Old/New Testament
Mawu a Bilidadi
25 Apo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,
2 “Ulamuliro ndi kuopsa ndi za Mulungu,
Iye amakhazikitsa bata mu ufumu wake kumwambako.
3 Kodi magulu ake ankhondo nʼkuwerengeka?
Kodi kuwala kwake sikuwalira ndani?
4 Kodi munthu angakhale bwanji wolungama pamaso pa Mulungu?
Kodi munthu wobadwa mwa mayi angakhale wangwiro?
5 Ngati mwezi sutha kuwala kwenikweni,
ndipo nyenyezi sizitha kuwala pamaso pake,
6 nanji tsono munthu amene ali ngati mphutsi,
mwana wa munthu amene ali ngati nyongolotsi!”
Mawu a Yobu
26 Pamenepo Yobu anayankha kuti,
2 “Wamuthandizadi munthu wopanda mphamvu!
Walimbitsadi dzanja la munthu wofowoka!
3 Wapereka malangizo kwa munthu amene alibe nzeru!
Ndipotu waonetsadi nzeru zochuluka!
4 Kodi wakuthandiza ndani kuti uyankhule mawu awa?
Ndipo ndi mzimu wa yani umene unayankhula pakamwa pako?
5 “Mizimu ya anthu akufa ikunjenjemera pansi pa madzi,
ndi zonse zokhala mʼmadzimo.
6 Dziko la anthu akufa ndi lapululu pamaso pa Mulungu;
chiwonongeko ndi chosaphimbidwa.
7 Mulungu anayala thambo la kumpoto pa phompho;
Iye anakoloweka dziko lapansi mʼmalo mwake pamene panali popanda nʼkanthu komwe.
8 Amasunga madzi ambiri mʼmitambo yake,
koma mitamboyo siphulika chifukwa cha kulemera kwa madziwo.
9 Iye amaphimba mwezi wowala,
amawuphimba ndi mitambo yake.
10 Mulungu anawalembera madzi malire wonga uta,
kukhala malire pakati pa kuwunika ndi mdima.
11 Mizati yochirikiza mitambo yakumwamba imanjenjemera,
ndi kudabwa pa kudzudzula kwake.
12 Ndi mphamvu zake anatontholetsa nyanja;
ndi nzeru zake anakantha chirombo cha mʼmadzi chija chotchedwa Rahabe.
13 Ndi mpweya wake anayeretsa zamumlengalenga,
dzanja lake linapha chinjoka chothawa chija.
14 Zimenezi ndi pangʼono chabe mwa ntchito yake;
tingomva pangʼono za Iye ngati kunongʼona!
Kodi ndani angathe kudziwa kukula kwa mphamvu zake?”
27 Ndipo Yobu anapitiriza kuyankhula kwake:
2 “Ndithu pali Mulungu wamoyo, amene wakana kundiweruza molungama,
Wamphamvuzonse, amene wawawitsa mtima wanga,
3 nthawi zonse pamene ndili ndi moyo,
mpweya wa Mulungu uli mʼmphuno mwanga,
4 pakamwa panga sipadzatuluka mawu oyipa,
lilime langa silidzayankhula zachinyengo.
5 Sindidzavomereza kuti inu mukunena zoona;
mpaka imfa yanga, sindidzataya ungwiro wanga.
6 Ndidzasunga chilungamo changa ndipo sindidzalola kuti chindichokere;
chikumbumtima changa sichidzanditsutsa nthawi yonse ya moyo wanga.
7 “Mdani wanga akhale ngati woyipa,
wondiwukira akhale ngati munthu wosalungama!
8 Nanga chiyembekezo cha munthu wosapembedza nʼchiyani pamene aphedwa,
pamene Mulungu achotsa moyo wake?
9 Kodi Mulungu amamva kulira kwake
pamene zovuta zamugwera?
10 Kodi adzapeza chikondwerero mwa Wamphamvuzonse?
Kodi adzapemphera kwa Mulungu nthawi zonse?
11 “Ndidzakuphunzitsani za mphamvu ya Mulungu ndipo
sindidzabisa njira za Wamphamvuzonse.
12 Inu mwadzionera nokha zonsezi.
Nanga bwanji mukuyankhula zopanda pake?
13 “Pano pali chilango chimene Mulungu amasungira woyipa,
cholowa chimene munthu wankhanza amalandira kuchokera kwa Wamphamvuzonse.
14 Angakhale ana ake achuluke chotani adzaphedwa ndi lupanga ndipo
zidzukulu zake zidzasowa zakudya.
15 Amene adzatsalireko adzafa ndi mliri,
ndipo akazi awo amasiye sadzawalira.
16 Ngakhale aunjike siliva ngati fumbi,
ndi kukundika zovala ngati mchenga,
17 zimene wasungazo wolungama ndiye adzavale,
ndipo anthu osalakwa ndiwo adzagawane siliva wakeyo.
18 Nyumba imene akuyimanga ili ngati mokhala kadziwotche,
ili ngati msasa umene mlonda amamanga.
19 Amapita kokagona ali wolemera koma kutha kwake nʼkomweko;
akatsekula maso ake, chuma chake chonse chapita.
20 Zoopsa zimamukokolola ngati madzi achigumula;
mphepo yamkuntho imamunyamula usiku.
21 Mphepo ya kummawa imamuwulutsa ndipo iye saonekanso ndipo
imamuchotsa pamalo pake.
22 Imakuntha pa iye osamuchitira chisoni,
pamene akuyesa kuthawa mphamvu zake mwaliwiro.
23 Mphepoyo imamuwomba ndithu
ndipo kuchokera pamalo pake imamuopseza.”
Petro Apulumuka Mʼndende
12 Inali nthawi yomweyi imene mfumu Herode anamanga ena a mu mpingo ndi cholinga chakuti awazunze. 2 Iye analamula kuti Yakobo mʼbale wa Yohane, aphedwe ndi lupanga. 3 Ataona kuti zimenezi zinakondweretsa Ayuda, anawonjeza ndi kugwiranso Petro. Izi zinachitika pa nthawi ya Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti. 4 Atamugwira Petro, namutsekera mʼndende, anamupereka kwa magulu anayi a asilikali kuti amuyangʼanire, gulu lililonse linali ndi asilikali anayi. Herode anafuna kumuzenga mlandu pamaso pa anthu onse chikondwerero cha Paska chitapita.
5 Kotero Petro anasungidwa mʼndende, koma mpingo unamupempherera kolimba kwa Mulungu.
6 Usiku woti mmawa mwake Herode amuzenga mlandu, Petro amagona pakati pa asilikali awiri, atamangidwa maunyolo awiri, ndiponso alonda atayima pa khomo. 7 Mwadzidzidzi mngelo wa Ambuye anaonekera ndipo kuwala kunawunika mʼchipindamo. Mngeloyo anamugwedeza Petro mʼnthiti ndi kumudzutsa. Iye anati, “Fulumira, imirira!” Ndipo maunyolo anagwa kuchoka mʼmanja a Petro.
8 Kenaka mngelo anati kwa iye, “Vala zovala ndi nsapato.” Ndipo Petro atachita izi mngeloyo anamuwuzanso kuti, “Funda chovala chako ndipo unditsate.” 9 Petro anatsatira natuluka mʼndende, koma sanazindikire kuti zimene mngeloyo amachita zimachitikadi; iye amaganiza kuti amaona masomphenya. 10 Iwo anadutsa gulu loyamba ndi lachiwiri la asilikali ndipo anafika pa chitseko chachitsulo cholowera mu mzinda. Chitsekocho chinatsekuka chokha ndipo anadutsa. Pamene anayenda kutalika kwa msewu umodzi, mwadzidzidzi mngelo uja anachoka.
11 Pamenepo Petro anazindikira nati, “Tsopano ndikudziwa mosakayika kuti Ambuye anatuma mngelo wake kudzandipulumutsa mʼmanja mwa Herode, ndi ku zoyipa zonse zimene Ayuda amafuna kundichitira.”
12 Atazindikira zimenezi anapita ku nyumba ya Mariya amayi ake a Yohane, wotchedwanso Marko, kumene kunasonkhana anthu ambiri ndipo amapemphera. 13 Petro anagogoda pa chitseko cha panja, ndipo mtsikana wantchito dzina lake Roda anabwera kuti adzatsekule chitseko. 14 Atazindikira mawu a Petro anakondwa kwambiri ndipo anabwerera osatsekula ndipo anafuwula kuti, “Petro ali pa khomopa!”
15 Anthuwo anati kwa iye, “Wopenga iwe!” Atalimbikira kunena kuti zinali zoona, iwo anati, “Ameneyo ndi mngelo wake.”
16 Koma Petro anapitiriza kugogoda ndipo atatsekula chitseko ndi kumuona, anthuwo anadabwa kwambiri. 17 Petro anakweza dzanja ndi kuwawuza kuti akhale chete ndipo anawafotokozera mmene Ambuye anamutulutsira mʼndende. Iye anati, “Uzani Yakobo ndi abale ena za zimenezi.” Kenaka anachoka napita kumalo ena.
18 Pamene kunacha kunali phokoso lalikulu pakati pa asilikali, iwo anafunsa kuti, “Kodi chamuchitikira Petro ndi chiyani?” 19 Herode atamufunafuna ndipo wosamupeza, anawafunsa asilikali ndipo analamulira kuti asilikaliwo aphedwe.
Imfa ya Herode
Kenaka Herode anachoka ku Yudeya ndi kupita ku Kaisareya ndipo anakhala kumeneko kwa kanthawi 20 Herode anakwiyira anthu a ku Turo ndi Sidoni; anthuwo anagwirizana zoti akambirane naye. Atapeza thandizo kuchokera kwa Blasito, wantchito wokhulupirika wa mfumu, anapempha kuti pakhale mtendere, chifukwa dziko lawo limadalira dziko la mfumuyo pa chakudya chawo.
21 Pa tsiku limene anasankha Herode, atavala zovala zake zaufumu, anakhala pa mpando wake ndipo anayankhula kwa anthuwo. 22 Anthuwo anafuwula nati, “Amenewa ndi mawu a mulungu osati a munthu ayi.” 23 Nthawi yomweyo mngelo wa Mulungu anamukantha chifukwa sanapereke ulemu kwa Mulungu ndipo anadyedwa ndi mphutsi nafa.
24 Koma Mawu a Mulungu anapitirirabe kufalikirafalikira.
25 Barnaba ndi Saulo atamaliza ntchito yawo anachoka ku Yerusalemu, atatenga Yohane wotchedwanso Marko.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.