Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Nyimbo ya Solomoni 1-3

Nyimbo ya Solomoni, nyimbo yoposa nyimbo zonse.

Mkazi

Undipsompsone ndi milomo yako
    chifukwa chikondi chako nʼchokoma kuposa vinyo.
Mafuta ako odzola ndi onunkhira bwino;
    dzina lako lili ngati mafuta onunkhira otsanulidwa.
    Nʼchifukwa chake atsikana amakukonda!
Nditenge ndipo ndizikutsata, tiye tifulumire!
    Mfumu indilowetse mʼchipinda chake.

Abwenzi

Ife timasangalala ndi kukondwera nawe,
    tidzatamanda chikondi chako kupambana vinyo.

Mkazi

Amachita bwinotu potamanda iwe!

Ndine wakuda, komatu ndine wokongola,
    inu akazi a ku Yerusalemu,
    ine ndine wakuda ngati tenti ya ku Kedara,
    ngati makatani a tenti ya Solomoni.
Musandiyangʼane monyoza chifukwa ndine wakuda,
    ndine wakuda chifukwa cha dzuwa.
Alongo anga anandikwiyira
    ndipo anandigwiritsa ntchito mʼminda ya mpesa;
    munda wangawanga sindinawusamalire.
Ndiwuze iwe, amene ndimakukonda, kumene umadyetsa ziweto zako
    ndi kumene umagoneka nkhosa zako nthawi yamasana.
Ndikhalirenji ngati mkazi wachiwerewere
    pambali pa ziweto za abwenzi ako?

Abwenzi

Ngati sukudziwa iwe wokongola kwambiri kuposa akazi ena,
    ngati sukudziwa, tsatira makwalala a nkhosa
ndipo udyetse ana ambuzi
    pambali pa matenti a abusa.

Mwamuna

Iwe bwenzi langa,
    uli ngati kavalo wamkazi ku magaleta a Farao.
10 Masaya ako ndi okongola ndi ndolo zamʼmakutuzo,
    khosi lako likukongola ndi mikanda yamiyala yamtengowapatali.
11 Tidzakupangira ndolo zagolide
    zokongoletsedwa ndi mikanda yasiliva.

Mkazi

12 Pamene mfumu inali pa malo ake odyera,
    mafuta anga onunkhira anamveka fungo lake.
13 Wokondedwa wanga ali ngati kathumba ka mure kwa ine,
    kamene kamakhala pakati pa mawere angawa.
14 Wokondedwa wanga ali ngati mpukutu wa maluwa ofiira,
    ochokera ku minda ya mpesa ya ku Eni-Gedi.

Mwamuna

15 Iwe wokondedwa wanga, ndiwe wokongoladi!
    Ndithu, ndiwe chiphadzuwa,
    maso ako ali ngati nkhunda.

Mkazi

16 Iwe bwenzi langa, ndiwe wokongoladi!
    Ndithu, ndiwe wokongoladi kwambiri!
    Ndipo malo athu ogonapo ndi msipu wobiriwira.

Mwamuna

17 Mitanda ya nyumba yathu ndi ya mkungudza,
    phaso lake ndi la mtengo wa payini.

Mkazi

Ine ndine duwa la ku Saroni,
    duwa lokongola la ku zigwa.

Mwamuna

Monga duwa lokongola pakati pa minga
    ndi momwe alili wokondedwa wanga pakati pa atsikana.

Mkazi

Monga mtengo wa apulosi pakati pa mitengo ya mʼnkhalango
    ndi momwe alili bwenzi langa pakati pa anyamata.
Ndimakondwera kukhala pansi pa mthunzi wako,
    ndipo chipatso chake ndi chokoma mʼkamwa mwanga.
Iye wanditengera ku nyumba yaphwando,
    ndipo mbendera yake yozika pa ine ndi chikondi.
Undidyetse keke ya mphesa zowuma,
    unditsitsimutse ndi ma apulosi,
    pakuti chikondi chandifowoketsa.
Mutu wanga watsamira dzanja lake lamanzere,
    ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira.
Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani
    pali gwape ndi mbawala yayikazi zakuthengo:
Musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa
    mpaka pamene chifunire ichocho.

Tamverani bwenzi langa!
    Taonani! Uyu akubwera apayu,
akulumphalumpha pa mapiri,
    akujowajowa pa zitunda.
Bwenzi langa ali ngati gwape kapena mwana wa mbawala.
    Taonani! Uyo wayima kuseri kwa khoma lathulo,
akusuzumira mʼmazenera,
    akuyangʼana pa mpata wa zenera.
10 Bwenzi langa anayankha ndipo anati kwa ine,
    “Dzuka bwenzi langa,
    wokongola wanga, ndipo tiye tizipita.
11 Ona, nyengo yozizira yatha;
    mvula yatha ndipo yapitiratu.
12 Maluwa ayamba kuoneka pa dziko lapansi;
    nthawi yoyimba yafika,
kulira kwa njiwa kukumveka
    mʼdziko lathu.
13 Mtengo wankhuyu ukubereka zipatso zake zoyambirira;
    mitengo ya mpesa ya maluwa ikutulutsa fungo lake.
Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga
    tiye tizipita.”

Mwamuna

14 Nkhunda yanga yokhala mʼmingʼalu ya thanthwe,
    mʼmalo obisala a mʼmbali mwa phiri,
onetsa nkhope yako,
    nʼtamvako liwu lako;
pakuti liwu lako ndi lokoma,
    ndipo nkhope yako ndi yokongola.
15 Mutigwirire nkhandwe,
    nkhandwe zingʼonozingʼono
zimene zikuwononga minda ya mpesa,
    minda yathu ya mpesa imene yayamba maluwa.

Mkazi

16 Bwenzi langa ndi wangadi ndipo ine ndine wake;
    amadyetsa gulu lake la ziweto pakati pa maluwa okongola.
17 Kamphepo kamadzulo kakayamba kuwuzira
    ndipo mithunzi ikayamba kuthawa,
unyamuke bwenzi langa,
    ndipo ukhale ngati gwape
kapena ngati mwana wa mbawala
    pakati pa mapiri azigwembezigwembe.
Usiku wonse ndili pa bedi langa
    ndinafunafuna amene mtima wanga umamukonda;
    ndinamufunafuna koma osamupeza.
Ndikudzuka tsopano ndipo ndidzayendayenda mu mzinda,
    mʼmisewu yake ndi mʼmabwalo ake;
ndidzamufunafuna amene mtima wanga umamukonda.
    Kotero ine ndinamufunafuna iyeyo koma osamupeza.
Alonda anandipeza
    pamene ankayendera mzinda.
    “Kodi mwamuonako amene mtima wanga umamukonda?”
Nditawapitirira pangʼono
    ndinamupeza amene mtima wanga umamukonda.
Ndinamugwira ndipo sindinamulole kuti achoke
    mpaka nditamulowetsa mʼnyumba ya amayi anga,
    mʼchipinda cha amene anandibereka.
Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani
    pali gwape ndi mbawala yayikazi zakuthengo:
Musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa
    mpaka pamene chifunire ichocho.

Kodi ndani amene akubwera kuchokera ku chipululu
    ngati utsi watolotolo,
wonunkhira mure ndi lubani,
    zopangidwa kuchokera ku zonunkhira zonse za anthu amalonda?
Ona! Chimenecho ndi chonyamulira Solomoni,
    choperekezedwa ndi asilikali 60,
    anthu amphamvu a ku Israeli,
onse atanyamula lupanga,
    onse odziwa bwino nkhondo,
aliyense ali ndi lupanga pambali pake,
    kukonzekera zoopsa za usiku.
Mfumu Solomoni anadzipangira chonyamulirachi;
    anachipanga ndi matabwa ochokera ku Lebanoni.
10 Milongoti yake anayipanga yasiliva,
    kumbuyo kwake kwa golide.
Mipando yake inakutidwa ndi nsalu yapepo,
    anakongoletsa mʼkati mwake ndi chikondi
    cha akazi a ku Yerusalemu.
11 Tukulani inu akazi a ku Ziyoni
    ndipo mudzaone mfumu Solomoni atavala chipewa chaufumu,
    chipewa chaufumu chimene amayi ake anamuveka
pa tsiku la ukwati wake,
    tsiku limene mtima wake unasangalala.

Agalatiya 2

Atumwi Alandira Paulo

Kenaka, patatha zaka khumi ndi zinayi, ndinapitanso ku Yerusalemu, nthawi iyi ndinapita ndi Barnaba. Ndinatenganso Tito kuti apite nafe. Ine ndinapita chifukwa Mulungu anachita kundionetsera kuti ndipite ndipo ndinakakumana ndi atsogoleri mu msonkhano mwamseri ndi kuwafotokozera Uthenga Wabwino umene ndimalalikira pakati pa anthu a mitundu ina. Ndinachita zimenezi kuti ndikhale ndi chitsimikizo kuopa kuti mwina ndinathamanga kapena ndimathamanga liwiro pachabe. Komatu ngakhale Tito, amene anali nane sanakakamizidwe kuti achite mdulidwe, ngakhale iyeyo anali Mgriki. Nkhani iyi inayambika chifukwa abale ena achinyengo amene analowerera pakati pathu kuti adzaone za ufulu umene tili nawo mwa Khristu Yesu ndikuti atisandutse akapolo. Ife sitinawagonjere ndi pangʼono pomwe, nʼcholinga chakuti choonadi cha Uthenga Wabwino chikhalebe ndi ife.

Koma kunena za aja ankaoneka ngati ofunika kwambiri, chimene iwo anali sichisintha kanthu kwa ine; chifukwa Mulungu alibe tsankho, iwowo sanawonjezepo kanthu pa uthenga wanga. Makamaka anaona kuti ine ndinapatsidwa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino kwa anthu a mitundu ina monga momwe Petro anapatsidwa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino kwa Ayuda. Pakuti Mulungu, amene amagwira ntchito mu utumiki wa Petro monga mtumwi kwa Ayuda, amagwiranso ntchito mu utumiki wanga monga mtumiki kwa anthu a mitundu ina. Yakobo, Petro ndi Yohane, amene ankatengedwa ngati mizati, atazindikira chisomo chimene chinapatsidwa kwa ine, anagwirana chanza ndi ine ndi Barnaba kusonyeza chiyanjano chathu. Iwo anavomereza kuti ife tipite kwa anthu a mitundu ina ndipo iwo apite kwa Ayuda. 10 Chimene iwo anapempha ndi chakuti ife tipitirize kukumbukira osauka, chinthu chimene ine ndinali okonzeka kuchichita.

Paulo Adzudzula Petro

11 Petro atafika ku Antiokeya, ine ndinamudzudzula pa gulu chifukwa anapezeka wolakwa. 12 Pakuti asanafike anthu otumidwa ndi Yakobo, iye ankadya pamodzi ndi anthu a mitundu ina. Koma atafika, iyeyo anachoka pakati pa anthuwo nakakhala pa yekha chifukwa ankaopa anthu a mʼgulu la mdulidwe. 13 Ayuda enanso anamutsata pochita zachinyengozi, kotero kuti ngakhale Barnaba anasocheretsedwa chifukwa cha chinyengo chawocho.

14 Koma nditaona kuti iwo sankachita molingana ndi choonadi cha Uthenga Wabwino, ndinawuza Petro pamaso pa anthu onse kuti, “Iwe ndiwe Myuda koma ukukhala ngati munthu wa mtundu wina, osati Myuda. Nanga nʼchifukwa chiyani ukukakamiza anthu a mitundu ina kuti akhale ngati Ayuda?

15 “Ife amene ndife Ayuda mwachibadwa, osati anthu a mitundu ina ochimwa, 16 tikudziwa kuti munthu salungamitsidwa pochita ntchito za lamulo koma ndi chikhulupiriro mwa Yesu Khristu. Chomwecho, ifenso tinakhulupirira Khristu Yesu kuti tilungamitsidwe mwachikhulupiriro mwa Khristu ndipo osati pochita ntchito za lamulo, chifukwa palibe amene adzalungamitsidwa pochita ntchito za lamulo.

17 “Tsono ngati ife, pamene tikufuna kulungamitsidwa mwa Khristu, zikuonekeratu poyera kuti ndifenso ochimwa, kodi zikutanthauza kuti Khristu amalimbikitsa uchimo? Ayi. Nʼkosatheka! 18 Ngati ine ndimanganso chimene ndinachigumula, ndikuonetsa kuti ndine wophwanya lamulo.

19 “Pakuti pamene ndinayesera kutsatira lamulo, lamulolo linandionetsa kuti ndine wochimwa. Choncho ndinasiya kutsatira lamulo kuti ndikhale ndi moyo kwa Mulungu. 20 Ndinapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano mʼthupi lino, ndi moyo mwachikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine. 21 Ine sindikukankhira kumbali chisomo cha Mulungu, chifukwa ngati chilungamo chikanapezeka pochita ntchito za lamulo, ndiye kuti Khristu anafa pachabe.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.