Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 5-6

Nyimbo ya Munda Wamphesa

Ndidzamuyimbira bwenzi langa
    nyimbo yokamba za munda wake wa mpesa:
Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesa
    pa phiri la nthaka yachonde.
Anatipula nachotsa miyala yonse
    ndipo anawokamo mipesa yabwino kwambiri.
Anamanga nsanja yolondera pakati pa mundawo
    ndipo anasemanso mopsinyira mphesa mʼmundamo.
Ndipo iye anayembekezera kuti mundawo udzabala mphesa zabwino,
    koma ayi, unabala mphesa zosadya.

“Tsopano, inu amene mumakhala mu Yerusalemu ndi inu anthu a ku Yuda,
    weruzani pakati pa ine ndi munda wanga wa mpesawu.
Kodi nʼchiyaninso china chimene ndikanachitira munda wanga wa mpesa
    kupambana chomwe ndawuchitira kale?
Pamene ndinkayembekezera kuti udzabala mphesa zabwino,
    bwanji unabala mphesa zosadya?
Tsopano ndikuwuzani
    chimene ndidzawuchitire munda wanga wa mpesa:
ndidzachotsa mpanda wake,
    ndipo mundawo udzawonongeka;
ndidzagwetsa khoma lake,
    ndipo nyama zidzapondapondamo.
Ndidzawusandutsa tsala,
    udzakhala wosatengulira ndi wosalimira
    ndipo mudzamera mkandankhuku ndi minga ina.
Ndidzalamula mitambo
    kuti isagwetse mvula pa mundapo.”

Munda wamphesa wa Yehova Wamphamvuzonse
    ndi Aisraeli,
ndipo anthu a ku Yuda ndiwo
    minda yake yomukondweretsa.
Ndipo Iye ankayembekezera chiweruzo cholungama, mʼmalo mwake anaona kuphana;
    mʼmalo mwa chilungamo Iye anamva kulira kwa anthu ozunzika.

Tsoka ndi Chiweruzo

Tsoka kwa inu amene mumangokhalira kulumikiza nyumba,
    ndipo mumangokhalira kuwonjezera minda,
mpaka mutalanda malo onse
    kuti muzikhalamo nokha mʼdzikomo.

Yehova Wamphamvuzonse wayankhula ine ndikumva kuti,

“Ndithudi nyumba zambirizo zidzasanduka mabwinja,
    nyumba zazikulu zokongolazo zidzakhala zopanda anthu.
10 Munda wamphesa wa maekala khumi udzatulutsa vinyo wodzaza mbiya imodzi,
    kufesa madengu khumi a mbewu, zokolola zake zidzangodzaza dengu limodzi.”

11 Tsoka kwa iwo amene amadzuka mmamawa
    nathamangira chakumwa choledzeretsa,
amene amamwa mpaka usiku
    kufikira ataledzera kotheratu.
12 Pa maphwando awo pamakhala azeze, apangwe,
    matambolini, zitoliro ndi vinyo,
ndipo sasamala ntchito za Yehova,
    salemekeza ntchito za manja ake.
13 Motero anthu anga adzatengedwa ukapolo
    chifukwa cha kusamvetsa zinthu;
atsogoleri awo olemekezeka adzafa ndi njala,
    ndipo anthu wamba ochuluka adzafa ndi ludzu.
14 Nʼchifukwa chake ku manda sikukhuta
    ndipo kwayasama kwambiri kukamwa kwake;
mʼmandamo mudzagweranso anthu otchuka a mu Yerusalemu pamodzi ndi anthu wamba ochuluka;
    adzagweramo ali wowowo, nʼkuledzera kwawoko.
15 Ndipo munthu aliyense adzatsitsidwa,
    anthu onse adzachepetsedwa,
    anthu odzikuza adzachita manyazi.
16 Koma Yehova Wamphamvuzonse adzalemekezedwa chifukwa cha chiweruzo chake cholungama.
    Ndipo Mulungu woyera adzadzionetsa kuti ndi woyera pochita chilungamo chake.
17 Tsono nkhosa zidzadya pamenepo ngati pabusa pawo;
    ana ankhosa adzadya mʼmabwinja a anthu olemera.

18 Tsoka kwa amene amadzikokera tchimo ndi zingwe zachinyengo,
    ndipo amadzikokera zoyipa ndi zingwe zokokera ngolo,
19 amene amanena kuti, “Yehova afulumire,
    agwire ntchito yake mwamsanga
    kuti ntchitoyo tiyione.
Ntchito zionekere,
    zimene Woyerayo wa Israeli akufuna kuchita,
    zichitike kuti tizione.”

20 Tsoka kwa amene zoyipa amaziyesa zabwino
    ndipo zabwino amaziyesa zoyipa,
amene mdima amawuyesa kuwala
    ndipo kuwala amakuyesa mdima,
amene zowawasa amaziyesa zotsekemera
    ndipo zotsekemera amaziyesa zowawasa.

21 Tsoka kwa amene amadziona ngati anzeru
    ndipo amadziyesa ochenjera.

22 Tsoka kwa zidakwa zimene zimayika mtima pa vinyo
    ndipo ndi akatswiri posakaniza zakumwa,
23 amene amamasula olakwa chifukwa cha chiphuphu
    koma amayipitsa mlandu wa munthu wosalakwa.
24 Nʼchifukwa chake monga momwe moto umawonongera chiputu
    ndipo monga momwe udzu wowuma umapsera mʼmalawi a moto,
momwemonso mizu yawo idzawola
    ndipo maluwa awo adzafota ndi kuwuluka ngati fumbi;
chifukwa akana malamulo a Yehova Wamphamvuzonse,
    ndipo anyoza mawu a Woyerayo wa Israeli.
25 Nʼchifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayakira anthu ake;
    watambasula dzanja lake pa anthuwo ndipo akuwakantha
Mapiri akugwedezeka,
    ndipo mitembo ya anthu yangoti mbwee mʼmisewu ngati zinyalala.

Komabe ngakhale watero, mkwiyo wake sunaleke,
    dzanja lake likanali chitambasulire;

26 Yehova wakweza mbendera kuyitana mtundu wa anthu akutali,
    akuyitana anthuwo ndi likhweru kuti abwere kuchokera ku mathero a dziko lapansi.
Awo akubwera,
    akubweradi mofulumira kwambiri!
27 Palibe ndi mmodzi yemwe amene akutopa kapena kupunthwa,
    palibe amene akusinza kapena kugona;
palibe lamba wa mʼchiwuno amene akumasuka,
    palibe chingwe cha nsapato chimene chaduka.
28 Mivi yawo ndi yakuthwa,
    mauta awo onse ndi okoka,
ziboda za akavalo awo nʼzolimba ngati mwala wansagalabwi,
    magaleta awo ndi aliwiro ngati kamvuluvulu.
29 Kufuwula kwawo kuli ngati kubangula kwa mkango,
    amabangula ngati misona ya mkango;
imadzuma pamene ikugwira nyama
    ndipo imapita nayo popanda ndi mmodzi yemwe woyipulumutsa.
30 Tsiku limenelo mitundu ya anthu idzabangula
    ngati mkokomo wa madzi a mʼnyanja.
Ndipo wina akakayangʼana dzikolo
    adzangoona mdima ndi zovuta;
    ngakhale kuwala kudzasanduka mdima chifukwa cha mitambo.

Masomphenya a Yesaya

Chaka chimene mfumu Uziya anamwalira, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu, wautali ndi wokwezedwa, ndipo mkanjo wawo unali wautali; kotero kuti unadzaza mʼNyumba ya Yehova. Pamwamba pawo panayimirira Aserafi, aliyense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi: awiri anaphimba nkhope zawo, awiri anaphimba mapazi awo, ndipo awiri ankawulukira. Ndipo Aserafiwo amafuwulirana kuti

“Woyera, woyera, woyera Yehova Wamphamvuzonse.
    Dziko lonse lapansi ladzaza ndi ulemerero wake.”

Chifukwa cha kufuwulako maziko a zitseko ndi ziwundo anagwedezeka ndipo mʼNyumba ya Yehova munadzaza utsi.

Tsono ine ndinafuwula kuti, “Tsoka langa ine! Ndatayika! Pakuti ndine munthu wapakamwa poyipa, ndipo ndimakhala pakati pa anthu a pakamwa poyipa, ndipo ndi maso anga ndaona mfumu Yehova Wamphamvuzonse.”

Pomwepo mmodzi mwa Aserafi aja anawulukira kwa ine ali ndi khala lamoto mʼdzanja lake, khala limene analichotsa ndi mbaniro pa guwa lansembe. Ndipo anandikhudza pakamwa panga ndi khala lamotolo nati, “Taona ndakhudza pa milomo yako ndi khalali; kulakwa kwako kwachotsedwa, machimo ako akhululukidwa.”

Kenaka ndinamva mawu a Ambuye akuti, “Kodi ndidzatuma yani? Ndipo ndani adzapite mʼmalo mwathu?”

Ndipo ine ndinati, “Ndilipo. Tumeni!”

Yehova anati, “Pita ndipo ukawawuze anthu awa:

“ ‘Kumva muzimva, koma osamvetsetsa;
    kupenya muzipenya koma osaona kanthu.’
10 Tsono anthu amenewa uwaphe mtima;
    uwagonthetse makutu,
    ndipo uwatseke mʼmaso.
Mwina angaone ndi maso awo,
    angamve ndi makutu awo,
    angamvetse ndi mitima yawo,
kenaka ndi kutembenuka mtima ndi kuchiritsidwa.”

11 Pamenepo ine ndinati, “Zimenezo ndi mpaka liti Inu Ambuye?”

Ndipo Iyeyo anandiyankha kuti,

“Mpaka mizinda itasanduka mabwinja
    nʼkusowa wokhalamo,
mpaka nyumba zitasowa anthu okhalamo,
    mpaka dziko litasanduka chipululu ndithu,
12 mpaka Yehova atasamutsira aliyense kutali,
    dziko nʼkusiyidwa kwathunthu.
13 Ndipo ngakhale chigawo chakhumi cha anthu chitatsala mʼdziko,
    nachonso chidzawonongedwa.
Koma monga momwe mitengo ya muwanga ndi thundu
    imasiyira chitsa pamene ayidula,
    chonchonso mbewu yoyera idzatsalira ngati chitsa chotsala mʼdziko.”

Aefeso 1

Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwachifuniro cha Mulungu.

Kulembera oyera mtima a ku Efeso, okhulupirika mwa Khristu Yesu:

Chisomo ndi mtendere kwa inu zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu.

Madalitso Auzimu mwa Khristu

Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, amene anatipatsa madalitso onse a uzimu kumwamba mwa Khristu. Dziko lapansi lisanalengedwe, Mulungu anatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi wopanda cholakwa pamaso pake. Mwa chikondi chake, Iye anakonzeratu kuti ife titengedwe ngati ana mwa Yesu Khristu, molingana ndi kukonda kwake ndi chifuniro chake. Anachita zimenezi kuti tiziyamika ulemerero wa chisomo chake, umene watipatsa kwaulere mwa Khristu amene amamukonda. Mwa Yesu Khristu, chifukwa cha magazi ake, ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo athu molingana ndi kuchuluka kwa chisomo cha Mulungu chimene anatipatsa mosawumira. Mwa nzeru zonse ndi chidziwitso, Iye watiwululira chifuniro chake chimene chinali chobisika, chimene anachikonzeratu mwa Khristu, molingana ndi kukoma mtima kwake. 10 Chimene anakonza kuti chichitike nʼchakuti, ikakwana nthawi yake asonkhanitsa pamodzi mwa Khristu zinthu zonse za kumwamba ndi pa dziko lapansi.

11 Iye anatisankhiratu mwa Khristu, atatikonzeratu molingana ndi machitidwe a Iye amene amachititsa zinthu zonse kuti zikwaniritse cholinga cha chifuniro chake, 12 nʼcholinga chakuti, ife amene tinali oyamba kukhala ndi chiyembekezo mwa Khristu, tiyamike ulemerero wake. 13 Ndipo inunso pamene munamva mawu a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, munayikidwanso mwa Khristu. Mutakhulupirira, anakusindikizani chizindikiro pokupatsani Mzimu Woyera amene Iye analonjeza. 14 Mzimu Woyerayo ndi chikole chotsimikizira kuti tidzalandira madalitso athu, ndipo kuti Mulungu anatiwombola kuti tikhale anthu ake. Iye anachita zimenezi kuti timuyamike ndi kumulemekeza.

Kuyamika ndi Kupemphera

15 Choncho, kuyambira pamene ndinamva za chikhulupiriro chanu mwa Ambuye Yesu ndi za chikondi chanu pa oyera mtima onse, 16 ine sindilekeza kuyamika Mulungu chifukwa cha inu. Ndimakukumbukirani mʼmapemphero anga. 17 Ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate a ulemerero akupatseni mzimu wa nzeru ndi wa vumbulutso, kuti mumudziwe kwenikweni. 18 Ndimapempheranso kuti maso a mitima yanu atsekuke ndi cholinga choti mudziwe chiyembekezo chimene Iye anakuyitanirani, chuma cha ulemerero chomwe chili mwa anthu oyera mtima. 19 Ndiponso ndikufuna kuti mudziwe mphamvu zake zazikulu koposa zimene zili mwa ife amene timakhulupirira. Mphamvuyi ndi yofanana ndi mphamvu yoposa ija 20 imene inagwira ntchito pamene Mulungu anaukitsa Khristu kwa akufa, namukhazika Iye ku dzanja lake lamanja mʼdziko la kumwamba. 21 Anamukhazika pamwamba pa ulamuliro onse ndi mafumu, mphamvu ndi ufumu, ndiponso pamwamba pa dzina lililonse limene angalitchule, osati nthawi ino yokha komanso imene ikubwerayo. 22 Ndipo Mulungu anayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake ndi kumusankha Iyeyo kukhala mutu pa chilichonse chifukwa cha mpingo, 23 umene ndi thupi lake, chidzalo cha Iye amene adzaza chilichonse mu njira iliyonse.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.