Old/New Testament
Nzeru
7 Mbiri yabwino ndi yopambana mafuta onunkhira bwino,
ndipo tsiku lomwalira ndi lopambana tsiku lobadwa.
2 Kuli bwino kupita ku nyumba yamaliro
kusiyana ndi kupita ku nyumba yamadyerero:
Pakuti imfa ndiye mathero a munthu aliyense;
anthu amoyo azichisunga chimenechi mʼmitima mwawo.
3 Chisoni nʼchabwino kusiyana ndi kuseka,
pakuti nkhope yakugwa ndi yabwino chifukwa imakonza mtima.
4 Mtima wa munthu wanzeru nthawi zonse umalingalira za imfa,
koma mitima ya zitsiru imalingalira za chisangalalo.
5 Kuli bwino kumva kudzudzula kwa munthu wanzeru
kusiyana ndi kumvera mayamiko a zitsiru.
6 Kuseka kwa zitsiru kuli ngati
kuthetheka kwa moto kunsi kwa mʼphika,
izinso ndi zopandapake.
7 Kuzunza ena kumasandutsa munthu wanzeru kukhala chitsiru,
ndipo chiphuphu chimawononga mtima.
8 Mathero ake a chinthu ndi abwino kupambana chiyambi chake,
ndipo kufatsa nʼkwabwino kupambana kudzikuza.
9 Usamafulumire kukwiya mu mtima mwako,
pakuti mkwiyo ndi bwenzi la zitsiru.
10 Usamafunse kuti, “Nʼchifukwa chiyani masiku amakedzana anali abwino kupambana masiku ano?”
pakuti si chinthu chanzeru kufunsa mafunso oterewa.
11 Nzeru ngati cholowa, ndi chinthu chabwino
ndipo imapindulitsa wamoyo aliyense pansi pano.
12 Nzeru ndi chitetezo,
monganso ndalama zili chitetezo,
koma phindu la chidziwitso ndi ili:
kuti nzeru zimasunga moyo wa munthu amene ali nazo nzeruzo.
13 Taganizirani zimene Mulungu wazichita:
ndani angathe kuwongola chinthu
chimene Iye anachipanga chokhota?
14 Pamene zinthu zili bwino, sangalala;
koma pamene zinthu sizili bwino, ganizira bwino:
Mulungu ndiye anapanga nthawi yabwinoyo,
ndiponso nthawi imene si yabwinoyo.
Choncho munthu sangathe kuzindikira
chilichonse cha mʼtsogolo mwake.
15 Pa moyo wanga wopanda phinduwu ndaona zinthu ziwiri izi:
munthu wolungama akuwonongeka mʼchilungamo chake,
ndipo munthu woyipa akukhala moyo wautali mʼzoyipa zake.
16 Usakhale wolungama kwambiri
kapena wanzeru kwambiri,
udziwonongerenji wekha?
17 Usakhale woyipa kwambiri,
ndipo usakhale chitsiru,
uferenji nthawi yako isanakwane?
18 Nʼkwabwino kuti utsate njira imodzi,
ndipo usataye njira inayo.
Munthu amene amaopa Mulungu adzapewa zinthu ziwiri zonsezi.
19 Nzeru zimapereka mphamvu zambiri kwa munthu wanzeru
kupambana olamulira khumi a mu mzinda.
20 Palibe munthu wolungama pa dziko lapansi
amene amachita zabwino zokhazokha ndipo sachimwa.
21 Usamamvetsere mawu onse amene anthu amayankhula,
mwina udzamva wantchito wako akukutukwana,
22 pakuti iwe ukudziwa mu mtima mwako
kuti nthawi zambiri iwenso unatukwanapo ena.
23 Zonsezi ndinaziyesa ndi nzeru zanga ndipo ndinati,
“Ine ndatsimikiza mu mtima mwanga kuti ndikhale wanzeru,”
koma nzeruyo inanditalikira.
24 Nzeru zimene zilipo,
zili kutali ndipo ndi zozama kwambiri,
ndani angathe kuzidziwa?
25 Kotero ndinayikapo mtima wanga kuti ndidziwe,
ndifufuze ndi kumafunafuna nzeru ndi mmene zinthu zimakhalira
ndipo ndinafunanso kudziwa kuyipa kwa uchitsiru
ndiponso kupusa kwake kwa misala.
26 Ndinapeza kanthu kowawa kupambana imfa,
mkazi amene ali ngati khoka,
amene mtima wake uli ngati khwekhwe,
ndipo manja ake ali ngati maunyolo.
Munthu amene amakondweretsa Mulungu adzathawa mkaziyo,
koma mkaziyo adzakola munthu wochimwa.
27 Mlaliki akunena kuti, “Taonani, chimene ndinachipeza ndi ichi:
“Kuwonjezera chinthu china pa china kuti ndidziwe mmene zinthu zimachitikira,
28 pamene ine ndinali kufufuzabe
koma osapeza kanthu,
ndinapeza munthu mmodzi wolungama pakati pa anthu 1,000,
koma pakati pawo panalibepo mkazi mmodzi wolungama.
29 Chokhacho chimene ndinachipeza ndi ichi:
Mulungu analenga munthu, anamupatsa mtima wolungama,
koma anthu anatsatira njira zawozawo zambirimbiri.”
8 Ndani angafanane ndi munthu wanzeru?
Ndani angadziwe kutanthauzira zinthu?
Nzeru imabweretsa chimwemwe pa nkhope ya munthu
ndipo imasintha maonekedwe ake awukali.
Za Kumvera Mfumu
2 Ine ndikuti, mvera lamulo la mfumu, chifukwa unalumbira pamaso pa Mulungu. 3 Usafulumire kuchoka pamaso pa mfumu. Usawumirire chinthu choyipa, pakuti mfumu idzachita chilichonse chomwe imasangalatsidwa nacho. 4 Popeza mawu a mfumu ali ndi mphamvu, ndani anganene kwa mfumuyo kuti, “Kodi mukuchita chiyani?”
5 Aliyense amene amamvera lamulo lake sadzapeza vuto lililonse,
ndipo munthu wanzeru amadziwa nthawi yoyenera ndi machitidwe ake.
6 Pakuti pali nthawi yoyenera ndiponso machitidwe a chinthu chilichonse,
ngakhale kuti mavuto ake a munthu amupsinja kwambiri.
7 Popeza palibe munthu amene amadziwa zamʼtsogolo,
ndani angamuwuze zomwe zidzachitika mʼtsogolo?
8 Palibe munthu amene ali ndi mphamvu yolamulira mpweya wa moyo kuti athe kuwusunga,
choncho palibe amene ali ndi mphamvu pa tsiku la imfa yake.
Nkhondo sithawika; tsono anthu ochita zoyipa,
kuyipa kwawoko sikudzawapulumutsa.
9 Zonsezi ndinaziona pamene ndinalingalira mu mtima mwanga, zonse zimene zimachitika pansi pano. Ilipo nthawi imene ena amalamulira anzawo mwankhanza. 10 Kenaka, ndinaona anthu oyipa akuyikidwa mʼmanda, iwo amene ankalowa ndi kumatuluka mʼmalo opatulika ndipo ankatamandidwa mu mzindawo pamene ankachita zimenezi. Izinso ndi zopandapake.
11 Pamene chigamulo cha anthu opalamula mlandu chikuchedwa, mitima ya anthu imadzaza ndi malingaliro ochita zolakwa. 12 Ngakhale munthu woyipa apalamule milandu yambirimbiri, nʼkumakhalabe ndi moyo wautali, ine ndikudziwa kuti anthu owopa Mulungu zinthu zidzawayendera bwino, omwe amapereka ulemu pamaso pa Mulungu. 13 Koma popeza oyipa saopa Mulungu zinthu sizidzawayendera bwino, ndipo moyo wawo sudzakhalitsa monga mthunzi.
14 Palinso chinthu china chopanda phindu chomwe chimachitika pa dziko lapansi: anthu olungama amalangidwa ngati anthu osalungama. Pamene oyipa amalandira zabwino ngati kuti ndi anthu abwino. 15 Nʼchifukwa chake ndikuti munthu azikondwerera moyo, pakuti munthu alibe chinanso chabwino pansi pano choposa kudya, kumwa ndi kumadzikondweretsa. Akamatero, munthuyo adzakhala ndi chimwemwe pa ntchito yake masiku onse a moyo wake amene Mulungu wamupatsa pansi pano.
16 Pamene ndinayikapo mtima wanga kuti ndidziwe nzeru ndi kuonetsetsa ntchito za munthu pa dziko lapansi, osapeza tulo usana ndi usiku, 17 pamenepo ndinaona zonse zimene Mulungu anazichita. Palibe munthu amene angathe kuzimvetsa zonse zimene zimachitika pansi pano. Ngakhale munthu ayesetse kuzifufuza, sangathe kupeza tanthauzo lake. Ngakhale munthu wanzeru atanena kuti iye amadziwa, sangathe kuzimvetsetsa zinthuzo.
Mathero a Zinthu Zonse ndi Wofanana
9 Ndinalingalira zonse ndanenazi ndipo ndinapeza kuti anthu olungama ndi anthu anzeru ali mʼmanja mwa Mulungu pamodzi ndi zimene amachita, koma palibe amene amadziwa zimene zikumudikira mʼtsogolo mwake, kaya chikondi kapena chidani. 2 Onsewa mathero awo ndi amodzi, anthu olungama ndi anthu oyipa, abwino ndi oyipa, oyera ndi odetsedwa, amene amapereka nsembe ndi amene sapereka nsembe.
Zomwe zimachitikira munthu wabwino,
zimachitikiranso munthu wochimwa,
zomwe zimachitikira amene amalumbira,
zimachitikiranso amene amaopa kulumbira.
3 Choyipa chimene chili mʼzonse zochitika pansi ndi ichi: Mathero a zonse ndi amodzi. Ndithu, mitima ya anthu ndi yodzaza ndi zoyipa, ndipo mʼmitima mwawo muli zamisala pamene ali ndi moyo, potsiriza pake iwo amakakhala pamodzi ndi anthu akufa. 4 Aliyense amene ali ndi moyo amakhala ndi chiyembekezo, pajatu galu wamoyo aposa mkango wakufa!
5 Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa,
koma akufa sadziwa kanthu;
alibe mphotho ina yowonjezera,
ndipo palibe amene amawakumbukira.
6 Chikondi chawo, chidani chawo
ndiponso nsanje yawo, zonse zinatha kalekale;
sadzakhalanso ndi gawo
pa zonse zochitika pansi pano.
7 Pita, kadye chakudya chako mokondwera ndi kumwa vinyo wako ndi mtima wosangalala, pakuti tsopano Mulungu akukondwera ndi zochita zako. 8 Uzivala zovala zoyera nthawi zonse, uzidzola mafuta mʼmutu mwako nthawi zonse. 9 Uzikondwerera moyo pamodzi ndi mkazi wako amene umamukonda, masiku onse a moyo uno wopanda phindu, amene Mulungu wakupatsa pansi pano. Pakuti mkaziyo ndiye gawo la moyo wako pa ntchito yako yolemetsa pansi pano. 10 Ntchito iliyonse imene ukuyigwira, uyigwire ndi mphamvu zako zonse, pakuti ku manda kumene ukupita kulibe kugwira ntchito, kulibe malingaliro, chidziwitso ndiponso nzeru.
11 Ine ndinaonanso chinthu china pansi pano:
opambana pa kuthamanga si aliwiro,
kapena opambana pa nkhondo si amphamvu,
ndiponso okhala ndi chakudya si anzeru,
kapena okhala ndi chuma si odziwa zambiri,
kapena okomeredwa mtima si ophunzira;
koma mwayi umangowagwera onsewa pa nthawi yake.
12 Kungoti palibe munthu amene amadziwa kuti nthawi yake idzafika liti:
monga momwe nsomba zimagwidwira mu ukonde,
kapena mmene mbalame zimakodwera mu msampha,
chimodzimodzinso anthu amakodwa mu msampha pa nthawi yoyipa,
pamene tsoka limawagwera mosayembekezera.
Nzeru Iposa Uchitsiru
13 Ine ndinaonanso pansi pano chitsanzo ichi cha nzeru chimene chinandikhudza kwambiri: 14 Panali mzinda waungʼono umene unali ndi anthu owerengeka. Ndipo mfumu yamphamvu inabwera kudzawuthira nkhondo, inawuzungulira ndi kumanga mitumbira yankhondo. 15 Tsono mu mzindamo munali munthu wosauka koma wanzeru, ndipo anapulumutsa mzindawo ndi nzeru zakezo. Koma palibe amene anakumbukira munthu wosaukayo. 16 Choncho ine ndinati, “Nzeru ndi yopambana mphamvu.” Koma nzeru ya munthu wosauka imanyozedwa, ndipo palibe amene amalabadirako za mawu ake.
17 Mawu oyankhula mofatsa a munthu wanzeru, anthu amawasamalira kwambiri
kupambana kufuwula kwa mfumu ya zitsiru.
18 Nzeru ndi yabwino kupambana zida zankhondo,
koma wochimwa mmodzi amawononga zinthu zambiri zabwino.
Mawu Otsiriza ndi Ochenjeza
13 Uwu ndi ulendo wachitatu ndikubwera kudzakuyenderani. “Nkhani itsimikizike ndi umboni wa anthu awiri kapena atatu.” 2 Ndinakuchenjezani kale pamene ndinali nanu ulendo wachiwiri uja. Tsopano ndikubwereza ndisanafike. Ndikabweranso sindidzachitira chifundo amene anachimwa poyamba paja kapena wina aliyense amene anachimwa, 3 popeza mufuna chitsimikizo chakuti Khristu akuyankhula kudzera mwa ine. Iye siwofowoka pofuna kuchita nanu koma ndi wamphamvu pakati panu. 4 Pofuna kutsimikizira, anapachikidwa ali wofowoka koma ali ndi moyo mwamphamvu ya Mulungu. Chomwechonso, ife ndife ofowoka mwa Iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi naye ndi mphamvu ya Mulungu, potumikira pakati panu.
5 Tadzisanthulani nokha kuti muone ngati muli mʼchikhulupiriro; dziyeseni nokha. Kodi simuzindikira kuti Khristu Yesu ali mwa inu, ngati si choncho mwalephera mayesowa? 6 Ndipo ndikhulupirira kuti mudzazindikira kuti ife sitinalephere mayesowo. 7 Tsopano tikupemphera kwa Mulungu kuti musadzachite kanthu kena kalikonse kolakwa. Osati chifukwa choti anthu aone kuti ife tapambana mayesowo koma kuti mudzachite zokhoza ngakhale anthu atamationa ngati olephera. 8 Pakuti sitingachite chilichonse chotsutsana ndi choonadi, koma chokhacho chovomerezana ndi choonadi. 9 Ife timasangalala kuti pamene tafowoka, inu muli amphamvu; ndipo pemphero lathu ndi lakuti mukhale angwiro. 10 Nʼchifukwa chake ndimalemba zinthu zoterezi pamene ndili kutali, kuti ndikabwera ndisadzagwiritse ntchito ulamuliro wanga mokalipa, uwu ndi ulamuliro umene Ambuye anandipatsa kuti ndikukuzeni inu osati kukuwonongani.
Malonje Otsiriza
11 Potsiriza abale, ndikuti tsalani bwino. Yesetsani kukhala angwiro, mvetsetsani pempho langa, khalani a mtima umodzi, khalani mwamtendere. Ndipo Mulungu wachikondi ndi mtendere adzakhala nanu.
12 Lonjeranani ndi mpsopsono wachiyero. 13 Anthu onse a Mulungu akupereka moni.
14 Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.