Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yobu 30-31

30 “Koma tsopano akundinyoza,
    ana angʼonoangʼono kwa ine,
anthu amene makolo awo sindikanawalola
    kuti azithandizana ndi agalu anga kuweta nkhosa zanga.
Kodi mphamvu zawo ndi za phindu lanji kwa ine,
    pakuti mphamvu zawo zinatha kale?
Anali atatheratu kuwonda ndi njala,
    ankayendayenda mʼdziko lopanda madzi,
    mʼchipululu usiku.
Ankathyola therere ndi masamba owawa,
    ndipo chakudya chawo chinali mizu ya mitengo ya masache.
Anapirikitsidwa pakati pa anthu anzawo,
    akuwakuwiza ngati kuti anali akuba.
Anawumirizidwa kukhala ku zigwembe za mitsinje yowuma,
    pakati pa matanthwe ndi mʼmaenje a mʼnthaka.
Ankalira ngati nyama kuthengo
    ndipo ankawunjikana pamodzi pa ziyangoyango.
Anali anthu achabechabe ndi wopanda dzina,
    anathamangitsidwa mʼdziko.

“Ndipo tsopano ana awo akundiyimba nyimbo zachipongwe;
    ineyo ndasanduka chisudzo chawo.
10 Iwo amanyansidwa nane ndipo amandithawa;
    akandiona salephera kundilavulira mʼmaso mwangamu.
11 Tsopano pakuti Mulungu wakhwefula uta wanga ndipo wandisautsa,
    iwowo analekeratu kundiopa.
12 Ku dzanja langa lamanja anthu akulimbana nane;
    andikumbira dzenje loti ndigweremo ndikamayenda,
    andipangira mitumbira ya nkhondo kuti alimbane nane.
13 Iwo anditsekera njira;
    akufuna kundichititsa ngozi,
    popanda wina aliyense wowaletsa.
14 Akundithamangitsa ngati madzi olowera pa mpanda wobowoka,
    iwo akubwererabwerera pakati pa chipasupasu.
15 Zoopsa zandithetsa mphamvu;
    ulemu wanga wachita ngati wauluzika ndi mphepo,
    chuma changa chija chazimirira ngati mtambo.

16 “Ndipo tsopano mtima wanga wachokamo;
    ndili mʼmasiku amasautso.
17 Mafupa anga akuphwanya usiku pakuti
    zowawa zanga sizikuleka.
18 Mʼmphamvu zake Mulungu wakhala ngati chovala changa;
    Iye wandigwira ngati chovala chondithina pa khosi.
19 Wandiponya mʼmatope,
    ndipo ndasanduka ngati fumbi ndi phulusa.

20 “Inu Mulungu, ine ndikulirira kwa Inu, koma simukundiyankha;
    ndikayimirira, Inu simundiyangʼana nʼkomwe.
21 Inuyo mumandichitira zankhanza;
    mumandizunza ndi dzanja lanu lamphamvu.
22 Mwandinyamulira ku mphepo ndipo mwandiwulutsa ndi mphepoyo;
    mwandiponya mʼmphepo ya mkuntho.
23 Ndikudziwa kuti Inu mudzandifikitsa ku imfa,
    kumalo kumene amoyo onse adzapitako.

24 “Ndithudi palibe munthu amene amalanga munthu wosweka mtima,
    amene akupempha thandizo mʼmasautso ake.
25 Kodi ine sindinalire nawo iwo amene anali pamavuto?
    Kodi mtima wanga sunamvere chisoni anthu osauka?
26 Koma pamene ndinkayembekezera zabwino, zoyipa ndiye zinandigwera;
    pamene ndinkafunafuna kuwala, mdima ndiye unandigwera.
27 Kuwawa kwa mʼkati mwanga sikukuleka;
    ndili mʼmasiku amasautso.
28 Ndikuyenda wothimbirira, komatu osati ndi dzuwa;
    ndimayimirira pa msonkhano ndi kupempha chithandizo molira.
29 Ndasanduka mʼbale wa nkhandwe,
    mnzawo wa akadzidzi.
30 Khungu langa layamba kuda ndipo likufunduka;
    thupi langa likutentha chifukwa cha kuphwanya kwa thupi.
31 Pangwe wanga wasanduka woyimbira maliro,
    ndipo chitoliro changa chikuyimbira anthu olira.

31 “Ndinachita pangano ndi maso anga
    kuti sindidzapenya namwali momusirira.
Kodi Mulungu kumwambako wandisungira zotani?
    Kodi cholowa changa chochokera kwa Wamphamvuzonse kumwambako nʼchotani?
Kodi si chiwonongeko kwa anthu oyipa,
    tsoka kwa iwo amene amachita zolakwa?
Kodi Mulungu saona zochita zanga,
    ndi kudziwa mayendedwe anga?

“Ngati ndachita zinthu mwachiphamaso,
    kapena kufulumira kukachita zachinyengo,
Mulungu andiyeze ndi muyeso wake wolungama
    ndipo Iye adzadziwa kuti ine ndine wosalakwa,
ngati mayendedwe anga asempha njira,
    ngati mtima wanga wakhumbira zimene maso anga aona,
    kapena ngati ndachita choyipa chilichonse.
Pamenepo ena adye zimene ndinadzala,
    ndipo zomera zanga zizulidwe.

“Ngati mtima wanga unakopekapo ndi mkazi,
    ndipo ngati ndinalakalaka mkazi wa mnansi wanga,
10 pamenepo mkazi wanga aphikire mwamuna wina chakudya,
    ndipo amuna ena azigona naye.
11 Pakuti zimenezo zikanakhala zochititsa manyazi,
    tchimo loyenera kulangidwa nalo.
12 Ndi moto umene umayaka mpaka chiwonongeko;
    ukanapsereza zokolola zanga.

13 “Ngati ndinkapondereza mlandu wa akapolo anga aamuna kapena aakazi,
    pamene ankabwera kwa ine ndi milandu yawo,
14 ndidzatani pamene Mulungu adzanditsutsa?
    Nanga ndidzayankha chiyani akadzandifunsa?
15 Kodi amene anapanga ine mʼmimba mwa amayi anga si yemwe anapanganso iwo?
    Kodi si mmodzi yemweyo amene anatipanga tonsefe mʼmimba mwa amayi athu?

16 “Ngati ndinawamana aumphawi zinthu zimene ankazikhumba,
    kapena kuwagwiritsa fuwa lamoto akazi amasiye amene amafuna thandizo kwa ine,
17 ngati chakudya changa ndinadya ndekha,
    wosagawirako mwana wamasiye,
18 chonsechotu kuyambira unyamata wanga ndinamulera monga abambo ake,
    ndipo moyo wanga wonse ndakhala ndikusamalira akazi amasiye,
19 ngati ndinaona wina aliyense akuzunzika ndi usiwa,
    kapena munthu wosauka alibe chofunda,
20 ndipo ngati iyeyo sananditamandepo
    chifukwa chomufunditsa ndi nsalu ya ubweya wankhosa,
21 ngati ndinaopsezapo mwana wamasiye,
    poganiza kuti ndinali ndi mphamvu mʼbwalo la milandu,
22 pamenepo phewa langa lipokonyeke,
    mkono wanga ukonyoke polumikizira pake.
23 Popeza ine ndinaopa kwambiri chiwonongeko chochokera kwa Mulungu,
    ndinachitanso mantha ndi ulemerero wake, sindikanatha kuchita zinthu zimenezi.

24 “Ngati ndinayika mtima wanga pa chuma
    kapena kunena kwa golide wabwino kwambiri kuti, ‘Iwe ndiye chitetezo changa,’
25 ngati ndinakondwera chifukwa choti chuma changa chinali chambiri,
    zinthu zimene manja anga anazipeza,
26 ngati pamene ndinaona dzuwa likuwala,
    kapena mwezi ukuyenda mwa ulemerero wake,
27 ndipo kuti mtima wanga unakopeka nazo
    nʼkuyika dzanja langa pakamwa mozilemekeza,
28 pamenepo zimenezinso zikanakhala machimo oti ndilangidwe nawo,
    chifukwa ndikanakhala wosakhulupirika kwa Mulungu wakumwamba.

29 “Ngati ndinasangalala ndi kuwonongeka kwa mdani wanga,
    kapena kusekera mavuto pamene mavuto anamugwera,
30 ine sindinachimwe ndi pakamwa panga
    potulutsa matemberero a mdani wanga kuti awonongeke,
31 ngati anthu amene ndimakhala nawo mʼnyumba mwanga sananenepo kuti,
    ‘Kodi ndani amene sakhuta ndi chakudya cha Yobu?’
32 Komatu mlendo sindinamusiye pa msewu usiku wonse,
    pakuti khomo langa linali lotsekuka nthawi zonse kwa alendo,
33 ngati ndinabisa tchimo langa monga amachitira anthu ena,
    kubisa kulakwa mu mtima mwanga
34 chifukwa choopa gulu la anthu,
    ndi kuchita mantha ndi mnyozo wa mafuko
    kotero ndinakhala chete ndipo sindinatuluke panja.

35 “Aa, pakanakhala wina wondimva!
    Tsopano ndikutsiriza mawu anga odzitetezera. Wamphamvuzonse andiyankhe;
    mdani wanga achite kulemba pa kalata mawu ake ondineneza.
36 Ndithu ine ndikanakoleka kalatayo pa phewa langa,
    ndikanayivala kumutu ngati chipewa chaufumu.
37 Ndikanamufotokozera zonse zimene ndinachita;
    ndikanafika pamaso pake ngati kalonga.

38 “Ngati minda yanga ikulira monditsutsa ine
    ndipo malo ake onse osalimidwa anyowa ndi misozi,
39 ngati ndinadya za mʼminda mwake osapereka ndalama
    kapena kukhumudwitsa anthu olima mʼmindamo,
40 pamenepo mʼmindamo mumere namsongole mʼmalo mwa tirigu
    ndi udzu mʼmalo mwa barele.”

Mawu a Yobu athera pano.

Machitidwe a Atumwi 13:26-52

26 “Abale, ana a Abrahamu, ndiponso inu a mitundu ina amene mumaopa Mulungu, Iye watumiza uthenga wachipulumutsowo kwa ife. 27 Anthu a ku Yerusalemu ndi atsogoleri awo sanazindikire Yesu, komabe pomuweruza Yesu anakwaniritsa mawu a Aneneri amene amawerengedwa Sabata lililonse. 28 Ngakhale sanapeze chifukwa choti afe, anapempha Pilato kuti amuphe. 29 Atachita zonse zimene zinalembedwa za Iye, iwo anamuchotsa pa mtengo ndipo anamuyika mʼmanda. 30 Koma Mulungu anamuukitsa, 31 ndipo kwa masiku ambiri anaonekera kwa amene anayenda naye kuchokera ku Galileya mpaka ku Yerusalemu. Iwowa tsopano ndi mboni zake kwa anthu a Israeli.

32 “Ife tikukuwuzani Uthenga Wabwino; umene Mulungu analonjeza makolo athu. 33 Iye wakwaniritsa zimenezi kwa ife ana awo, poukitsa Yesu kuchokera kwa akufa. Monga zinalembedwa mu Salimo lachiwiri kuti,

“Iwe ndiwe mwana wanga;
    lero ine ndakhala Atate ako.”

34 Zakuti Mulungu anamuukitsa kuti asawole konse, zinanenedwa mʼmawu awa:

“ ‘Ine, ndidzakupatsa madalitso opatulika ndi odalirika amene ndinalonjeza Davide.’

35 Nʼchifukwa chakenso zinalembedwa mu Salimo lina kuti,

“ ‘Simudzalekerera woyera wanu kuti awole.’

36 “Pakuti pamene Davide anatsiriza kutumikira Mulungu mu mʼbado wake, anamwalira, iye anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake ndipo thupi lake linawola. 37 Koma amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa sanawole ayi.

38 “Nʼchifukwa chake, abale anga, dziwani kuti mwa Yesu chikhululukiro cha machimo chikulalikidwa. 39 Kudzera mwa Iye aliyense amene akhulupirira, alungamitsidwa kuchoka ku tchimo lililonse limene silingachoke ndi Malamulo a Mose. 40 Samalani kuti zimene aneneri akunena zisakuchitikireni inu:

41 “ ‘Onani, inu anthu onyoza,
    dabwani ndipo wonongekani,
chifukwa ine ndidzachita china chake mʼmasiku anu,
    inu simudzazikhulupirira
    ngakhale wina atakufotokozerani!’ ”

42 Pamene Paulo ndi Barnaba amatuluka mʼSunagoge, anthu anawapempha kuti adzapitirize kuyankhula zinthu zimenezi Sabata linalo. 43 Atatha mapemphero, Ayuda ambiri ndi anthu odzipereka otembenukira ku Chiyuda anatsatira Paulo ndi Barnaba, iwo anayankhula ndi anthuwo ndipo anawapempha kuti apitirire mʼchisomo cha Mulungu.

44 Pa Sabata linalo pafupifupi anthu onse a mu mzindawo anasonkhana kudzamva Mawu a Ambuye. 45 Pamene Ayuda anaona gulu la anthu, anachita nsanje ndipo anayankhula zamwano kutsutsana ndi zimene Paulo amanena.

46 Ndipo Paulo ndi Barnaba anawayankha molimba mtima kuti, “Ife tinayenera kuyankhula Mawu a Mulungu kwa inu poyamba. Popeza inu mwawakana ndi kudziyesa nokha osayenera moyo wosatha, ife tsopano tikupita kwa anthu a mitundu ina. 47 Pakuti izi ndi zimene Ambuye anatilamula ife:

“ ‘Ine ndakuyika iwe ukhale kuwunika kwa anthu a mitundu ina,
    kuti ukafikitse chipulumutso ku malekezero a dziko lapansi!’ ”

48 Anthu a mitundu ina atamva izi, anakondwa ndipo analemekeza Mawu Ambuye; ndipo onse amene anawasankha kuti alandire moyo osatha anakhulupirira.

49 Mawu a Ambuye anafalikira mʼchigawo chonse. 50 Koma Ayuda anawutsa mitima ya akazi otchuka opembedza Mulungu ndi akulu a mu mzindamo. Iwo anabweretsa mazunzo kwa Paulo ndi Barnaba ndipo anawathamangitsa mʼchigawo chawo. 51 Tsono iwo anasasa fumbi la ku mapazi awo powatsutsa, ndipo anapita ku Ikoniya. 52 Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chimwemwe ndiponso ndi Mzimu Woyera.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.