Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 116-118

116 Ndimakonda Yehova pakuti Iyeyo amamva mawu anga;
    Iye amamva kulira kwanga kopempha chifundo.
Pakuti ananditchera khutu,
    ndidzayitana Iye masiku onse a moyo wanga.

Zingwe za imfa zinandizinga,
    zoopsa za ku dziko la anthu akufa zinandigwera;
    ndinapeza mavuto ndi chisoni.
Pamenepo ndinayitana dzina la Yehova:
    “Inu Yehova, pulumutseni!”

Yehova ndi wokoma mtima ndi wolungama
    Mulungu wathu ndi wodzaza ndi chifundo.
Yehova amateteza munthu wodzichepetsa mtima;
    pamene ndinali ndi chosowa chachikulu, Iye anandipulumutsa.

Pumula iwe moyo wanga,
    pakuti Yehova wakuchitira zokoma.

Pakuti Inu Yehova mwapulumutsa moyo wanga ku imfa,
    maso anga ku misozi,
    mapazi anga kuti angapunthwe,
kuti ine ndiyende pamaso pa Yehova
    mʼdziko la anthu amoyo.
10 Ine ndinakhulupirira; choncho ndinati,
    “Ndasautsidwa kwambiri.”
11 Ndipo ndili mʼnkhawa yanga ndinati,
    “Anthu onse ndi abodza.”

12 Ndingamubwezere chiyani Yehova,
    chifukwa cha zokoma zake zonse zimene wandichitira?
13 Ndidzakweza chikho cha chipulumutso
    ndipo ndidzayitana dzina la Yehova.
14 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova
    pamaso pa anthu ake onse.

15 Imfa ya anthu oyera mtima
    ndi yamtengowapatali pamaso pa Yehova.
16 Inu Yehova, zoonadi ndine mtumiki wanu:
    ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu;
    Inu mwamasula maunyolo anga.

17 Ndidzapereka nsembe yachiyamiko kwa Inu
    ndipo ndidzayitanira pa dzina la Yehova.
18 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova
    pamaso pa anthu ake onse,
19 mʼmabwalo a nyumba ya Yehova,
    mʼkati mwako iwe Yerusalemu.

Tamandani Yehova.
117 Tamandani Yehova, inu anthu a mitundu yonse;
    mulemekezeni Iye, inu mitundu ya anthu.
Pakuti chikondi chake pa ife ndi chachikulu,
    ndipo kukhulupirika kwa Yehova nʼkosatha.

Tamandani Yehova.
118 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
    pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha.

Israeli anene kuti:
    “Chikondi chake ndi chosatha.”
Banja la Aaroni linene kuti,
    “Chikondi chake ndi chosatha.”
Iwo amene amaopa Yehova anene kuti:
    “Chikondi chake ndi chosatha.”

Ndili mʼmasautso anga ndinalirira Yehova,
    ndipo Iye anayankha pondichotsa mʼmasautsowo.
Yehova ali nane; sindidzachita mantha.
    Munthu angandichite chiyani?
Yehova ali nane; Iye ndiye thandizo langa.
    Ndidzayangʼana adani anga mwachipambano.

Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova
    kusiyana ndi kudalira munthu.
Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova
    kusiyana ndi kudalira mafumu.

10 Anthu a mitundu yonse anandizinga,
    koma mʼdzina la Yehova ndinawawononga.
11 Anandizinga mbali zonse,
    koma mʼdzina la Yehova ndinawawononga.
12 Anandizinga ngati njuchi,
    koma anatha msanga ngati moto wapaminga;
    mʼdzina la Yehova ndinawawononga.

13 Anandikankha uku ndi uko ndipo ndinali pafupi kugwa,
    koma Yehova anandithandiza.
14 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;
    Iye wakhala chipulumutso changa.

15 Mfuwu wachimwemwe ndi chipambano
    ukumveka mʼmatenti a anthu olungama mtima kuti:
“Dzanja lamanja la Yehova lachita zamphamvu!
16     Dzanja lamanja la Yehova latukulidwa mmwamba
    Dzanja lamanja la Yehova lachita zamphamvu!”

17 Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo
    ndipo ndidzalalika za ntchito ya Yehova.
18 Yehova wandilanga koopsa,
    koma sanandipereke ku imfa.

19 Tsekulireni zipata zachilungamo,
    kuti ndifike kudzayamika Yehova.
20 Ichi ndicho chipata cha Yehova
    chimene olungama mtima okha adzalowerapo.
21 Ndidzakuyamikani chifukwa Inu munandiyankha;
    mwakhala chipulumutso changa.

22 Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana
    wasanduka wapangodya;
23 Yehova ndiye wachita zimenezi
    ndipo nʼzodabwitsa pamaso pathu.
24 Lero ndiye tsiku limene Yehova walipanga;
    tiyeni tikondwere ndi kusangalala nalo.

25 Inu Yehova, tipulumutseni;
    Yehova, tipambanitseni.
26 Wodala amene akubwera mʼdzina la Yehova.
    Tikukudalitsani kuchokera ku nyumba ya Yehova.
27 Yehova ndi Mulungu,
    ndipo kuwala kwake kwatiwunikira Ife.
Lowani nawo pa mʼdipiti wa ku chikondwerero mutanyamula nthambi mʼdzanja lanu,
    mpaka ku nyanga za guwa.

28 Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani;
    Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakukwezani.

29 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
    pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha.

1 Akorinto 7:1-19

Ukwati

Tsopano pa zinthu zomwe munandilembera nʼkwabwino kuti munthu asakwatire. Koma chifukwa choti chigololo chawanda, mwamuna aliyense akhale naye mkazi wakewake ndipo mkazi aliyense akhale naye mwamuna wakewake. Mwamuna akwaniritse udindo wake wa pa banja kwa mkazi wake, ndipo chimodzimodzi mkazi kwa mwamuna wake. Thupi la mkazi wokwatiwa si la iye mwini yekha koma ndi la mwamuna wakenso. Momwemonso, thupi la mwamuna si la iye mwini yekha koma ndi la mkazi wakenso. Musamakanizane, pokhapokha mutagwirizana awiri kuti mwakanthawi mudzipereke kumapemphero. Kenaka mukhalirenso pamodzi kuopa kuti Satana angakuyeseni chifukwa cholephera kudziretsa. Ndikunena zimenezi mokulolani chabe osati mokulamulani. Ine ndikanakonda anthu akanakhala ngati ine. Koma poti munthu aliyense ali ndi mphatso yakeyake yochokera kwa Mulungu, wina mphatso yake, wina yakenso.

Tsono kwa osakwatira onse, ndi akazi amasiye ndikuti, ndi bwino kwa iwo kukhala osakwatira monga mmene ndilili inemu. Koma ngati sangathe kudziretsa, akwatire, popeza ndi bwino kukwatira kusiyana ndi kudzizunza ndi chilakolako.

10 Kwa amene ali pa banja ndikupatsani lamulo ili (osati langa koma la Ambuye): Mkazi asalekane ndi mwamuna wake. 11 Koma ngati atatero, asakwatiwenso, apo ayi, abwerere kwa mwamuna wakeyo. Ndipo mwamuna asaleke mkazi wake.

12 Kwa ena onse ndikunena izi (ineyo osati Ambuye); ngati mʼbale wina ali ndi mkazi wosakhulupirira ndipo mkaziyo walola kukhala pa banja ndi mʼbaleyo, ameneyo asamuleke. 13 Ngati mayi wina ali ndi mwamuna wosakhulupirira ndipo mwamunayo walola kukhala pa banja ndi mayiyo, ameneyo asamuleke. 14 Pakuti mwamuna wosakhulupirirayo amayeretsedwa chifukwa cha mkazi wakeyo, ndipo mkazi wosakhulupirira amayeretsedwa chifukwa cha mwamuna wokhulupirirayo. Kupanda apo ana anu akanakhala odetsedwa, koma mmene zililimu ndi oyeretsedwa.

15 Koma ngati wosakhulupirira achoka, mulekeni achoke. Zikatero ndiye kuti mwamuna kapena mkazi wokhulupirirayo sali womangikanso. Mulungu anatiyitana kuti tikhale mu mtendere. 16 Kodi iwe, mkazi, ungadziwe bwanji kuti mwina nʼkupulumutsa mwamuna wako? Kapena iwe, mwamuna, ungadziwe bwanji kuti mwina nʼkupulumutsa mkazi wako?

Kukhala Moyo Wosinthika

17 Koma aliyense akhale moyo umene Ambuye anamupatsa, umene Mulungu anamuyitanira. Ili ndiye lamulo limene ndalikhazikitsa mʼmipingo yonse. 18 Ngati pamene munthu amayitanidwa anali atachita mdulidwe, asavutike nʼkubisa za mdulidwe wakewo. Ngatinso pamene munthu amayitanidwa nʼkuti asanachite mdulidwe, asachite mdulidwe. 19 Mdulidwe si kanthu, kusachita mdulidwe si kanthunso. Chofunika nʼkusunga malamulo a Mulungu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.