Old/New Testament
Salimo. Nyimbo yothokoza.
100 Fuwulani kwa Yehova mwachimwemwe, inu dziko lonse lapansi.
2 Mulambireni Yehova mosangalala;
bwerani pamaso pake ndi nyimbo zachikondwerero.
3 Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu.
Iye ndiye amene anatipanga ndipo ife ndife ake;
ndife anthu ake, nkhosa za pabusa pake.
4 Lowani ku zipata zake ndi chiyamiko
ndi ku mabwalo ake ndi matamando;
muyamikeni ndi kutamanda dzina lake.
5 Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya;
kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado.
Salimo la Davide.
101 Ndidzayimba za chikondi ndi chiweruzo chanu cholungama;
kwa Inu Yehova ndidzayimba matamando.
2 Ndidzatsata njira yolungama;
nanga mudzabwera liti kwa ine?
Ndidzayenda mʼnyumba mwanga
ndi mtima wosalakwa.
3 Sindidzayika chinthu chilichonse choyipa
pamaso panga.
Ine ndimadana ndi zochita za anthu opanda chikhulupiriro;
iwo sadzadziphatika kwa ine.
4 Anthu a mtima wokhota adzakhala kutali ndi ine;
ine sindidzalola choyipa chilichonse kulowa mwa ine.
5 Aliyense wosinjirira mnansi wake mseri
ameneyo ndidzamuletsa;
aliyense amene ali ndi maso amwano ndi mtima wodzikuza,
ameneyo sindidzamulekerera.
6 Maso anga adzakhala pa okhulupirika mʼdziko,
kuti akhale pamodzi ndi ine;
iye amene mayendedwe ake ndi wosalakwa
adzanditumikira.
7 Aliyense wochita chinyengo
sadzakhala mʼnyumba mwanga.
Aliyense woyankhula mwachinyengo
sadzayima pamaso panga.
8 Mmawa uliwonse ndidzatontholetsa anthu
onse oyipa mʼdziko;
ndidzachotsa aliyense wochita zoyipa
mu mzinda wa Yehova.
Pemphero la munthu wosautsidwa, pamene walefuka, nakhuthulira pamaso pa Yehova kulira kwakeko.
102 Yehova imvani pemphero langa;
kulira kwanga kopempha thandizo kufike kwa Inu.
2 Musandibisire nkhope yanu
pamene ndili pa msautso.
Munditcherere khutu;
pamene ndiyitana ndiyankheni msanga.
3 Pakuti masiku anga akupita ngati utsi;
mafupa anga akunyeka ngati nkhuni zoyaka.
4 Mtima wanga wakanthidwa ndipo ukufota ngati udzu;
ndipo ndimayiwala kudya chakudya changa.
5 Chifukwa cha kubuwula kwanga kofuwula
ndatsala chikopa ndi mafupa okhaokha.
6 Ndili ngati kadzidzi wa ku chipululu,
monga kadzidzi pakati pa mabwinja.
7 Ndimagona osapeza tulo; ndakhala
ngati mbalame yokhala yokha pa denga.
8 Tsiku lonse adani anga amandichita chipongwe;
iwo amene amandinyoza, amagwiritsa ntchito dzina langa ngati temberero.
9 Pakuti ndimadya phulusa ngati chakudya changa
ndi kusakaniza chakumwa changa ndi misozi
10 chifukwa cha ukali wanu waukulu,
popeza Inu mwandinyamula ndi kunditayira kumbali.
11 Masiku anga ali ngati mthunzi wa kumadzulo;
Ine ndikufota ngati udzu.
12 Koma Inu Yehova, muli pa mpando wanu waufumu kwamuyaya;
kudziwika kwanu ndi kokhazikika ku mibado yonse.
13 Inu mudzadzuka ndi kuchitira chifundo Ziyoni
pakuti ndi nthawi yoti muonetse kukoma mtima kwanu pa iyeyo;
nthawi yoyikika yafika.
14 Pakuti miyala yake ndi yokondedwa kwa atumiki anu;
fumbi lake lokha limawachititsa kuti amve chisoni.
15 Mitundu ya anthu idzaopa dzina la Yehova,
mafumu onse a dziko lapansi adzalemekeza ulemerero wanu.
16 Pakuti Yehova adzamanganso Ziyoni
ndi kuonekera mu ulemerero wake.
17 Iye adzayankha pemphero la anthu otayika;
sadzanyoza kupempha kwawo.
18 Zimenezi zilembedwe chifukwa cha mibado ya mʼtsogolo,
kuti anthu amene sanabadwe adzatamande Yehova:
19 “Yehova anayangʼana pansi kuchokera ku malo ake opatulika mmwamba,
kuchokera kumwamba anayangʼana dziko lapansi,
20 kuti amve kubuwula kwa anthu a mʼndende,
kuti apulumutse amene anayenera kuphedwa.”
21 Kotero dzina la Yehova lidzalengezedwa mu Ziyoni
ndi matamando ake mu Yerusalemu,
22 pamene mitundu ya anthu ndi maufumu
adzasonkhana kuti alambire Yehova.
23 Iye anathyola mphamvu zanga pa nthawi ya moyo wanga;
Iyeyo anafupikitsa masiku anga.
24 Choncho Ine ndinati:
“Musandichotse, Inu Mulungu wanga, pakati pa masiku a moyo wanga;
zaka zanu zimakhalabe pa mibado yonse.
25 Pachiyambi Inu munakhazikitsa maziko a dziko lapansi
ndipo mayiko akumwamba ndi ntchito ya manja anu.
26 Izi zidzatha, koma Inu mudzakhalapo;
zidzatha ngati chovala.
Mudzazisintha ngati chovala
ndipo zidzatayidwa.
27 Koma Inu simusintha,
ndipo zaka zanu sizidzatha.
28 Ana a atumiki anu adzakhala pamaso panu;
zidzukulu zawo zidzakhazikika pamaso panu.”
1 Paulo, woyitanidwa mwachifuniro cha Mulungu kuti akhale mtumwi wa Khristu Yesu ndi mʼbale wathu Sositene.
2 Kupita ku mpingo wa Mulungu ku Korinto, kwa oyeretsedwa mwa Khristu Yesu ndi oyitanidwa kukhala opatulika ndiponso kwa onse amene amapemphera mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu mʼdziko lonse lapansi, amene ndi Ambuye wawo ndi wathunso.
3 Landirani chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye athu Yesu Khristu.
Kuthokoza
4 Nthawi zonse ndimayamika Mulungu chifukwa cha inu chifukwa cha chisomo chake chopatsidwa kwa inu mwa Khristu Yesu. 5 Pakuti mwa Iye mwalemekezedwa mʼnjira iliyonse, mʼkuyankhula kwanu konse ndi mʼkudziwa kwanu konse, 6 chifukwa umboni wathu pa za Khristu unatsimikizidwa mwa inu. 7 Choncho inu simusowa mphatso yauzimu iliyonse pamene mukudikira mofunitsitsa kuti Ambuye athu Yesu Khristu avumbulutsidwe. 8 Adzakulimbikitsani mpaka kumapeto kuti mudzakhale wopanda mlandu pa tsiku lobwera Ambuye athu Yesu Khristu. 9 Mulungu amene wakuyitanani inu mu chiyanjano ndi Mwana wake Yesu Khristu Ambuye athu ngokhulupirika.
Kugawikana mu Mpingo
10 Ndidandaulira inu, abale, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu kuti nonsenu muvomerezane wina ndi mnzake kuti pasakhale kugawikana pakati panu ndi kuti mukhale amodzi kwenikweni mu nzeru ndi mʼmaganizo. 11 Abale anga, ena a ku nyumba ya Kloe andidziwitsa kuti pali mkangano pakati panu. 12 Chimene ndikutanthauza ndi ichi: wina amati, “Ndimatsatira Paulo,” wina, “Ndimatsatira Apolo,” wina, “Ndimatsatira Kefa,” winanso, “Ndimatsatira Khristu.”
13 Kodi Khristu wagawikana? Kodi Paulo anapachikidwa pa mtanda chifukwa cha inu? Kodi munabatizidwa mʼdzina la Paulo? 14 Ine ndikuyamika kuti sindinabatizepo mmodzi mwa inu kupatula Krispo ndi Gayo, 15 mwakuti palibe amene anganene kuti anabatizidwa mʼdzina langa. 16 (Inde, ine ndinabatizanso a mʼbanja la Stefano, koma sindikumbukira ngati ndinabatizanso wina aliyense). 17 Pakuti Khristu sananditume ine kudzabatiza, koma kudzalalikira Uthenga Wabwino, osati ndi mawu anzeru za umunthu, kuopa kuti mtanda wa Khristu ungakhale wopanda mphamvu.
Khristu ndiye Nzeru ndi Mphamvu za Mulungu
18 Pakuti uthenga wa mtanda ndi chopusa kwa iwo amene akuwonongeka, koma kwa ife amene tikupulumutsidwa uthengawu ndi mphamvu ya Mulungu. 19 Pakuti kwalembedwa kuti,
“Ine ndidzawononga nzeru za anthu anzeru;
luntha la anthu aluntha Ine ndidzalinyoza.”
20 Munthu wanzeru ali kuti? Munthu wozama ndi maphunziro ali kuti? Munthu wodziwa zakuya zamakono ali kuti? Kodi Mulungu sanazipusitse nzeru za dziko lapansi? 21 Tsono poti mwa nzeru za Mulungu dziko lapansi mu nzeru zake silinamudziwe Iye, Mulungu amakondweretsedwa kuti kudzera mu chopusa cha zomwe zinalalikidwa apulumutse iwo amene akhulupirira. 22 Ayuda amafuna zizindikiro zodabwitsa ndipo Agriki amafunafuna nzeru, 23 koma ife timalalikira Khristu wopachikidwa. Chitsa chokhumudwitsa kwa Ayuda ndi chopusa kwa a mitundu ina. 24 Koma kwa iwo amene Mulungu anawayitana, Ayuda ndi Agriki omwe, Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndi nzeru za Mulungu. 25 Pakuti za Mulungu zooneka ngati zopusa, ndi za nzeru kuposa nzeru za munthu, ndipo za Mulungu zooneka ngati zofowoka, zili ndi mphamvu kuposa mphamvu za munthu.
26 Abale taganizirani mmene munalili musanayitanidwe. Si ambiri a inu munali a nzeru, si ambiri a inu munali a mphamvu zamakopedwe. Si ambiri a inu munali obadwa pa ulemerero. 27 Koma Mulungu anasankha zinthu zopusa za dziko lapansi kuti achititse manyazi anzeru. Mulungu anasankha zinthu zofowoka za dziko lapansi kuti achititse manyazi amphamvu. 28 Anasankha zinthu zapansipansi ndi zopeputsidwa za dziko la pansi lino, zinthu zimene kulibe, kuti asukulutse zimene zilipo, 29 kuti munthu asanyade pamaso pa Mulungu. 30 Nʼchifukwa cha Iye kuti inu muli mwa Khristu Yesu, amene wakhala nzeru ya kwa Mulungu, kwa ife, kunena kuti kulungama kwathu, chiyero ndi chipulumutso. 31 Choncho poti zinalembedwa kuti, “Ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire mwa Ambuye.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.