Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yobu 36-37

36 Ndipo Elihu anapitirira kuyankhula nati:

“Mundilole pangʼono pokha ndipo ndikuonetsani
    kuti zilipo zambiri zoti ziyankhulidwe mʼmalo mwa Mulungu.
Nzeru zanga ndimazitenga kutali;
    ndidzaonetsa kulungama kwa Mlengi wanga.
Ndithudi mawu anga si abodza;
    wanzeru zangwiro ali ndi inu.

“Mulungu ndi wamphamvu, koma sanyoza anthu;
    Iye ndi wamphamvu, ndipo ndi wokhazikika pa cholinga chake.
Salola oyipa kuti akhalebe ndi moyo
    koma amapereka ufulu kwa anthu osautsidwa.
Iye saleka kuyangʼanira anthu olungama;
    amawayika kuti alamulire pamodzi ndi mafumu
    ndipo amawalemekeza mpaka muyaya.
Koma ngati anthu amangidwa ndi unyolo,
    ndipo akondwa ndi zingwe zamasautso,
Iye amawafotokozera zomwe anachita,
    kuti iwo anachimwa modzikuza.
10 Mulungu amawatsekula makutu kuti amve malangizo ake
    ndipo amawalamula kuti alape zoyipa zawo.
11 Ngati iwo amumvera ndi kumutumikira,
    adzatsiriza masiku a moyo wawo mwamtendere,
    adzatsiriza zaka zawo mosangalala.
12 Koma ngati samvera,
    adzaphedwa ndi lupanga
    ndipo adzafa osadziwa kanthu.

13 “Anthu osapembedza amasunga mkwiyo mu mtima mwawo;
    akawalanga, safuwulira kwa Iye kupempha thandizo.
14 Amafa akanali achinyamata,
    pakati pa amuna achiwerewere a kumalo azipembedzo.
15 Koma ovutika, Iye amawapulumutsa pa mavuto awo;
    Mulungu amawayankhula mʼmasautso awowo.

16 “Iye akukukopani inu kuti muchoke mʼmasautso,
    kuti mupite ku malo aakulu kumene kulibe chokutchingani,
    kumalo a mpumulo kumene kuli chakudya chabwino kwambiri.
17 Koma tsopano inu mwapezeka wopalamula chifukwa cha kuyipa kwanu;
    chiweruzo ndi chilungamo chakugwerani.
18 Muchenjere kuti wina asakukopeni ndi chuma;
    musalole kuti chiphuphu chachikulu chikusocheretseni.
19 Kodi chuma chanu
    kapena mphamvu zanu zonse
    zingakusungeni kotero kuti simungakhale pa masautso?
20 Musalakalake kuti usiku ubwere,
    pakuti ndiyo nthawi imene anthu adzawonongeka.
21 Muchenjere kuti musatembenukire ku uchimo,
    chifukwa uchimowo ndiwo unabweretsa kuzunzika kwanu.

22 “Taonani, Mulungu ndi wamkulu ndiponso ndi wamphamvu.
    Kodi ndi mphunzitsi uti amene angafanane naye?
23 Kodi ndani amene anamuwuzapo Mulungu zoti achite,
    kapena kumuwuza kuti, ‘Inu mwachita chinthu cholakwa?’
24 Kumbukirani kutamanda ntchito zake
    zimene anthu amaziyamika mʼnyimbo.
25 Anthu onse amaziona ntchitozo;
    anthuwo amaziona ali kutali.
26 Ndithudi, Mulungu ndi wamkulu, sitimudziwa nʼpangʼono pomwe!
    Chiwerengero cha zaka zake nʼchosadziwika.

27 “Mulungu ndiye amakweza timadontho tamadzi kuthambo,
    timene timasungunuka nʼkukhala mvula;
28 mitambo imagwetsa mvulayo
    ndipo mvulayo imavumbwa pa anthu mokwanira.
29 Kodi ndani amene angadziwe momwe mitambo imayendera,
    momwe Iye amabangulira kuchokera kumalo ake?
30 Taonani momwe amawalitsira zingʼaningʼani pa malo ake onse,
    zimafika ngakhale pansi pa nyanja.
31 Umu ndi mmene Iye amalamulira mitundu ya anthu
    ndi kuwapatsa chakudya chochuluka.
32 Amadzaza manja ake ndi zingʼaningʼani,
    ndipo amazilamulira kuti zigwe pamalo pamene Iye akufuna.
33 Mabingu ake amalengeza za kubwera kwa mvula yamkuntho;
    ngʼombe nazo zimalengeza za kubwera kwake.

37 “Mtima wanga ukulumphalumpha pa chimenechinso
    ndipo ukuchoka mʼmalo mwake.
Tamverani! Tamverani kubangula kwa liwu lake,
    kugunda kumene kukuchokera mʼkamwa mwake.
Iye amaponya chingʼaningʼani chake pansi pa thambo lonse
    ndipo amachitumiza ku dziko lapansi.
Pambuyo pake kubangula kwake kumamveka.
    Iye amabangula ndi liwu lake laulemerero.
Pamene wabangula,
    palibe chimene amalephera kuchita.
Liwu la Mulungu limabangula mʼnjira zambiri zodabwitsa
    Iye amachita zinthu zazikulu zimene sitingathe kuzimvetsa.
Amalamula chisanu chowundana kuti, ‘Igwa pa dziko lapansi,’
    ndipo amalamulanso mvula yamawawa kuti, ‘Khala mvula yamphamvu.’
Kuti anthu onse amene anawalenga athe kuzindikira ntchito yake.
    Iye amalepheretsa anthu kugwira ntchito zawo.
Zirombo zimakabisala
    ndipo zimakhala mʼmaenje mwawo.
Mphepo yamkuntho imatuluka ku malo ake,
    kuzizira kumatuluka mʼmphepo yamkunthoyo.
10 Mpweya wa Mulungu umawunditsa madzi
    ndipo madzi a mʼnyanja amawuma kuti gwaa.
11 Iye amadzaza mitambo ndi madzi a mvula,
    amabalalitsa zingʼaningʼani zake kuchokera mʼmitambomo.
12 Mulungu amayendetsa mitamboyo
    mozungulirazungulira dziko lonse lapansi
    kuti ichite zonse zimene Iye akufuna pa dziko lapansi.
13 Iye amagwetsa mvula kuti alange anthu,
    kapena kubweretsa chinyontho pa dziko lapansi kuti aonetse chikondi chake.

14 “Abambo Yobu, tamvani izi;
    imani ndipo muganizire ntchito zodabwitsa za Mulungu.
15 Kodi mukudziwa momwe Mulungu amayendetsera mitambo
    ndi kuchititsa kuti kukhale zingʼaningʼani?
16 Kodi mukudziwa momwe Mulungu amayalira mitambo,
    ntchito zodabwitsa za Iye amene ndi wanzeru zangwiro?
17 Inu amene mʼzovala zanu mumatuluka thukuta
    pamene kunja kwatentha chifukwa cha mphepo yakummwera,
18 kodi mungathe kuthandizana naye kutambasula thambo
    limene ndi lolimba ngati chitsulo?

19 “Tiwuzeni ife zoti tikanene kwa Iye;
    sitingathe kufotokoza mlandu wathu chifukwa cha mdima umene uli mwa ife.
20 Kodi nʼkofunika kumudziwitsa Mulungu kuti ndili naye mawu?
    Kodi kutero sikuchita ngati kupempha kuti ndiwonongeke?
21 Tsopano munthu sangathe kuyangʼana dzuwa,
    ndi kunyezimira mlengalenga,
    kuwomba kwa mphepo kutachotsa mitambo yonse.
22 Kuwala kwake kumaonekera cha kumpoto;
    Mulungu amabwera ndi ulemerero woopsa.
23 Wamphamvuzonse sitingathe kumufikira pafupi ndi wa mphamvu zoposa;
    pa chiweruzo chake cholungama ndi mʼchilungamo chake chachikulu Iye sapondereza anthu ozunzika.
24 Nʼchifukwa chake anthu amamuopa kwambiri,
    kodi saganizira za onse amene amaganiza kuti ndi anzeru?”

Machitidwe a Atumwi 15:22-41

Kalata Yopita kwa Anthu a Mitundu ina

22 Pamenepo atumwi ndi akulu ampingo, pamodzi ndi mpingo onse, anagwirizana zosankha anthu ena pakati pawo kuti awatume ku Antiokeya pamodzi ndi Paulo ndi Bamaba. Iwo anasankha Yudasi, wotchedwa Barsaba ndi Sila, anthu awiri amene anali atsogoleri pakati pa abale, 23 kuti akapereke kalata yonena kuti,

Kuchokera kwa atumwi ndi akulu ampingo, abale anu,

Kwa anthu a mitundu ina okhulupirira a ku Antiokeya, Siriya ndi Kilikiya:

Tikupereka moni.

24 Ife tamva kuti anthu ena ochokera pakati pathu, amene sitinawatume anakusokonezani maganizo ndi kukuvutitsani ndi zimene amakuwuzani. 25 Tsono ife tagwirizana kuti, tisankhe anthu ena ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi abale athu okondedwa Paulo ndi Barnaba, 26 anthu amene anapereka moyo wawo chifukwa cha dzina la Ambuye athu Yesu Khristu. 27 Nʼchifukwa chake, tikutumiza Yudasi ndi Sila kuti adzachitire umboni ndi mawu a pakamwa pawo za zimene ife talemba. 28 Pakuti zinakomera Mzimu Woyera ndiponso ife kuti tisakusenzetseni katundu wina, kupatula zoyenera zokhazi: 29 Mupewe kudya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano, musadye magazi, kapena nyama yopha mopotola ndiponso musachite dama. Mudzachita bwino mukapewa zimenezi.

Tsalani bwino.

30 Anthu aja anatumidwa ndipo anafika ku Antiokeya, kumene anasonkhanitsa mpingo pamodzi napereka kalatayo. 31 Anthuwo anawerenga kalatayo ndipo abalewo anakondwa chifukwa cha mawu ake achirimbikitso. 32 Yudasi ndi Sila amene analinso aneneri, ananena zambiri zowalimbikitsa ndi kuwapatsa mphamvu abalewo. 33 Atakhala kumeneko kwa kanthawi, abale aja anatsanzikana nawo mwamtendere kuti abwerere kwa amene anawatuma. 34 Koma Sila anasankha kuti akhale komweko. 35 Koma Paulo ndi Barnaba anatsalira ku Antiokeya kumene iwo pamodzi ndi ena ambiri anaphunzitsa ndi kulalikira Mawu a Ambuye.

Paulo Asiyana ndi Barnaba

36 Patapita masiku ena Paulo anati kwa Barnaba, “Tiyeni tibwerere kuti tikaone abale ku mizinda yonse imene tinalalika Mawu a Ambuye ndipo tikaone mmene akuchitira.” 37 Barnaba anafuna kutenga Yohane, wotchedwanso Marko, kuti apite nawo. 38 Koma Paulo anaganiza kuti sichinali cha nzeru kumutenga Yohane chifukwa iye anawathawa ku Pamfiliya ndipo sanapitirire nawo pa ntchito. 39 Iwo anatsutsana kwambiri kotero kuti anapatukana. Barnaba anatenga Marko ndipo anakwera sitima ya pamadzi kupita ku Kupro. 40 Paulo anasankha Sila. Abale atawapempherera kwa Ambuye kuti alandire chisomo, ananyamuka. 41 Iye anadutsa ku Siriya ndi ku Kilikiya kupita akulimbikitsa mipingo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.