Old/New Testament
94 Inu Yehova, ndinu Mulungu wobwezera chilango,
Inu Mulungu amene mumabwezera chilango, wonetsani kuwala kwanu.
2 Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi;
bwezerani kwa odzikuza zowayenera.
3 Kodi mpaka liti anthu oyipa Inu Yehova,
mpaka liti anthu oyipa adzalumpha ndi chimwemwe?
4 Amakhuthula mawu onyada;
onse ochita zoyipa ndi odzaza ndi kudzikuza.
5 Amaphwanya anthu anu, Inu Yehova;
amapondereza cholowa chanu.
6 Amaphanso amayi a masiye ndi alendo okhala nawo mʼdziko;
amapha ana amasiye.
7 Iwo amati, “Yehova sakuona;
Mulungu wa Yakobo salabadirako.”
8 Samalani, inu anthu opanda nzeru pakati pa anthu;
zitsiru inu, kodi mudzakhala liti anzeru?
9 Kodi Iye amene anapanga khutu sangathe kumva?
Kodi Iye amene anapanga diso sangathe kuona?
10 Kodi Iye amene amalangiza mitundu ya anthu sangathenso kulanga?
Kodi Iye amene amaphunzitsa munthu angasowe nzeru?
11 Yehova amadziwa maganizo a munthu;
Iye amadziwa kuti maganizowo ndi achabechabe.
12 Wodala munthu amene Inu Yehova mumamulangiza,
munthu amene mumamuphunzitsa kuchokera mulamulo lanu;
13 mumamupumitsa pa nthawi ya mavuto,
mpaka woyipa atakumbiridwa dzenje.
14 Pakuti Yehova sadzawakana anthu ake;
Iye sadzasiya cholowa chake.
15 Chiweruzo chidzakhazikikanso pa chilungamo,
ndipo onse olungama mtima adzachitsata.
16 Ndani adzadzuka chifukwa cha ine kulimbana ndi anthu oyipa?
Ndani adzayimirira mʼmalo mwanga kulimbana ndi anthu ochita zoyipa?
17 Yehova akanapanda kundithandiza,
bwenzi nditakakhala msanga ku malo achete a imfa.
18 Ndikanena kuti, “Phazi langa likuterereka,”
chikondi chanu, Inu Yehova, chimandichirikiza.
19 Pamene nkhawa inakula mʼkati mwanga,
chitonthozo chanu chinabweretsa chimwemwe mʼmoyo mwanga.
20 Kodi mpando waufumu woyipa ungathe kugwirizana nanu
umene umabweretsa masautso chifukwa cha malamulo ake?
21 Iwo amasonkhana pamodzi kulimbana ndi wolungama
ndi kugamula kuti wosalakwa aphedwe.
22 Koma Yehova wakhala linga langa,
ndipo Mulungu ndiye thanthwe limene ndimathawirako.
23 Iye adzawabwezera chifukwa cha machimo awo
ndi kuwawononga chifukwa cha kuyipa kwawo;
Yehova Mulungu wathu adzawawononga.
95 Bwerani, tiyeni timuyimbire Yehova mwachimwemwe,
tiyeni tifuwule kwa Thanthwe la chipulumutso chathu
2 Tiyeni tibwere pamaso pake ndi chiyamiko
ndipo mupembedzeni Iyeyo ndi zida zoyimbira ndi nyimbo.
3 Pakuti Yehova ndi Mulungu wamkulu,
mfumu yayikulu pamwamba pa milungu yonse.
4 Mʼmanja mwake muli maziko ozama a dziko lapansi,
ndipo msonga za mapiri ndi zake.
5 Nyanja ndi yake, pakuti anayilenga ndi Iye,
ndipo manja ake anawumba mtunda wowuma.
6 Bwerani, tiyeni tiwerame pomulambira,
tiyeni tigwade pamaso pa Yehova Mlengi wathu;
7 pakuti Iye ndiye Mulungu wathu
ndipo ife ndife anthu a pabusa pake,
ndi nkhosa za mʼdzanja lake.
Lero ngati inu mumva mawu ake,
8 musawumitse mitima yanu monga momwe munachitira pa Meriba,
monga munachitira tsiku lija pa Masa mʼchipululu.
9 Kumene makolo anu anandiyesa ndi kundiputa,
ngakhale anaona zimene Ine ndinazichita.
10 Kwa zaka makumi anayi ndinali wokwiya ndi mʼbado umenewo;
ndipo ndinati, “Iwo ndi anthu amene mitima yawo imasochera
ndipo sanadziwe njira zanga.”
11 Choncho ndili chikwiyire, ndinalumbira kuti,
“Iwowa sadzalowa ku malo anga a mpumulo.”
96 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano;
Imbirani Yehova dziko lonse lapansi.
2 Imbirani Yehova, tamandani dzina lake;
lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
3 Lengezani ulemerero wake pakati pa mayiko,
ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.
4 Pakuti wamkulu ndi Yehova ndipo ndi woyenera kwambiri kumutamanda;
ayenera kuopedwa kupambana milungu yonse.
5 Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano,
koma Yehova analenga mayiko akumwamba.
6 Ulemu ndi ufumu zili pamaso pake,
mphamvu ndi ulemerero zili mʼmalo ake opatulika.
7 Perekani kwa Yehova, inu mabanja a anthu a mitundu ina,
perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.
8 Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake;
bweretsani chopereka ndipo mulowe mʼmabwalo ake.
9 Lambirani Yehova mu ulemerero wa chiyero chake;
njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi.
10 Nenani pakati pa mitundu ya anthu, “Yehova akulamulira.”
Dziko lonse lakhazikika molimba, silingasunthidwe;
Iye adzaweruza mitundu ya anthu molungama.
11 Mayiko akumwamba asangalale, dziko lapansi likondwere;
nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo;
12 minda ikondwere pamodzi ndi chilichonse chili mʼmenemo.
Pamenepo mitengo yonse ya mʼnkhalango idzayimba ndi chimwemwe;
13 idzayimba pamaso pa Yehova,
pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi;
adzaweruza dziko lonse mwachilungamo
ndi mitundu ya anthu onse mʼchoonadi.
Paulo Mtumwi wa Anthu a Mitundu Ina
14 Abale anga, ine mwini ndikutsimikiza kuti inuyo ndinu abwino, odzaza ndi chidziwitso ndi okhoza kulangizana wina ndi mnzake. 15 Ine ndakulemberani inu molimba mtima pa fundo zina, kukhala ngati kukukumbutsaninso za zimenezo, chifukwa cha chisomo chimene Mulungu anandipatsa ine 16 kukhala mtumiki wa Khristu Yesu wa a mitundu ina ndi udindo wa wansembe, kulalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti a mitundu ina akhale nsembe yolandiridwa kwa Mulungu, yopatsidwa ndi Mzimu Woyera.
17 Choncho, ine ndikunyadira mwa Khristu Yesu potumikira Mulungu wanga. 18 Ine sindidzayesera kuyankhula za kanthu kalikonse koma zimene Khristu wazichita kudzera mwa ine zotsogolera a mitundu ina kuti amvere Mulungu mwa zimene ndinanena ndi kuzichita 19 mwamphamvu ya zizindikiro ndi zodabwitsa kudzera mwamphamvu ya Mzimu Woyera. Choncho kuchokera ku Yerusalemu ndi kuzungulira ku Iluriko, ine ndalalikira kwathunthu Uthenga Wabwino wa Khristu. 20 Chakhala chilakolako changa nthawi zonse kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kumene Khristu sadziwika, kuti ine ndisamange pa maziko a wina wake. 21 Koma monga kwalembedwa kuti,
“Iwo amene sanawuzidwe za Iye adzaona,
ndi iwo amene sanamve adzazindikira.”
22 Ichi nʼchifukwa chake ine ndakhala ndikuletsedwa kawirikawiri kubwera kwa inu.
Paulo Akonza Zopita ku Roma
23 Koma tsopano popeza kulibenso malo anga woti ndigwire ntchito mʼmadera awa, ndakhala ndikufuna kukuonani kwa zaka zambiri. 24 Ine ndikukonza kuti nditero pamene ndipita ku Spaniya. Ine ndikuyembekeza kudzakuchezerani pamene ndikudutsa ndi kuti inu mudzathandize popitiriza ulendo wanga, nditasangalala ndi kukhala nanu kwa kanthawi. 25 Koma tsopano, ine ndili pa ulendo wopita ku Yerusalemu potumikira oyera mtima akumeneko. 26 Pakuti kunakomera a ku Makedoniya ndi a ku Akaya kupereka thandizo kwa osauka pakati pa oyera mtima mu Yerusalemu. 27 Iwo chinawakomera kuchita ichi, ndipo ndithu anali ndi ngongole kwa iwo. Pakuti ngati a mitundu ina anagawana ndi Ayuda madalitso auzimu, iwo ali ndi ngongole kwa Ayuda kuti agawane nawo madalitso awo a ku thupi. 28 Tsono ine nditamaliza ntchito iyi ndi kutsimikiza kuti alandira chipatsochi, ndidzadzera kwanuko kudzakuchezerani pa ulendo wanga popita ku Spaniya. 29 Ine ndikudziwa kuti pamene ndidzabwera kwa inu, ndidzafika ndili wodzaza ndi madalitso a Khristu.
30 Abale, ine ndikukupemphani, mwa Ambuye athu Yesu Khristu ndi mwachikondi cha Mzimu, kuti mukhale nane pa kulimbika kwanga pondipempherera kwa Mulungu. 31 Pempherani kuti ine ndilanditsidwe kwa osakhulupirira a ku Yudeya ndi kuti utumiki wanga mu Yerusalemu ukhale ovomerezeka ndi oyera mtima. 32 Kuti mwachifuniro cha Mulungu ndibwere kwa inu ndi chimwemwe kuti ndidzapumule pamodzi ndi inu. 33 Mulungu wamtendere akhale ndi inu nonse. Ameni.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.