Old/New Testament
137 Mʼmbali mwa mitsinje ya ku Babuloni tinakhala pansi ndi kulira
pamene tinakumbukira Ziyoni.
2 Kumeneko, pa mitengo ya misondozi
tinapachika apangwe athu,
3 pakuti anthu otigwira ukapolo anatipempha kuti tiyimbe nyimbo.
Otizunza athu anafuna nyimbo zachisangalalo;
iwo anati, “Tiyimbireni imodzi mwa nyimbo za ku Ziyoni!”
4 Tingayimbe bwanji nyimbo za Yehova
mʼdziko lachilendo?
5 Ndikakuyiwala iwe Yerusalemu,
dzanja langa lamanja liyiwale luso lake.
6 Lilime langa limamatire ku nkhama za mʼkamwa mwanga
ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu,
ngati sindiyesa iwe
chimwemwe changa chachikulu.
7 Kumbukirani, Inu Yehova, zimene Aedomu anachita
pa tsiku limene Yerusalemu anagonja.
Iwowo anafuwula kuti, “Mugwetseni pansi, mugwetseni pansi
mpaka pa maziko ake!”
8 Iwe mwana wa mkazi wa Babuloni, woyenera kuwonongedwa,
wodalitsika ndi yemwe adzakubwezera
pa zimene watichitira.
9 Amene adzagwira makanda ako
ndi kuwakankhanthitsa pa miyala.
Salimo la Davide.
138 Ndidzakuyamikani Yehova ndi mtima wanga wonse;
ndidzayimba nyimbo zokutamandani pamaso pa “milungu.”
2 Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera
ndipo ndidzayamika dzina lanu
chifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu,
pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anu
kupambana zinthu zonse.
3 Pamene ndinayitana, munandiyankha;
munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima.
4 Mafumu onse a dziko lapansi akuyamikeni Yehova,
pamene amva mawu a pakamwa panu.
5 Iwo ayimbe za njira za Yehova,
pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.
6 Ngakhale kuti Yehova ngokwezeka, amasamalira odzichepetsa,
koma anthu onyada amawadziwira chapatali.
7 Ngakhale ndiyende pakati pa masautso,
mumasunga moyo wanga;
mumatambasula dzanja lanu kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga,
mumandipulumutsa ndi dzanja lanu lamanja.
8 Yehova adzakwaniritsa cholinga chake pa ine;
chikondi chanu chosasinthika Yehova, ndi chosatha
musasiye ntchito ya manja anu.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
139 Inu Yehova, mwandisanthula
ndipo mukundidziwa.
2 Inu mumadziwa pamene ndikhala pansi ndi pamene ndidzuka;
mumazindikira maganizo anga muli kutali.
3 Mumapenyetsetsa pamene ndikutuluka ndi kugona kwanga;
mumadziwa njira zanga zonse.
4 Mawu asanatuluke pa lilime langa
mumawadziwa bwinobwino, Inu Yehova.
5 Mumandizinga kumbuyo ndi kutsogolo komwe;
mwasanjika dzanja lanu pa ine.
6 Nzeru zimenezi ndi zopitirira nzeru zanga,
ndi zapamwamba kuti ine ndizipeze.
7 Kodi ndingapite kuti kufuna kuzemba Mzimu wanu?
Kodi ndingathawire kuti kuchoka pamaso panu?
8 Ndikakwera kumwamba, Inu muli komweko;
ndikakagona ku malo a anthu akufa, Inu muli komweko.
9 Ngati ndiwulukira kotulukira dzuwa,
ngati ndikakhala ku malekezero a nyanja,
10 kumenekonso dzanja lanu lidzanditsogolera,
dzanja lanu lamanja lidzandigwiriziza.
11 Ndikanena kuti, “Zoonadi, mdima udzandibisa ndithu
ndipo kuwunika kukhale mdima mondizungulira,”
12 komabe mdimawo sudzakhala mdima kwa Inu;
usiku udzawala ngati masana,
pakuti mdima uli ngati kuwunika kwa Inu.
13 Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga;
munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga.
14 Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa;
ntchito zanu ndi zodabwitsa,
zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.
15 Mapangidwe anga sanabisike pamaso panu
pamene ndimapangidwa mʼmalo achinsinsi,
pamene ndinkawumbidwa mwaluso mʼmimba ya amayi anga.
16 Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe.
Masiku onse amene anapatsidwa kwa ine, analembedwa mʼbuku lanu
asanayambe nʼkuwerengedwa komwe.
17 Zolingalira zanu pa ine ndi zamtengowapatali, Inu Mulungu,
ndi zosawerengeka ndithu!
18 Ndikanaziwerenga,
zikanakhala zochuluka kuposa mchenga;
pamene ndadzuka, ndili nanube.
19 Ndi bwino mukanangopha anthu oyipa, Inu Mulungu!
Chokereni inu anthu owononga anzanu!
20 Amayankhula za Inu ndi zolinga zoyipa;
adani anu amagwiritsa ntchito dzina lanu molakwika.
21 Kodi ine sindidana nawo amene amakudani, Inu Yehova?
Kodi sindinyansidwa nawo amene amakuwukirani?
22 Ndimadana nawo kwathunthu;
ndi adani anga.
23 Santhuleni, Inu Mulungu ndipo mudziwe mtima wanga;
Yeseni ndipo mudziwe zolingalira zanga.
24 Onani ngati muli mayendedwe aliwonse oyipa mwa ine,
ndipo munditsogolere mʼnjira yanu yamuyaya.
Kupambana kwa Chikondi
13 Ngakhale nditamayankhula mʼmalilime a anthu ndi a angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chinganga chaphokoso kapena ngati chitsulo chosokosera. 2 Ngati ndili ndi mphatso ya uneneri, nʼkumazindikira zinsinsi ndi kudziwa zonse, ndipo ngati ndili ndi chikhulupiriro chosuntha mapiri, koma wopanda chikondi, ine sindili kanthu. 3 Ngati ndipereka zanga zonse kwa osauka ndi kupereka thupi langa kuti alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ine sindipindula kanthu.
4 Chikondi nʼcholeza mtima, chikondi nʼchokoma mtima, chilibe nsanje, sichidzikuza, sichidzitamandira. 5 Chikondi chilibe mwano, sichodzikonda, sichipsa mtima msanga, sichisunga mangawa. 6 Chikondi sichikondwera ndi zoyipa koma chimakondwera ndi choonadi. 7 Chimatchinjiriza nthawi zonse, chimakhulupirika nthawi zonse, chimakhala ndi chiyembekezo nthawi zonse, chimapirira nthawi zonse.
8 Chikondi ndi chosatha. Koma mphatso ya uneneri idzatha, pamene pali kuyankhula malilime adzatha, pamene pali chidziwitso chidzatha. 9 Pakuti timadziwa zinthu pangʼono chabe ndipo timanenera pangʼono chabe. 10 Koma changwiro chikadzaoneka ndipo chopereweracho chidzatha. 11 Pamene ndinali mwana ndinkayankhula ngati mwana, ndinkaganiza ngati mwana, ndinkalingalira ngati mwana. Koma nditakula, zonse zachibwana ndinazisiya. 12 Pakuti tsopano tiona zinthu mosaoneka bwino ngati mʼgalasi loonera; kenaka tidzaziona maso ndi maso. Tsopano ndidziwa mosakwanira koma kenaka ndidzadziwa mokwanira, monga mmene Mulungu akundidziwira ine.
13 Ndipo tsopano zatsala zinthu zitatu: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma chachikulu pa zonsezi ndi chikondi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.