Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Miyambo 8-9

Nzeru Ikuyitana

Kodi nzeru sikuyitana?
    Kodi nzeru yomvetsa zinthu sinakweze mawu ake?
Nzeru imayima pa zitunda mʼmbali mwa njira,
    imayima pa mphambano ya misewu.
Imafuwula pafupi ndi zipata zolowera mu mzinda,
    pa makomo olowera imafuwula kuti,
Inu anthu, ndikuyitana inu;
    ndikuyitanatu anthu onse.
Inu amene simudziwa kanthunu khalani ochenjera;
    inu amene ndi opusa, khalani ndi mtima womvetsa zinthu.
Mverani, pakuti ndikukuwuzani zinthu zofunika kwambiri;
    ndatsekula pakamwa panga ndipo payankhula zolungama.
Pakamwa panga pamayankhula zoona
    ndimanyansidwa ndi kuyankhula zoyipa.
Mawu onse a pakamwa panga ndi olungama;
    mʼmawu angawo mulibe zokhotakhota kapena zopotoka.
Kwa anthu ozindikira, mawu anga onse ndi woona;
    kwa anthu amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu, mawu angawo ndi okhoza.
10 Landirani malangizo anga mʼmalo mwa siliva,
    nzeru zomvetsa zinthu mʼmalo mwa golide wabwino.
11 Paja nzeru ndi yabwino kwambiri kuposa miyala yamtengowapatali,
    ndipo zonse zimene ungazifune sizingafanane ndi nzeru.

12 Ine nzeru, ndimakhala pamodzi ndi kuchenjera.
    Ine ndimadziwa zinthu ndiponso ndimalingalira zinthu bwino.
13 Kuopa Yehova ndiko kudana ndi zoyipa.
    Ine ndimadana ndi kunyada, kudzitama,
    kuchita zoyipa, ndiponso kuyankhula zonyenga.
14 Ndine mwini uphungu ndi maganizo abwino;
    ndili ndi nzeru yomvetsa zinthu ndiponso mphamvu.
15 Ndine amene ndimathandiza mafumu kulamulira.
    Ndimawathandiza olamulira kukhazikitsa malamulo olungama.
16 Ndine amene ndimathandiza akalonga polamula.
    Ndinenso amene ndimathandiza akuluakulu onse kulamulira bwino dziko.
17 Ndimakonda amene amandikonda,
    ndipo amene amandifunafuna amandipeza.
18 Ine ndili ndi chuma ndi ulemu,
    chuma ndi kupindula pa ntchito kokhazikika.
19 Chipatso changa ndi chabwino kuposa golide, ngakhale golide wosalala;
    zimene ine ndimabereka zimaposa siliva wabwino kwambiri.
20 Ndimachita zinthu zolungama.
    Ine sindipatuka mʼnjira za chilungamo.
21 Ndimapereka chuma kwa amene amandikonda
    ndi kudzaza nyumba zawo zosungiramo chuma.

22 “Yehova anandilenga ine nzeru monga ntchito yake yoyamba.
    Mwa ntchito zake zakalekale yoyamba ndinali ine.
23 Ndinapangidwa kalekalelo,
    pachiyambi penipeni dziko lapansi lisanalengedwe.
24 Nyanja, akasupe odzaza ndi madzi,
    zonsezi kulibe pamene ine ndinkabadwa.
25 Mapiri asanakhazikitsidwe pa malo awo,
    mapiri angʼonoangʼono asanakhalepo, ine ndinali nditabadwa kale,
26 lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake;
    lisanalengedwe dothi loyamba la dziko lapansi.
27 Ine ndinalipo pamene Yehova ankakhazikitsa mlengalenga,
    pamene ankalemba malire a nyanja yozama,
28 pamene anakhazikitsa mitambo ya mlengalenga
    ndi kukhazikitsa akasupe a madzi ozama,
29 pamene anayikira nyanja malire
    kuti madzi asadutse malirewo,
ndiponso pamene ankayika malire a dziko lapansi.
30     Tsono ine ndinali pambali pake ngati mmisiri;
ndikumukondweretsa tsiku ndi tsiku,
    kusangalala nthawi zonse pamaso pake.
31 Ndinkasangalala ndi dziko lake lonse
    ndiponso kumakondwera nawo anthu onse.”

32 “Ndiye tsono ana inu, ndimvereni;
    odala anthu amene amasunga njira zanga.
33 Mverani malangizo anga kuti mukhale ndi nzeru;
    musanyozere mawu anga.
34 Wodala munthu amene amandimvera,
    amene amakhala pa khomo panga tsiku ndi tsiku,
    kudikirira pa chitseko changa.
35 Paja aliyense amene apeza ine wapeza moyo
    ndipo Yehova amamukomera mtima.
36 Koma amene alephera kundipeza, amadzipweteka yekha;
    onse amene amandida amakonda imfa.”

Za Nzeru ndi Uchitsiru

Nzeru inamanga nyumba yake;
    inayimika nsanamira zake zisanu ndi ziwiri.
Inapha ziweto zake ndipo yasakaniza vinyo wake;
    inasakaniza vinyo wake ndi kuyala tebulo lake.
Nzeruyo inatuma adzakazi ake,
    kuti akakhale pamwamba penipeni pa mzinda ndi kukalengeza kuti,
“Aliyense amene ali munthu wamba, abwere kuno!”
    Kwa onse opanda nzeru inkanena kuti,
“Bwerani, dzadyeni chakudya changa
    ndipo dzamweni vinyo amene ndakonza.
Lekani zopusa zanu kuti mukhale ndi moyo;
    yendani njira ya nzeru yomvetsa zinthu.”

Aliyense amene amayesa kukonza munthu wonyoza amadziputira minyozo;
    aliyense amene amadzudzula munthu woyipa amadetsa mbiri yake.
Usadzudzule munthu wonyoza kuti angadzadane nawe;
    dzudzula munthu wanzeru ndipo adzakukonda.
Ukalangiza munthu wanzeru ndiye adzapitirira kukhala wanzeru;
    ukaphunzitsa munthu wolungama ndiye adzawonjezera kuphunzira kwake.

10 Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru;
    kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu.
11 Chifukwa cha ine nzeru, masiku ako adzachuluka,
    ndipo zaka za moyo wako zidzawonjezeredwa.
12 Ngati ndiwe wanzeru, nzeru yakoyo idzakupindulitsa;
    ngati ndiwe wonyoza ena, udzavutika wekha.

13 Uchitsiru ndi mkazi waphokoso,
    wopulikira ndiponso wosadziwa zinthu.
14 Iye amakhala pa mpando, pa khomo la nyumba yake,
    pamalo aatali a mu mzinda,
15 kuti aziyitana anthu ongodutsa,
    amene akunka nayenda njira zawo.
16 Amati, “Onse amene ndi anthu wamba abwere kuno,”
    ndipo kwa wopanda nzeru amati,
17 “Madzi akuba ndiye amatsekemera;
    chakudya chodya mobisa ndi chokoma!”
18 Koma amunawo sadziwa kuti akufa ali kale komweko,
    ndi kuti alendo ake alowa kale mʼmanda akuya.

2 Akorinto 3

Akhristu ndi Kalata Yochokera kwa Khristu

Kodi tayambanso kudzichitira umboni tokha? Kapena kodi ifenso tikufuna makalata otivomereza kwa inu, kapena ochokera kwa inu monga anthu ena? Inu ndinu kalata yathu, yolembedwa pa mitima yathu, yodziwika ndi yowerengedwa ndi aliyense. Inu mukuonetsa kuti ndinu kalata yochokera kwa Khristu, zotsatira za utumiki wathu, osati yolembedwa ndi inki koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo, osati pa miyala yosemedwa koma mʼmitima ya anthu.

Kulimba mtima kumeneku tili nako pamaso pa Mulungu kudzera mwa Khristu. Sikuti mwa ife muli kanthu kotiganizitsa kuti tingathe kugwira ntchitoyi patokha, koma kulimba mtima kwathu kumachokera kwa Mulungu. Iye watipatsa kulimba mtima kuti tikhale atumiki a pangano latsopano, osati malamulo olembedwa koma a Mzimu; pakuti malamulo olembedwa amapha koma Mzimu amapereka moyo.

Ulemerero wa Pangano Latsopano

Koma ngati utumiki umene unabweretsa imfa uja, wolembedwa ndi malemba pa mwalawu, unabwera ndi ulemerero mwakuti Aisraeli sanathe kuyangʼanitsitsa nkhope ya Mose chifukwa cha ulemerero wa pa nkhopeyo, ngakhale kuti unali kunka nuzilala, kodi nanga utumiki wa Mzimu sudzaposa apa? Ngati utumiki umene umatsutsa anthu unali ndi ulemerero, nanga koposa kotani ulemerero wa utumiki wobweretsa chilungamo! 10 Pakuti zimene zinali ndi ulemerero, tsopano zilibenso ulemerero pofananitsa ndi ulemerero wopambanawo. 11 Ndipo ngati zosakhalitsa zinabwera ndi ulemerero, koposa kotani ulemerero wamuyayawo!

12 Choncho, popeza tili ndi chiyembekezo chotere, ndife olimba mtima kwambiri. 13 Ife sitili ngati Mose amene amaphimba nkhope yake kuopa kuti Aisraeli angaone kuti kunyezimira kwa nkhope yake kumazilala. 14 Koma nzeru zawo zinawumitsidwa, pakuti mpaka lero chophimbira chomwecho chikanalipo pamene akuwerenga Chipangano Chakale. Sichinachotsedwebe, chifukwa chimachotsedwa ngati munthuyo ali mwa Khristu yekha. 15 Ngakhale lero lomwe lino akuwerenga mabuku a Mose pali chophimbabe mitima yawo. 16 Koma pamene aliyense atembenukira kwa Ambuye, “chophimbacho chimachotsedwa.” 17 Tsono Ambuye ndi Mzimu, ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye, pali ufulu. 18 Ife tonse, amene ndi nkhope zosaphimba timaonetsera ulemerero wa Ambuye, tikusinthika kufanana ndi ulemerero wake, umene ukunka nuchulukirachulukira, wochokera kwa Ambuye, amene ndi Mzimu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.