Old/New Testament
Tsoka kwa Mtundu Wopanduka
30 Yehova akuti, “Tsoka kwa ana ondipandukira
amene amachita zowakomera iwo okha osati Ine,
nachita mgwirizano wawowawo
koma osati motsogozedwa ndi Ine.
Choncho amanka nachimwirachimwira.
2 Amapita ku Igupto kukapempha thandizo
koma osandifunsa;
amathawira kwa Farao kuti awateteze,
ku Igupto amafuna malo opulumulira.
3 Koma chitetezo cha Farao chidzakhala manyazi anu,
malo a mthunzi a ku Igupto mudzachita nawo manyazi.
4 Ngakhale kuti nduna zawo zili ku Zowani,
ndipo akazembe awo afika kale ku Hanesi,
5 aliyense wa ku Yuda adzachita manyazi
chifukwa cha anthu opanda nawo phindu,
amene sabweretsa thandizo kapena phindu,
koma manyazi ndi mnyozo.”
6 Uthenga wonena za nyama za ku Negevi:
Akazembe akuyenda mʼdziko lovuta ndi losautsa,
mʼmene muli mikango yayimuna ndi yayikazi,
mphiri ndi njoka zaululu.
Iwo amasenzetsa abulu ndi ngamira chuma chawo,
kupita nazo kwa mtundu wa anthu
umene sungawathandize.
7 Amapita ku Igupto amene thandizo lake ndi lachabechabe.
Nʼchifukwa chake dzikolo ndalitcha
Rahabe chirombo cholobodoka.
8 Yehova anandiwuza kuti, “Tsopano pita,
ukalembe zimenezi mʼbuku iwo akuona
ndipo lidzakhala ngati umboni wosatha
masiku a mʼtsogolo.
9 Amenewa ndi anthu owukira, onama ndi
osafuna kumvera malangizo a Yehova.
10 Iwo amawuza alosi kuti,
‘Musationerenso masomphenya!’
Ndipo amanena kwa mneneri kuti,
‘Musatinenerenso zoona,’
mutiwuze zotikomera,
munenere za mʼmutu mwanu.
11 Patukani pa njira ya Yehova,
lekani kutsata njira ya Yehova;
ndipo tisamvenso mawu
a Woyerayo uja wa Israeli!”
12 Nʼchifukwa chake Woyerayo wa Israeli akunena kuti,
“Popeza inu mwakana uthenga uwu,
mumakhulupirira zopondereza anzanu
ndipo mumadalira kuchita zoyipa,
13 choncho tchimo linalo lidzakhala ngati mingʼalu
pa khoma lalitali ndi lopendama
limene linagwa mwadzidzidzi ndi mwamsangamsanga.
14 Lidzaphwanyika ngati mbiya
imene yanyenyekeratu,
mwakuti pakati pake sipadzapezeka phale ngakhale
lopalira moto mʼngʼanjo
kapena lotungira madzi mʼchitsime.”
15 Zimene Ambuye Yehova, Woyerayo wa Israeli ananena ndi izi:
“Ngati mubwerera ndi kupuma mudzapulumuka,
ngati mukhala chete ndi kukhulupirira mudzakhala amphamvu,
koma inu munakana zimenezi.
16 Inu mukuti, ‘Ayi ife tidzathawa,
tidzakwera pa akavalo aliwiro.’
Zoonadi kuti mudzakwera pa akavalo aliwiro,
koma okuthamangitsani adzakhalanso aliwiro.
17 Anthu 1,000 mwa inu adzathawa
poona mdani mmodzi;
poona adani asanu okha
nonsenu mudzathawa.
Otsala anu
adzakhala ngati mbendera pa phiri,
ndi ngati chizindikiro cha pa chulu.”
18 Komatu Yehova akufunitsitsa kuti akukomereni mtima,
iye ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo.
Pakuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo.
Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!
19 Inu anthu a ku Ziyoni, amene mukhala mu Yerusalemu simudzaliranso. Mulungu adzakukomerani mtima pamene adzamva kulira kwanu kopempha thandizo! Ndipo akadzamva, adzakuyankhani. 20 Ngakhale Ambuye adzakulowetseni mʼmasautso, aphunzitsi anu sadzakhala kakasi; inu mudzawaona ndi maso anuwo. 21 Ngati mudzapatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva mawu kumbuyo kwanu woti, “Njira ndi iyi; yendani mʼmenemo.” 22 Pamenepo mudzawononga mafano anu okutidwa ndi siliva ndiponso zifanizo zanu zokutidwa ndi golide; mudzawataya ngati zinthu zonyansa ndipo mudzati, “Zichoke zonsezi!”
23 Yehova adzakugwetseraninso mvula pa mbewu zanu zimene mukadzale mʼnthaka, ndipo chakudya chimene mudzakolole chidzakhala chabwino ndi chochuluka. Tsiku limenelo ngʼombe zanu zidzadya msipu wochuluka. 24 Ngʼombe ndi abulu amene amalima mʼmunda adzadya chakudya chamchere, chopetedwa ndi foloko ndi fosholo. 25 Pa tsiku limene adani anu adzaphedwa ndi nsanja zawo kugwa, mitsinje ya madzi idzayenda pa phiri lililonse lalikulu ndi pa phiri lililonse lalingʼono. 26 Mwezi udzawala ngati dzuwa, ndipo kuwala kwa dzuwa kudzawonjezereka kasanu nʼkawiri, ngati kuwala kwa tsiku limodzi. Yehova adzamanga mabala a anthu ake ndi kupoletsa zilonda zimene Iye anachititsa polanga anthu ake.
27 Taonani, Yehova akubwera kuchokera kutali,
ndipo mkwiyo wake ndiwonyeka ndi chiweruzo chake chidzakhala chopweteka.
Iye wayankhula mwaukali kwambiri,
ndipo mawu ake ali ngati moto wonyeka.
28 Mpweya wake uli ngati mtsinje wosefukira,
wa madzi ofika mʼkhosi.
Iye adzasefa anthu a mitundu ina ndi sefa wosakaza;
Iye akuyika zitsulo mʼkamwa mwa anthu a mitundu ina ngati akavalo,
kuti ziwasocheretse.
29 Ndipo inu mudzayimba
mokondwa monga mumachitira usiku pa chikondwerero chopatulika.
Mudzasangalala
ngati anthu oyimba zitoliro
popita ku phiri la Yehova,
thanthwe la Israeli.
30 Anthu adzamva liwu la ulemerero la Yehova
ndipo adzaona dzanja lake likutsika pa iwo
ndi mkwiyo woopsa, pamodzi ndi moto wonyeketsa,
mphenzi, namondwe ndi matalala.
31 Asiriya adzaopa liwu la Yehova,
ndipo Iye adzawakantha ndi ndodo.
32 Yehova akamadzalanga adani ake ndi ndodo,
anthu ake adzakhala akuvina nyimbo
zoyimbira matambolini ndi azeze,
Yehova ndiye ati adzamenyane ndi Asiriyawo.
33 Malo otenthera zinthu akonzedwa kale;
anakonzera mfumu ya ku Asiriya.
Dzenje la motolo ndi lozama ndi lalikulu,
ndipo muli nkhuni zambiri;
mpweya wa Yehova,
wangati mtsinje wa sulufule,
udzayatsa motowo pa nkhunizo.
Tsoka kwa Amene Amadalira Igupto
31 Tsoka kwa amene amapita ku Igupto kukapempha chithandizo,
amene amadalira akavalo,
nakhulupirira kuchuluka kwa magaleta awo ankhondo
ndiponso mphamvu za asilikali awo okwera pa akavalo,
koma sakhulupirira Woyerayo wa Israeli,
kapena kupempha chithandizo kwa Yehova.
2 Komatu Yehovayo ndi wanzeru ndipo angathe kuwononga,
ndipo sasintha chimene wanena.
Adzalimbana ndi anthu ochita zoyipa,
komanso ndi amene amathandiza anthu ochita zoyipa.
3 Aigupto ndi anthu chabe osati Mulungu;
akavalo awo ndi nyama chabe osati mizimu.
Yehova akangotambasula dzanja lake,
amene amapereka chithandizo adzapunthwa,
amene amalandira chithandizocho adzagwa;
onsewo adzathera limodzi.
4 Zimene Yehova akunena kwa ine ndi izi:
“Monga mkango kapena msona wamkango umabangula
ukagwira nyama yake,
ndipo suopsedwa kapena kusokonezeka
ndi kufuwula kwa abusa amene akulimbana nayo,
momwemonso palibe chingaletse
Yehova Wamphamvuzonse
kubwera kudzatchinjiriza
phiri la Ziyoni ndi zitunda zake.
5 Monga mbalame zowuluka pamwamba pa zisa zake,
Yehova Wamphamvuzonse adzatchinjiriza Yerusalemu;
ndi kumupulumutsa,
iye adzawupitirira ndi kuwulanditsa.”
6 Inu Aisraeli, bwererani kwa Iye amene munamuwukira kwakukulu. 7 Pakuti tsiku limenelo nonsenu mudzataya mafano anu a siliva ndi golide amene mumapanga ndi manja anu auchimo.
8 “Aasiriya adzaphedwa ku nkhondo ndi mphamvu osati za munthu.
Lupanga, osati la munthu, lidzawawononga.
Adzathawa ku nkhondo ndipo anyamata awo
adzagwira ntchito yathangata.
9 Mfumu yawo idzamwalira ndi mantha,
ndipo atsogoleri awo ankhondo adzathawa ndi mantha
kusiya pambuyo mbendera yawo ya nkhondo.”
Akutero Yehova, amene moto wake uli mu Ziyoni,
ndipo ngʼanjo yake ili mu Yerusalemu.
4 Tsono abale anga, ndimakukondani ndipo ndikukulakalakani. Ndinu chimwemwe changa ndi chipewa cha ulemerero wanga. Abwenzi okondedwa, chilimikani choncho mwa Ambuye.
2 Ndikudandaulira Euodiya ndi Suntuke kuti akhale ndi mtima umodzi mwa Ambuye. 3 Inde, ndikupempha iwe mnzanga pa ntchitoyi, thandiza amayiwa amene ndagwira nawo ntchito ya Uthenga Wabwino pamodzi ndi Klementonso ndi ena onse antchito anzanga amene mayina awo ali mʼbuku lamoyo.
Malangizo Otsiriza
4 Nthawi zonse muzikondwa mwa Ambuye. Ndikubwerezanso; muzikondwa! 5 Kufatsa kwanu kuzioneka pamaso pa anthu onse. Ambuye anu ali pafupi. 6 Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu. 7 Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
8 Potsiriza, abale, muziyika mtima wanu pa zinthu zilizonse zabwino ndi zotamandika monga, zinthu zoona, zinthu zolemekezeka, zinthu zolungama, zinthu zoyera, zinthu zokongola ndi zinthu zosiririka. 9 Muzichita chilichonse chimene mwaphunzira kapena kulandira kapena kumva kuchokera kwa ine kapena mwaona mwa ine. Ndipo Mulungu wamtendere adzakhala nanu.
Kuthokoza Chifukwa cha Mphatso
10 Ndikukondwa kwambiri mwa Ambuye kuti patapita nthawi tsopano mwayambanso kuonetsa kuti mumandiganizira. Zoonadi, mwakhala mukundikumbukira, koma munalibe mpata woti muonetsere zimenezi. 11 Sindikunena izi chifukwa choti ndikusowa thandizo, poti ine ndaphunzira kukhala wokwaniritsidwa ndi zimene ndili nazo. 12 Ndimadziwa kusauka nʼkutani, ndipo ndimadziwa kulemera nʼkutani. Ndaphunzira chinsinsi chokhala wokhutitsidwa mwa njira ina iliyonse, kaya nʼkudya bwino kapena kukhala ndi njala, kaya kukhala ndi chuma kapena umphawi. 13 Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.
14 Komatu munachita bwino kundithandiza mʼmavuto anga. 15 Ndipo inu Afilipi mukudziwa kuti masiku oyambirira olalikira Uthenga Wabwino, nditachoka ku Makedoniya, panalibe mpingo ndi umodzi omwe umene unagwirizana nane pa nkhani yopereka ndi kulandira, kupatula inu. 16 Pakuti ngakhale pamene ndinali ku Tesalonika, munanditumizira kangapo zondithandiza pa zosowa zanga. 17 Osati ndikufuna mphatso zanu, koma ndikufuna kuti pa zimene muli nazo pawonjezerekepo phindu. 18 Ndalandira zonse ndipo ndili nazo zokwanira zoposa zosowa zanga popeza ndalandira kwa Epafrodito mphatso zochuluka zimene munatumiza. Ndizo zopereka za fungo labwino, nsembe zolandiridwa zokondweretsa Mulungu. 19 Ndipo Mulungu wanga adzakwaniritsa zosowa zanu monga mwa chuma chake chaulemerero mwa Khristu Yesu.
20 Kwa Mulungu ndi Atate athu, kukhale ulemerero mpaka muyaya. Ameni.
Malonje Otsiriza
21 Perekani moni kwa oyera mtima onse mwa Khristu Yesu. Abale amene ali ndi ine akupereka moni wawo. 22 Oyera mtima onse akupereka moni, makamaka iwo a ku nyumba ya Kaisara.
23 Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu. Ameni.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.