Old/New Testament
Za Chilango cha Igupto ndi Kusi
20 Mʼchaka chimene mkulu wankhondo wotumidwa ndi mfumu ya ku Asiriya, anabwera ku Asidodi ndi kuwuthira nkhondo ndi kuwulanda, 2 nthawi imeneyo Yehova anawuza Yesaya mwana wa Amozi kuti, “Pita kavule chiguduli ndi nsapato zako.” Ndipo iye anaterodi, ankangoyenda wamaliseche ndiponso wopanda nsapato.
3 Kenaka Yehova anati, “Monga momwe mtumiki wanga Yesaya wakhala akuyendera wamaliseche ndiponso wopanda nsapato kwa zaka zitatu ngati chizindikiro ndi chenjezo kwa dziko la Igupto ndi Kusi, 4 momwemonso mfumu ya ku Asiriya idzatenga ukapolo anthu a ku Igupto ndi a ku Kusi, anyamata ndi okalamba. Iwo adzakhala amaliseche ndi opanda nsapato, matako ali pa mtunda. Zimenezi zidzachititsa manyazi Igupto. 5 Amene ankadalira Kusi, ndiponso amene ankadzitukumula chifukwa cha Igupto adzakhumudwa ndi kuchita manyazi. 6 Tsiku limenelo anthu amene amakhala mʼmbali mwa nyanja adzati, ‘Taonani zomwe zawachitikira amene ife tinkawadalira, amene ife tinkathawirako kuti atithandize ndi kutipulumutsa kwa mfumu ya ku Asiriya! Nanga ife tidzapulumuka bwanji?’ ”
Za Chilango cha Babuloni
21 Uthenga wonena za chipululu cha mʼmbali mwa Nyanja.
Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya adzabwera ngati kamvuluvulu amene akuwomba modutsa mʼmbali ya nyanja,
kuchokera ku chipululu,
dziko lochititsa mantha.
2 Ine ndaona zinthu zoopsa mʼmasomphenya:
Wonyenga akunyenga, wofunkha akufunkha komanso owononga akuwononga.
Elamu, yambani nkhondo! Mediya, zingani mzinda!
Ine ndidzathetsa mavuto onse amene anayambitsa Ababuloni.
3 Chifukwa cha zimenezi thupi langa likunjenjemera ndi mantha,
ndikumva ululu ngati wa mayi amene akubereka;
ndikuvutika kwambiri ndi zimene ndikumva,
ndathedwa nzeru ndi zimene ndikuziona.
4 Mtima wanga ukugunda,
ndipo ndikunjenjemera ndi mantha;
chisisira chimene ndakhala ndikuchifuna
chasanduka chinthu choopsa kwa ine.
5 Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya akukonza matebulo,
akuyala mphasa,
akudya komanso kumwa!
Mwadzidzidzi anamva mawu akuti, “Dzukani inu ankhondo,
pakani mafuta zishango zanu!”
6 Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi;
“Pita, kayike mlonda
kuti azinena zimene akuziona.
7 Taonani, anthu akubwera ali pa akavalo
ndipo akuyenda awiriawiri,
okwera pa bulu
kapena okwera pa ngamira,
mlondayo akhale tcheru kwambiri.”
8 Ndipo mlondayo anafuwula kuti,
“Ambuye anga, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa nsanja yolondera;
Usiku uliwonse ndimakhala pa malo anga olondera.
9 Taonani, uyo munthu akubwera atakwera pa galeta
ali ndi gulu la akavalo.
Mmodzi wa iwo akuti,
‘Babuloni wagwa, wagwa!
Mafano onse a milungu yake
agwa pansi ndipo aphwanyika!’ ”
10 Inu anthu anga opunthidwa ndi kupetedwa ngati tirigu,
ine ndikukuwuzani zimene ndamva
ndikukuwuzani Uthenga wochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse,
Mulungu wa Israeli.
Za Chilango cha Edomu
11 Uthenga wonena za Duma:
Munthu wina akundiyitana kuchokera ku Seiri kuti,
“Iwe mlonda, usikuwu utha liti?
Iwe mlonda, utha liti kodi usikuwu?”
12 Mlonda akuyankha kuti,
“Kukucha, koma kudanso.
Ngati ukufuna kufunsa, funsa tsopano;
ndipo ubwerenso udzafunse.”
Za Chilango cha Arabiya
13 Uthenga wonena za Arabiya:
Inu anthu amalonda a ku Dedani,
amene usiku mumagona mʼzithukuluzi za ku Arabiya,
14 perekani madzi kwa anthu aludzu.
Inu anthu a ku Tema
perekani chakudya kwa anthu othawa nkhondo.
15 Iwo akuthawa malupanga,
lupanga losololedwa,
akuthawa uta wokokakoka
ndiponso nkhondo yoopsa.
16 Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi: “Chaka chimodzi chisanathe, potsata mmene amawerengera munthu waganyu, ulemerero wonse wa Kedara udzatheratu. 17 Mwa anthu okoka uta, ankhondo a ku Kedara opulumuka adzakhala owerengeka.” Wayankhula ndi Yehova Mulungu wa Israeli.
Za Chilango cha Yerusalemu
22 Uthenga wonena za Chigwa cha Masomphenya:
Kodi chachitika nʼchiyani,
kuti nonsenu mukwere pa madenga?
2 Iwe mzinda wodzaza ndi chisangalalo chodzaza tsaya,
iwe mzinda waphokoso ndi wosokonekera?
Anthu ako ophedwa aja sanaphedwe ndi lupanga,
kapena kufera pa nkhondo.
3 Atsogoleri ako onse ngakhale anathawa limodzi;
koma anagwidwa osadziteteza nʼkomwe.
Inu munapezeka ndipo nonse pamodzi munatengedwa ukapolo,
ngakhale munathawa pamene mdani akanali patali.
4 Nʼchifukwa chake Ine ndinati, “Chokani pamaso panga;
ndilekeni ndilire ndi mtima wowawa.
Musayesere kunditonthoza
chifukwa cha kuwonongeka kwa anthu anga.”
5 Lero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse walola kuti tione
mavuto ndi kugonjetsedwa ndiponso chisokonezo
mʼChigwa cha Masomphenya.
Malinga agumuka,
komanso anthu akanalira mofuwula ku mapiri.
6 Ankhondo a ku Elamu anadza pa magaleta
ndi akavalo ali ndi mivi mʼmanja.
Ankhondo a ku Kiri anakonzeka ndi zishango.
7 Zigwa zanu zachonde ndi zodzaza ndi magaleta,
ndipo asilikali okwera pa akavalo ayikidwa pa zipata za mzinda;
8 zonse zoteteza Yuda zachotsedwa.
Ndipo tsiku limenelo munayangʼanayangʼana
zida zankhondo zomwe zinali mʼnyumba yaufumu ya nkhalango;
9 inu munaona kuti makoma ambiri a mzinda wa Davide
anali ndi malo ambiri ogumuka;
munasunga madzi
mu chidziwe chakumunsi.
10 Munawerenga nyumba zonse za mu Yerusalemu
ndipo munagwetsa nyumba zina kuti mulimbitse linga logumuka lija.
11 Pakati pa makoma awiri munamanga chitsime
chosungiramo madzi ochokera ku dziwe lakale,
koma inu simunadalire Mulungu amene anapanga zimenezi,
kapena kusamalako za Iye amene anazilenga kale lomwe.
12 Pa tsiku limenelo, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse
anakuyitanani kuti mulire ndi kukhetsa misozi;
kumeta mutu wanu mpala
ndi kuvala ziguduli.
13 Koma mʼmalo mwake inu munakondwa ndi kusangalala;
munapha ngʼombe ndi nkhosa;
munadya nyama ndi kumwa vinyo.
Inu mumati, “Tiyeni tidye ndi kumwa
pakuti mawa tifa!”
14 Yehova Wamphamvuzonse wandiwululira mondinongʼoneza kuti, “Tchimo limeneli sindidzakhululuka mpaka tsiku la kufa kwanu,” akutero Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse.
15 Chimene Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Pita, ukanene kwa Sabina kapitawo,
amene amayangʼanira nyumba yaufumu:
16 Kodi ukuchita chiyani kuno, nanga ndani anakupatsa chilolezo
kuti udzikumbire manda kuno,
kudzikumbira manda pa phiri
ndi kudzisemera malo opumulira mʼthanthwe?
17 “Samalira, Yehova watsala pangʼono kukugwira zolimba
ndi kukuponya mwamphamvu, iwe munthu wamphamvu.
18 Iye adzakukulunga kwambiri ngati mpira
ndipo adzakuponyera mʼdziko lalikulu.
Kumeneko ndiko ukafere
ndipo kumeneko ndiko kudzatsalire magaleta ako.
Ndipo udzasanduka wochititsa manyazi nyumba ya mbuye wako.
19 Ine ndidzakuchotsa pa ukapitawo wako
ndipo ndidzakutsitsa pa udindo wako.
20 “Tsiku limenelo ndidzayitanitsa mtumiki wanga, Eliyakimu mwana wa Hilikiya. 21 Ndidzamuveka mkanjo wako ndi kumangira lamba wako mʼchiwuno mwake ndi kumupatsa ulamuliro wako. Iye adzakhala kholo la amene amakhala mu Yerusalemu ndiponso a fuko la Yuda. 22 Ndidzamupatsa ulamuliro wa banja la Davide. Adzatsekula ndipo palibe adzatseke, adzatseka popanda wina kutsekula. 23 Ufumu wake udzakhala wokhazikika ngati chikhomo chokhomedwa pa malo olimba. Anthu adzalemekeza nyumba ya abale ake chifukwa cha iye. 24 Ana ndi abale a nyumba ya abambo ake adzakhala ngati katundu pa iye ngati ziwiya zopanda ntchito zimene zapachikidwa pa chikhomo.
25 “Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Tsiku limeneli chikhomo chokhomedwa kwambiri chija sichidzalimbanso; chidzazuka ndipo chidzagwa ndipo zonse zopachikidwa zidzawonongedwa.’ ” Yehova wayankhula chomwechi.
Ana ndi Makolo Awo
6 Inu ana, mverani makolo anu mwa Ambuye, pakuti zimenezi ndi zoyenera. 2 “Lemekeza abambo ndi amayi ako.” Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo. 3 Ngati ulemekeza abambo ako ndi amayi ako, “zinthu zidzakuyendera bwino ndipo udzasangalala ndi moyo wautali pa dziko lapansi.” 4 Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye.
Antchito ndi Mabwana Awo
5 Inu antchito, mverani mabwana anu mwaulemu ndi mwamantha ndi moona mtima, monga momwe mungamvere Khristu. 6 Musawamvere pamene akukuonani kuti akukomereni mtima, koma ngati akapolo a Khristu ochita chifuniro cha Mulungu kuchokera mu mtima mwanu. 7 Tumikirani ndi mtima wonse, ngati kuti mukutumikira Ambuye, osati anthu. 8 Inu mukudziwa kuti Ambuye adzamupatsa munthu aliyense mphotho chifukwa cha ntchito yake yabwino imene anagwira, kaya munthuyo ndi kapolo kapena mfulu.
9 Ndipo inu mabwana, muziwachitiranso chimodzimodzi antchito anu. Musamawaopseze, popeza mukudziwa kuti Mbuye wawo ndi wanunso, nonse Mbuye wanu ali kumwamba, ndipo Iyeyo alibe tsankho.
Zida Zankhondo za Mulungu
10 Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye ndi mwa mphamvu zake zazikulu. 11 Valani zida zonse za Mulungu kuti muthe kuyima ndi kukana machenjerero a Satana. 12 Pakuti sitikulimbana ndi thupi ndi magazi, koma tikulimbana ndi maufumu, maulamuliro, mphamvu za dziko la mdima, ndi mphamvu zoyipa kwambiri zauzimu zamlengalenga. 13 Choncho valani zida zonse za Mulungu, kuti pamene tsiku loyipa kwambiri lifika, mudzathe kuyima chilili, ndipo mutatha kuchita zonse, mudzayimabe mwamphamvu. 14 Tsono imani mwamphamvu, mutamangira choonadi ngati lamba mʼchiwuno mwanu, mutavala chilungamo ngati chitsulo chotchinjiriza pa chifuwa. 15 Valani Uthenga Wabwino wamtendere ku mapazi anu ngati nsapato. 16 Kuwonjezera pa zonsezi, nyamulani chishango cha chikhulupiriro, ndipo ndi chimenechi mudzatha kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya oyipayo. 17 Valani chipewa cha chipulumutso ndi kutenga lupanga la mzimu, limene ndi Mawu a Mulungu. 18 Ndipo mupemphere mwa Mzimu nthawi zonse, mʼmitundu yonse ya mapemphero ndi zopempha. Ndipo pozindikira izi, khalani achangu kupempherera oyera mtima nthawi zonse.
19 Mundipempherere inenso, kuti nthawi iliyonse pamene nditsekula pakamwa panga, andipatse mawu kuti ndiwulule zinsinsi za Uthenga Wabwino mopanda mantha. 20 Ndine kazembe wa Uthenga Wabwinowu ngakhale ndili womangidwa mʼndende. Pempherani kuti ndilalikire mopanda mantha, monga ndiyenera.
Mawu Otsiriza
21 Tukiko, mʼbale wanga wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye, adzakuwuzani zonse kuti inunso mudziwe mmene ndilili ndi zimene ndikuchita. 22 Ine ndikumutumiza kwa inu, kuti mudziwe za moyo wathu, ndi kuti akulimbikitseni.
23 Mtendere, chikondi pamodzi ndi chikhulupiriro kuchokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi abale onse. 24 Chisomo kwa onse amene amakonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosatha.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.