Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 32-33

Ufumu Wachilungamo

32 Taonani, kudzakhala mfumu ina imene idzalamulira mwachilungamo,
    ndipo akalonga ake adzaweruza molungama.
Munthu aliyense adzakhala ngati pothawirapo mphepo
    ndi malo obisalirapo namondwe,
adzakhala ngati mitsinje ya mʼchipululu,
    ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu la mʼdziko lowuma.

Ndipo maso a anthu openya sadzakhalanso otseka,
    ndipo makutu a anthu akumva adzamvetsetsa.
Anthu a mtima wopupuluma adzadziwa ndi kuchita zinthu mofatsa,
    ndipo anthu ovutika kuyankhula adzayankhula mosadodoma ndi momveka.
Chitsiru sichidzatchedwanso munthu waulemu wake
    ndipo munthu woyipa sadzalemekezedwa.
Pakuti munthu opusa amayankhula zauchitsiru,
    amaganiza kuchita zoyipa:
Iye amachita zoyipira Mulungu,
    ndipo amafalitsa zolakwika zokhudza Yehova;
anjala sawapatsa chakudya
    ndipo aludzu sawapatsa madzi.
Munthu woyipa njira zake ndi zoyipanso,
    iye kwake nʼkulingalira zinthu zoyipa.
Amalingalira zakuti awononge anthu aumphawi ndi mabodza ake
    ngakhale kuti waumphawiyo akuyankhula zoona.
Koma munthu wolemekezeka amalingaliranso kuchita zinthu zabwino,
    Iye amakhazikika pa zinthu zabwinozo.

Akazi a ku Yerusalemu

Khalani maso, inu akazi
    amene mukungokhala wopanda kulingalira kuti kunja kulinji
ndipo imvani mawu anga.
    Inu akazi odzitama, imvani zimene ndikunena!
10 Pakapita chaka ndi masiku pangʼono
    inu akazi amatama mudzanjenjemera;
chifukwa mitengo ya mphesa idzakanika
    ndipo zipatso sizidzaoneka.
11 Nthunthumirani inu okhala mosatekesekanu;
    ndipo njenjemerani, inu akazi omadzikhulupirira nokhanu.
Vulani zovala zanu,
    ndipo valani ziguduli mʼchiwuno mwanu.
12 Dzigugudeni pachifuwa mwachisoni chifukwa minda yachonde,
    ndi mphesa yawonongeka.
13 Mʼdziko la anthu anga
    mwamera minga ndi mkandankhuku.
Zoona, mulilire nyumba zonse zachikondwerero
    ndi mzinda uno umene unali wachisangalalo.
14 Nyumba yaufumu idzasiyidwa,
    mzinda waphokoso udzakhala wopanda anthu;
malinga ndi nsanja zidzasanduka chipululu mpaka muyaya.
    Abulu adzasangalalamo ndipo ziweto zidzapezamo msipu.
15 Yehova adzatipatsa mzimu wake,
    ndipo dziko lachipululu lidzasanduka munda wachonde,
    ndipo munda wachonde udzakhala ngati nkhalango.
16 Tsono mʼchipululu mudzakhala chiweruzo cholungama
    ndipo mʼminda yachonde mudzakhala chilungamo.
17 Mtendere udzakhala chipatso chachilungamo;
    zotsatira za chilungamo zidzakhala bata ndi kudzidalira mpaka muyaya.
18 Anthu anga adzakhala mʼmidzi yamtendere,
    mʼnyumba zodalirika,
    ndi malo osatekeseka a mpumulo.
19 Ngakhale nkhalango idzawonongedwa ndi matalala
    ndipo mzinda udzagwetsedwa mpaka pansi,
20 inutu mudzakhala odalitsika ndithu.
    Mudzadzala mbewu zanu mʼmbali mwa mtsinje uliwonse,
    ndipo ngʼombe zanu ndi abulu anu zidzadya paliponse.

Msautso ndi Thandizo

33 Tsoka kwa iwe, iwe wowonongawe,
    amene sunawonongedwepo!
Tsoka kwa iwe, iwe mthirakuwiri,
    iwe amene sunanyengedwepo!
Iwe ukadzaleka kuwononga,
    udzawonongedwa,
ukadzasiya umʼthirakuwiri, adzakuwononga,
    ndipo ukadzaleka kuchita zachinyengo adzakunyenga.

Inu Yehova, mutikomere mtima ife;
    tikulakalaka Inu.
Tsiku ndi tsiku mutitchinjirize ndi mkono wanu,
    ndipo mutipulumutse pa nthawi ya masautso.
Mukatulutsa liwu lanu longa bingu mitundu ya anthu imathawa;
    pamene Inu mwadzambatuka mitundu ya anthu imabalalika.
Zofunkha za ku nkhondo za mitundu ina Aisraeli adzazisonkhanitsa ngati mmene limachitira dzombe.
    Iwo adzalumphira zofunkhazo monga mmene limachitira dzombe.

Yehova wakwezeka kwambiri pakuti amakhala pamwamba pa zonse
    adzadzaza Ziyoni ndi chilungamo ndi chipulumutso.
Iye adzakupatsani mtendere pa nthawi yanu,
    adzakupatsani chipulumutso chochuluka, nzeru zambiri ndi chidziwitso chochuluka;
    kuopa Yehova ngati madalitso.

Taonani, anthu awo amphamvu akulira mofuwula mʼmisewu;
    akazembe okhazikitsa mtendere akulira kwambiri.
Mʼmisewu yayikulu mulibe anthu,
    mʼmisewu mulibe anthu a paulendo.
Mdaniyo ndi wosasunga pangano.
    Iye amanyoza mboni.
    Palibe kulemekezana.
Dziko likulira ndipo likunka likutha.
    Nkhalango ya Lebanoni ikuchita manyazi, yafota.
Chigwa cha chonde cha Saroni chasanduka chachidalala.
    Masamba a mitengo ya ku Basani ndi Karimeli akuyoyoka.

10 Yehova akunena kuti, “Tsopano ndidzadzambatuka
    ndipo ndidzaonetsa mphamvu zanga,
    ndipo ndidzakwezedwa.
11 Zolingalira zanu nʼzachabechabe
    ngati udzu wamanyowa.
    Mpweya wamoto udzakupserezani.
12 Anthu a mitundu ina adzatenthedwa ngati miyala ya njereza;
    ndi ngati minga yodulidwa.”

13 Inu amene muli kutali, imvani zimene ndachita;
    inu amene muli pafupi, dziwani mphamvu zanga
14 Mu mzinda wa Ziyoni anthu ochimwa agwidwa ndi mantha;
    anthu osapembedza Mulungu akunjenjemera:
Iwo akunena kuti, “Ndani wa ife angathe kukhala mʼmoto wonyeketsa?
    Ndani wa ife angathe kukhala moto wosatha?”
15 Angathe kuti ndi amene amachita zolungama
    ndi kuyankhula zoona,
amene amakana phindu lolipeza monyenga
    ndipo salola manja ake kulandira ziphuphu,
amene amatseka makutu ake kuti angamve mawu opangana kupha anzawo
    ndipo amatsinzina kuti angaone zoyipa.
16 Munthu wotere ndiye adzakhale pa nsanja,
    kothawira kwake kudzakhala mʼmalinga a mʼmapiri.
Azidzalandira chakudya chake
    ndipo madzi sadzamusowa.

17 Nthawi imeneyo maso a ana adzaona mfumu ya maonekedwe wokongola
    ndi kuona dziko lotambasukira kutali.
18 Mu mtima mwanu muzidzalingalira zoopsa zinachitika kale zija:
    “Ali kuti mkulu wa Asilikali uja?
    Ali kuti wokhometsa misonkho uja?
    Ali kuti mkulu woyangʼanira nsanja?”
19 Simudzawaonanso anthu odzikuza aja,
    anthu aja achiyankhulo chosadziwika,
    chachilendo ndi chosamveka.

20 Taonani Ziyoni, mzinda wa zikondwerero zachipembedzo chathu;
    maso anu adzaona Yerusalemu,
    mzinda wamtendere, tenti imene sidzachotsedwa,
zikhomo zake sizidzazulidwa,
    kapena zingwe zake kuduka.
21 Kumeneko Yehova adzaonetsa ulemerero wake
    ndipo mzindawo udzakhala kasupe wa mitsinje yayikulu.
Ngalawa za zopalasa sizidzapitamo,
    sitima zapamadzi zikuluzikulu sizidzayendamo.
22 Pakuti Yehova ndi woweruza wathu,
    Yehova ndiye wotilamulira,
Yehova ndiye mfumu yathu;
    ndipo ndiye amene adzatipulumutse.

23 Zingwe za sitima zapamadzi za adani athu zamasuka,
    sizikutha kulimbitsa mlongoti wake,
    matanga ake sakutheka kutambasuka.
Ngakhale tidzagawana zofunkha zochuluka kwambiri
    ndipo ngakhale olumala adzatenga zofunkhazo.
24 Palibe ndi mmodzi yemwe wokhala mʼZiyoni adzanene kuti, “Ndikudwala”
    ndipo anthu onse okhala mʼmenemo machimo awo adzakhululukidwa.

Akolose 1

Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwachifuniro cha Mulungu, ndi Timoteyo mʼbale wathu.

Kulembera abale oyera mtima ndi okhulupirira a ku Kolose mwa Khristu.

Chisomo ndi mtendere kwa inu zochokera kwa Mulungu Atate athu.

Kuyamika ndi Pemphero

Timayamika Mulungu Atate wa Ambuye athu Yesu Khristu, nthawi zonse pamene tikukupemphererani. Timayamika chifukwa tinamva za chikhulupiriro chanu mwa Khristu Yesu ndi za chikondi chanu pa oyera mtima onse. Chikhulupiriro ndi chikondi, gwero lake ndi chiyembekezo chomwe muli nacho chodzalandira zimene anakusungirani kumwamba. Munamva kale za zimenezi kudzera mʼmawu a choonadi, Uthenga Wabwino umene unafika kwa inu. Pa dziko lonse lapansi Uthenga Wabwino ukubereka chipatso ndi kukula monga momwe zakhala zikuchitikira pakati panu kuyambira tsiku limene munawumva ndi kuzindikira chisomo cha Mulungu mu choonadi chonse. Inu munaphunzira zimenezi kuchokera kwa Epafra, mtumiki mnzathu wokondedwa, amene ndi mtumiki wokhulupirika wa Khristu mʼmalo mwathu. Iye anatiwuza za chikondi chanu chimene Mzimu anakupatsani.

Chifukwa cha ichi, kuyambira tsiku limene tinamva za inu, sitinasiye kukupemphererani ndi kumupempha Mulungu kuti akudzazeni ndi chidziwitso cha chifuniro chake kudzera mu nzeru yonse yauzimu ndi kumvetsetsa. 10 Ndipo tikupempherera zimenezi ndi cholinga chakuti inu mukhale moyo oyenera Ambuye ndi kumukondweretsa mʼnjira zonse. Kubereka chipatso pa ntchito iliyonse yabwino, ndi kukula mʼchidziwitso cha Mulungu. 11 Timapempheranso kuti Mulungu akulimbikitseni ndi mphamvu yake yonse ya ulemerero wake, kuti muzipirira zonse ndi mitima yofatsa ndi ya chimwemwe 12 ndi kuyamika Atate nthawi zonse, amene wakuyenerezani kuti mulandire nawo chuma cha oyera mtima mu ufumu wa kuwunika. 13 Pakuti Iye anatipulumutsa ku ulamuliro wa mdima ndi kutibweretsa mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa. 14 Mwa Iyeyu ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo.

Kupambana Koposa kwa Khristu

15 Mwanayu ndiye chithunzi cha Mulungu wosaonekayo. Iye ndiye Mwana wake woyamba kubadwa ndi wolamulira zolengedwa zonse. 16 Pakuti zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye. Zinthu zakumwamba ndi za pa dziko lapansi, zooneka ndi zosaoneka, maufumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu. Zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye ndipo anazilengera Iyeyo. 17 Iyeyo analipo zinthu zonse zisanalengedwe ndipo zinthu zonse zimamangika pamodzi mwa Iye. 18 Iye ndiyenso mutu wa thupi, limene ndi mpingo. Iye ndiye chiyambi chake, woyamba kuuka kwa akufa, kuti Iyeyo akhale wopambana zonse. 19 Pakuti kunamukomera Mulungu kuti umulungu wake wonse ukhalemo mwa Khristu. 20 Ndipo kudzera mwa Iye Mulungu ayanjanitsenso zinthu zonse ndi Iye mwini, zinthu za pa dziko lapansi, kapena zinthu za kumwamba. Iye anachita mtendere kudzera mʼmagazi ake, wokhetsedwa pa mtanda.

21 Kale inu munali kutali ndi Mulungu ndipo munali adani a Mulungu mʼmaganizo mwanu chifukwa cha khalidwe lanu loyipa. 22 Koma tsopano Iye anakuyanjanitsani mʼthupi la Khristu kudzera mu imfa kuti akuperekeni pamaso pake oyera, opanda banga ndi opanda chotsutsidwa nacho 23 ngati mupitirirabe kukhala mʼchikhulupiriro chanu, okhazikika ndi olimba, osasunthidwa kuchoka pa chiyembekezo chimene munachigwira mu Uthenga Wabwino. Uwu ndi Uthenga Wabwino umene munawumva, umene wakhala ukulalikidwa kwa olengedwa onse a pansi pa thambo, ndi umenenso, ine Paulo ndinakhala mtumiki wake.

Utumiki wa Paulo ku Mpingo

24 Tsopano ine ndikukondwa kuti ndinavutika chifukwa cha inu, ndipo ndikukwaniritsa mʼthupi langa zimene zikuperewera pa masautso a Khristu, chifukwa cha thupi lake, limene ndi Mpingo. 25 Ine ndakhala mtumiki wake mwa lamulo limene Mulungu anandipatsa kuti ndipereke Mawu a Mulungu athunthu, 26 chinsinsi chimene chakhala chikubisika kwa nthawi ndi mibado, koma tsopano chawululidwa kwa oyera mtima. 27 Kwa iwo amene Mulungu anawasankha kuti awadziwitse pakati pa a mitundu ina, ulemerero wa chuma cha chinsinsi ichi, amene ndi Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero.

28 Ife tikulalikira Khristu, kulangiza ndi kuphunzitsa aliyense mwa nzeru zonse kuti timupereke aliyense wangwiro mwa Khristu. 29 Ndi cholinga chimenechi, ine ndikugwira ntchito molimbika ndi mwamphamvu zonse zimene Iye anachita mwa ine.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.