Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yobu 28-29

28 Pali mgodi wa siliva
    ndiponso malo oyengerapo golide.
Chitsulo amachikumba pansi,
    ndipo mkuwa amawusungunula ku miyala yamkuwa.
Munthu amalowa mu mdima atatenga nyale,
    amafunafuna miyala mpaka ku malire a mgodiwo,
    kufuna mkuwa mu mdima wandiweyani.
Amakumba njira zapansi mu mgodimo, kutali ndi kumene kumakhala anthu,
    kumalo kumene phazi la munthu silinapondeko;
    iye amakhala ali lende pansipo namazungulira uku ndi uku.
Nthaka, imene imatulutsa zakudya,
    kunsi kwake kumachita ngati kwasandulizika ndi moto;
miyala ya safiro imachokera mʼmatanthwe ake,
    ndipo mʼfumbi lake mumakhala miyala yagolide.
Palibe mbalame yodya zinzake imene imadziwa njira yobisikayi,
    palibe kamtema amene anayiona.
Zirombo zolusa sizipondamo mʼnjiramo,
    ndipo mkango sudzeranso mʼmenemo.
Munthu amaphwanya matanthwe olimba,
    ndipo amagubuduza mapiri kuyambira mʼtsinde.
10 Amabowola njira mʼmatanthwewo;
    ndipo amaona chuma chonse cha mʼphirimo.
11 Amaletsa mitsinje ya pansipo kuti isayendenso,
    motero amatulutsira poyera zinthu zobisika.

12 “Koma nzeru zingapezeke kuti?
    Kodi kumvetsa zinthu kumakhala kuti?
13 Munthu sadziwa kufunika kwake kwa nzeruzo;
    nzeruyo sipezeka pa dziko lino la anthu amoyo.
14 Phompho likuti, ‘Sizipezeka mwa ine muno.’
    Nyanja ikuti, ‘Mwa ine munonso ayi.’
15 Nzeru sungazigule ndi golide wabwino kwambiri,
    mtengo wake sungawuyerekeze ndi siliva wambiri.
16 Nzeru singagulidwe ndi golide wa ku Ofiri,
    kapena ndi miyala ya onikisi kapena ya safiro.
17 Nzeru sungayiyerekeze ndi golide kapena mwala wa galasi,
    sungayigule ndi zokometsera zagolide.
18 Miyala ya korali ndi krisitali siyoyeneranso ndi kuyitchula nʼkomwe;
    mtengo wa nzeru ndi woposa miyala ya rubi.
19 Nzeru sungayiyerekeze ndi miyala ya topazi ya ku Kusi;
    nzeru singagulidwe ndi golide wabwino kwambiri.

20 “Kodi tsono nzeru zimachokera kuti?
    Kodi kumvetsa zinthu kumakhala kuti?
21 Malo ake ndi obisika kwa zamoyo zonse,
    ndi obisika ngakhale kwa mbalame zamlengalenga.
22 Chiwonongeko ndi imfa zikuti,
    ‘Tangomva mphekesera chabe ya zimenezo!’
23 Mulungu yekha ndiye amadziwa njira yake yopita kumeneko,
    ndipo Iye yekha amadziwa kumene nzeru imakhala,
24 pakuti Iye amayangʼana mpaka ku malekezero a dziko lapansi
    ndipo amaona zonse za kunsi kwa thambo.
25 Iye atapatsa mphepo mphamvu zake,
    nayeza kuzama kwa nyanja,
26 atakhazikitsa lamulo loti mvula izigwa
    ndi kukonza njira ya chingʼaningʼani cha bingu,
27 pamenepo ndi pamene anayangʼana nzeruzo naziyeza mtengo wake;
    nazikhazikitsa ndi kuzisanthula bwino lomwe.
28 Ndipo Iye anati kwa munthu,
    ‘Taonani, kuopa Ambuye, ndiye nzeru zimenezo
    ndipo kuthawa zoyipa ndiye kumvetsa zinthu kumeneko.’ ”

29 Yobu anapitiriza kuyankhula kwake:

“Aa! Ndikanakhala momwe ndinalili miyezi yapitayi,
    masiku amene Mulungu ankandiyangʼanira,
pamene nyale yake inkandiwunikira
    ndipo ndi kuwunika kwakeko ine ndinkatha kuyenda mu mdima!
Ndithu, masiku amene ndinali pabwino kwambiri,
    pamene ubwenzi wa Mulungu unkabweretsa madalitso pa nyumba yanga,
nthawi imene Wamphamvuzonse anali nane,
    ndipo ana anga anali atandizungulira mʼmbalimu,
pamene popondapo ine panali patakhathamira mafuta a mkaka,
    ndipo pa thanthwe pamatuluka mitsinje ya mafuta a olivi.

“Pamene ndinkapita pa chipata cha mzinda
    ndi kukhala pa mpando wanga pabwalo,
anyamata amati akandiona ankapatuka
    ndipo anthu akuluakulu ankayimirira;
atsogoleri ankakhala chete
    ndipo ankagwira pakamwa pawo;
10 anthu otchuka ankangoti duu,
    ndipo malilime awo anali atamatirira ku nkhama zawo.
11 Aliyense amene anamva za ine anayankhula zabwino zanga,
    ndipo iwo amene anandiona ankandiyamikira,
12 chifukwa ndinkapulumutsa mʼmphawi wofuna chithandizo,
    ndiponso mwana wamasiye amene analibe aliyense womuthandiza.
13 Munthu amene anali pafupi kufa ankandidalitsa;
    ndinkasangalatsanso mkazi wamasiye.
14 Chilungamo chinali ngati chovala changa;
    chiweruzo cholungama ndiye chinali mkanjo ndi nduwira yanga.
15 Ndinali ngati maso kwa anthu osapenya;
    ndinali ngati mapazi kwa anthu olumala.
16 Ndinali ngati abambo kwa anthu aumphawi;
    ndinkayimira mlendo pa mlandu wake.
17 Ndinkawononga mphamvu za anthu oyipa
    ndi kulanditsa amene anali atagwidwa.

18 “Ndinkaganiza kuti, ‘Ndidzafera mʼnyumba yanga,
    masiku a moyo wanga ali ochuluka ngati mchenga.
19 Mizu yanga idzatambalalira ku madzi,
    ndipo mame adzakhala pa nthambi zanga usiku wonse.
20 Ulemerero wanga udzakhala wosaguga mwa ine,
    ndipo uta wanga udzakhala watsopano nthawi zonse mʼdzanja langa.’

21 “Anthu ankamvetsera zimene ndinkanena mwachidwi,
    ankadikira atakhala chete kuti amve malangizo anga.
22 Ndikayankhula, iwo sankayankhulanso;
    mawu anga ankawagwira mtima.
23 Ankayembekezera ine monga momwe amayembekezera mvula
    ndipo ankalandira mawu anga ngati mvula ya mʼmalimwe.
24 Ndikawasekerera, iwo sankatha kukhulupirira;
    kuwala kwa nkhope yanga chinali chinthu chamtengowapatali kwa iwowo.
25 Ndinkawasankhira njira yawo ndipo ndinkawatsogolera ngati mfumu;
    ndinkakhala ngati mfumu pakati pa gulu lake lankhondo;
    ndinali ngati msangalatsi pakati pa anthu olira.”

Machitidwe a Atumwi 13:1-25

Barnaba ndi Saulo Atumidwa ndi Mpingo

13 Mu mpingo wa ku Antiokeya munali aneneri ndi aphunzitsi awa: Barnaba, Simeoni, Lukia wa ku Kurene, Manayeni (amene analeredwa pamodzi ndi mfumu Herode), ndiponso Saulo. Iwo pamene ankapembedza Ambuye ndi kusala kudya, Mzimu Woyera anati, “Mundipatulire Barnaba ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndinawayitanira.” Ndipo atasala kudya ndi kupemphera anasanjika manja awo pa iwo nawatumiza.

Ku Kupro

Barnaba ndi Saulo motumidwa ndi Mzimu Woyera, anapita ku Selukeya ndipo kuchokera kumeneko anakwera sitima ya pamadzi kupita ku Kupro. Pamene anafika ku Salamisi, analalikira Mawu a Mulungu mʼMasunagoge a Ayuda. Iwo anali ndi Yohane monga wowatumikira.

Iwo anayenda pa chilumba chonse mpaka anafika ku Pafo, kumeneko anapezanako ndi Myuda, wamatsenga amene analinso mneneri wonama dzina lake Barayesu. Iyeyu, amathandiza mkulu wa boma, Sergio Paulo. Mkulu wa bomayu, munthu wanzeru, anayitana Barnaba ndi Saulo chifukwa anafuna kumva Mawu a Mulungu. Koma Elima wamatsengayo, (Elima tanthauzo lake ndi wamatsenga), anatsutsana nawo ndipo anafuna kumuletsa mkulu wa bomayo kuti asakhulupirire. Koma Saulo, amenenso amatchedwa Paulo, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera anamuyangʼanitsitsa Elima ndipo anati, 10 “Iwe ndiwe mwana wa mdierekezi ndiponso mdani wa chilungamo! Ndiwe wodzaza ndi chinyengo cha mtundu uliwonse ndi kuchenjera konse. Kodi sudzaleka kupotoza njira zolungama za Ambuye? 11 Tsopano dzanja la Ambuye likukutsutsa iwe. Udzakhala wosaona ndipo kwa kanthawi sudzatha kuona kuwala kwa dzuwa.”

Nthawi yomweyo khungu ndi mdima zinamugwera ndipo anafunafuna munthu woti amugwire dzanja kuti amutsogolere. 12 Pamene mkulu wa bomayo anaona zimene zinachitika anakhulupirira pakuti anadabwa ndi chiphunzitso cha Ambuye.

Antiokeya wa ku Pisidiya

13 Kuchokera ku Pafo, Paulo ndi anzake anayenda pa sitima ya pamadzi kupita ku Perga wa ku Pamfiliya, kumeneko Yohane anawasiya nabwerera ku Yerusalemu. 14 Kuchokera ku Perga anapita ku Pisidiya wa ku Antiokeya. Pa tsiku la Sabata analowa mʼsunagoge, nakhala pansi. 15 Atawerenga mawu a mʼMalamulo ndi Aneneri, akulu a sunagoge anawatumizira mawu ndi kuti, “Abale ngati muli ndi mawu olimbikitsa nawo anthuwa, nenani.”

16 Atayimirira, Paulo anakweza dzanja lake ndi kuti, “Inu Aisraeli ndiponso inu a mitundu ina amene mumapembedza Mulungu, tandimverani! 17 Mulungu wa Aisraeli anasankha makolo athu ndipo anawapatsa chuma chambiri pamene amakhala ku Igupto. Anawatulutsa mʼdzikomo ndi dzanja lake lamphamvu. 18 Ndipo Iye anapirira khalidwe lawo mʼchipululu kwa zaka makumi anayi. 19 Mulungu anawagonjetsera mitundu isanu ndi iwiri ya ku Kanaani ndipo anapereka dzikolo kwa Israeli kuti likhale lawo. 20 Izi zonse zinatenga zaka 450.

“Zitatha izi, Mulungu anawapatsa oweruza mpaka nthawi ya mneneri Samueli. 21 Kenaka anthu anapempha kuti awapatse mfumu, ndipo anawapatsa Sauli mwana wa Kisi, wa fuko la Benjamini amene analamulira zaka makumi anayi. 22 Mulungu atamuchotsa Sauli, anayika Davide kukhala mfumu yawo. Mulungu anamuchitira umboni kuti, ‘Ndapeza Davide mwana wa Yese munthu wa pamtima panga; iye adzachita zonse zimene ine ndikufuna kuti iye achite.’

23 “Kuchokera mwa zidzukulu za munthu ameneyu, Mulungu anawutsa Yesu kukhala Mpulumutsi wa Aisraeli, monga analonjezera. 24 Yesu asanabwere, Yohane analalikira kwa anthu onse Aisraeli za kutembenuka mtima ndi ubatizo. 25 Pamene Yohane amatsiriza ntchito yake anati: ‘Mukuganiza kuti ine ndine yani? Ine sindine ameneyo ayi, koma Iye akubwera pambuyo panga, amene ine sindine woyenera kumasula zingwe za nsapato zake.’

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.