Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Mlaliki 1-3

Zapansipano Nʼzopandapake

Mawu a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya ku Yerusalemu:

“Zopandapake! Zopandapake!”
    atero Mlaliki.
“Zopandapake kotheratu!
    Zopandapake.”

Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zake zonse
    zimene amasautsidwa nazo pansi pano?
Mibado imabwera ndipo mibado imapita,
    koma dziko lapansi limakhalapobe nthawi zonse.
Dzuwa limatuluka ndipo dzuwa limalowa
    ndipo limapita mwamsanga kumene limatulukira.
Mphepo imawombera cha kummwera
    ndi kukhotera cha kumpoto;
imawomba mozungulirazungulira,
    kumangobwererabwerera komwe yachokera.
Mitsinje yonse imakathira ku nyanja,
    koma nyanjayo sidzaza;
kumene madziwo amachokera,
    amabwereranso komweko.
Zinthu zonse ndi zotopetsa,
    kutopetsa kwake ndi kosaneneka.
Maso satopa ndi kuona
    kapena khutu kukwaniritsidwa ndi kumva.
Zomwe zinalipo kale zidzakhalaponso,
    zomwe zinachitika kale zidzachitikanso.
    Ndiye kuti chatsopano palibiretu pansi pano.
10 Kodi chilipo chinthu chimene wina anganene kuti,
    “Taona! Ichi ndiye chatsopano?”
Chinalipo kale, kalekale;
    chinalipo ife kulibe.
11 Anthu akale sakumbukiridwa,
    ngakhale amene adzabwera mʼtsogolomu
sadzakumbukiridwa ndi iwo
    amene adzabwere pambuyo pawo.

Nzeru Nʼzopandapake

12 Ine, Mlalikine, ndinali mfumu ya Israeli mu Yerusalemu. 13 Ndinayika mtima wanga pophunzira ndi kufunafuna mwa nzeru zinthu zonse zimene zimachitika pansi pa thambo. Ndi ntchito yolemetsa ndithu imene Mulungu anayipereka kwa anthu! 14 Ine ndaona zinthu zonse zochitika pansi pano; zinthu zonsezo ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.

15 Chinthu chokhota sichingathe kuwongoledwa;
    chimene palibe sichingathe kuwerengedwa.

16 Ine ndinaganiza mu mtima mwanga, “Taona, ine ndakula ndi kukhala wa nzeru zochuluka kupambana aliyense amene analamulirapo Yerusalemu ndisanabadwe; ndaphunzira nzeru zochuluka ndi luntha.” 17 Ndipo ndinadzipereka kuti ndithe kumvetsa kuti nzeru nʼchiyani, misala nʼchiyani, uchitsiru nʼchiyani, koma ndinazindikira ichi, kuti kuteronso nʼkungodzivuta chabe.

18 Pakuti nzeru zochuluka zimabweretsa chisoni chochulukanso:
    chidziwitso chochuluka, zowawa zochulukanso.

Zosangalatsa Nʼzopandapake

Ine ndinaganiza mu mtima mwanga, “Tsopano ndiyese zosangalatsa kuti ndipeze zomwe ndi zabwino.” Koma izi zinaonekanso kuti ndi zopandapake. “Kuseka,” ndinati, “imeneyo ndi misala. Ndipo kodi chisangalalo chimabweretsa phindu lanji?” Ndinayesa kudzisangalatsa ndi vinyo, koma umenewu unali uchitsiru, pamenepo nʼkuti maganizo anga akutsogozedwa ndi nzeru. Ine ndinkati mwina kapena njira yotero nʼkukhala yopambana, imene anthu amatsata pofuna kusangalala pa masiku owerengeka a moyo wawo.

Ndinagwira ntchito zikuluzikulu: Ndinadzimangira nyumba ndi kuwoka mipesa. Ndinalima madimba ndi minda yamitengo; ndipo ndinadzalamo mitengo ya zipatso za mitundu yonse. Ndinakumba mayiwe osungiramo madzi woti ndizithirira minda ya mitengo yodzalidwa ija. Ndinagula akapolo aamuna ndi akapolo aakazi, ndiponso ndinali ndi akapolo ena omwe anabadwira mʼnyumba mwanga. Ndinalinso ndi ngʼombe ndi nkhosa zambiri kupambana aliyense mu Yerusalemu amene analipo ndisanabadwe. Ndinadzikundikira siliva ndi golide, ndiponso chuma chochokera kwa mafumu ndi madera awo. Ndinali ndi amuna ndi akazi oyimba ndiponso azikazi; zinthu zokondweretsa mtima wa munthu. Ndinali munthu wotchuka kupambana wina aliyense mu Yerusalemu amene analipo ndisanabadwe. Mu zonsezi nzeru zanga zinali nane.

10 Sindinadzimane chilichonse chimene maso anga anachifuna;
    mtima wanga sindinawumane zokondweretsa.
Mtima wanga unakondwera ndi ntchito yanga yonse,
    ndipo iyi ndiyo inali mphotho ya ntchito zanga zonse zolemetsa.
11 Koma pamene ndinayamba kuyangʼanayangʼana zonse zimene ndinachita ndi manja anga,
    ndi zimene ndinazivutikira kuti ndizipeze,
zonsezi zinali zopandapake; kungodzivuta chabe,
    palibe chomwe ndinapindula pansi pano.

Nzeru ndi Uchitsiru Nʼzopandapake

12 Kenaka maganizo anga anayamba kulingalira zakuti nzeru nʼchiyani,
    komanso kuti misala ndi uchitsiru nʼchiyani.
Kodi munthu wodzalowa ufumu tsopanoyo angachite chiyani
    choposa chimene chinachitidwa kale?
13 Ndinaona kuti nzeru ndi yopambana uchitsiru,
    monga momwe kuwala kumapambanira mdima.
14 Munthu wanzeru amayenda maso ali patsogolo,
    pamene chitsiru chimayenda mʼchimbulimbuli;
koma ndinazindikira kuti chomwe
    chimawachitikira onsewo ndi chimodzi.

15 Pamenepo ndinalingalira mu mtima mwanga,

“Zochitikira chitsiru zidzandichitikiranso ine.
    Nanga tsono phindu langa nʼchiyani pakukhala wanzeru?”
Ndinati mu mtima mwanga,
    “Ichinso ndi chopandapake.”
16 Pakuti munthu wanzeru, pamodzinso ndi chitsiru sadzakumbukiridwa nthawi yayitali;
    mʼmasiku amʼtsogolo awiriwo adzayiwalika.
Mmene chimafera chitsiru ndi mmenenso amafera wanzeru!

Kugwira Ntchito Nʼkopandapake

17 Kotero ndinadana nawo moyo chifukwa ntchito zimene zimagwiridwa pansi pano ndi zosautsa kwa ine. Ntchito zonsezo ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe. 18 Ine ndinadana nazo ntchito zonse zimene ndinazigwira pansi pano, chifukwa ndinayenera kudzazisiyira wina amene adzalowa mʼmalo mwanga. 19 Ndipo ndani amadziwa kuti munthu ameneyo adzakhala wanzeru kapena chitsiru? Komabe munthuyo adzakhala wolamulira zonse zimene ndinazichita pansi pano mwa nzeru zanga. Izinso ndi zopandapake. 20 Motero ndinayamba kutaya mtima chifukwa cha ntchito zonse zimene ndinazivutikira pansi pano. 21 Pakuti munthu atha kugwira ntchito yake mwanzeru, chidziwitso ndi luntha, ndipo kenaka nʼkusiyira wina amene sanakhetserepo thukuta. Izinso ndi zopandapake ndiponso tsoka lalikulu. 22 Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zonse zolemetsa ndi zodetsa nkhawa zimene amazichita pansi pano? 23 Masiku ake onse amakhala achisoni, ntchito yake imakhala yovuta; ngakhale usiku womwe, mtima wake supumula. Izinso ndi zopandapake.

24 Kwa munthu palibe chabwino china kuposa kudya, kumwa ndi kukondwerera ntchito zake. Izinso ndaona kuti ndi zochokera kwa Mulungu, 25 pakuti popanda Iye, ndani angadye ndi kupeza chisangalalo? 26 Munthu amene amakondweretsa Mulungu, Mulunguyo amamusandutsa wanzeru, wozindikira ndi wachisangalalo, koma wochimwa, Mulungu amamupatsa ntchito yosonkhanitsa ndi kusunga chuma kuti adzachipereke kwa amene Mulunguyo amakondwera naye. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.

Chilichonse Chili ndi Nthawi

Chinthu chilichonse chili ndi nthawi yake,
    ndi nyengo yake yomwe anayika Mulungu:

    Nthawi yobadwa ndi nthawi yomwalira,
    nthawi yodzala ndi nthawi yokolola.
    Nthawi yakupha ndi nthawi yochiritsa,
    nthawi yogwetsa ndi nthawi yomanga.
    Nthawi yomva chisoni ndi nthawi yosangalala,
    nthawi yolira maliro ndi nthawi yovina.
    Nthawi yotaya miyala ndi nthawi yokundika miyala,
    nthawi yokumbatirana ndi nthawi yoleka kukumbatirana.
    Nthawi yofunafuna ndi nthawi yoleka kufunafuna,
    nthawi yosunga ndi nthawi yotaya.
    Nthawi yongʼamba ndi nthawi yosoka,
    nthawi yokhala chete ndi nthawi yoyankhula.
    Nthawi yokondana ndi nthawi yodana,
    nthawi ya nkhondo ndi nthawi ya mtendere.

Kodi wantchito amapeza phindu lanji pa ntchito yake yolemetsa? 10 Ine ndinaona chipsinjo chimene Mulungu anayika pa anthu. 11 Iye anapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthawi yake. Anayika nzeru zamuyaya mʼmitima ya anthu; komabe anthuwo sangathe kuzindikira zomwe Mulungu wachita kuyambira pa chiyambi mpaka chimaliziro. 12 Ine ndikudziwa kuti palibenso kanthu kabwino kwa anthu kopambana kusangalala ndi kuchita zabwino pamene ali ndi moyo. 13 Ndi mphatso ya Mulungu kwa munthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ndi ntchito zake zolemetsa. 14 Ndikudziwa kuti chilichonse chimene Mulungu amachita chidzakhala mpaka muyaya; palibe zimene zingawonjezedwe kapena kuchotsedwa. Mulungu amazichita kuti anthu azimuopa.

15 Chilichonse chimene chilipo chinalipo kale,
    ndipo chimene chidzakhalapo chinalipo poyamba;
    Mulungu amabwezanso zakale zimene zinapita kuti zichitikenso.

16 Ndipo ndinaona chinthu chinanso pansi pano:

ku malo achiweruzo, kuyipa mtima kuli komweko,
    ku malo achilungamo, kuyipa mtima kuli komweko.

17 Ndinalingalira mu mtima mwanga kuti;

“Mulungu adzaweruza
    olungama pamodzi ndi oyipa omwe,
pakuti anayika nthawi yochitikira chinthu chilichonse,
    nthawi ya ntchito iliyonse.”

18 Ndinalingaliranso kuti, “Kunena za anthu, Mulungu amawayesa ndi cholinga choti awaonetse kuti iwo ali ngati nyama. 19 Zimene zimachitikira munthu, zomwezonso zimachitikira nyama; chinthu chimodzi chomwecho chimachitikira onse: Monga munthu amafa momwemonso nyama imafa. Zonsezi zimapuma mpweya umodzimodzi omwewo; munthu saposa nyama. Zonsezi ndi zopandapake. 20 Zonse zimapita kumodzimodzi; zonsezi zimachokera ku fumbi, ndipo zimabwereranso ku fumbi komweko. 21 Kodi ndani amene amadziwa ngati mzimu wa munthu umakwera kumwamba, ndipo mzimu wa nyama umatsikira kunsi kwa dziko?”

22 Kotero ndinaona kuti palibe chinthu chabwino kwa munthu kuposa kuti munthu azisangalala ndi ntchito yake, pakuti ichi ndiye chake chenicheni. Pakuti ndani amene angamubweretse kuti adzaone zimene zidzamuchitikira iye akadzamwalira?

2 Akorinto 11:16-33

Paulo Anyadira Mazunzo Ake

16 Ndibwereze kunena kuti, wina aliyense asandiyese chitsiru. Koma ngati mutero, mundilandire monga mmene mukhoza kulandirira chitsiru, kuti ndinyadirepo pangʼono. 17 Kudzinyadira kwangaku, sindikuyankhula monga mmene Ambuye akufunira koma ngati chitsiru. 18 Popeza ambiri akudzitama monga dziko lapansi limachitira, inenso ndidzitamanso. 19 Inu mumalolera kukhala ndi zitsiru mokondwera chifukwa mumati ndinu anzeru! 20 Kunena zoona mumangololera aliyense; amene amakusandutsani akapolo, kapena amene amakudyerani masuku pamutu, kapena amene amakupezererani, kapena amene amadzitukumula, kapena amene amakumenyani khofi. 21 Ndikuvomera mwamanyazi kuti ife sitinali olimba mtima kuti nʼkuchita zinthu zimenezi.

Ndikuyankhula ngati chitsiru kuti chimene wina aliyense akhoza kudzitama nacho, Inenso ndikhoza kudzitama nachonso. 22 Kodi iwo ndi Ahebri? Inenso ndine Mhebri. Kodi iwo ndi Aisraeli? Inenso ndine Mwisraeli. Kodi iwo ndi zidzukulu za Abrahamu? Inenso ndine mdzukulu wa Abrahamu. 23 Kodi iwo ndi atumiki a Khristu? Ndikuyankhula ngati wamisala. Ine ndine woposa iwowo. Ndagwira ntchito kwambiri kupambana iwo, ndakhala ndikuyikidwa mʼndende kawirikawiri, ndakwapulidwapo kwambiri, kawirikawiri ndinali pafupi kufa. 24 Andikwapulapo kasanu zikoti zija za Ayuda, makumi anayi kuchotsapo chimodzi. 25 Katatu anandimenya ndi ndodo. Kamodzi anandigendapo miyala. Katatu sitima yathu ya panyanja inasweka, ndipo ndinakhala usiku ndi usana ndi kuyandama pa nyanja. 26 Ndakhala ndikuyenda maulendo ataliatali. Moyo wanga wakhala ukukumana ndi zoopsa pa mitsinje, zoopsa za achifwamba, zoopsa zochokera kwa abale anga Ayuda, zoopsa zochokera kwa anthu akunja. Ndinakumana ndi zoopsa mʼmizinda, mʼmidzi, pa nyanja, ndi pakati pa abale onyenga. 27 Ndakhala ndikugwira ntchito molimbika ndipo kawirikawiri ndakhala ndikuchezera usiku wonse osagona. Ndakhala ndikumva njala ndi ludzu ndipo kawirikawiri ndakhala wopanda chakudya. Ndakhala ndi kuzizidwa ndi wosowa zovala. 28 Kuwonjezera pa zonsezi, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa chipsinjo cha nkhawa ya mipingo yonse. 29 Ndani ali wofowoka, ine wosakhala naye mʼkufowoka kwakeko? Ndani amene mnzake amuchimwitsa, ine wosavutika mu mtima?

30 Ngati nʼkoyenera kudzitamandira, ndidzadzitamandira pa zinthu zimene zimaonetsa kufowoka kwanga. 31 Mulungu, Atate a Ambuye Yesu, amene tiyenera kumutamanda nthawi zonse, akudziwa kuti sindikunama. 32 Ku Damasiko, bwanamkubwa woyimira Mfumu Areta, anayika alonda kuzungulira mzinda wonse kuti andigwire. 33 Koma abale anandiyika mʼdengu nanditsitsira pa chipupa kudzera pa zenera la mpandawo, motero ndinapulumuka mʼmanja mwake.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.