Old/New Testament
Nyimbo ya Matamando
26 Tsiku limenelo anthu a mʼdziko la Yuda adzayimba nyimbo iyi.
Tili ndi mzinda wolimba.
Mulungu amawuteteza ndi zipupa
ndi malinga.
2 Tsekulani zipata za mzinda
kuti mtundu wolungama
ndi wokhulupirika ulowemo.
3 Inu mudzamupatsa munthu
wa mtima wokhazikika
mtendere weniweni.
4 Mudalireni Yehova mpaka muyaya,
chifukwa Yehova Mulungu ndiye Thanthwe losatha.
5 Iye amatsitsa anthu amene amadziyika pamwamba,
iye amagwetsa pansi mzinda wodzitukumula,
amagumula makoma ake
ndi kuwagwetsa pansi pa fumbi penipeni.
6 Mapazi a anthu akuwupondereza,
mapazi a anthu oponderezedwa,
mapazi anthu osauka.
7 Njira ya munthu wolungama ndi yosalaza,
Inu Wolungamayo, mumasalaza njira ya wolungama.
8 Inde Yehova, timayenda mʼnjira zanu zolungama,
ife timayembekezera Inu;
mitima yathu imakhumba kukumbukira
ndi kulemekeza dzina lanu.
9 Moyo wanga umalakalaka Inu usiku wonse;
nthawi yammawa ndimafunafuna Inu.
Pamene muweruza dziko lapansi
anthu amaphunzira kuchita chilungamo.
10 Ngakhale mukomere mtima anthu oyipa,
saphunzira chilungamo.
Amachita zoyipa mʼdziko la chilungamo,
ndipo sazindikira ululu wa Yehova.
11 Inu Yehova, mwatukula dzanja lanu kuti muwalange,
koma iwo sakuliona dzanjalo.
Aloleni anthu aone ndi kuchita manyazi poona mmene mukondera anthu anu;
ndipo moto umene mwasonkhera adani anu uwapsereze.
12 Yehova, mumatipatsa mtendere;
ndipo zonse zimene ife tinazichita munatichitira ndinu.
13 Inu Yehova Mulungu wathu, ngakhale takhala tikulamulidwa ndi ena mʼmalo mwanu,
koma ife timalemekeza dzina lanu lokha.
14 Iwo tsopano sadzadzukanso;
mizimu yawo sidzabwera kudzativutitsa
pakuti mwawalanga ndipo mwawawononga;
palibenso amene amawakumbukira.
15 Inu Yehova, mwaukulitsa mtundu wathu;
mwauchulukitsa ndithu
ndipo mwalandirapo ulemu;
mwaukuza mbali zonse za dziko.
16 Yehova, anthu anu anabwera kwa Inu pamene anali mʼmasautso;
pamene munawalanga,
iwo anapemphera kwa Inu.
17 Monga mayi woyembekezera pamene nthawi yake yobereka yayandikira
amamva kupweteka ndipo amalira ndi ululu,
ifenso tinali chimodzimodzi pamaso panu, Inu Yehova.
18 Ife chimodzimodzi tinamva ululu, ngati mayi pa nthawi yobala mwana,
koma sitinapindulepo kanthu,
kapena kupulumutsa dziko lapansi;
sitinabadwitse anthu atsopano pa dziko pano.
19 Koma anthu anu amene anafa adzakhalanso ndi moyo;
matupi awo adzadzuka.
Iwo amene ali ku fumbi tsopano
adzadzuka ndi kuyimba mosangalala.
Monga mame amafewetsa pansi kutsitsimutsa zomera,
momwenso Yehova adzaukitsa anthu amene anafa kale.
20 Abale anga, pitani mukalowe mʼnyumba zanu
ndipo mukadzitsekere;
mukabisale kwa kanthawi kochepa
mpaka ukali wake utatha.
21 Taonani, Yehova akubwera kuchokera kumene amakhala;
akubwera kudzalanga anthu a dziko lapansi chifukwa cha machimo awo.
Dziko lapansi lidzawulula magazi amene anakhetsedwa pa dzikolo;
dziko lapansi silidzabisanso mitembo ya anthu ophedwa.
Za Munda Wamphesa wa Yehova
27 Tsiku limenelo,
Yehova ndi lupanga lake
lakuthwa, lalikulu ndi lamphamvu,
adzalanga Leviyatani chinjoka chothawa chija,
Leviyatani chinjoka chodzikulunga;
adzapha chirombo choopsa cha mʼnyanja.
2 Tsiku limenelo Yehova adzati,
“Tidzayimba nyimbo ya munda wamphesa wobereka bwino:
3 Ine, Yehova, ndimawuyangʼanira;
ndimawuthirira nthawi zonse.
Ndimawulondera usana ndi usiku
kuti wina angawononge.
4 Ine sindinakwiye.
Ngati mkandankhuku ndi minga zikanaoneka ndikanalimbana nazo!
Ndikachita nazo nkhondo;
ndikanazitentha zonse ndi moto.
5 Koma ngati apo ayi, abweretu kwa Ine adani angawo kuti ndidzawateteze;
apangane nane za mtendere,
ndithu, apangane nane za mtendere.”
6 Masiku akubwerawo Yakobo adzazika mizu,
Israeli adzaphukira ndi kuchita maluwa,
ndipo adzadzaza dziko lonse lapansi ndi zipatso.
7 Kodi Yehova anakantha Israeli
ngati momwe anakanthira anthu amene anazunza Israeli?
Kapena kodi Yehova anapha Israeli
ngati mmene anthu ena anaphera Israeli?
8 Yehova mwawalanga powapirikitsa ndi kuwatumiza ku ukapolo,
mwawachotsa ndi mpweya wanu woopsa,
monga zimachitikira pa tsiku la mkuntho wochokera kummawa.
9 Yehova adzakhululuka kulakwa kwa Yakobo.
Iwo adzaonetsa kuti alapadi pamene adzaphwanya miyala yonse ya guwa lachikunja,
ngati mmene anthu amaphwanyira miyala yanjereza
mpaka kukhala ngati fumbi lokhalokha.
Sipadzapezekanso mafano a Asera
kapena maguwa ofukiza lubani.
10 Mzinda wamalinga uja wasanduka bwinja,
wasanduka malo osiyidwa, ndi kutayidwa ngati chipululu;
kumeneko amadyetselako ana angʼombe
kumeneko zimapumulako ziweto
ndi kumwetula nthambi za mitengo kotheratu.
11 Pamene nthambi za mitengoyo zauma, zimathyoka
ndipo amayi amabwera nazitola ndi kuzisandutsa nkhuni.
Pakuti awa ndi anthu opanda nzeru;
kotero Mulungu amene anawapanga sadzachitira chisoni,
ndipo Mlengi wawo sawakomera mtima.
12 Tsiku limenelo Yehova adzasonkhanitsa pamodzi anthu ake mmodzimmodzi kumalo opunthira tirigu, kuchokera ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku mtsinje wa ku Igupto. 13 Ndipo tsiku limenelo lipenga lalikulu lidzalira. Amene akuzunzika ku Asiriya iwo amene ali ku ukapolo ku Igupto adzabwera ndi kudzalambira Yehova pa phiri lopatulika mu Yerusalemu.
Kutsanzira Kudzichepetsa kwa Khristu
2 Ngati muli ndi chilimbikitso chilichonse chifukwa cholumikizana ndi Khristu, ngati muli ndi chitonthozo chifukwa cha chikondi chake, ngati muli ndi mtima umodzi mwa Mzimu, ndipo ngati mumakomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, 2 tsono tsirizani chimwemwe changa pokhala amaganizo ofanana, achikondi chimodzimodzi, amodzi mu mzimu ndi acholinga chimodzinso. 3 Musachite kalikonse ndi mtima odzikonda chabe kapena odzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa ndipo aliyense aziona mnzake ngati womuposa iyeyo. 4 Musamangofuna zokomera inu nokha koma aliyense azifuna zokomeranso ena.
5 Pa ubale wanu wina ndi mnzake, mukhale ndi mtima wofanana ndi wa Khristu Yesu:
6 Iyeyu, pokhala Mulungu ndithu,
sanatenge kufanana ndi Mulungu kukhala chinthu choyenera kuchigwiritsa.
7 Koma anadzichepetsa kotheratu
nakhala ndi khalidwe ngati la kapolo
ndi kukhala munthu ngati anthu ena onse.
8 Ndipo pokhala munthu choncho
anadzichepetsa yekha
ndipo anamvera mpaka imfa yake,
imfa yake ya pamtanda!
9 Choncho Mulungu anamukweza Iye kukhala wapamwamba kwambiri,
ndipo anamupatsa dzina loposa dzina lina lililonse
10 kuti pakumva dzina la Yesu, bondo lililonse limugwadire,
kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi pansi pa dziko,
11 ndipo lilime lililonse livomereze kuti Yesu Khristu ndi Ambuye
kuchitira ulemu Mulungu Atate.
Kuwala monga Nyenyezi
12 Tsono, abwenzi anga okondedwa, monga mwakhala omvera nthawi zonse, osati pamene ndinali nanu pokha, koma tsopano koposa pamene ndili kutali. Pitirizani kugwira ntchito ya chipulumutso chanu mwa mantha ndi kunjenjemera, 13 pakuti ndi Mulungu amene amagwira ntchito mwa inu kuti mufune ndi kuchita zimene zimamukondweretsa Iyeyo.
14 Muzichita zonse mosawiringula kapena mosatsutsapo, 15 kuti mukhale wopanda cholakwa ndi angwiro, ana a Mulungu wopanda cholakwika mu mʼbado uno wachinyengo ndi wosocheretsa. Mukatero mudzawala pakati pawo ngati nyenyezi zakumwamba 16 powawuza mawu amoyo. Ndipo ine ndidzatha kunyadira pa tsiku la Khristu kuti sindinathamange kapena kugwira ntchito pachabe. 17 Koma ngakhale ndikuthiridwa ngati nsembe ya chakumwa yoperekedwa pa nsembe ndi pa utumiki wochokera mʼchikhulupiriro chanu, ndine wokondwa ndi wosangalala pamodzi ndi inu nonse. 18 Chomwechonso, inu khalani okondwa ndi osangalala nane pamodzi.
Timoteyo ndi Epafrodito
19 Ngati Ambuye Yesu alola, ndikukhulupirira kuti ndidzamutuma Timoteyo msanga kwanuko, kuti mwina ndingadzasangalale ndikadzamva za moyo wanu. 20 Ndilibenso wina monga iyeyu amene ali ndi chidwi chenicheni pa za moyo wanu. 21 Pakuti aliyense amangofuna zokomera iye yekha osati zokomera Yesu Khristu. 22 Koma inu mukudziwa kuti Timoteyo wadzionetsa yekha, chifukwa watumikira ndi ine pa ntchito ya Uthenga Wabwino monga mwana ndi abambo ake. 23 Choncho ndikuyembekezera kumutuma msanga ndikangodziwa mmene zinthu zanga ziyendere. 24 Ndipo ndikukhulupirira kuti Ambuye akalola ine mwini ndidzafikanso kwanuko posachedwapa.
25 Koma ndikuganiza kuti nʼkofunika kuti ndikutumizireni mʼbale wanga Epafrodito, mtumiki mnzanga ndi msilikali mnzanga, amenenso ndi mtumiki wanu amene munamutumiza kuti adzandithandize pa zosowa zanga. 26 Pakuti akukulakalakani nonsenu ndipo akusauka mu mtima chifukwa munamva kuti akudwala. 27 Zoonadi ankadwala ndipo anatsala pangʼono kumwalira. Koma Mulungu anamuchitira chifundo, ndipo sanangomuchitira chifundo iye yekhayu komanso ine, kuti chisoni changa chisachuluke. 28 Choncho khumbo langa lofulumiza kumutumiza lakula, kuti pamene mumuonenso musangalale komanso kuti nkhawa yanga ichepe. 29 Mulandireni mwa Ambuye ndi chimwemwe chachikulu, ndipo anthu onga iyeyu muziwachitira ulemu. 30 Iyeyu anatsala pangʼono kufa chifukwa cha ntchito ya Khristu, anayika moyo pa chiswe kuti akwaniritse thandizo limene inu simukanatha.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.