Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 7-8

Yesaya Achenjeza Ahazi

Pamene Ahazi mwana wa Yotamu, mdzukulu wa Uziya anali mfumu ya Yuda, Rezini mfumu ya Siriya ndi Peka mwana wa Remaliya, mfumu ya Israeli anabwera kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu, koma sanathe kuwugonjetsa.

Tsono nyumba ya Davide inawuzidwa kuti, “Dziko la Siriya lagwirizana ndi Efereimu.” Choncho mfumu Ahazi ndi anthu ake ananjenjemera, monga momwe mitengo ya mʼnkhalango imagwedezekera ndi mphepo.

Pamenepo Yehova anawuza Yesaya kuti, “Tuluka, iwe ndi mwana wako Seariyasubu, mupite mukakumane ndi Ahazi kumapeto kwa ngalande yamadzi yochokera ku Dziwe Lakumtunda, pa msewu wopita ku Munda wa mmisiri wochapa nsalu. Ukamuwuze kuti, ‘Chenjera, khala phee ndipo usaope. Usataye mtima chifukwa cha zitsa ziwiri zomwe zikufuka, chifukwa cha ukali woopsa wa Rezini ndi Siriya, ndiponso wa Peka mwana wa Remaliya. Mfumu ya Siriya, Efereimu ndi mwana wa Remaliya apangana kuti akuchitire choyipa. Akunena kuti, ‘Tiyeni tikalimbane ndi Yuda. Tiyeni tiliwononge ndi kuligawa; tiligawane pakati pathu, ndipo tilonge ufumu mwana wa Tabeeli kumeneko.’ Komabe zimene akunena Ambuye Yehova ndi izi:

“ ‘Zimenezo sizidzatheka,
    sizidzachitika konse,
pakuti Siriya amadalira Damasiko,
    ndipo Damasiko amadalira mfumu Rezini basi.
Zisanathe zaka 65
    Efereimu adzawonongedwa kotheratu, sadzakhalanso mtundu wa anthu.
Dziko la Efereimu limadalira Samariya
    ndipo Samariya amadalira mwana wa Remaliya basi.
Mukapanda kulimbika pa chikhulupiriro chanu,
    ndithu simudzalimba konse.’ ”

10 Yehova anayankhulanso ndi Ahazi, 11 “Pempha chizindikiro kwa Yehova Mulungu wako, chikhale chozama ngati manda kapena chachitali ngati mlengalenga.”

12 Koma Ahazi anati, “Ine sindipempha; sindikufuna kuyesa Yehova.”

13 Apo Yesaya anati, “Imva tsopano, iwe nyumba ya Davide! Kodi sikokwanira kutopetsa anthu? Kodi mudzayeseranso kutopetsa Mulungu wanga? 14 Nʼchifukwa chake Ambuye mwini adzakupatsani chizindikiro: Onani, namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli. 15 Azidzadya chambiko ndi uchi, mpaka atadziwa kukana choyipa ndi kusankha chabwino. 16 Koma nthawi yokana choyipa ndi kusankha chabwino kwa mwanayo isanafike, mayiko a mafumu awiri amene amakuopsaniwo adzakhala atasanduka bwinja. 17 Yehova adzabweretsa pa inu, pa anthu anu ndiponso pa nyumba ya bambo wanu masiku a mavuto woti sanakhalepo kuyambira tsiku limene Efereimu anapatukana ndi Yuda. Yehova adzabweretsa mfumu ya ku Asiriya.”

18 Tsiku limenelo Yehova adzalizira likhweru ntchentche zochokera ku mitsinje yakutali ku Igupto, ndiponso njuchi zochokera ku dziko la Asiriya. 19 Onsewo adzafika ndi kudzakhazikika mu zigwa zozama, mʼmingʼalu ya matanthwe ndi mʼzitsamba zonse zaminga ndiponso ponse pamene pali malo omwetsera ziweto. 20 Tsiku limenelo Ambuye adzalemba ganyu ometa ochokera kutsidya kwa Mtsinje, ndiye mfumu ya ku Asiriya, kudzameta tsitsi lanu la ku mutu ndi la mʼmiyendo ndi ndevu zomwe. 21 Tsiku limenelo adzangosunga ngʼombe yayikazi yayingʼono ndi mbuzi ziwiri. 22 Ndipo chifukwa cha kuchuluka kwa mkaka umene ziwetozi zidzapereka, munthuyo azidzadya chambiko. Aliyense amene adzatsalire mʼdzikomo azidzadya chambiko ndi uchi. 23 Tsiku limenelo, paliponse pamene panali mitengo ya mpesa 1,000 ndipo mtengo wake ndi wokwana masekeli asiliva 1,000, padzamera mkandankhuku ndi minga. 24 Anthu adzapita kumeneko kukachita uzimba ali ndi uta ndi mivi, popeza kuti mʼdziko monsemo mudzakhala mkandankhuku ndi minga. 25 Ndipo mʼmapiri monse mʼmene kale munkalimidwa ndi khasu, simudzapitamo kuopa mkandankhuku ndi minga; malowo adzasanduka odyetserako ngʼombe ndi nkhosa.

Asiriya, Chida cha Yehova

Yehova anati kwa ine, “Tenga cholembapo chachikulu ndipo ulembepo malemba odziwika bwino: Kusakaza-Kwamsanga Kufunkha-Kofulumira. Ndipo ndidzayitana wansembe Uriya ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya kuti akhale mboni zanga zodalirika.”

Ndipo ine ndinapita kwa mneneri wamkazi, ndipo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna. Ndipo Yehova anati kwa ine, “Umutche dzina lakuti, ‘Kusakaza-Kwamsanga Kufunkha-Kofulumira.’ Mwanayo asanayambe kudziwa kuyitana kuti, ‘Ababa’ kapena ‘Amama’ chuma cha Damasiko ndi zofunkha za Samariya zidzatengedwa ndi mfumu ya ku Asiriya.”

Yehova anayankhulanso ndi Ine;

“Popeza anthu a dziko ili akana
    madzi anga oyenda mwachifatse a ku Siloamu,
ndipo akukondwerera Rezini
    ndi mwana wa Remaliya,
nʼchifukwa chake Ambuye ali pafupi kubweretsa
    madzi amkokomo a mtsinje wa Yufurate kudzalimbana nawo;
    mfumu ya ku Asiriya ndi gulu lake lonse lankhondo.
Madziwo adzasefukira mʼngalande zake zonse
    ndi mʼmagombe ake onse.
Ndipo adzalowa mwamphamvu mʼdziko la Yuda, adzasefukira,
    adzapitirira mpaka kumuyesa mʼkhosi.
Mapiko ake otambasuka adzaphimba dziko lako lonse,
    iwe Imanueli!”

Chitani phokoso lankhondo, inu mitundu ya anthu, ndipo munjenjemere!
    Tamverani, inu mayiko onse akutali.
Konzekerani nkhondo ndipo munjenjemere!
    Konzekerani nkhondo ndipo munjenjemere!
10 Konzani kachitidwe kanu kankhondo, koma simudzaphula kanthu,
    kambiranani zochita, koma zidzalephereka,
pakuti Mulungu ali nafe.

Yehova Achenjeza Mneneri

11 Yehova anandiyankhula ine mwamphamvu, ndipo anandichenjeza kuti ndisamayende mʼnjira za anthuwa. Iye anati:

12 “Usamanene kuti ndi chiwembu,
    chilichonse chimene anthuwa amati ndi chiwembu
usamaope zimene anthuwa amaziopa,
    ndipo usamachite nazo mantha.
13 Yehova Wamphamvuzonse ndiye amene uyenera kumuona kuti ndi woyera,
    ndiye amene uyenera kumuopa,
    ndiye amene uyenera kuchita naye mantha,
14 ndipo ndiye amene adzakhala malo opatulika;
    koma kwa anthu a ku Yuda ndi kwa anthu a ku Israeli adzakhala
mwala wopunthwitsa,
    mwala umene umapunthwitsa anthu,
thanthwe limene limagwetsa anthu.
    Ndipo kwa anthu a mu Yerusalemu adzakhala ngati msampha ndi khwekhwe.
15 Anthu ambiri adzapunthwapo
    adzagwa ndi kuthyokathyoka,
    adzakodwa ndi kugwidwa.”

16 Manga umboniwu
    ndipo umate malamulowa pamaso pa ophunzira anga.
17 Ndidzayembekezera Yehova,
    amene akubisira nkhope yake nyumba ya Yakobo.
Ine ndidzakhulupirira Iyeyo.

18 Onani, ine ndili pano pamodzi ndi ana amene Yehova wandipatsa, ndife zizindikiro ndi zodabwitsa kwa Aisraeli zochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse, amene amakhala pa Phiri la Ziyoni.

19 Anthu akakuwuza kuti kafunsire kwa oyankhula ndi mizimu, amene amayankhula monongʼona ndi mongʼungʼudza, kodi anthu sayenera kukafunsira kwa Mulungu wawo? Chifukwa chiyani amafunsira kwa anthu akufa mʼmalo mwa kwa anthu amoyo, 20 kuti akalandireko mawu enieni ndi malangizo? Ngati anthuwo sayankhula monga mwa mawu awa, mwa iwo mulibe kuwala. 21 Anthu adzayendayenda mʼdziko movutika kwambiri ali ndi njala; pamene afowokeratu ndi njala, iwo adzakwiya kwambiri ndipo adzayangʼana kumwamba ndi kutemberera mfumu yawo ndi Mulungu wawo. 22 Ndipo akadzayangʼana pa dziko lapansi adzangoona mavuto okhaokha ndi mdima woopsa ndi wodetsa nkhawa, ndipo adzaponyedwa mu mdima wandiweyani.

Aefeso 2

Amene anali Akufa Alandira Moyo

Kunena za inu, kale munali akufa chifukwa cha zolakwa zanu ndi machimo anu, mmene inu munkakhalamo pamene munkatsatira njira za dziko lapansi ndi za ulamuliro waufumu wa mlengalenga, mzimu umene ukugwira ntchito tsopano mwa amene samvera. Nthawi ina tonsefe tinalinso ndi moyo wonga wawo, tinkachitanso zilizonse zimene matupi ndi maganizo athu ankafuna. Mwachibadwa chathu, tinali oyenera chilango monga anthu ena onse. Koma chifukwa cha chikondi chake chachikulu pa ife, Mulungu amene ndi olemera mʼchifundo, anatipanga kukhala amoyo ndi Khristu ngakhale pamene ife tinali akufa mu zolakwa zathu. Koma tinapulumutsidwa mwachisomo. Ndipo Mulungu anatiukitsa pamodzi ndi Khristu ndi kutikhazika pamodzi ndi Iye mmwamba mwa Khristu Yesu, ndi cholinga chakuti mʼnthawi imene ikubwera, Iyeyo adzaonetse chuma choposa cha chisomo chake, choonetsedwa mwa kukoma mtima kwake kwa ife mwa Khristu Yesu. Pakuti mwapulumutsidwa mwachisomo, kudzera mʼchikhulupiriro ndipo izi sizochokera mwa inu eni, koma ndi mphatso ya Mulungu, osati ndi ntchito, kuti wina aliyense asadzitamandire. 10 Pakuti ndife ntchito ya Mulungu, olengedwa mwa Khristu Yesu kuti tichite ntchito zabwino, zimene Mulungu anazikonzeratu kale kuti tizichite.

Umodzi mwa Khristu

11 Chifukwa chake kumbukirani kuti poyamba inu amene munali anthu a mitundu ina mwachibadwa ndipo munkatchedwa “osachita mdulidwe” ndi amene amadzitcha okha “a mdulidwe” (zimene zinachitika mʼthupi ndi manja a anthu). 12 Kumbukirani kuti nthawi imene inu munali wopanda Khristu, simunkawerengedwa ngati nzika za Israeli ndipo munali alendo pa pangano la lonjezo, wopanda chiyembekezo ndi opanda Mulungu mʼdziko lapansi. 13 Koma tsopano mwa Khristu Yesu, inu amene nthawi ina munali kutali, mwabweretsedwa pafupi kudzera mʼmagazi a Khristu.

14 Pakuti Iye mwini ndiye mtendere wathu, amene anachita kuti awiri akhale mmodzi ndipo anagumula chotchinga, khoma la udani lotilekanitsa, 15 pothetsa mʼthupi lake lamulo pamodzi ndi zolamulira zake ndi malangizo. Cholinga chake chinali chakuti alenge mwa Iye mwini, munthu mmodzi watsopano kuchokera kwa abwino, motero nʼkupanga mtendere, 16 ndi kuyanjanitsa onse awiriwa mʼthupi lake kwa Mulungu, kudzera pa mtanda, umene Iye anaphapo udani wawo. 17 Iye anabwera ndipo analalikira mtendere kwa inu amene munali kutali ndi mtendere ndiponso kwa iwonso amene anali pafupi. 18 Pakuti mwa Iye, ife tonse titha kufika kwa Atate mwa Mzimu mmodzi.

19 Kotero kuti, inu sindinunso alendo ndi adani, koma nzika pamodzi ndi anthu a Mulungu ndiponso a mʼbanja la Mulungu. 20 Ndinu okhazikika pa maziko a atumwi ndi a aneneri, pamodzi ndi Khristu Yesu mwini ngati mwala wa pa ngodya. 21 Mwa Iyeyo, nyumba yonse yalumikizidwa pamodzi ndipo yakwezedwa kukhala Nyumba yoyera mwa Ambuye. 22 Ndipo mwa Iye, inunso mukamangidwa pamodzi ndi ena onse kukhala nyumba yokhalamo imene Mulungu amakhala mwa Mzimu wake.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.