Old/New Testament
45 Yehova akuyankhula ndi wodzozedwa wake
Koresi amene anamugwira dzanja lamanja
kuti agonjetse mitundu ya anthu
ndi kuwalanda mafumu zida zawo zankhondo,
ndi kutsekula zitseko
kuti zipatazo zisadzatsekedwenso ndi ichi:
2 Ine ndidzayenda patsogolo pako,
ndi kusalaza mapiri;
ndidzaphwanya zitseko za mkuwa
ndi kuthyola mipiringidzo ya chitsulo.
3 Ndidzakupatsa chuma chobisika mu mdima,
katundu wa pamalo obisika,
kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova
Mulungu wa Israeli, amene ndakuyitana pokutchula dzina.
4 Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobo,
chifukwa cha wosankhidwa wanga Israeli,
Ine ndakuyitana pokutchula dzina
ndipo ndakupatsa dzina laulemu
ngakhale iwe sukundidziwa Ine.
5 Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina;
kupatula Ine palibenso Mulungu wina.
Ndidzakupatsa mphamvu,
ngakhale sukundidziwa Ine,
6 kotero kuti kuchokera kummawa mpaka kumadzulo
anthu adzadziwa kuti palibe wina koma Ine ndekha.
Ine ndine Yehova,
ndipo palibenso wina.
7 Ndimalenga kuwala ndi mdima,
ndimabweretsa madalitso ndi tsoka;
ndine Yehova, amene ndimachita zonsezi.
8 “Iwe thambo gwetsa mvula kuchokera kumwamba;
mitambo ivumbwe mivumbi ya chilungamo.
Dziko lapansi litsekuke,
ndipo chipulumutso chiphuke kuti
chilungamo chimereponso;
Ine Yehova, ndine ndalenga zimenezi.
9 “Tsoka kwa wokangana ndi mlengi wake,
ngakhale kuti ali ngati phale chabe pakati pa mapale anzake.
Kodi dongo lingafunse munthu wowumba kuti,
‘Kodi ukuwumba chiyani?’
Kodi ntchito yako inganene kuti,
‘Ulibe luso?’
10 Tsoka kwa wofunsa abambo ake kuti,
‘Kodi munabereka chiyani?’
Kapena amayi ake kuti,
‘Kodi mufuna kubereka chiyani?’
11 “Yehova
Woyerayo wa Israeli, ndiponso Mlengi wake akunena,
zokhudza zinthu zimene zikubwera ndi izi:
Kodi iwe ukundifunsa za ana anga,
kapena kundilamula pa zokhudza ntchito zanga?
12 Ndine amene ndinapanga dziko lapansi
ndikulenga munthu kuti akhalemo.
Ine ndi manja anga ndinayalika thambo;
ndimalamulira zolengedwa zonse za mlengalenga.
13 Ndine amene ndidzawutsa Koresi kuti chilungamo changa chikwaniritsidwe:
ndipo ndidzawongolera njira zake zonse.
Iye adzamanganso mzinda wanga
ndi kumasula anthu anga amene ali mu ukapolo,
wopanda kupereka ndalama kapena mphotho,
akutero Yehova Wamphamvuzonse.”
14 Yehova akuti,
“Chuma cha ku Igupto ndi chuma cha malonda cha Kusi chidzakhala chanu.
Anthu amphamvu zawo ndi athanzi a ku Seba
adzabwera kwa inu
ndipo adzakhala anthu anu;
iwo adzidzakutsatani pambuyo panu
ali mʼmaunyolo.
Adzakugwadirani
ndi kukupemphani, ponena kuti,
‘Ndithudi Mulungu ali ndi inu, ndipo palibenso wina;
palibenso mulungu wina.’ ”
15 Zoonadi inu muli ndi Mulungu wobisika
amene ali Mulungu ndi Mpulumutsi wa Israeli.
16 Onse amene amapanga mafano adzawachititsa manyazi ndi kuwanyozetsa.
Adzakhala osokonezeka maganizo.
17 Koma Yehova adzapulumutsa Israeli
ndi chipulumutso chamuyaya;
simudzachitanso manyazi kapena kunyozeka
mpaka kalekale.
18 Yehova
analenga zinthu zakumwamba,
Iye ndiye Mulungu;
amene akulenga dziko lapansi,
ndi kulikhazikitsa,
sanalipange kuti likhale lopanda kanthu,
koma analipanga kuti anthu akhalemo.
Iyeyu akunena kuti:
Ine ndine Yehova,
ndipo palibenso wina.
19 Ine sindinayankhule mwachinsinsi,
pamalo ena a mdima;
Ine sindinaziwuze zidzukulu za Yakobo kuti,
“Ndifunefuneni ku malo kopanda kanthu.”
Ine Yehova, ndimayankhula zoona;
ndikunena zolungama.
20 Yehova akuti, “Sonkhanani pamodzi ndipo mubwere;
yandikirani, inu amene munapulumuka pothawa nkhondo kwa anthu a mitundu ina.
Ndinu opanda nzeru amene mumanyamula mafano a mitengo,
amene mumapemphera kwa milungu imene singathe kupulumutsa.
21 Fotokozani mlandu wanu,
mupatsane nzeru nonse pamodzi.
Kodi ndani ananeneratu zimenezi kalekale?
Ndani anazifotokozeratu zimenezi nthawi yamakedzana?
Kodi si Ineyo Yehova?
Ndipo palibenso Mulungu wina kupatula Ine,
Mulungu wolungama ndi Wopulumutsa,
palibenso wina kupatula Ine.
22 “Tembenukirani kwa Ine kuti mupulumuke,
inu anthu onse a pa dziko lapansi,
pakuti Ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina.
23 Ndalumbira ndekha,
pakamwa panga patulutsa mawu owona,
mawu amene sadzasinthika konse akuti,
bondo lililonse lidzagwada pamaso panga;
anthu onse adzalumbira potchula dzina langa.
24 Iwo adzanene kwa Ine kuti,
‘Chilungamo ndi mphamvu zimapezeka mwa Yehova yekha.’ ”
Onse amene anamuwukira Iye
adzabwera kwa Iye ndipo adzachita manyazi.
25 Koma mwa Yehova zidzukulu zonse za Israeli
zidzapambana ndi kupeza ulemerero.
Za Kupasuka kwa Babuloni ndi Mafano Ake
46 Beli wagwada pansi, Nebo wawerama;
nyama zonyamula katundu za nyamula milungu yawo.
Mafano awo asanduka katundu wolemera pa msana pa ngʼombe.
Asandukadi ngati katundu pa msana pa nyama zotopa.
2 Nyamazo zikuwerama ndi kufuna kugwa ndi milunguyo;
sizikutha kupulumutsa katunduyo,
izo zomwe zikupita ku ukapolo.
3 Mverani Ine, Inu nyumba ya Yakobo,
inu nonse otsala a mʼnyumba ya Israeli,
Ine ndakhala ndi kukusamalirani kuyambira mʼmimba ya amayi anu,
ndakhala ndikukunyamulani chibadwire chanu.
4 Mpaka pamene mudzakalambe ndi kumera imvi
ndidzakusamalirani ndithu.
Ndinakulengani ndipo ndidzakunyamulani,
ndidzakusamalirani ndi kukulanditsani.
5 “Kodi inu mudzandifanizira ndi yani, kapena mufananitsa ndi yani?
Kodi mudzandiyerekeza kapena kundifanizitsa ndi yani?
6 Anthu ena amakhuthula golide mʼzikwama zawo
ndipo amayeza siliva pa masikelo;
amalemba ntchito mʼmisiri wosula kuti awapangire mulungu,
kenaka iwo amagwada pansi ndikupembedza kamulunguko.
7 Amanyamula nʼkumayenda nayo milunguyo pa mapewa awo;
amayikhazika pa malo pake ndipo imakhala pomwepo.
Singathe kusuntha pamalo pakepo.
Ngakhale wina apemphere kwa milunguyo singathe kuyankha;
kapena kumupulumutsa ku mavuto ake.
8 “Kumbukirani zimenezi ndipo muchite manyazi,
Muzilingalire mu mtima, inu anthu owukira.
9 Kumbukirani zinthu zakale zinthu zamakedzana;
chifukwa Ine ndine Mulungu
ndipo palibe wina ofanana nane.
10 Ndinaneneratu zakumathero kuchokera pachiyambi pomwe.
Kuyambira nthawi yamakedzana ndinaloseratu zoti zidzachitike.
Ndikanena zimene ndifuna kuchita ndipo zimachitikadi.
Chilichonse chimene ndafuna ndimachichita.
11 Ndikuyitana chiwombankhanga kuchokera kummawa.
Ndikuyitana kuchokera ku dziko lakutali munthu amene adzakwaniritsa cholinga changa.
Zimene ndanena ndidzazikwaniritsadi;
zimene ndafuna ndidzazichitadi.
12 Ndimvereni, inu anthu owuma mtima,
inu amene muli kutali ndi chipulumutso.
13 Ndikubweretsa pafupi tsiku la chipulumutso changa;
sichili kutali.
Tsikulo layandikira
ndipo sindidzachedwa kukupulumutsani
ndi kupereka ulemerero wanga kwa Israeli.
3 Nʼchifukwa chake pamene sitinathenso kupirira, tinaganiza kuti kunali bwino kuti atisiye tokha ku Atene. 2 Tinatuma Timoteyo, mʼbale wathu ndi mnzathu wogwira naye ntchito ya Mulungu yofalitsa Uthenga Wabwino wa Khristu, kuti adzakulimbitseni mitima ndi kukukhazikitsani mʼchikhulupiriro chanu, 3 ndi cholinga chakuti wina asasunthike ndi mavutowa. Inu mukudziwa bwino lomwe kuti ndife oyenera kukumana ndi zimenezi. 4 Kunena zoona, pamene tinali nanu, tinkakuwuzani kuti tidzayenera kuzunzidwa. Ndipo monga mukudziwa bwino, zimenezi zinachitikadi. 5 Nʼchifukwa chake, pamene sindikanathanso kupirira, ndinatuma Timoteyo kuti adzaone mmene chikhulupiriro chanu chilili. Ndinkaopa kuti mwina wonyengayo, wakunyengani mʼnjira ina yake ndi kuti ntchito zathu zasanduka zosapindula.
Nkhani Yolimbikitsa Kuchokera kwa Timoteyo
6 Koma tsopano Timoteyo wabwera kuchokera kwanuko ndipo watibweretsera nkhani yabwino ya chikhulupiriro chanu ndi chikondi chanu. Iye watiwuzanso kuti masiku onse mumatikumbukira mokondwa, ndipo kuti mumafunitsitsa kutionanso, monga momwe ifenso timalakalakira kukuonani inuyo. 7 Motero abale, mʼmasautso ndi mʼmazunzo athu onse, chikhulupiriro chanu chatilimbikitsa. 8 Ife tsopano tili moyodi, pakuti mukuyima molimbika mwa Ambuye. 9 Tingathe bwanji kuyamika Mulungu mokwanira poona chimwemwe chonse chimene tili nacho pamaso pa Mulungu wathu chifukwa cha inu? 10 Usana ndi usiku timapemphera ndi mtima wonse kuti tionanenso nanu, ndi kukwaniritsa zimene zikusowa pa chikhulupiriro chanu.
11 Tikupempha kuti Mulungu ndi Atate athu mwini, ndi Ambuye athu Yesu, atikonzere njira yabwino kuti tidzafike kwanuko. 12 Ambuye achulukitse chikondi chanu ndi kuti chisefukire kwa wina ndi mnzake ndiponso kwa wina aliyense, monga momwe chikondi chathu chichitira kwa inu. 13 Iye alimbikitse mitima yanu kuti mukhale opanda cholakwa ndi oyera mtima pamaso pa Mulungu ndi Atate athu pamene Ambuye athu Yesu akubwera ndi oyera ake onse.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.