Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 39-40

Nthumwi Zochokera ku Babuloni

39 Nthawi imeneyo Merodaki-Baladani, mwana wa Baladani mfumu ya ku Babuloni anatumiza nthumwi kwa Hezekiya nawapatsira makalata ndi mphatso, pakuti anamva za kudwala kwake ndi kuti anachira. Hezekiya anawalandira mwasangala ndipo anawaonetsa zonse zimene zinali mʼnyumba zake zosungiramo siliva, golide, zokometsera zakudya, mafuta abwino kwambiri, zida zonse zankhondo ndiponso zonse zimene zinkapezeka mʼnyumba zake zosungiramo chuma. Panalibe kanthu kalikonse ka mʼnyumba yaufumu kapena mu ufumu wake onse kamene sanawaonetse.

Tsono mneneri Yesaya anapita kwa mfumu Hezekiya ndipo anamufunsa kuti, “Kodi anthu aja anakuwuzani chiyani, ndipo anachokera kuti?”

Hezekiya anayankha kuti, “Anachokera ku dziko lakutali, ku Babuloni.”

Mneneri anafunsanso kuti, “Kodi mʼnyumba yanu yaufumu anaonamo chiyani?”

Hezekiya anati, “Anaona chilichonse cha mʼnyumba yanga yaufumu. Palibe ndi chimodzi chomwe za mʼnyumba yosungiramo chuma changa chimene sindinawaonetse.”

Pamenepo Yesaya anati kwa Hezekiya, “Imvani mawu a Yehova Wamphamvuzonse: Yehova akuti, nthawi idzafika ndithu pamene zonse za mʼnyumba mwanu ndi zonse zimene makolo anu anazisonkhanitsa mpaka lero lino, zidzatengedwa kupita nazo ku Babuloni. Sipadzatsalapo ndi kanthu kamodzi komwe. Ndipo ena mwa ana anu, obala inu amene adzatengedwanso, ndipo adzawasandutsa adindo ofulidwa mʼnyumba ya mfumu ya ku Babuloni.”

Hezekiya anayankha kuti, “Mawu a Yehova amene mwayankhula ndi abwino.” Ponena izi iye ankaganiza kuti, “Padzakhala mtendere ndi chitetezo masiku a moyo wanga onse.”

Mawu a Chitonthozo kwa Anthu a Mulungu

40 Atonthozeni, atonthozeni anthu anga,
    akutero Mulungu wanu.
Ayankhuleni moleza mtima anthu a ku Yerusalemu
    ndipo muwawuzitse
kuti nthawi ya ukapolo wawo yatha,
    tchimo lawo lakhululukidwa.
Ndawalanga mokwanira
    chifukwa cha machimo awo onse.

Mawu a wofuwula mʼchipululu akuti,
“Konzani njira ya Yehova
    mʼchipululu;
wongolani njira zake;
    msewu owongoka wa Mulungu wathu mʼdziko lopanda kanthu.
Chigwa chilichonse achidzaze.
    Phiri lililonse ndi chitunda chilichonse azitsitse;
Dziko lokumbikakumbika alisalaze,
    malo azitundazitunda awasandutse zidikha.
Ndipo ulemerero wa Yehova udzaonekera,
    ndipo mitundu yonse ya anthu idzawuona,
            pakuti wanena zimenezi ndi Yehova.”

Wina ananena kuti, “Lengeza.”
    Ndipo ine ndinati, “Kodi ndifuwule chiyani?

“Pakuti anthu onse ali ngati udzu
    ndipo kukongola kwawo kuli ngati maluwa akuthengo.
Udzu umanyala ndipo maluwa amafota
    chifukwa cha kuwomba kwa mpweya wa Yehova.”
    Mawu aja anatinso, “Ndithudi anthu sasiyana ndi udzu.
Udzu umanyala ndipo maluwa amafota,
    koma mawu a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka muyaya.”

Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Ziyoni,
    kwera pa phiri lalitali.
Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Yerusalemu,
    fuwula kwambiri,
kweza mawu, usachite mantha;
    uza mizinda ya ku Yuda kuti,
    “Mulungu wanu akubwera!”
10 Taonani, Ambuye Yehova akubwera mwamphamvu,
    ndipo dzanja lake likulamulira,
taonani akubwera ndi mphotho yake
    watsogoza zofunkha zako za ku nkhondo.
11 Iye adzasamalira nkhosa zake ngati mʼbusa:
    Iye adzasonkhanitsa ana ankhosa aakazi mʼmanja mwake
ndipo Iye akuwanyamula pachifuwa chake
    ndi kutsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.

12 Kodi ndani akhoza kuyeza kuchuluka kwa madzi a mʼnyanja ndi chikhatho chake,
    kapena kuyeza kutalika kwa mlengalenga ndi dzanja lake?
Ndani akhoza kuyeza dothi lonse la dziko lapansi mʼdengu,
    kapena kuyeza kulemera kwa
    mapiri ndi zitunda ndi pasikelo?
13 Ndani anapereka malangizo kwa Mzimu wa Yehova
    kapena kumuphunzitsa Iye monga phungu wake?
14 Kodi Yehova anapemphapo nzeru kwa yani kuti akhale wopenya,
    kapena kuti aphunzire njira yoyenera ndi nzeru?
Iye anapempha nzeru kwa yani
    ndi njira ya kumvetsa zinthu?

15 Ndithudi mitundu ya anthu ili ngati dontho la madzi ochoka mu mtsuko.
    Iwo akungoyesedwa ngati fumbi chabe pa sikelo;
    mʼmanja mwa Yehova zilumba nʼzopepuka ngati fumbi.
16 Nkhalango ya ku Lebanoni singakwanire nkhuni zosonkhera moto pa guwa lansembe,
    ngakhale nyama zake sizingakwanire kupereka nsembe zopsereza.
17 Pamaso pa Yehova mitundu yonse ya anthu ili ngati chinthu chopandapake;
    Iye amayiwerengera ngati chinthu chopanda phindu
    ndi cha chabechabe.

18 Kodi tsono Mulungu mungamuyerekeze ndi yani?
    Kodi mungamufanizire ndi chiyani?
19 Likakhala fano, mʼmisiri ndiye analipanga
    ndipo mʼmisiri wa golide amalikuta ndi golide
    naliveka mkanda wasiliva.
20 Mʼmphawi amene sangathe kupeza ngakhale chopereka nsembe chotere
    amasankha mtengo umene sudzawola,
nafunafuna mʼmisiri waluso woti
    amupangire fano limene silingasunthike.

21 Kodi simukudziwa?
    Kodi simunamve?
Kodi sanakuwuzeni kuyambira pachiyambi pomwe?
    Kodi simunamvetsetse chiyambire cha dziko lapansi?
22 Yehova amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba ndiye analenga dziko lapansi,
    Iye amaona anthu a dziko lapansi ngati ziwala.
Ndipo anafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchinga,
    nayikunga ngati tenti yokhalamo.
23 Amatsitsa pansi mafumu amphamvu
    nasandutsa olamula a dziko kukhala achabechabe.
24 Inde, iwo ali ngati mbewu zimene zangodzalidwa kumene
    kapena kufesedwa chapompano,
    ndi kungoyamba kuzika mizu kumene
ndi pamene mphepo imawombapo nʼkuziwumitsa
    ndipo kamvuluvulu amaziwulutsa ngati mankhusu.

25 Woyera uja akuti, “Kodi mudzandiyerekeza Ine ndi yani?
    Kapena kodi alipo wofanana nane?”
26 Tayangʼanani mlengalenga ndipo onani.
    Kodi ndani analenga zonsezi mukuzionazi?
Yehova ndiye amene amazitsogolera ngati gulu la ankhondo,
    nayitana iliyonse ndi dzina lake.
Ndipo popeza Iye ali ndi nyonga zambiri,
    palibe ndi imodzi yomwe imene inasowapo.

27 Iwe Yakobo, chifukwa chiyani umanena
    ndi kumadandaula iwe Israeli, kuti,
“Yehova sakudziwa mavuto anga,
    Mulungu wanga sakusamala zomwe zikundichitikira ine?”
28 Kodi simukudziwa?
    Kodi simunamve?
Yehova ndiye Mulungu wamuyaya,
    ndiyenso Mlengi wa dziko lonse lapansi.
Iye sadzatopa kapena kufowoka
    ndipo palibe amene angadziwe maganizo ake.
29 Iye amalimbitsa ofowoka
    ndipo otopa amawawonjezera mphamvu.
30 Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufowoka,
    ndipo achinyamata amapunthwa ndi kugwa;
31 koma iwo amene amakhulupirira Yehova
    adzalandira mphamvu zatsopano.
Adzawuluka ngati chiwombankhanga;
    adzathamanga koma sadzalefuka,
    adzayenda koma sadzatopa konse.

Akolose 4

Mabwana, antchito anu muzikhala nawo mwachilungamo ndi moyenera, podziwa kuti nanunso muli nawo Ambuye anu mmwamba.

Malangizo Ena

Pempherani modzipereka, mukhale atcheru ndiponso oyamika. Ndipo muzitipemphereranso ife kuti Mulungu atitsekulire khomo la uthenga wathu, kuti tilalikire chinsinsi cha Khristu, chimene ndine womangidwa nacho mʼndende. Pempherani kuti ndilalikire momveka bwino, monga ndikuyenera. Mayendedwe anu pakati pa akunja, akhale anzeru ndipo mugwiritse ntchito mpata uliwonse umene muli nawo. Mayankhulidwe anu nthawi zonse akhale odzaza ndi chisomo ndi okoma, kuti mudziwe kuyankha aliyense.

Mawu Otsiriza

Tukiko adzakuwuzani zonse za ine. Iye ndi mʼbale wokondedwa, mtumiki wokhulupirika ndiponso wantchito mnzanga mwa Ambuye. Ine ndikumutumiza kwa inu ndi cholinga choti mudziwe zimene tikukumana nazo ndiponso kuti alimbikitse mitima yanu. Iye akubwera ndi Onesimo, mʼbale wathu wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ndi mmodzi mwa inu. Iwo adzakuwuzani zonse zimene zikuchitika kuno.

10 Aristariko, wamʼndende mnzanga akupereka moni, Marko akuperekanso moni, msuweni wa Barnaba. (Inu munawuzidwa kale za Iye. Iye akabwera kwanuko, mulandireni). 11 Yesu wotchedwa Yusto, akuperekanso moni. Amenewa ndi Ayuda okhawo pakati pa atumiki anzanga mu ufumu wa Mulungu, ndipo aonetsa kuti ndi chitonthozo kwa ine. 12 Epafra ndi mmodzi mwa inu ndiponso mtumiki wa Khristu Yesu, akupereka moni. Iyeyu nthawi zonse amakupemphererani mwamphamvu, kuti mukhazikike pa chifuniro chonse cha Mulungu, mukhale okhwima ndi otsimikiza kwathunthu. 13 Ine ndikumuchitira umboni kuti amagwira ntchito mwamphamvu chifukwa cha inu ndiponso kwa amene ali ku Laodikaya ndi Herapoli. 14 Luka, dotolo wathu wokondedwa ndi Dema, akupereka moni. 15 Perekani moni kwa abale a ku Laodikaya, ndiponso kwa Numfa ndi mpingo wa mʼnyumba mwake.

16 Kalata iyi ikawerengedwa pakati panu, muonetsetse kuti ikawerengedwenso ku mpingo wa ku Laodikaya ndipo inunso muwerenge kalata yochokera ku Laodikaya.

17 Uzani Arkipo kuti, “Wonetsetsa kuti wamaliza ntchito imene unayilandira mwa Ambuye.”

18 Ine Paulo, ndikulemba ndi dzanja langa moni uwu. Kumbukirani kuti ndili mu unyolo. Chisomo chikhale ndi inu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.