Old/New Testament
Mawu a Elihu
32 Tsono anthu atatuwa analeka kumuyankha Yobu, chifukwa chakuti iyeyo ankadziona kuti ndi wolungama. 2 Koma Elihu, mwana wa Barakeli, wa fuko la Buzi, wa banja la Ramu, anapsera mtima kwambiri Yobu chifukwa choti Yobuyo anakana kuvomera kuti anachimwa ndi kuti Mulungu anakhoza pomulanga. 3 Anapseranso mtima abwenzi ake atatu aja chifukwa sanapeze njira yomutsutsira Yobu, ngakhale iwo anamupeza kuti anali wolakwa. 4 Tsono Elihu anadikira kuti ayankhule ndi Yobu chifukwa choti abwenziwo anali akuluakulu kupambana iyeyo. 5 Koma Elihu ataona kuti anthu atatuwo analibe mawu oti ayankhulenso, iye anapsa mtima.
6 Choncho Elihu mwana wa Barakeli wa fuko la Buzi anati:
“Ine ndine wamngʼono,
inuyo ndinu akuluakulu,
nʼchifukwa chake ndimaopa,
ndimachita mantha kuti ndikuwuzeni zimene ndimadziwa.
7 Ndimaganiza kuti, ‘Ayambe ndi akuluakulu kuyankhula;
anthu amvulazakale ndiwo amaphunzitsa nzeru.’
8 Koma mzimu wa Mulungu mwa munthu,
mpweya wa Wamphamvuzonse, ndi umene umapereka nzeru zomvetsa zinthu.
9 Si okalamba amene ali ndi nzeru,
si amvulazakale okha amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu zimene zili zoyenera.
10 “Nʼchifukwa chake ndikuti, ‘Mvereni;
inenso ndikukuwuzani zimene ndikuzidziwa.’
11 Ndadikira nthawi yonseyi,
ndimamvetsera mwachidwi zimene mumayankhula,
pamene mumafunafuna mawu oti muyankhule,
12 ineyo ndinakumvetseranidi.
Koma palibe ndi mmodzi yemwe wa inu amene anatsutsa Yobu;
palibe aliyense wa inu amene anamuyankha mawu ake.
13 Musanene kuti, ‘Ife tapeza nzeru;
Mulungu ndiye amutsutse, osati munthu.’
14 Koma Yobu sanayankhule motsutsana ndi ine,
ndipo ine sindimuyankha monga mmene inu mwamuyankhira.
15 “Iwo asokonezeka ndipo alibe choti ayankhulenso;
mawu awathera.
16 Kodi ine ndidikire chifukwa iwo sakuyankhula tsopano,
pakuti angoyima phee wopanda yankho?
17 Inenso ndiyankhulapo tsopano;
nanenso ndinena zimene ndikudziwa.
18 Pakuti ndili nawo mawu ambiri,
ndipo mtima wanga ukundikakamiza;
19 mʼkati mwanga ndili ngati botolo lodzaza ndi vinyo,
ngati matumba a vinyo watsopano amene ali pafupi kuphulika.
20 Ndiyenera kuyankhula kuti mtima utsike;
ndiyenera kutsekula pakamwa panga ndi kuyankha.
21 Sindidzakondera munthu wina aliyense,
kapena kuyankhula zoshashalika,
22 pakuti ndikanakhala wa luso loyankhula moshashalika,
Mlengi wanga akanandilanga msanga.”
33 “Koma tsopano, inu abambo Yobu chonde mverani mawu anga;
mutcherere khutu zonse zimene ndinene.
2 Tsopano ndiyamba kuyankhula;
mawu anga ali pa msonga ya lilime langa.
3 Mawu anga akuchokera mu mtima wolungama;
pakamwa panga pakuyankhula zoonadi zimene ndikuzidziwa.
4 Mzimu wa Mulungu wandiwumba,
mpweya wa Wamphamvuzonse umandipatsa moyo.
5 Mundiyankhe ngati mungathe;
konzekani tsopano kuti munditsutse.
6 Ine ndili monga inu pamaso pa Mulungu;
nanenso ndinachokera ku dothi.
7 Musachite mantha ndipo musandiope ayi,
Ine sindikupanikizani kwambiri ayi.
8 “Koma inu mwayankhula ine ndikumva,
ndamva mawu anuwo onena kuti,
9 ‘Ndine wolungama mtima ndi wopanda tchimo;
ndine woyera mtima ndipo ndilibe cholakwa.
10 Komatu Mulungu wapeza zifukwa zoti anditsutsire nazo;
Iye akundiyesa ngati mdani wake.
11 Iyeyo wamanga mapazi anga mʼzigologolo,
akulonda mayendedwe anga onse.’
12 “Koma ine ndi kuti kwa inu, inuyo simukukhoza pa zimenezi,
pakuti Mulungu ndi wamkulu kupambana munthu.
13 Chifukwa chiyani mukudandaula kwa Iye
kuti sayankha mawu ena aliwonse a munthu?
14 Pajatu Mulungu amayankhula mwa njira zosiyanasiyana,
ngakhale munthu sazindikira zimenezi.
15 Mʼmaloto, mʼmasomphenya usiku,
pamene anthu ali mʼtulo tofa nato
pamene akungosinza chabe pa bedi,
16 amawanongʼoneza mʼmakutu
ndi kuwaopseza ndi machenjezo ake,
17 kumuchotsa munthu ku zoyipa,
ndi kuthetseratu kunyada kwake,
18 kumulanditsa munthu ku manda,
kuti moyo wake usawonongeke ndi lupanga.
19 “Mwina Mulungu amalanga munthu ndi matenda ndi ululu ali pa bedi pake,
nthawiyo thupi lake lonse limangophwanya,
20 kuti asakhalenso ndi chilakolako cha chakudya,
ndipo amanyansidwa ndi chakudya chabwino chomwe.
21 Thupi lake limawonda
ndipo mafupa ake, omwe anali obisika, tsopano amaonekera poyera.
22 Munthuyo amayandikira ku manda,
moyo wake umayandikira kwa amene amabweretsa imfa.
23 “Koma patakhala mngelo ngati mthandizi,
mmodzi mwa ambirimbiri oterewa,
adzafotokoza zimene zili zoyenera,
24 kudzamukomera mtima ndi kunena kuti,
‘Mupulumutseni kuti asapite ku manda;
ine ndapeza cholowa mʼmalo mwa moyo wake,’
25 pamenepo thupi lake lidzasanduka lasee ngati la mwana;
ndipo adzabwezeretsedwanso kukhala ngati mʼmasiku a unyamata wake.
26 Akapemphera kwa Mulungu, iyeyo adzalandiridwa.
Mulungu adzamulandira mwa chimwemwe
ndipo adzamubwezeretsa pamalo ake oyamba.
27 Ndipo adzabwera kwa anzake ndi kunena kuti,
‘Ndinachimwa ndipo sindinachite zolungama,
koma sindinalangidwe koyenerana ndi kuchimwa kwanga.
28 Iye anapulumutsa moyo wanga kuti usapite ku manda,
ndipo ndidzakhala ndi moyo ndi kuonanso kuwala kwa dzuwa.’
29 “Mulungu amachita zonsezi kwa munthu
kawirikawiri,
30 kupulumutsa moyo wa munthuyo ku manda,
kuti athe kuonanso kuwala kwa moyo.
31 “Abambo Yobu, tcherani khutu ndipo mundimvere;
khalani chete kuti ndiyankhule.
32 Ngati muli nʼchoti munene, ndiyankheni;
yankhulani, pakuti ine ndikufuna mupezeke wolungama.
33 Koma ngati sichoncho, mundimvere;
khalani chete ndipo ine ndidzakuphunzitsani nzeru.”
Ku Ikoniya
14 Ku Ikoniya, Paulo ndi Barnaba analowanso mʼsunagoge ya Ayuda. Kumeneko iwo anaphunzitsa momveka bwino kotero kuti anthu ambiri Achiyuda ndi anthu a mitundu ina anakhulupirira. 2 Koma Ayuda amene anakana kukhulupirira anawutsa anthu a mitundu ina nawononga maganizo awo kutsutsana ndi abale. 3 Ndipo Paulo ndi Barnaba anakhala kumeneko nthawi yayitali, nalalikira molimba mtima za Ambuye amene anawapatsa mphamvu yochitira zozizwitsa ndi zizindikiro zodabwitsa pochitira umboni mawu a chisomo. 4 Anthu a mu mzindamo anagawikana; ena anali mbali ya Ayuda, ena mbali ya atumwi. 5 Pamenepo anthu a mitundu ina ndi Ayuda, pamodzi ndi atsogoleri awo anakonza chiwembu choti azunze atumwiwo ndi kuwagenda ndi miyala. 6 Koma atazindikira zimenezi, anathawira ku Lusitra ndi Derbe, mizinda ya ku Lukaoniya, ndiponso ku dziko lozungulira mizindayo, 7 kumene anapitiriza kulalikira Uthenga Wabwino.
Ku Lusitra ndi ku Derbe
8 Ku Lusitra kunali munthu wolumala miyendo, amene sanayendepo chibadwire chake. 9 Iyeyu, amamvetsera pamene Paulo amayankhula. Paulo anamuyangʼanitsitsa ndipo anaona kuti anali ndi chikhulupiriro choti achiritsidwe nacho. 10 Ndipo Paulo anamuyitana mofuwula nati, “Imirira!” Atamva zimenezi, munthuyo anayimirira, nayamba kuyenda.
11 Gulu la anthu litaona zimene Paulo anachitazi, linafuwula mʼChilukaoniya kuti, “Milungu yatitsikira yooneka ngati anthu!” 12 Barnaba anamutcha Zeusi ndipo Paulo anamutcha Herimesi chifukwa ndiye amatsogolera kuyankhula. 13 Wansembe wa Zeusi amene nyumba yopembedzera Zeusiyo inali kunja pafupi ndi mzindawo, anabweretsa ngʼombe yayimuna yovekedwa nkhata za maluwa pa chipata cha mzindawo chifukwa iyeyo pamodzi ndi anthu ena onse aja amafuna kudzipereka nsembe kwa Paulo ndi Barnaba.
14 Koma Barnaba ndi Paulo atamva zimenezi, anangʼamba zovala zawo, nathamangira pakati pa gulu la anthuwo, akufuwula kuti, 15 “Anthu inu, bwanji mukuchita zimenezi? Ifenso ndife anthu monga inu nomwe. Ife takubweretserani Uthenga Wabwino, kuti musiye zinthu zachabezi ndi kutsata Mulungu wamoyo, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo. 16 Kale Iye analola anthu a mitundu ina yonse kutsata njira zawozawo. 17 Komabe wakhala akudzichitira yekha umboni: Iye amaonetsa kukoma mtima kwake pogwetsa mvula kuchokera kumwamba ndi zipatso pa nyengo yake. Amakupatsani chakudya chambiri ndipo amadzaza mitima yanu ndi chimwemwe.” 18 Ngakhale ndi mawu awa, anavutika kuletsa gulu la anthu kuti asapereke nsembe kwa iwo.
19 Kenaka kunabwera Ayuda ena kuchokera ku Antiokeya ndi Ikoniya nakopa gulu la anthu lija. Iwo anamugenda miyala Paulo namukokera kunja kwa mzindawo, kuganiza kuti wafa. 20 Koma ophunzira atamuzungulira, Pauloyo anayimirira nalowanso mu mzindawo. Mmawa mwake iye ndi Barnaba anachoka ndi kupita ku Derbe.
Paulo ndi Barnaba Abwerera ku Antiokeya wa ku Siriya
21 Iwo analalikira Uthenga Wabwino mu mzindawo ndipo anthu ambiri anatembenuka mtima ndi kukhala ophunzira. Kenaka anabwerera ku Lusitra, ku Ikoniya ndi ku Antiokeya. 22 Kumeneko analimbikitsa mitima ya ophunzira ndi kuwapatsa mphamvu kuti akhalebe woona mʼchikhulupiriro. Iwo anati, “Ife tiyenera kudutsa mʼmasautso ambiri kuti tikalowe mu ufumu wa Mulungu.” 23 Paulo ndi Barnaba anasankha akulu ampingo pa mpingo uliwonse, ndipo atapemphera ndi kusala kudya anawapereka kwa Ambuye amene anamukhulupirira. 24 Atadutsa Pisidiya, anafika ku Pamfiliya. 25 Atalalikira Mawu ku Perga, anapita ku Ataliya.
26 Ku Ataliyako, anakwera sitima ya pamadzi kubwerera ku Antiokeya kumene anayitanidwa mwachisomo cha Mulungu kuti agwire ntchito imene tsopano anali atayitsiriza. 27 Atangofika ku Antiokeya, anasonkhanitsa pamodzi mpingo ndipo anafotokoza zonse zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo ndiponso mmene Iye anatsekulira a mitundu ina njira ya chikhulupiriro. 28 Ndipo anakhala kumeneko ndi ophunzira nthawi yayitali.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.