Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 97-99

97 Yehova akulamulira, dziko lapansi lisangalale;
    magombe akutali akondwere.

Mitambo ndi mdima waukulu zamuzungulira;
    chilungamo ndi kuweruza molungama ndiwo maziko a mpando wake waufumu.
Moto umapita patsogolo pake
    ndi kunyeketsa amaliwongo kumbali zonse.
Zingʼaningʼani zake zimawalitsa dziko lonse;
    dziko lapansi limaona ndipo limanjenjemera.
Mapiri amasungunuka ngati phula pamaso pa Yehova,
    pamaso pa Ambuye a dziko lonse lapansi.
Mayiko akumwamba amalengeza za chilungamo chake,
    ndipo mitundu yonse ya anthu imaona ulemerero wake.

Onse amene amalambira mafano osema amachititsidwa manyazi,
    iwo amene amanyadira mafano;
    mulambireni, inu milungu yonse!

Ziyoni akumva ndipo akukondwera,
    midzi ya Yuda ikusangalala
    chifukwa cha maweruzo anu Yehova.
Pakuti Inu Yehova ndi Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi;
    ndinu wokwezeka kupambana milungu yonse.

10 Iwo amene amakonda Yehova adane ndi zoyipa
    pakuti Iye amayangʼanira miyoyo ya amene amamukhulupirira
    ndipo amawapulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa
11 Kuwala kumafika pa anthu olungama,
    ndi chimwemwe kwa olungama mtima.
12 Kondwerani mwa Yehova Inu olungama
    ndipo tamandani dzina lake loyera.

Salimo.

98 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,
    pakuti Iyeyo wachita zinthu zodabwitsa;
dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera
    zamuchitira chipulumutso.
Yehova waonetsa chipulumutso chake
    ndipo waulula chilungamo chake kwa anthu a mitundu ina.
Iye wakumbukira chikondi chake
    ndi kukhulupirika kwake pa Aisraeli;
malekezero onse a dziko lapansi aona
    chipulumutso cha Mulungu wathu.

Fuwulani mwachimwemwe kwa Yehova, dziko lonse lapansi,
    muyimbireni nyimbo mofuwula ndi mokondwera.
Imbirani Yehova nyimbo ndi zeze,
    ndi zeze ndi mawu a kuyimba,
ndi malipenga ndi kuliza kwa nyanga ya nkhosa yayimuna
    fuwulani mwachimwemwe pamaso pa Yehova Mfumu.

Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo,
    dziko lonse ndi onse amene amakhala mʼmenemo.
Mitsinje iwombe mʼmanja mwawo,
    mapiri ayimbe pamodzi mwachimwemwe;
izo ziyimbe pamaso pa Yehova,
    pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi.
Adzaweruza dziko lonse mwachilungamo,
    ndi mitundu ya anthu mosakondera.
99 Yehova akulamulira,
    mitundu ya anthu injenjemere;
Iye wakhala pa mpando wake waufumu, pakati pa akerubi,
    dziko lapansi ligwedezeke.
Mʼziyoni wamkulu ndi Yehova;
    Iye ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.
Anthu atamande dzina lanu lalikulu ndi loopsa kwambiri,
    Iye ndi woyera.

Mfumu yamphamvu, iyo imakonda chilungamo
    Inu mwakhazikitsa khalidwe losakondera;
mwachita zolungama ndi zoyenera mwa Yakobo.
Kwezani Yehova Mulungu wathu
    ndipo mulambireni pa mapazi ake;
    Iye ndi woyera.

Mose ndi Aaroni anali ena mwa ansembe ake,
    Samueli anali pamodzi ndi iwo amene anayitana pa dzina lake;
iwo anayitana Yehova
    ndipo Iyeyo anawayankha.
Iye anayankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo;
    iwo anasunga malamulo ake ndi zophunzitsa zomwe anawapatsa.

Inu Yehova Mulungu wathu,
    munawayankha iwo;
Inu kwa Israeli munali Mulungu wokhululuka,
    ngakhale munawalanga pa zochita zawo zoyipa.
Kwezani Yehova Mulungu wathu
    ndipo mumulambire pa phiri lake loyera,
    pakuti Yehova Mulungu wathu ndi woyera.

Aroma 16

Mawu Olawirana

16 Ine ndikupereka kwa inu mlongo wathu Febe, mtumiki wa mpingo wa ku Kenkreya. Ine ndikukupemphani kuti mumulandire mwa Ambuye mʼnjira yoyenera oyera mtima ndi kumupatsa thandizo lililonse limene akulifuna kuchokera kwa inu, pakuti iye wakhala thandizo lalikulu kwa anthu ambiri kuphatikiza ine.

Perekani moni kwa Prisila ndi Akura, atumiki anzanga mwa Khristu Yesu. Iwo anapereka miyoyo yawo chifukwa cha ine. Osati ine ndekha komanso mipingo yonse ya a mitundu ina ikuyamika.

Perekaninso moni kwa mpingo umene umasonkhana mʼnyumba mwawo.

Perekani moni kwa mʼbale wanga wokondedwa Epeneto, amene ndi woyamba kukhulupirira Khristu mʼchigawo cha Asiya.

Perekani moni kwa Mariya, amene wakhala akukugwirirani ntchito kwambiri.

Perekani moni kwa Androniko ndi Yuniya abale anga amene anali mʼndende pamodzi ndi ine. Iwo amadziwika ndi atumwi, ndipo iwo anali mwa Khristu ine ndisanakhale.

Perekani moni kwa Ampliato, amene ine ndimamukonda mwa Ambuye.

Perekani moni kwa Urbano, mtumiki mnzathu mwa Khristu ndi wokondedwa wanga Staku.

10 Perekani moni kwa Apele, woyesedwa ndi wovomerezeka mwa Khristu.

Perekani moni kwa a mʼbanja la Aristobulo.

11 Perekani moni kwa Herodiona, mʼbale wanga.

Perekani moni kwa a mʼbanja la Narkiso amene ali mwa Ambuye.

12 Perekani moni kwa Trufena ndi Trufosa, amayi aja amene amagwira ntchito ya Ambuye molimbika.

Perekani moni kwa mnzanga wokondedwa Persida, mayi winanso amene wagwira ntchito kwambiri mwa Ambuye.

13 Perekani moni kwa Rufo, wosankhidwa mwa Ambuye, ndi amayi ake, amene akhala amayi anganso.

14 Perekani moni kwa Asunkrito, Felego, Herima, Patroba, Herima ndi abale amene ali nawo pamodzi.

15 Perekani moni kwa Filologo, Yuliya, Neriya ndi mlongo wake, ndi Olumpa ndi oyera mtima onse amene ali nawo pamodzi.

16 Mupatsane moni wina ndi mnzake mwachikondi choona.

Mipingo yonse ya Khristu ikupereka moni.

17 Abale, ine ndikukupemphani kuti musamale chifukwa cha amene ayambitsa mipatuko ndi kuyika zokhumudwitsa panjira yanu, motsutsana ndi chiphunzitso chimene mwachiphunzira. Muwapewe iwo. 18 Pakuti otero sakutumikira Ambuye athu Khristu koma zilakolako zawo. Ndi mawu okoma ndi oshashalika iwo amanamiza anthu osalakwa. 19 Aliyense anamva za kumvera kwanu, choncho ndine odzaza ndi chimwemwe chifukwa cha inu. Koma ine ndikufuna kuti inu mukhale anzeru pa zabwino, ndi wopanda cholakwa pa zimene zili zoyipa.

20 Mulungu wamtendere adzaphwanya Satana msanga pansi pa mapazi anu.

Chisomo cha Ambuye athu Yesu chikhale ndi inu.

21 Timoteyo, mtumiki mnzanga, akupereka moni. Nawonso, Lusio, Yasoni ndi Sosipatro, abale anga akutero.

22 Ine Tertio, amene ndalemba kalatayi, ndi kupereka moni mwa Ambuye.

23 Gayo, amene chifukwa cha chisamaliro chake, ine ndi mpingo wonse kuno tikusangalala, akupereka moni.

Erasto, amene ndi msungichuma wa mzinda wonse ndiponso mʼbale wathu Kwato, akupereka moni.

24 Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse. Ameni.

25 Tsopano kwa Iye amene ali ndi mphamvu yokhazikitsa monga mwa uthenga wanga wabwino ndikulalikidwa kwa Yesu Khristu, monga mwa vumbulutso lachinsinsi chobisika kwa nthawi yayitali, 26 koma tsopano chavumbulutsidwa ndi kudziwika kudzera mʼMalemba a uneneri mwa lamulo la Mulungu wosatha, kuti mitundu yonse ikhulupirire ndi kumvera Iye, 27 kwa Mulungu yekhayo wanzeru kukhale ulemerero kwamuyaya kudzera mwa Yesu Khristu! Ameni.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.