Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Miyambo 1-2

Mawu Oyamba: Cholinga ndi Mutu

Iyi ndi miyambi ya Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israeli:

Ndi yothandiza kuti munthu adziwe nzeru ndi malangizo;
    kuti amvetse mawu a matanthauzo ozama;
kuti alandire malangizo othandiza kuti achite zinthu mwanzeru,
    akhale wangwiro, wachilungamo ndiponso wosakondera.
Ndi yothandiza munthu wamba kuti aphunzire nzeru za kuchenjera,
    achinyamata kudziwa zinthu bwino ndi kulingalira.
Munthu wanzeru amvetse bwino miyamboyi kuti awonjezere kuphunzira kwake,
    ndi munthu womvetsa zinthu bwino apatepo luso,
kuti azimvetsa miyambi ndi mafanizo,
    mawu a anthu anzeru ndi mikuluwiko.

Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru.
    Zitsiru zimanyoza nzeru ndi malangizo.

Malangizo kuti Asunge Nzeru

Malangizo kwa Achinyamata

Mwana wanga, mvera malangizo a abambo ako
    ndipo usakane mawu okuwongolera a amayi ako.
Ali ngati sangamutu yokongola ya maluwa pamutu pako
    ndiponso ali ngati mkanda mʼkhosi mwako.

10 Mwana wanga, ngati anthu oyipa afuna kukukopa
    usamawamvere.
11 Akadzati, “Tiye kuno;
    tikabisale kuti tiphe anthu,
    tikabisalire anthu osalakwa;
12 tiwameze amoyo ngati manda,
    ndi athunthu ngati anthu otsikira mʼdzenje.
13 Motero tidzapeza zinthu zosiyanasiyana zamtengowapatali
    ndi kudzaza nyumba zathu ndi zolanda;
14 Bwera, chita nafe maere,
    ndipo tidzagawana chuma chathu tonse.”
15 Mwana wanga, usayende nawo pamodzi,
    usatsagane nawo mʼnjira zawozo.
16 Iwowatu amangofuna zoyipa zokhazokha,
    amathamangira kukhetsa magazi.
17 Nʼkopanda phindu kutchera msampha
    mbalame zikuona!
18 Koma anthu amenewa amangobisalira miyoyo yawo yomwe;
    amangodzitchera okha msampha!
19 Awa ndiwo mathero a anthu opeza chuma mwankhanza;
    chumacho chimapha mwiniwake.

Chenjezo Pomwe Tikana Nzeru

20 Nzeru ikufuwula mu msewu,
    ikuyankhula mokweza mawu mʼmisika;
21 ikufuwula pa mphambano ya misewu,
    ikuyankhula pa zipata za mzinda kuti,

22 “Kodi inu anthu osachangamukanu, mudzakondwera ndi kusachangamuka mpaka liti?
    Nanga anthu onyogodola adzakondabe kunyogodola mpaka liti?
    Kapena opusa adzadana ndi nzeru mpaka liti?
23 Tamverani mawu anga a chidzudzulo.
    Ine ndikukuwuzani maganizo anga
    ndi kukudziwitsani mawu anga.
24 Popeza ndinakuyitanani koma inu munakana kumvera.
    Ndinayesa kukuthandizani koma panalibe amene anasamala.
25 Uphungu wanga munawunyoza.
    Kudzudzula kwanga simunakusamale.
26 Ndiye inenso ndidzakusekani mukadzakhala mʼmavuto;
    ndidzakunyogodolani chikadzakugwerani chimene mumachiopacho.
27 Chiwonongeko chikadzakugwerani ngati namondwe,
    tsoka likadzakufikirani ngati kamvuluvulu,
    mavuto ndi masautso akadzakugwerani.

28 “Tsono mudzandiyitana koma sindidzayankha;
    mudzandifunafuna, koma simudzandipeza.
29 Popeza iwo anadana ndi chidziwitso
    ndipo sanasankhe kuopa Yehova,
30 popeza iwo sanasamale malangizo anga
    ndipo ananyoza chidzudzulo changa.
31 Tsono adzadya zipatso zoyenera mayendedwe awo
    ndi kukhuta ndi ntchito zimene anachita kwa ena.
32 Pakuti anthu osachangamuka amaphedwa chifukwa cha kusochera kwawo,
    ndipo zitsiru zimadziwononga zokha chifukwa cha mphwayi zawo.
33 Koma aliyense wondimvera adzakhala mwa bata;
    adzakhala mosatekeseka posaopa chilichonse.”

Ubwino Wanzeru

Mwana wanga, ngati ulandira mawu anga
    ndi kusunga malamulo anga mu mtima mwako,
ndiponso kutchera khutu lako ku nzeru
    ndi kuyikapo mtima pa kumvetsa zinthu;
ngati upempha kuti uzindikire zinthu
    inde kupempha ndi mtima wonse kuti ukhale womvetsa zinthu,
ngati ufunafuna nzeruyo ngati siliva
    ndi kuyisakasaka ngati chuma chobisika,
ndiye udzamvetsa bwino tanthauzo la kuopa Yehova;
    ndipo udzapezanso tanthauzo la kumudziwa Yehova.
Pakuti Yehova ndiye amapereka nzeru,
    ndipo mʼkamwa mwake mumachokera chidziwitso ndi kumvetsa zinthu.
Anthu olungama zinthu zimawayendera bwino chifukwa Yehova amakhala nawo.
    Paja Yehova ndiye chishango cha amene amayenda mwangwiro,
pakuti ndiye mlonda wa njira zolungama.
    Iye amasamala mayendedwe a anthu ake okhulupirika.

Choncho udzamvetsa tanthauzo la ungwiro, chilungamo,
    kusakondera ndi njira iliyonse yabwino.
10 Pakuti nzeru idzalowa mu mtima mwako,
    kudziwa zinthu kudzakusangalatsa.
11 Kuganizira bwino za mʼtsogolo kudzakusunga;
    kumvetsa zinthu bwino kudzakuteteza.

12 Nzeru idzakupulumutsa ku mayendedwe oyipa,
    kwa anthu amabodza,
13 amene amasiya njira zolungama
    namayenda mʼnjira zamdima,
14 amene amakondwera pochita zoyipa
    namasangalala ndi kuyipa kwa ntchito zawo zonyansa.
15 Amenewa ndi anthu a njira zawo zokhotakhota,
    ndipo makhalidwe awo ndi achinyengo.

16 Nzeruyo idzakupulumutsanso kwa mkazi wachigololo;
    kwa mkazi wachilendo woyankhula moshashalika,
17 amene wasiya mwamuna wa chitsikana wake
    ndi kuyiwala pangano limene anachita pamaso pa Mulungu wake.
18 Pakuti nyumba yake imatsetserekera ku imfa;
    njira zake zimamufikitsa ku manda.
19 Opita kwa iye palibe ndi mmodzi yemwe amabwerera
    kapena kupezanso njira zamoyo.

20 Choncho iwe uziyenda mʼnjira za anthu abwino,
    uzitsata njira za anthu ochita chilungamo.
21 Pakuti anthu olungama ndiwo ati adzakhale mʼdziko
    ndipo anthu angwiro ndiwo ati adzakhazikike mʼmenemo;
22 Koma anthu oyipa adzachotsedwa mʼdzikomo,
    ndipo anthu onyenga adzachotsedwamo.

1 Akorinto 16

Ndalama Zothandizira Akhristu a ku Yerusalemu

16 Tsopano za zopereka zothandiza anthu a Ambuye a ku Yerusalemu. Muchite zomwe ndinawuza mipingo ya ku Galatiya kuti ichite. Pa tsiku loyamba la sabata lililonse, aliyense wa inu azipatula ndalama molingana ndi zomwe wapezera. Asunge, kuti ndikabwera pasadzakhalenso msonkhamsonkha. Pamenepo, ndikadzafika, ndidzawapatsa makalata a umboni anthu amene mudzawasankhe ndi kuwatuma kuti akapereka mphatso zanu ku Yerusalemu. Ngati kutaoneka kuti nʼkoyenera kuti ndipite nawo, adzapita nane limodzi.

Paulo Afotokoza za Maulendo ake ndi Zina

Ndidzafika kwanuko nditadutsa ku Makedoniya pakuti ndikuyembekezera kudzera ku Makedoniyako. Mwina ndidzakhala nanu kanthawi kochepa kapenanso nyengo yonse yozizira, kuti mudzandithandize kupitiriza ulendo wanga kulikonse kumene ndingapite. Sindikufuna kuti ndikuoneni tsopano mongodutsa chabe, koma ndikuyembekezera kudzakhala nanu kwa kanthawi, ngati Ambuye alola. Koma ndikhala ndili ku Efeso mpaka nthawi ya Pentekosite, pakuti mwayi waukulu wapezeka woti nʼkugwira ntchito yaphindu, koma pali ambiri amene akutsutsana nane.

10 Ngati Timoteyo afike kwanuko, onetsetsani kuti pasakhale zina zomuchititsa mantha pamene ali pakati panu, pakuti iye akugwira ntchito ya Ambuye monga ine. 11 Wina aliyense asamunyoze. Muthandizeni kupitiriza ulendo wake mwamtendere kubwereranso kuli ine. Ndikumuyembekeza pamodzi ndi abale ena.

12 Tsono kunena za mʼbale wathu, Apolo, ndinamuwumiriza kwambiri kuti abwere kwa inu abale, ndipo iye sanafune kupita tsopano. Koma akadzapeza mpata wabwino adzabwera.

13 Khalani tcheru; khazikikani mʼchikhulupiriro chanu; limbani mtima; khalani amphamvu. 14 Chitani zonse mwachikondi.

15 Mukudziwa kuti a mʼbanja la Stefano ndiye anali oyamba kutembenuka mtima ku Akaya, ndipo akhala akudzipereka kutumikira oyera mtima. Choncho ndikukudandaulirani, inu abale, 16 kuti muziwamvera anthu oterewa, ndiponso aliyense wogwira nawo ntchitoyi modzipereka. 17 Ndikondwera kuti Stefano, Fortunato ndi Akayiko afika, chifukwa akhala akundithandiza pakuti inu simuli nane. 18 Pakuti anatsitsimutsa mzimu wanga ndi wanu womwe. Anthu a mtundu oterewa ngofunika kuwalemekeza.

Mawu Otsiriza

19 Mpingo wa mʼchigawo cha ku Asiya ukupereka moni. Akula ndi Prisila akuperekanso moni wachisangalalo, mwa Ambuye, ndiponso mpingo umene umakumana mʼnyumba mwawo ukupereka moni. 20 Abale onse kuno akupereka moni wawo. Patsanani moni wachikondi chenicheni.

21 Ineyo Paulo, ndikulemba ndi dzanja langa mawu awa akuti moni.

22 Ngati wina sakonda Ambuye akhale wotembereredwa. Maranatha! (Ambuye athu bwerani)!

23 Chisomo cha Ambuye Yesu chikhale ndi inu.

24 Chikondi changa chikhale ndi nonsenu mwa Khristu Yesu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.