanani pamodzi inu nonse ndipo mvetserani:
    Ndani mwa mafano anu amene analoseratu za zinthu izi?
Wokondedwa wa Yehova uja adzachita
    zomwe Iye anakonzera Babuloni;
    dzanja lake lidzalimbana ndi Kaldeya.
15 Ine, Inetu, ndayankhula;
    ndi kumuyitana
ndidzamubweretsa ndine
    ndipo adzakwaniritsa zolinga zake.

16 “Bwerani pafupi ndipo mvetserani izi:

“Kuyambira pachiyambi sindinayankhule mobisa;
    pa nthawi imene zinkachitika zimenezi Ine ndinali pomwepo.”

Ndipo tsopano Ambuye Yehova wandipatsa Mzimu wake
    ndi kundituma.

17 Yehova, Mpulumutsi wanu,
    Woyerayo wa Israeli akuti,
“Ine ndine Yehova Mulungu wanu,
    amene ndimakuphunzitsa kuti upindule,
    ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuyitsata.
18 Ngati iwe ukanangosamalira zolamulira zanga,
    bwenzi mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje,
    ndi chipulumutso chako ngati mafunde a pa nyanja.
19 Zidzukulu zako zikanachuluka ngati mchenga,
    ana ako akanachuluka ngati fumbi;
dzina lawo silikanachotsedwa pamaso panga
    ndipo silikanafafanizidwa konse.”

20 Tulukani mʼdziko la Babuloni!
    Thawani dziko la Kaldeya!
Lengezani zimenezi ndi mawu a chisangalalo
    ndipo muzilalikire
mpaka kumathero a dziko lapansi;
    muzinena kuti, “Yehova wawombola Yakobo mtumiki wake.”
21 Iwo sanamve ludzu pamene Yehova ankawatsogolera mʼchipululu;
    anawapatsa madzi otuluka mʼthanthwe;
anangʼamba thanthwelo ndipo
    munatuluka madzi.

22 “Palibe mtendere kwa anthu ochimwa,” akutero Yehova.

Mtumiki wa Yehova

49 Mverani Ine, inu anthu a pa zilumba
    tcherani khutu, inu anthu a mayiko akutali:
Yehova anandiyitana ine ndisanabadwe,
    ananditchula dzina ndili mʼmimba ya amayi anga.
Iye anasandutsa pakamwa panga kukhala ngati lupanga lakuthwa,
    anandibisa mu mthunzi wa dzanja lake;
Iye anandisandutsa ngati muvi wakuthwa
    ndipo anandibisa mʼchimake.
Iye anati kwa ine, “Ndiwe mtumiki wanga, Israeli.
    Anthu adzanditamanda chifukwa cha iwe.”
Koma Ine ndinati, “Ine ndinkaganiza kuti ndinagwira ntchito
    ndi kuwononga mphamvu zanga pachabe,
koma ayi, zondiyenera zili mʼmanja a Yehova,
    ndipo mphotho yanga ili mʼmanja mwa Mulungu wanga.”

Yehova anandiwumba ine
    mʼmimba mwa amayi anga kuti ndikhale mtumiki wake
kuti ndibweze fuko la Yakobo kwa Iye
    ndi kusonkhanitsa Israeli kwa Iye,
choncho ndimalemekezeka mʼmaso mwa Yehova,
    ndipo ndimapeza mphamvu mwa Mulungu wanga.
Yehovayo tsono akuti,
“Nʼchinthu chochepa kwambiri kwa iwe kuti ukhale mtumiki wanga,
    kuti udzutse mafuko a Yakobo
    ndi kuwabweretsa kwawo Aisraeli amene anapulumuka.
Choncho iwe udzakhala ngati chowunikira,
    udzafikitsa uthenga wa chipulumutso changa ku mathero a dziko lapansi.”

Yehova Mpulumutsi ndi Woyerayo wa Israeli akuyankhula,
    Woyerayo wa Israeli akunena,
amene mitundu ya anthu inamuda,
    amenenso anali kapolo wa mafumu ankhanza uja kuti,
“Mafumu adzaona ntchito ya chipulumutso changa ndipo adzayimirira.
    Akalonga nawonso adzagwada pansi.
Zimenezi zidzachitika chifukwa cha Yehova amene ndi wokhulupirika
    ndi Woyerayo wa Israeli amene wakusankha iwe.”

Kubwezeretsedwa kwa Israeli

Yehova akuti,

“Pa nthawi imene ndinakukomera mtima ndinakuyankha,
    ndipo pa tsiku lachipulumutso ndinakuthandiza;
ndinakusunga ndi kukusandutsa
    kuti ukhale pangano kwa anthu,
kuti dziko libwerere mwakale
    ndi kuti cholowa changa chowonongeka chija ndichigawegawenso.
Ndidzawuza a mʼndende kuti atuluke
    ndi a mu mdima kuti aonekere poyera.

“Adzapeza chakudya mʼmphepete mwa njira
    ndi msipu pa mʼmalo owuma.
10 Iwo sadzamva njala kapena ludzu,
    kutentha kwa mʼchipululu kapena dzuwa silidzawapsereza;
chifukwa Iye amene amawachitira chifundo adzawatsogolera
    ndi kuwaperekeza ku akasupe a madzi.
11 Mapiri anga onse ndidzawasandutsa njira yoyendamo,
    ndipo misewu yanga yayikulu ndidzayikweza.
12 Taonani, anthu anga adzachokera kutali,
    ena kumpoto, ena kumadzulo,
    enanso adzachokera ku chigawo cha Asuwani.”

13 Imbani mwachimwemwe, inu zolengedwa zamlengalenga;
    kondwera, iwe dziko lapansi;
    imbani nyimbo inu mapiri!
Pakuti Yehova watonthoza mtima anthu ake,
    ndipo wachitira chifundo anthu ake ovutika.

14 Koma Ziyoni anati, “Yehova wandisiya,
    Ambuye wandiyiwala.”

15 “Kodi amayi angathe kuyiwala mwana wawo wakubere
    ndi kusachitira chifundo mwana amene anabereka iwo eni?
Ngakhale iye angathe kuyiwala,
    Ine sindidzakuyiwala iwe!
16 Taona, ndakulemba iwe mʼzikhantho zanga;
    makoma ako ndimawaona nthawi zonse.
17 Amisiri odzakumanganso akubwerera mofulumira,
    ndipo amene anakupasula akuchokapo.
18 Kweza maso ako ndipo uyangʼaneyangʼane
    ana ako onse akusonkhana ndipo akubwera kwa iwe.
Yehova akuti, ‘Ine Yehova wamoyo,
    anthu ako adzakhala ngati chinthu chodzikongoletsa
    chimene mkwatibwi wavala pa mkono pake.’

19 “Ngakhale unasanduka bwinja ndi kuwonongedwa
    ndipo dziko lako ndi kusakazidwa,
chifukwa cha kuchuluka kwa anthu malo okhalamo adzakhala operewera
    ndipo amene anakuwononga iwe aja adzakhala kutali.
20 Ana obadwa nthawi yako yachisoni
    adzanena kuti,
‘Malo ano atichepera,
    tipatse malo ena woti tikhalemo.’
21 Tsono iwe udzadzifunsa kuti,
    ‘Kodi ndani anandiberekera ana amenewa?
Ana anga onse anamwalira ndipo sindinathenso kukhala ndi ana ena;
    ndinapita ku ukapolo ndipo ndinachotsedwa.
    Ndani anawalera ana amenewa?
Ndinatsala ndekha,
    nanga awa, achokera kuti?’ ”

22 Zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi,

“Taonani, Ine ndidzakodola Anthu a mitundu ina kuti abwere.
    Ndidzawakwezera anthu a mitundu ina mbendera yanga kuti abwere.
Tsono adzabwera ndi ana ako aamuna atawanyamula mʼmanja mwawo
    ndipo adzanyamula ana ako aakazi pa mapewa awo.
23 Mafumu adzakhala abambo wongokulera
    ndipo akazi a mafumu adzakhala amayi wongokulera.
Iwo adzagwetsa nkhope
    zawo pansi.
Ndiye inu mudzazindikira kuti Ine ndine Yehova;
    iwo amene amadalira Ine sadzakhumudwa.”

24 Kodi mungathe kulanda anthu ankhondo zofunkha zawo,
    kapena kupulumutsa anthu ogwidwa mʼdzanja la munthu wankhanza?

25 Koma zimene Yehova akunena ndi izi,

“Ankhondo adzawalanda amʼndende awo,
    ndipo munthu woopsa adzamulanda zofunkha zawo;
ndidzalimbana ndi amene amalimbana nanu,
    ndipo ndidzapulumutsa ana anu.
26 Anthu amene anakuponderezani adzadya mnofu wawo omwe;
    adzamwa magazi awo omwe ngati aledzera ndi vinyo.
Zikadzatero anthu onse adzadziwa
    kuti Ine Yehova, ndine Mpulumutsi wanu,
    Momboli wanu, Wamphamvu wa Yakobo.”

1 Atesalonika 4

Moyo Wokondweretsa Mulungu

Potsiriza, abale, tinakulangizani kale momwe mukuyenera kukhalira kuti mukondweretse Mulungu, monga momwe mukukhaliramo. Tsopano tikukupemphani ndi kukulimbikitsani mwa Ambuye Yesu kuti muchite zimenezi koposa kale. Inu mukudziwa malangizo amene tinakupatsani mwa ulamuliro wa Ambuye Yesu.

Ndi chifuniro cha Mulungu kuti muyeretsedwe: kuti mupewe dama; aliyense wa inu aphunzire kulamulira thupi lake mʼnjira yoyera ndi yaulemu, osati yotsata chilakolako chonyansa monga amachitira akunja, amene sadziwa Mulungu. Pa zimenezi munthu asachimwire mʼbale wake kapena kumuonerera. Ambuye adzalanga anthu onse amene amachita machimo amenewa, monga tinakuwuzani kale ndi kukuchenjezani. Pakuti Mulungu sanatiyitane kuti tizichita zonyansa, koma kuti tikhale oyera mtima. Choncho, aliyense amene akukana malangizo awa sakukana munthu koma Mulungu, Mulungu weniweniyo amene amakupatsani Mzimu Woyera.

Tsono kunena za kukondana wina ndi mnzake, nʼkosafunikira kuti tikulembereni, popeza ndi Mulungu amene anakuphunzitsani za kukondana wina ndi mnzake. 10 Ndipo kunena zoona, mumakonda abale onse a mʼbanja la Mulungu a ku Makedoniya. Komabe, abale tikukulimbikitsani kuti muzichita zimenezi koposa kale.

11 Yesetsani kuti mukhale moyo wofatsa. Aliyense asamale ntchito yakeyake ndi kugwira ntchito ndi manja ake. 12 Mukatero akunja adzalemekeza makhalidwe anu a tsiku ndi tsiku, ndi kuti inuyo mukhale osadalira wina aliyense.

Kubweranso kwa Ambuye

13 Abale, ife sitikufuna mukhale osadziwa za amene akugona, kapena kumva chisoni ngati anthu ena opanda chiyembekezo. 14 Ife timakhulupirira kuti Yesu anamwalira naukanso. Moteronso timakhulupirira kuti amene anamwalira ali mwa Yesu, Mulungu adzawaukitsa nʼkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo. 15 Molingana ndi mawu a Ambuye mwini, tikukuwuzani kuti, ife amene tikanali ndi moyo, otsala mpaka kubwera kwa Ambuye, sitidzawasiya kumbuyo amene anagona kale. 16 Pakuti Ambuye mwini adzatsika kuchokera kumwamba, ndi mfuwu waulamuliro, ndi liwu la mngelo wamkulu, ndi kulira kwa lipenga la Mulungu, ndipo akufa amene ali mwa Yesu adzauka poyamba. 17 Kenaka, ife amene tili ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa pamodzi ndi iwo mʼmitambo kukakumana ndi Ambuye mlengalenga. Tsono ife tidzakhala ndi Ambuye mpaka muyaya. 18 Nʼchifukwa chake tsono muzilimbikitsana ndi mawu amenewa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.