Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 14-16

14 Yehova adzachitira chifundo Yakobo;
    adzasankhanso Israeli
    ndi kuwalola kuti akhalenso mʼdziko lawo.
Alendo adzabwera kudzakhala nawo
    ndi kudziphatika okha kukhala ngati a mʼnyumba ya Yakobo.
Anthu a mitundu ina adzaperekeza a Israeli
    ku dziko lawo.
Tsono Aisraeli adzasandutsa anthu a mitundu ina aja
    kukhala antchito awo aamuna ndi aakazi mʼdziko la Yehova.
Ndiye kuti Aisraeli adzasandutsa akapolo anthu amene kale anali ambuye awo.
    Iwo adzasandutsa akapolo anthu amene kale ankawalamulira ndi kuwazunza.

Yehova akadzakupumitsani ku zowawa ndi mavuto, ndiponso kuntchito yakalavulagaga imene ankakugwiritsani, mudzayankhula monyogodola mfumu ya Babuloni kuti,

Wopsinja uja watha!
    Ukali wake uja watha!
Yehova wathyola chikwapu cha anthu oyipa,
    Iye waphwanya ndodo ya olamulira.
Mfumu ya ku Babuloni inkakantha mitundu ya anthu mwaukali
    powamenya kosalekeza,
Iyo inkagonjetsa anthu a mitundu ina mwaukali
    ndikuwazunza kosalekeza.
Koma tsopano mayiko onse ali pa mpumulo ndi pa mtendere;
    ndipo akuyimba mokondwa.
Ngakhale mitengo ya payini ndi mikungudza ya ku Lebanoni
    ikuyimba za iwe mokondwa ndipo ikuti,
“Chigwetsedwere chako pansi,
    palibe wina anabwera kudzatigwetsa.”

Ku manda kwatekeseka
    kuti akulandire ukamabwera;
mizimu ya anthu akufa, aja amene anali atsogoleri
    a dziko lapansi, yadzutsidwa.
Onse amene anali mafumu a mitundu ya anthu
    ayimiritsidwa pa mipando yawo.
10 Onse adzayankha;
    adzanena kwa iwe kuti,
“Iwenso watheratu mphamvu ngati ife;
    Iwe wafanana ndi ife.”
11 Ulemerero wako wonse walowa mʼmanda,
    pamodzi ndi nyimbo za azeze ako;
mphutsi zayalana pogona pako
    ndipo chofunda chako ndi nyongolotsi.

12 Wagwa pansi bwanji kuchoka kumwamba,
    iwe nthanda, mwana wa mʼbandakucha!
Wagwetsedwa pansi pa dziko lapansi,
    Iwe amene unagonjetsapo mitundu ya anthu!
13 Mu mtima mwako unkanena kuti,
    “Ndidzakwera mpaka kumwamba;
ndidzakhazika mpando wanga waufumu
    pamwamba pa nyenyezi za Mulungu;
ndidzakhala pa mpando waufumu pa phiri losonkhanirako,
    pamwamba penipeni pa phiri la kumpoto.
14 Ndidzakwera pamwamba pa mitambo;
    ndidzafanana ndi Wammwambamwamba.”
15 Koma watsitsidwa mʼmanda
    pansi penipeni pa dzenje.

16 Anthu akufa adzakupenyetsetsa
    nadzamalingalira za iwe nʼkumati,
“Kodi uyu ndi munthu uja anagwedeza dziko lapansi
    ndi kunjenjemeretsa maufumu,
17 munthu amene anasandutsa dziko lonse chipululu,
    amene anagwetsa mizinda yake
    ndipo sankalola kuti anthu ogwidwa abwerere kwawo?”

18 Mafumu onse a mitundu ya anthu akugona mwaulemu
    aliyense mʼmanda akeake.
19 Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako,
    ngati nthambi yowola ndi yonyansa.
Mtembo wako waphimbidwa ndi anthu ophedwa;
    amene anabayidwa ndi lupanga,
    anatsikira mʼdzenje lamiyala
ngati mtembo woponderezedwa.
20     Sudzayikidwa nawo mʼmanda mwaulemu,
chifukwa unawononga dziko lako
    ndi kupha anthu ako.

Zidzukulu za anthu oyipa
    sizidzakumbukika nʼpangʼono pomwe.
21 Konzani malo woti muphere ana ake aamuna
    chifukwa cha machimo a makolo awo;
kuti angadzuke ndi kulanda dziko lapansi
    ndi kulidzaza dziko lonselo ndi mizinda yawo.

22 Yehova Wamphamvuzonse akuti,
    “Ine ndidzathira nkhondo mzinda wa Babuloni.
Ndidzachotseratu mu Babuloni dzina lake ndi onse otsaliramo.
    Ndiye kuti sipadzakhala ana kapena zidzukulu,”
            akutero Yehova.
23 “Ndidzawusandutsa mzindawo malo okhalamo anungu
    ndiponso dambo lamatope;
ndidzawusesa ndi tsache lowononga,”
    akutero Yehova Wamphamvuzonse.

Za Kulangidwa kwa Asiriya

24 Yehova Wamphamvuzonse walumbira kuti,

“Ndithudi, monga ndaganizira ndidzachitadi choncho,
    ndipo monga momwe ndatsimikizira zidzakhala momwemo ndithu.
25 Ndidzawawononga Asiriya mʼdziko langa;
    ndidzawapondereza ndi mapazi pa mapiri anga;
ndidzachotsa goli lawo pa anthu anga,
    ndipo ndidzachotsa katundu wawo pa mapewa awo.”

26 Izi ndizo ndakonza kuti zichitike pa dziko lonse lapansi,
    ndatambasula dzanja pa anthu a mitundu yonse.
27 Pakuti Yehova Wamphamvuzonse watsimikiza, ndipo ndani angamuletse?
    Dzanja lake latambasulidwa ndipo ndani angalibweze?

Za Kulangidwa kwa Afilisti

28 Uthenga uwu unabwera chaka chimene mfumu Ahazi anamwalira:

29 Musakondwere inu Afilisti nonse
    kuti Asiriya amene anali ngati ndodo yokukanthani anathedwa;
chifukwa kuchokera ku njoka yomweyi (mfumu ya Aasiriya) mudzatuluka mphiri,
    ndipo chipatso chake chidzakhala njoka yaliwiro ndiponso yaululu.
30 Osaukitsitsa adzapeza chakudya
    ndipo amphawi adzakhala mwamtendere.
Koma anthu ako ndidzawawononga ndi njala,
    ndipo njalayo idzapha ngakhale opulumuka ako.

31 Lirani kwambiri, anthu a pa chipata! Fuwulani kwambiri, anthu a mu mzinda!
    Njenjemerani ndi mantha, inu Afilisti nonse!
Mtambo wa utsi ukuchokera kumpoto,
    ndipo palibe wamantha pakati pa ankhondo ake.
32 Kodi tidzawayankha chiyani
    amithenga a ku Filisitiya?
“Yehova wakhazikitsa Ziyoni,
    ndipo mu mzinda wakewu, anthu ozunzika apeza populumukira.”

Za Kulangidwa kwa Mowabu

15 Uthenga wonena za Mowabu:

Popeza kuti mu usiku umodzi wokha mzinda wa Ari wa ku Mowabu wawonongedwa,
    wawonongedwa pa usiku umodzi wokha.
Mzinda wa Kiri wawonongedwa,
    wawonongedwa pa usiku umodzi wokha.
Anthu a ku Diboni akupita ku nyumba ya milungu yawo,
    akupita ku malo awo achipembedzo kukalira;
    anthu a ku Mowabu akulirira mofuwula mzinda wa Nebo ndi wa Medeba.
Mutu uliwonse wametedwa mpala,
    ndipo ndevu zonse zametedwa.
Mʼmisewu akuvala ziguduli;
    pa madenga ndi mʼmabwalo
aliyense akulira mofuwula,
    misozi ili pupupu.
Anthu a ku Hesiboni ndi Eleali akulira mofuwula,
    mawu awo akumveka mpaka ku Yahazi.
Kotero asilikali a ku Mowabu akulira mofuwula,
    ndipo ataya mtima.

Inenso ndikulirira Mowabu;
    chifukwa othawa nkhondo ake akupita akulira ku chikweza cha Luluti mpaka ku Zowari
    ndi Egilati-Selisiya
akupita akulira ku chikweza cha Luhiti,
    Akulira mosweka mtima
pa njira yopita ku Horonaimu;
    akulira mosweka mtima chifukwa cha chiwonongeko chawo.
Madzi a ku Nimurimu aphwa
    ndipo udzu wauma;
zomera zawonongeka
    ndipo palibe chomera chobiriwira chatsala.
Kotero kuti chuma chomwe anachipeza ndi kuchisunga,
    achitenga kuti awoloke nacho chigwembe cha Misondozi.
Kulira kwawo kukumveka mʼdziko lonse la Mowabu;
    kulira kwawo kosweka mtima kukumveka
    mpaka ku Egilaimu ndi Beeri-Elimu.
Madzi a ku Dimoni afiira ndi magazi,
    komabe ndidzabweretsa zina zambiri pa Dimoni,
mkango woti udzagwire aliyense othawa mu Mowabu
    ndi aliyense wotsala mʼdzikomo.
16 Anthu a ku Mowabu
    atumiza mphatso za ana ankhosa onenepa,
kuchokera ku Sela kudutsa chipululu
    mpaka kukafika ku phiri la Ziyoni.
Monga momwe mbalame zimawulukira uku ndi uku
    akazimwaza mʼchisa,
momwemonso akazi a ku Mowabu
    akuyendayenda ku madooko a Arinoni.

Amowabu aja anawuza a ku Yuda kuti,
    “Tiwuzeni chochita, gamulani zoti tichite.
Inu mutiteteze kwa adani anthu.
    Mukhale ngati mthunzi wathu dzuwa lili pa liwombo.
Mutibise,
    musatipereke ife othawa nkhondo kwa adani athu.
Lolani kuti anthu othawa nkhondo a ku Mowabu azikhala pakati panu;
    mukhale populumukira pawo kwa wowonongayo.”

Nthawi idzafika ndipo wozunzayo sadzakhalaponso,
    kuwononga kudzaleka;
    waukaliyo adzachoka mʼdzikomo.
Mpando waufumu udzakhazikitsidwa mwachikondi;
    mmodzi mwa zidzukulu za Davide adzakhalapo mokhulupirika.
Iyeyo poweruza adzatsata chilungamo
    ndipo adzalimbikitsa kuchita zachilungamo.

Tinamva kuti Mowabu anadzikuza kwambiri.
    Kunyada kwawo
ndi kunyogodola kwawo ndi kudzitama kwawo,
    zonse ndi zopanda phindu.
Nʼchifukwa chake Amowabu akulira kwambiri;
    iwo akulirira dziko lawo.
Akubuma momvetsa chisoni
    chifukwa cha makeke a mphesa a ku Kiri Hareseti.
Minda ya ku Hesiboni yauma,
    minda ya mpesa ya ku Sibina yaguga.
Atsogoleri a mitundu ina anapondaponda
    minda ya mpesa wabwino,
imene nthambi zake zinakafika ku Yazeri,
    mpaka kutambalalira ku chipululu.
Mizu yake inakafika
    mpaka ku tsidya la nyanja.
Kotero Ine ndikulira, monga mmene akulirira anthu a ku Yazeri,
    chifukwa cha minda ya mpesa ya ku Sibima.
Inu anthu a ku Hesiboni, inu anthu a ku Eleali,
    ndikukunyowetsani ndi misozi!
Mwalephera kupeza zokolola,
    chifukwa cha nkhondo imene inawononga zokolola zonse.
10 Chimwemwe ndi chisangalalo zalekeka ku minda yanu ya zipatso;
    palibe amene akuyimba kapena kufuwula mʼminda ya mpesa;
palibe amene akupsinya vinyo ku malo opsinyira mphesa,
    pakuti ndathetsa kufuwula.
11 Chifukwa chake moyo wanga ukulira ngati pangwe kulirira Mowabu,
    mtima wanga ukubuwula chifukwa cha Kiri Hareseti.
12 Ngakhale anthu a ku Mowabu
    apite ku malo awo achipembedzo
koma amangodzitopetsa ndi kutaya nthawi chabe
    chifukwa sizidzatheka.

13 Awa ndi mawu amene Yehova wayankhula kale zokhudza Mowabu. 14 Koma tsopano Yehova akuti, “Zisanathe zaka zitatu, potsata mʼmene munthu waganyu amawerengera, ulemerero wa Mowabu udzakhala utatheratu ndipo anthu ake ambiri adzakhala atawonongeka, ndipo opulumuka ake adzakhala ochepa ndi ofowoka.”

Aefeso 5:1-16

Choncho, monga ana okondedwa, tsatirani chitsanzo cha Mulungu. Muzikondana monga Khristu anakonda ife nadzipereka yekha chifukwa cha ife monga chopereka cha fungo lokoma ndi nsembe kwa Mulungu.

Koma pakati panu pasamveke nʼpangʼono pomwe zadama, kapena za mtundu wina uliwonse wa chodetsa, kapena za umbombo, chifukwa izi ndi zosayenera kwa anthu oyera a Mulungu. Musamatukwane, kuyankhula zopusa kapena kunena nthabwala zopanda pake, zomwe ndi zosayenera, koma mʼmalo mwake muziyamika. Dziwani ichi, palibe wadama, wochita zonyansa kapena waumbombo, munthu wotero ali ngati wopembedza mafano, amenewa alibe malo mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu. Musalole wina akunamizeni ndi mawu opanda pake, pakuti chifukwa cha zinthu ngati izi mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa amene samvera. Nʼchifukwa chake musamayanjane nawo anthu otere.

Pajatu inu nthawi ina munali mdima, koma tsopano ndinu kuwunika mwa Ambuye. Mukhale ngati ana akuwunika (pakuti pamene pali kuwunika pamapezekaponso zabwino zonse, chilungamo ndi choonadi). 10 Inu mufufuze chimene chimakondweretsa Ambuye. 11 Musayanjane nazo ntchito zosapindulitsa za mdima, koma mʼmalo mwake muzitsutse. 12 Pakuti ndi zochititsa manyazi ngakhale kutchula zomwe zimachitika mseri. 13 Koma kuwala kumawunikira zinthu, ndipo chilichonse chimaonekera poyera. Choncho chilichonse choonekera poyera chimasandukanso kuwala. 14 Nʼchifukwa chake Malemba akuti,

“Dzuka, wamtulo iwe,
    uka kwa akufa,
    ndipo Khristu adzakuwalira.”

15 Samalani makhalidwe anu, musakhale ngati opanda nzeru koma ngati anzeru. 16 Gwiritsani ntchito mpata uliwonse, chifukwa masiku ano ndi oyipa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.