Old/New Testament
Za Ufumu Wamtendere wa Mesiya
11 Padzatuluka mphukira pa tsinde la Yese
ndipo nthambi idzaphukira kuchokera ku mizu yake.
2 Mzimu wa Yehova udzakhala pa iye
Mzimu wanzeru ndi wa kumvetsa zinthu,
Mzimu wauphungu ndi wamphamvu,
Mzimu wachidziwitso ndi wakuopa Yehova.
3 Ndipo kuopa Yehova ndiye chidzakhale chinthu chomukondweretsa.
Iye sadzaweruza potsata zooneka pamaso,
kapena kugamula mlandu potsata zakumva;
4 koma amphawi adzawaweruza mwachilungamo,
adzaweruza mwachilungamo mlandu wa anthu osauka a dziko lapansi.
Iye adzakantha dziko lapansi ndi mawu ake;
atalamula Iyeyu anthu oyipa adzaphedwa.
5 Chilungamo chidzakhala ngati lamba wake
ndipo kukhulupirika kudzakhala ngati chomangira mʼchiwuno mwake.
6 Mʼmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wankhosa,
kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwana wambuzi,
mwana wangʼombe ndi mwana wa mkango adzadyera limodzi
ndipo mwana wamngʼono adzaziweta.
7 Ngʼombe yayikazi ndi chimbalangondo zidzadya pamodzi,
ana awo adzagona pamodzi,
ndipo mkango udzadya udzu ngati ngʼombe.
8 Mwana wakhanda adzasewera pa dzenje la mamba,
ndipo mwana wamngʼono adzapisa dzanja lake ku phanga la mphiri osalumidwa.
9 Sipadzakhala chilichonse chopweteka kapena chowononga
pa phiri lopatulika la Yehova,
pakuti anthu a dziko lapansi adzadzaza ndi nzeru yotha kudziwa Yehova
monga momwe nyanja imadzazira ndi madzi.
10 Tsiku limenelo mfumu yatsopano yochokera pa Muzu wa Yese idzakhala ngati chizindikiro kwa anthu a mitundu yonse. Mitundu ya anthu idzasonkhana kwa Iye, ndipo malo awo okhalapo adzakhala aulemerero. 11 Tsiku limenelo Ambuye adzatambasula dzanja lake kachiwiri kuti awombole anthu ake otsalira ku Asiriya, ku Igupto, ku Patirosi, Kusi, ku Elamu, ku Sinana, ku Hamati ndi pa zilumba za nyanja yamchere.
12 Adzakwezera mitundu ya anthu mbendera,
ndipo adzasonkhanitsa otayika a ku Israeli;
Iye adzasonkhanitsa anthu obalalika a ku Yuda
kuchokera ku mbali zonse zinayi za dziko lapansi.
13 Nsanje ya Efereimu idzatha,
ndipo adani a Yuda adzatha;
Efereimu sadzachitira nsanje Yuda,
ngakhale Yuda sadzamuda Efereimu.
14 Yuda ndi Efereimu adzathira nkhondo pa Afilisti mbali ya kumadzulo;
ndipo onsewo pamodzi adzalanda zinthu za anthu a kummawa.
Adzalimbana ndi Edomu ndi Mowabu,
ndipo Aamoni adzawagonjera.
15 Yehova adzaphwetsa
mwendo wa nyanja ya Igupto;
adzatambasula dzanja lake ndipo adzawombetsa mphepo yotentha
pa mtsinje wa Yufurate.
Iye adzawugawa mtsinjewo kukhala timitsinje tisanu ndi tiwiri
kuti anthu athe kuwoloka powuma atavala nsapato.
16 Padzakhala msewu waukulu woti ayendepo anthu ake otsalira
amene anatsalira ku Asiriya,
monga mmene panali msewu waukulu woyendapo Israeli
pamene amachokera ku Igupto.
Nyimbo za Mayamiko
12 Tsiku limenelo aliyense wa inu adzati:
“Ndikukuyamikani, Inu Yehova;
chifukwa ngakhale munandipsera mtima,
mkwiyo wanu wachoka,
ndipo mwanditonthoza.
2 Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga;
ndidzamudalira ndipo sindidzachita mantha.
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;
Iye wakhala chipulumutso changa.”
3 Mudzakondwera popeza Yehova
ali ngati chitsime cha chipulumutso chanu.
4 Tsiku limenelo mudzati:
“Yamikani Yehova, tamandani dzina lake;
mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu,
ndipo mulalike kuti dzina lake ndi lopambana.
5 Imbirani Yehova, pakuti wachita ntchito zazikulu;
zimenezi zidziwike pa dziko lonse lapansi.
6 Fuwulani ndi kuyimba mwachimwemwe, inu anthu a ku Ziyoni;
pakuti Woyerayo wa Israeli ndi wamkulu pakati panu.”
Kulangidwa Kwa Babuloni
13 Uthenga onena za Babuloni umene Yesaya mwana wa Amozi anawulandira:
2 Kwezani mbendera yankhondo pa phiri loti see,
muwafuwulire ankhondo;
muwakodole kuti adzalowe pa zipata
za anthu olemekezeka.
3 Ine Yehova, ndalamulira ankhondo anga;
ndasonkhanitsa ankhondo anga kuti akhale zida zanga zolangira
amene amadzikuza ndi chipambano changa.
4 Tamvani phokoso ku mapiri,
likumveka ngati phokoso la gulu lalikulu la anthu!
Tamvani phokoso pakati pa maufumu,
ngati kuti mitundu ya anthu ikusonkhana pamodzi!
Yehova Wamphamvuzonse akukhazika asilikali ake mokonzekera
kuchita nkhondo.
5 Iwo akuchokera ku mayiko akutali,
kuchokera kumalekezero a dziko
Yehova ali ndi zida zake za nkhondo
kuti adzawononge dziko la Babuloni.
6 Lirani mofuwula, pakuti tsiku la Yehova layandikira;
lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuzonse.
7 Zimenezi zinafowoketsa manja onse,
mtima wa munthu aliyense udzachokamo.
8 Anthu adzagwidwa ndi mantha aakulu,
zowawa ndi masautso zidzawagwera;
adzamva zowawa zonga amamva mayi pobereka.
Adzayangʼanana mwamantha,
nkhope zawo zikufiira ngati malawi amoto.
9 Taonani, tsiku la Yehova likubwera,
tsiku lopanda chisoni, lawukali ndi lamkwiyo;
kudzasandutsa dziko kuti likhale chipululu
ndi kuwononga anthu ochimwa a mʼmenemo.
10 Nyenyezi zakumwamba ndiponso zonse zamlengalenga
sizidzaonetsa kuwala kwawo.
Dzuwa lidzada potuluka,
ndipo mwezi sudzawala konse.
11 Ndidzalanga dziko lonse chifukwa cha zolakwa zake,
anthu oyipa ndidzawalanga chifukwa cha machimo awo.
Ndidzathetsa kunyada kwa odzikuza,
ndipo ndidzatsitsa kudzitukumula kwa anthu ankhanza.
12 Ndidzasandutsa anthu kukhala ovuta kupeza kuposa mmene amasowera golide wabwino.
Iwo sazidzapezekapezeka kuposa mmene amasowera golide wa ku Ofiri.
13 Tsono ndidzagwedeza miyamba
ndipo dziko lapansi lidzachoka pa maziko ake.
Izi zidzachitika chifukwa cha ukali wa Wamphamvuzonse
pa tsiku la mkwiyo wake woopsa.
14 Ngati mbawala zosakidwa,
ngati nkhosa zopanda wozikusa,
munthu aliyense adzabwerera kwa anthu akwawo,
aliyense adzathawira ku dziko lake.
15 Aliyense amene atadzapezeke ndi kugwidwa
adzaphedwa momubaya ndi lupanga.
16 Ana awo akhanda adzaphwanyidwa iwo akuona;
nyumba zawo zidzafunkhidwa ndipo akazi awo adzagwiriridwa.
17 Taona, Ine ndidzadzutsa Amedi amene safuna siliva
ndipo sasangalatsidwa ndi golide,
kuti amenyane ndi Ababuloni.
18 Adzapha anyamata ndi mauta awo;
sadzachitira chifundo ana
ngakhale kumvera chisoni ana akhanda.
19 Babuloni, ufumu wake ndi waulemerero kuposa mafumu onse.
Anthu ake amawunyadira.
Koma Yehova adzawuwononga
ngati mmene anawonongera Sodomu ndi Gomora.
20 Anthu sadzakhalamonso
kapena kukhazikikamo pa mibado yonse;
palibe Mwarabu amene adzayimike tenti yake,
palibe mʼbusa amene adzawetamo ziweto zake.
21 Koma nyama zakuthengo ndizo zidzakhale kumeneko,
nyumba zake zidzadzaza ndi nkhandwe;
mu mzindamo muzidzakhala akadzidzi,
ndipo atonde akuthengo azidzalumphalumphamo.
22 Mu nsanja zake muzidzalira afisi,
mʼnyumba zake zokongola muzidzalira nkhandwe.
Nthawi yake yayandikira
ndipo masiku ake ali pafupi kutha.
Umodzi Mʼthupi la Khristu
4 Ine monga wamʼndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukulimbikitsani kuti mukhale moyo woyenera mayitanidwe amene munalandira. 2 Mukhale odzichepetsa kwathunthu ndi ofatsa; mukhale oleza mtima, ololerana wina ndi mnzake mwachikondi. 3 Muyesetse kusunga umodzi wa Mzimu; umodzi umene umatimangirira pamodzi mu mtendere. 4 Pali thupi limodzi ndiponso Mzimu mmodzi, monganso pali chiyembekezo chimodzi chimene anakuyitanirani. 5 Pali Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi; 6 Mulungu mmodzi ndi Atate a onse, ndipo ali mwa onse.
7 Koma aliyense wa ife wapatsidwa chisomo molingana ndi muyeso wa mphatso ya Khristu. 8 Nʼchifukwa chake akunena kuti,
“Iye atakwera kumwamba,
anatenga chigulu cha a mʼndende
ndipo anapereka mphatso kwa anthu.”
9 Kodi mawu akuti, “Iye anakwera” akutanthauza chiyani, ngati Iyeyo sanatsikire kunsi kwa dziko lapansi? 10 Iye amene anatsika ndi yemweyo anakwera koposa mʼmayiko a kumwamba onse, ndi cholinga choti zinthu zonse zikhale zodzaza ndi Iye. 11 Iye ndiye amene anapereka mphatso kwa ena kuti akhale atumwi ndi ena aneneri, ena alaliki, ndi ena abusa ndi aphunzitsi. 12 Ntchito yawo ndi kukonza oyera mtima kuti agwire ntchito ya utumiki kuti thupi la Khristu lilimbikitsidwe. 13 Izi zidzatifikitsa tonse ku umodzi wachikhulupiriro, kumudziwa Mwana wa Mulungu, kukhwima msinkhu ndi kufika pa muyeso wangwiro weniweni wopezeka mwa Khristu.
14 Motero sitidzakhalanso makanda, ogwedezekagwedezeka ndi mafunde, otengekatengeka ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso ndi kuchenjera kwa anthu achinyengo amene amasocheretsa anthu ndi kuchenjera kwawo. 15 Mʼmalo mwake, poyankhula choonadi mwachikondi, tidzakula mu zinthu zonse ndi kukhala thupi la Khristu, amene ndi Mutu, omwe ndi mpingo. 16 Mwa Iye thupi lonse lalumikizidwa ndi kugwirana pamodzi ndi mitsempha yothandizira. Likukula ndi kudzilimbitsa lokha mwachikondi, pomwe chiwalo chilichonse chikugwira ntchito yake.
Malangizo pa Makhalidwe a Chikhristu
17 Tsono ine ndikukuwuzani izi, ndipo ndikunenetsa mwa Ambuye, kuti musayendenso monga amachitira anthu a mitundu ina potsata maganizo awo opanda pake. 18 Maganizo awo ndi odetsedwa, ndi osiyanitsidwa ndi moyo wa Mulungu chifukwa cha umbuli umene uli mwa iwo chifukwa cha kuwuma mtima kwawo. 19 Popeza sazindikiranso kanthu kalikonse, adzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite mtundu uliwonse wa zoyipa ndi zilakolako zosatha.
20 Koma inu simunadziwe Khristu mʼnjira yotere. 21 Zoonadi munamva za Iye ndipo munaphunzitsidwa mwa Iye molingana ndi choonadi chimene chili mwa Yesu. 22 Inu munaphunzitsidwa molingana ndi moyo wanu wakale, kuchotsa umunthu wakale, umene ukupitirira kuwonongeka ndi zilakolako zachinyengo; 23 kuti mukonzedwe mwatsopano mʼmitima mwanu; 24 ndi kuti muvale umunthu watsopano, wolengedwa kuti ufanane ndi Mulungu mu chilungamo chenicheni ndi chiyero.
25 Chifukwa chake, aliyense wa inu aleke kunama ndipo ayankhule zoona kwa mʼbale wake, pakuti ife tonse ndife ziwalo za thupi limodzi. 26 Kwiyani koma musachimwe. Dzuwa lisalowe mukanali chikwiyire. 27 Musamupatse mpata Satana. 28 Iye amene wakhala akuba asabenso, koma agwire ntchito ndi kuchita kenakake kaphindu ndi manja ake, kuti akhale ndi kenakake kogawana ndi amene akusowa.
29 Mʼkamwa mwanu musatuluke mawu aliwonse onyansa, koma okhawo amene ndi othandiza kulimbikitsa ena molingana ndi zosowa zawo, kuti athandize amene akawamve. 30 Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu amene mwasindikizidwa naye chizindikiro cha tsiku la kuwomboledwa. 31 Chotsani kuzondana, ukali ndi kupsa mtima, chiwawa ndi kuyankhula zachipongwe, pamodzi ndi choyipa chilichonse. 32 Mukomerane mtima ndi kuchitirana chifundo wina ndi mnzake. Khululukiranani wina ndi mnzake, monga momwe Mulungu anakukhululukirani mwa Khristu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.