Old/New Testament
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
31 Mwa Inu Yehova, ine ndimathawiramo;
musalole nʼkomwe kuti ndichititsidwe manyazi;
mundipulumutse chifukwa cha chilungamo chanu.
2 Tcherani khutu lanu kwa ine,
bwerani msanga kudzandilanditsa;
mukhale thanthwe langa lothawirapo,
linga lolimba kundipulumutsa ine.
3 Popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa,
chifukwa cha dzina lanu tsogolereni ndi kundiwongolera.
4 Ndimasuleni mu msampha umene anditchera
pakuti ndinu pothawirapo panga.
5 Mʼmanja mwanu ndipereka mzimu wanga;
womboleni Yehova Mulungu wachoonadi.
6 Koma ine ndimadana nawo amene amamamatira mafano achabechabe;
ine ndimadalira Yehova.
7 Ndidzakondwa ndi kusangalala mʼchikondi chanu
popeza Inu munaona masautso anga
ndipo mumadziwa kuwawa kwa moyo wanga.
8 Inu simunandipereke kwa mdani
koma mwayika mapazi anga pa malo otakasuka.
9 Mundichitire chifundo Inu Yehova pakuti ndili pa mavuto;
maso anga akulefuka ndi chisoni,
mʼmoyo mwanga ndi mʼthupi mwanga momwe mukupweteka.
10 Moyo wanga ukunyeka chifukwa cha kuwawidwa mtima
ndi zaka zanga chifukwa cha kubuwula;
mphamvu zanga zatha chifuwa cha masautso,
ndipo mafupa anga akulefuka.
11 Chifukwa cha adani anga onse,
ndine wonyozeka kwambiri ndi anansi anga;
ndine chochititsa manyazi kwa abwenzi anga.
Iwo amene amandiona mu msewu amandithawa.
12 Ine ndinayiwalika kwa iwo ngati kuti ndinamwalira;
ndakhala ngati mʼphika wosweka.
13 Pakuti ine ndamva zonena zoyipa za anthu ambiri;
zoopsa zandizungulira mbali zonse;
iwo akukonza chiwembu kuti alimbane nane,
kuti atenge moyo wanga.
14 Koma ndikudalira Inu Yehova;
ndikunena kuti, “Ndinu Mulungu wanga.”
15 Masiku anga ali mʼmanja mwanu;
ndipulumutseni kwa adani anga
ndi kwa iwo amene akundithamangitsa.
16 Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu;
pulumutseni mwa chikondi chanu chosatha.
17 Yehova musalole kuti ndichite manyazi,
pakuti ndalirira kwa Inu;
koma oyipa achititsidwe manyazi
ndipo agone chete mʼmanda.
18 Milomo yawo yabodzayo ikhale chete,
pakuti chifukwa cha kunyada
ayankhula modzikuza kutsutsana ndi wolungama.
19 Ndi waukulu ubwino wanu
umene mwawasungira amene amakuopani,
umene mumapereka anthu akuona
kwa iwo amene amathawira kwa Inu.
20 Mu mthunzi wa pamalo popezeka panu muwabisa,
kuwateteza ku ziwembu za anthu;
mʼmalo anu okhalamo mumawateteza
kwa anthu owatsutsa.
21 Matamando akhale kwa Yehova,
pakuti anaonetsa chikondi chake chodabwitsa kwa ine
pamene ndinali mu mzinda wozingidwa.
22 Ndili mʼnkhawa zanga ndinati,
“Ine ndachotsedwa pamaso panu!”
Komabe Inu munamva kupempha chifundo kwanga
pamene ndinapempha thandizo kwa Inu.
23 Kondani Yehova oyera mtima ake onse!
Yehova amasunga wokhulupirika
koma amalanga kwathunthu anthu odzikuza.
24 Khalani ndi nyonga ndipo limbani mtima,
inu nonse amene mumayembekezera Yehova.
Salimo la Davide. Malangizo.
32 Ngodala munthu
amene zolakwa zake zakhululukidwa;
amene machimo ake aphimbidwa.
2 Ngodala munthu
amene machimo ake Yehova sawawerengeranso pa iye
ndipo mu mzimu mwake mulibe chinyengo.
3 Pamene ndinali chete,
mafupa anga anakalamba
chifukwa cha kubuwula kwanga tsiku lonse.
4 Pakuti usana ndi usiku
dzanja lanu linandipsinja;
mphamvu zanga zinatha
monga nthawi yotentha yachilimwe.
Sela
5 Kotero ine ndinavomereza tchimo langa kwa Inu,
sindinabise mphulupulu zanga.
Ndinati, “Ine ndidzawulula
zolakwa zanga kwa Yehova,
ndipo Inu munandikhululukira
mlandu wa machimo anga.”
Sela
6 Choncho aliyense okhulupirika apemphere kwa Inuyo
pomwe mukupezeka;
ndithu pamene madzi amphamvu auka,
sadzamupeza.
7 Inu ndi malo anga obisala;
muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizinga
ndi nyimbo zachipulumutso.
Sela
8 Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo;
ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira.
9 Usakhale ngati kavalo kapena bulu,
zimene zilibe nzeru,
koma ziyenera kuwongoleredwa ndi zitsulo za mʼkamwa ndi pamutu,
ukapanda kutero sizibwera kwa iwe.
10 Zowawa ndi zambiri za anthu oyipa
koma chikondi chosatha cha Yehova
chimamuzinga munthu amene amadalira Iye.
11 Kondwerani mwa Yehova inu olungama;
imbani, inu nonse amene muli owongoka mtima!
16 Koma mwana wa mlongo wake wa Paulo atamva za chiwembuchi, anapita ku malo a asilikali aja namufotokozera Paulo.
17 Paulo anayitana mmodzi wa wolamulira asilikali 100 aja, namuwuza kuti, “Pita naye mnyamatayu kwa mkulu wa asilikali. Iyeyu ali ndi mawu oti akamuwuze.” 18 Anamutengadi mnyamatayo napita naye kwa mkulu wa asilikali uja, nati, “Wamʼndende uja Paulo anandiyitana, nandipempha kuti ndibweretse mnyamatayu kwa inu chifukwa ali ndi kanthu koti akuwuzeni.”
19 Mkulu wa asilikali uja anagwira dzanja mnyamatayo napita naye paseli ndipo anamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kuti undiwuze chiyani?”
20 Mnyamatayo anati, “Ayuda agwirizana zoti akupempheni kuti mawa mubwere ndi Paulo ku Bwalo Lalikulu, ngati kuti akufuna kudziwa bwino za iye. 21 Inu musawamvere, chifukwa pali anthu opitirira makumi anayi amene akumudikirira pa njira. Iwo alumbira kuti sadya kapena kumwa mpaka atapha Paulo. Panopa ndi okonzeka kale, akungodikira kuti muwavomere pempho lawo.”
22 Mkulu wa asilikaliyo anawuza mnyamatayo kuti apite koma anamuchenjeza kuti, “Usawuze munthu aliyense kuti wandifotokozera zimenezi.”
Paulo Apita ku Kaisareya
23 Kenaka mkulu wa asilikaliyo anayitana awiri a asilikali olamulira asilikali 100 nawalamula kuti, “Uzani asilikali 200, asilikali 70 okwera pa akavalo ndi 200 onyamula mikondo kuti akonzeke kupita ku Kaisareya usiku omwe uno nthawi ya 9 koloko. 24 Mumukonzerenso Paulo akavalo woti akwerepo kuti akafike bwino kwa bwanamkubwa Felike.”
25 Iye analemba kalata iyi:
26 Ine Klaudiyo Lusiya,
Kwa wolemekezeka, bwanamkubwa Felike:
Ndikupereka moni.
27 Munthuyo Ayuda anamugwira ndipo anali pafupi kumupha, koma ine ndinapita ndi asilikali nʼkukamulanditsa pakuti ndinamva kuti ndi nzika ya Chiroma. 28 Ndinkafuna kudziwa mlandu umene anapalamula, choncho ndinapita naye ku Bwalo lawo Lalikulu. 29 Ine ndinapeza kuti amamuyimba mlandu wa nkhani ya malamulo awo, koma panalibe mlandu woyenera kumuphera kapena kumuyika mʼndende. 30 Nditawuzidwa kuti amukonzera chiwembu munthuyu, ine ndamutumiza kwa inu msanga. Ine ndalamulanso amene akumuyimba mlanduwo kuti abwere kwa inu kudzafotokoza nkhaniyo.
31 Pamenepo asilikali aja anatenga Paulo monga anawalamulira napita naye ku Antipatri usiku. 32 Mmawa mwake iwo anabwerera ku malo a asilikali nasiya okwera pa akavalo kuti apitirire ndi Paulo. 33 Asilikali okwera pa akavalowo atafika ku Kaisareya anapereka kalatayo kwa bwanamkubwa, namuperekanso Paulo. 34 Bwanamkubwayo anawerenga kalatayo ndipo anamufunsa Paulo za dera limene amachokera. Atazindikira kuti amachokera ku Kilikiya, 35 iye anati, “Ndidzamva mlandu wako okuyimba mlandu akabwera kuno.” Ndipo analamulira kuti asilikali adzimulondera Paulo ku nyumba ya mfumu Herode.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.