Old/New Testament
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
126 Yehova atabwezera akapolo ku Ziyoni,
tinali ngati amene akulota.
2 Pakamwa pathu panadzaza ndi kuseka;
malilime athu ndi nyimbo zachimwemwe.
Pamenepo kunanenedwa pakati pa anthu kuti,
“Yehova wawachitira zinthu zazikulu.”
3 Yehova watichitira zinthu zazikulu,
ndipo tadzazidwa ndi chimwemwe.
4 Tibwezereni madalitso athu, Inu Yehova,
monga mitsinje ya ku Negevi.
5 Iwo amene amafesa akulira,
adzakolola akuyimba nyimbo zachimwemwe.
6 Iye amene amayendayenda nalira,
atanyamula mbewu yokafesa,
adzabwerera akuyimba nyimbo zachimwemwe,
atanyamula mitolo yake.
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Salimo la Solomoni.
127 Yehova akapanda kumanga nyumba,
omanga nyumbayo agwira ntchito pachabe.
Yehova akapanda kulondera mzinda,
mlonda akanangolondera pachabe.
2 Mumangodzivuta nʼkulawirira mmamawa
ndi kusagona msanga madzulo,
kuvutikira chakudya choti mudye,
pakuti Iye amapereka tulo kwa amene amawakonda.
3 Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova,
ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.
4 Ana a pa unyamata ali ngati mivi mʼmanja
mwa munthu wankhondo.
5 Wodala munthu
amene motengera mivi mwake mwadzaza.
Iwo sadzachititsidwa manyazi
pamene alimbana ndi adani awo pa zipata.
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
128 Odala ndi onse amene amaopa Yehova,
amene amayenda mʼnjira zake.
2 Udzadya chipatso cha ntchito yako;
madalitso ndi chuma zidzakhala zako.
3 Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka
mʼkati mwa nyumba yako;
ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi
kuzungulira tebulo lako.
4 Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwa
amene amaopa Yehova.
5 Yehova akudalitse kuchokera mʼZiyoni
masiku onse a moyo wako;
uwone zokoma za Yerusalemu,
6 ndipo ukhale ndi moyo kuti udzaone zidzukulu zako.
Mtendere ukhale ndi Israeli.
19 Kodi ndikutanthauza kuti nsembe zoperekedwa kwa mafano ndi kanthu konse, kapena kuti mafano ndi kanthu konse? 20 Ayi. Nsembe za osakhulupirira zimaperekedwa kwa ziwanda, osati kwa Mulungu, ndipo sindikufuna kuti muziyanjana ndi ziwandazo. 21 Simungamwe chikho cha Ambuye, ndi kukamweranso chikho cha ziwanda. Simungadyere pa tebulo la Ambuye ndiponso la ziwanda. 22 Kodi tikufuna kuwutsa mkwiyo wa Ambuye? Kodi ndife amphamvu kuposa Iye?
Ufulu wa Munthu Wokhulupirira
23 Mutha kunena kuti, “Zinthu zonse nʼzololedwa,” komatu si zonse zili za phindu. “Zinthu zonse nʼzololedwa,” komatu si zonse zimathandiza. 24 Munthu aliyense asafunefune zokomera iye yekha, koma zokomeranso ena.
25 Idyani nyama iliyonse imene amagulitsa pa msika, osafunsa mafunso okhudzana ndi chikumbumtima chanu. 26 Popeza kuti, “Dziko lapansi ndi la Ambuye ndi zonse za mʼmenemo ndi zake.”
27 Ngati wosakhulupirira akuyitanani kuti mukadye naye, inuyo ndi kuvomera kupitako, mukadye chilichonse chimene akakupatseni ndipo musakafunse mafunso okhudzana ndi chikumbumtima chanu. 28 Koma ngati wina akuwuzani kuti, “Izi zaperekedwa nsembe,” musadye zimenezo, pofuna kuthandiza amene wakuwuzaniyo komanso chifukwa cha chikumbumtima. 29 Ndikunena za chikumbumtima cha winayo osati chanu. Tsono mungafunse kuti, nʼchifukwa chiyani ufulu wanga ukuphwanyidwa chifukwa cha chikumbumtima cha munthu wina? 30 Ngati ndikuyamika Mulungu chifukwa cha chakudya, nanga munthu angandinyoze bwanji pa zinthu zomwe ndayamikira nazo Mulungu?
31 Nʼchifukwa chake chilichonse mungadye kapena kumwa, kapena chimene mungachite, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu. 32 Musakhumudwitse aliyense, kaya ndi Myuda, Mgriki, kapena mpingo wa Mulungu. 33 Mu zonse ndikuyesetsa kukondweretsa aliyense mʼnjira iliyonse. Popeza sindikufunafuna zokondweretsa ine ndekha koma zokomera ambiri kuti apulumutsidwe.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.