Old/New Testament
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
68 Adzuke Mulungu, adani ake amwazikane;
adani ake athawe pamaso pake.
2 Monga momwe mphepo imachotsera utsi; Inu muwawulutsire kutali.
Monga phula limasungunukira pa moto,
oyipa awonongeke pamaso pa Mulungu.
3 Koma olungama asangalale
ndi kukondwera pamaso pa Mulungu;
iwo akondwere ndi kusangalala.
4 Imbirani Mulungu imbirani dzina lake matamando,
mukwezeni Iye amene amakwera pa mitambo;
dzina lake ndi Yehova ndipo sangalalani pamaso pake.
5 Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye,
ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.
6 Mulungu amakhazikitsa mtima pansi osungulumwa mʼmabanja,
amatsogolera amʼndende ndi kuyimba;
koma anthu osamvera amakhala ku malo owuma a dziko lapansi.
7 Pamene munatuluka kutsogolera anthu anu, Inu Mulungu,
pamene munayenda kudutsa chipululu,
8 dziko lapansi linagwedezeka, miyamba inakhuthula pansi mvula,
pamaso pa Mulungu, Mmodzi uja wa ku Sinai.
Pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israeli.
9 Munapereka mivumbi yochuluka, Inu Mulungu;
munatsitsimutsa cholowa chanu cholefuka.
10 Anthu anu anakhala mʼmenemo
ndipo munapatsa anthu osauka zimene zinkawasowa chifukwa cha ubwino wanu Mulungu.
11 Ambuye analengeza mawu,
ndipo gulu linali lalikulu la iwo amene anapita kukawafalitsa;
12 “Mafumu ndi ankhondo anathawa mwaliwiro;
mʼmisasa anthu anagawana zolanda pa nkhondo.
13 Ngakhale mukugona pakati pa makola a ziweto,
mapiko a nkhunda akutidwa ndi siliva,
nthenga zake ndi golide wonyezimira.”
14 Pamene Wamphamvuzonse anabalalitsa mafumu mʼdziko,
zinali ngati matalala akugwa pa Zalimoni.
15 Mapiri a Basani ndi mapiri aulemerero;
mapiri a Basani, ndi mapiri a msonga zambiri.
16 Muyangʼaniranji mwansanje inu mapiri a msonga zambiri,
pa phiri limene Mulungu analisankha kuti azilamulira,
kumene Yehova mwini adzakhalako kwamuyaya?
17 Magaleta a Mulungu ndi osawerengeka,
ndi miyandamiyanda;
Ambuye wabwera kuchokera ku Sinai, walowa mʼmalo ake opatulika.
18 Pamene Inu munakwera mmwamba,
munatsogolera a mʼndende ambiri;
munalandira mphatso kuchokera kwa anthu,
ngakhale kuchokera kwa owukira,
kuti Inu Mulungu, mukhale kumeneko.
19 Matamando akhale kwa Ambuye, kwa Mulungu Mpulumutsi wathu
amene tsiku ndi tsiku amasenza zolemetsa zathu.
20 Mulungu wathu ndi Mulungu amene amapulumutsa;
Ambuye Wamphamvuzonse ndiye amene amatipulumutsa ku imfa.
21 Ndithu Mulungu adzaphwanya mitu ya adani ake,
zipewa za ubweya za iwo amene amapitiriza kuchita machimo awo.
22 Ambuye akunena kuti, “Ndidzawabweretsa kuchokera ku Basani;
ndidzawabweretsa kuchokera ku nyanja zozama.
23 Kuti muviyike mapazi anu mʼmagazi a adani anu,
pamene malilime a agalu anu akudyapo gawo lawo.”
24 Mayendedwe aulemu a anthu anu aonekera poyera, Inu Mulungu;
mayendedwe olemekeza Mulungu wanga ndi Mfumu yanga yokalowa mʼmalo opatulika.
25 Patsogolo pali oyimba nyimbo pakamwa, pambuyo pawo oyimba nyimbo ndi zipangizo;
pamodzi ndi iwo pali atsikana akuyimba matambolini.
26 Tamandani Mulungu mu msonkhano waukulu;
tamandani Yehova mu msonkhano wa Israeli.
27 Pali fuko lalingʼono la Benjamini, kuwatsogolera,
pali gulu lalikulu la ana a mafumu a Yuda,
ndiponso pali ana a mafumu a Zebuloni ndi Nafutali.
28 Kungani mphamvu zanu Mulungu;
tionetseni nyonga zanu, Inu Mulungu, monga munachitira poyamba.
29 Chifukwa cha Nyumba yanu ku Yerusalemu,
mafumu adzabweretsa kwa Inu mphatso.
30 Dzudzulani chirombo pakati pa mabango,
gulu la ngʼombe zazimuna pakati pa ana angʼombe a mitundu ya anthu.
Mochititsidwa manyazi, abweretse mitanda ya siliva.
Balalitsani anthu a mitundu ina amene amasangalatsidwa ndi nkhondo.
31 Nthumwi zidzachokera ku Igupto;
Kusi adzadzipereka yekha kwa Mulungu.
32 Imbirani Mulungu Inu mafumu a dziko lapansi
imbirani Ambuye matamando.
Sela
33 Kwa Iye amene amakwera pa mitambo yakalekale ya mmwamba
amene amabangula ndi mawu amphamvu.
34 Lengezani za mphamvu za Mulungu,
amene ulemerero wake uli pa Israeli
amene mphamvu zake zili mʼmitambo.
35 Ndinu woopsa, Inu Mulungu mʼmalo anu opatulika;
Mulungu wa Israeli amapereka mphamvu ndi nyonga kwa anthu ake.
Matamando akhale kwa Mulungu!
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Potsata mayimbidwe a “Akakombo.”
69 Pulumutseni Inu Mulungu,
pakuti madzi afika mʼkhosi
2 Ine ndikumira mʼthope lozama
mʼmene mulibe popondapo.
Ndalowa mʼmadzi ozama;
mafunde andimiza.
3 Ndafowoka ndikupempha chithandizo;
kummero kwanga kwawuma gwaa,
mʼmaso mwanga mwada
kuyembekezera Mulungu wanga.
4 Iwo amene amadana nane popanda chifukwa
ndi ochuluka kuposa tsitsi la kumutu kwanga;
ambiri ndi adani anga popanda chifukwa,
iwo amene akufunafuna kundiwononga.
Ndikukakamizidwa kubwezera
zomwe sindinabe.
5 Mukudziwa uchitsiru wanga, Inu Mulungu,
kulakwa kwanga sikuli kobisika kwa Inu.
6 Iwo amene amadalira Inu
asanyozedwe chifukwa cha ine,
Inu Ambuye Wamphamvuzonse.
Iwo amene amafunafuna Inu
asachititsidwe manyazi chifukwa cha ine,
Inu Mulungu wa Israeli.
7 Pakuti ndimapirira kunyozedwa chifukwa cha Inu,
ndipo manyazi amaphimba nkhope yanga.
8 Ndine mlendo kwa abale anga,
munthu wakudza kwa ana aamuna a amayi anga;
9 pakuti changu chochitira nyumba yanu chandiphetsa
ndipo chipongwe cha iwo amene amanyoza Inu chandigwera.
10 Pamene ndikulira ndi kusala kudya,
ndiyenera kupirira kunyozedwa;
11 pomwe ndavala chiguduli,
anthu amandiseweretsa.
12 Iwo amene amakhala pa chipata amandinena,
ndipo ine ndine nyimbo ya zidakwa.
13 Koma ndikupempha kwa Inu Ambuye,
pa nthawi yanu yondikomera mtima;
mwa chikondi chanu chachikulu
Inu Mulungu, mundiyankhe pondipulumutsa.
14 Mundilanditse kuchoka mʼmatope,
musalole kuti ndimire,
pulumutseni ine kwa iwo
amene amadana nane, kuchoka mʼmadzi ozama.
15 Musalole kuti chigumula chindimeze,
kuya kusandimeze
ndipo dzenje lisatseke pakamwa pake kundimiza.
16 Ndiyankheni Inu Yehova mwa ubwino wanu wa chikondi chanu;
mwa chifundo chanu chachikulu tembenukirani kwa ine.
17 Musabisire nkhope yanu mtumiki wanu,
ndiyankheni msanga, pakuti ndili pa mavuto.
18 Bwerani pafupi ndi kundilanditsa;
ndiwomboleni chifukwa cha adani anga.
19 Inu mukudziwa momwe ndanyozedwera,
kunyozedwa ndi kuchititsidwa manyazi; adani anga onse ali pamaso panu.
20 Mnyozo waswa mtima wanga
ndipo wandisiya wopanda thandizo lililonse;
ndinafunafuna ena woti andichitire chisoni,
koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti anditonthoze, sindinapeze ndi mmodzi yemwe.
21 Iwo anayika ndulu mʼchakudya changa
ndi kundipatsa vinyo wosasa chifukwa cha ludzu.
22 Chakudya chomwe chayikidwa patsogolo pawo chikhale msampha;
chikhale chobwezera chilango ndiponso khwekhwe.
23 Maso awo adetsedwe kotero kuti asaonenso
ndipo misana yawo ipindike mpaka kalekale.
24 Khuthulirani ukali wanu pa iwo;
mkwiyo wanu woyaka moto uwathe mphamvu.
25 Malo awo akhale wopanda anthu
pasapezeke ndi mmodzi yemwe wokhala mʼmatenti awo.
26 Pakuti iwo amazunza amene inu munamuvulaza
ndi kuyankhula zowawa kwa amene munawapweteka.
27 Awonjezereni kulakwa pa kulakwa kwawo,
musalole kuti akhale ndi gawo pa chipulumutso chanu.
28 Iwo afufutidwe mʼbuku la amoyo
ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama.
29 Ndikumva zowawa ndi kuzunzika;
lolani chipulumutso chanu, Inu Mulungu, chinditeteze.
30 Ine ndidzatamanda dzina la Mulungu mʼnyimbo,
ndidzalemekeza Iye ndi chiyamiko.
31 Izi zidzakondweretsa Yehova kupambana ngʼombe,
kupambananso ngʼombe yayimuna, pamodzi ndi nyanga ndi ziboda zake.
32 Wosauka adzaona ndipo adzasangalala,
Inu amene mumafunafuna Mulungu, mitima yanu ikhale ndi moyo!
33 Yehova amamvera anthu osowa
ndipo sanyoza anthu ake omangidwa.
34 Kumwamba ndi dziko lapansi zitamanda Iye,
nyanja ndi zonse zomwe zimayenda mʼmenemo,
35 pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni
ndi kumanganso mizinda ya Yuda,
anthu adzakhala kumeneko ndipo dzikolo lidzakhala lawo;
36 ana atumiki ake adzalitenga kukhala cholowa chawo,
ndipo iwo amene amakonda dzina lake adzakhala kumeneko.
Moyo Watsopano mwa Khristu
8 Choncho, tsopano amene ali mwa Khristu Yesu alibe mlandu owatsutsa 2 chifukwa mwa Khristu Yesu, lamulo la Mzimu Woyera amene amapereka moyo, lawamasula ku lamulo la tchimo ndi la imfa. 3 Pakuti zimene Malamulo sanathe kuzichita, popeza anali ofowoka chifukwa cha khalidwe lathu la uchimo, Mulungu anazichita potumiza Mwana wake mʼchifanizo cha munthu ochimwa kuti akhale nsembe yauchimo. Ndipo Iye anagonjetsa tchimo mʼthupi la munthu, 4 ndi cholinga chakuti chilungamo chofunikira cha lamulo chikwaniritsidwe kwathunthu mwa ife amene sitikhala monga mwachikhalidwe chathu cha uchimo koma mwa Mzimu.
5 Pakuti anthu amene amakhala monga mwa makhalidwe oyipa a thupi amayika malingaliro awo pa zinthu zathupi. Koma amene amakhala monga mwa Mzimu amayika malingaliro awo pa zinthu za Mzimu. 6 Kuyika mtima pa zathupi ndi imfa koma kuyika mtima pa za Mzimu ndi moyo ndi mtendere. 7 Pakuti mtima umene wakhazikika pa zathupi ndi wodana ndi Mulungu. Sunagonjere lamulo la Mulungu ndipo sungathe kutero. 8 Ndipo anthu amene amalamulidwa ndi khalidwe lauchimo sangathe kukondweretsa Mulungu.
9 Koma inu simulamulidwanso ndi khalidwe lanu lauchimo koma ndi Mzimu ngati Mzimu wa Mulungu akhaladi mwa inu. Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu, iyeyu si wa Khristu. 10 Ndipo ngati Khristu ali mwa inu, thupi lanu ndi lakufa chifukwa cha uchimo, koma mzimu wanu ndi wamoyo chifukwa cha chilungamo. 11 Ndipo ngati Mzimu wa Mulungu amene anaukitsa Yesu kwa akufa akhala mwa inu, Iyeyo amene anaukitsa Khristu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu amene amafa kudzera mwa Mzimu wake amene amakhala mwa inu.
12 Kotero abale, ife tili ndi zoti tikwaniritse, koma osati za khalidwe lathu lauchimo, kumachita zofuna zake. 13 Pakuti ngati inu mukhala monga mwa khalidwe lauchimo, mudzafa. Koma ngati mwa Mzimu mupha ntchito zoyipa zathupi, mudzakhala ndi moyo. 14 Onse amene amatsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu ndi ana a Mulungu. 15 Mzimu amene inu munalandira samakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha, koma Mzimu amakusandutsani ana. Ndipo mwa Iye ife timafuwula kuti, “Abba, Atate.” 16 Mzimu mwini amavomerezana ndi mzimu wathu kuti ife ndife ana a Mulungu. 17 Tsono ngati tili ana ake, ndiye kuti ndife olowa mʼmalo a Mulungu ndi olowa mʼmalo pamodzi ndi Khristu. Ngati ife timva zowawa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.
Ulemerero wa Mʼtsogolo
18 Ine ndiganiza kuti masautso amene tikuwamva nthawi ino, sakufanana ndi ulemerero umene udzaonetsedwa mwa ife. 19 Pakuti chilengedwe chikudikira ndi chiyembekezo kuonetsedwa poyera kwa ana a Mulungu. 20 Pakuti chilengedwe sichinasankhe kugonjera zopanda pake, koma mwachifuniro cha Iye amene analola kuti chigonjere. Koma chili ndi chiyembekezo 21 chakuti chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi ndi kulandiranso ufulu ndi ulemerero wa ana a Mulungu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.