Old/New Testament
Mawu a Elifazi
22 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,
2 “Kodi munthu nʼkukhala waphindu kwa Mulungu?
Kodi munthu wanzeru angamupindulire Iye?
3 Kodi Wamphamvuzonse akanapeza chabwino chotani iweyo ukanakhala wolungama?
Kodi iyeyo akanapeza phindu lanji makhalidwe ako akanakhala angwiro?
4 “Kodi nʼchifukwa choti umamuopa, kuti azikudzudzula,
kuti azifuna kukukokera ku mlandu?
5 Kodi osati nʼchifukwa chakuti kuyipa kwako nʼkwakukulu?
Kodi machimo ako si opanda malire?
6 Iwe unkawumiriza abale ako kuti akupatse chikole popanda chifukwa;
umalanda anthu zovala zawo ndi kuwasiya amaliseche.
7 Sunawapatse madzi anthu otopa,
ndipo unawamana chakudya anthu anjala,
8 ngakhale unali munthu wamphamvu, wokhala ndi malo akeake,
munthu waulemu wake, wokhala mʼdzikomo.
9 Ndipo akazi amasiye unawachotsa wopanda kanthu,
ndipo unapondereza ana amasiye.
10 Nʼchifukwa chake misampha yakuzungulira,
nʼchifukwa chake tsoka ladzidzidzi lakuchititsa mantha,
11 nʼchifukwa chake kuli mdima kuti sungathe kuona kanthu,
nʼchifukwa chakenso madzi achigumula akumiza.
12 “Kodi Mulungu sali kutalitali kumwamba?
Ndipo ona nyenyezi zili mmwamba kwambirizo, ona kutalika kwake pamene zililipo!
13 Komabe iweyo ukunena kuti, ‘Kodi Mulungu amadziwa chiyani?
Kodi Iye amaweruza mu mdima woterewu?
14 Mitambo yakuda yamuphimba, kotero kuti Iye sakutiona
pamene akuyendayenda pamwamba pa thambopo.’
15 Kodi iwe udzayendabe mʼnjira yakale
imene anthu oyipa ankayendamo?
16 Iwo anachotsedwa nthawi yawo isanakwane,
maziko awo anakokoloka ndi madzi achigumula.
17 Anthuwo anati kwa Mulungu, ‘Tichokereni!
Kodi Wamphamvuzonse angatichitire chiyani?’
18 Chonsecho ndi Iye amene anadzaza nyumba zawo ndi zinthu zabwino,
choncho ine sindigwirizana ndi uphungu wa anthu oyipa.
19 “Anthu olungama amaona kuwonongeka kwawo ndipo amakondwera;
anthu osalakwa amangoseka, akamuona woyipa akulangidwa.
20 Amanena kuti, ‘Ndithudi adani athu awonongeka
ndipo moto wawononga chuma chawo!’
21 “Gonjera Mulungu kuti ukhale naye pamtendere;
ukatero udzaona zabwino.
22 Landira malangizo a pakamwa pake
ndipo usunge mawu ake mu mtima mwako.
23 Ukabwerera kwa Wamphamvuzonse udzabwezeretsedwa;
ukachotsa zoyipa zonse zimene zimachitika mʼnyumba mwako,
24 ndipo chuma chamtengowapatali nuchiona ngati fumbi,
golide wa ku Ofiri numutaya ku miyala ya ku zigwa.
25 Pamenepo Wamphamvuzonseyo adzakhala golide wako,
siliva wako wamtengowapatali.
26 Pamenepo udzakondwera naye Wamphamvuzonse
ndipo udzakweza nkhope yako kwa Mulungu.
27 Udzamupempha ndipo adzakumvera,
ndipo udzapereka zimene unalonjeza.
28 Chimene watsimikiza kuti uchite, chidzachitikadi,
kuwala kudzakuwunikira pa njira yako.
29 Pamene anthu agwetsedwa pansi, iwe nʼkunena kuti, ‘Akwezeni!’
Pamenepo Iye adzapulumutsa anthu oponderezedwa.
30 Iye adzapulumutsa ngakhale munthu amene ndi wolakwa,
ameneyo adzapulumutsidwa kudzera mʼkulungama kwako.”
Yobu
23 Pamenepo Yobu anayankha kuti,
2 “Leronso kudandaula kwanga nʼkwakukulu kwambiri;
Iye akundilanga kwambiri ngakhale ndi kubuwula.
3 Ndikanangodziwa kumene ndikanamupeza Mulungu;
ndikanangopita kumene amakhalako!
4 Ndikanafotokoza mlandu wanga pamaso pake
ndipo ndikanayankhula mawu odziteteza.
5 Ndikanadziwa mawu amene Iye akanandiyankha,
ndi kulingalira bwino zimene akananena!
6 Kodi Iye akanalimbana nane mwa mphamvu zake zazikulu?
Ayi, Iye sakanayankhula zinthu zotsutsana nane.
7 Kumeneko munthu wolungama akanafotokoza mlandu wake pamaso pake,
ndipo woweruzayo akanandipeza wosalakwa nthawi zonse.
8 “Taonani, ndikapita kummawa, Iye kulibe kumeneko,
ndikapita kumadzulo sinditha kumupeza kumeneko.
9 Akamagwira ntchito kumpoto, sindimuona kumeneko
akapita kummwera, sindimuona.
10 Koma Iye amadziwa mmene ndimayendera;
Iyeyo akandiyesa adzandipeza kuti ndili ngati golide.
11 Mapazi anga akhala akuponda mʼmapazi ake;
ndasunga njira yake ndipo sindinayitaye.
12 Sindinapatuke kusiya malamulo ochokera pakamwa pake;
ndasunga mawu a pakamwa pake kupambana chakudya changa cha tsiku ndi tsiku.
13 “Koma Iyeyo ndi wosasinthika, ndipo ndani angatsutsane naye?
Iye amachita chilichonse chimene wafuna.
14 Iye amachita chimene watsimikiza kuti chindichitikire,
ndipo malingaliro oterowa ali nawobe.
15 Nʼchifukwa chake ndikuchita mantha kwambiri pamaso pake;
ndikamaganiza zonsezi ndimamuopa.
16 Mulungu walefula mtima wanga;
Wamphamvuzonse wandiopseza kwambiri.
17 Komatu sindinachititsidwe mantha ndi mdima,
ndi mdima wandiweyani umene waphimba nkhope yanga.
24 “Chifukwa chiyani Wamphamvuzonse sayikiratu nthawi yoti aweruze?
Chifukwa chiyani iwo amene amadziwa Iyeyo amayembekezera pachabe masiku oterewa?
2 Anthu amasuntha miyala ya mʼmalire, kuti akuze dziko lawo;
amadyetsa ziweto zimene aba.
3 Amalanda abulu a ana amasiye
ndipo amatenganso ngʼombe ya mkazi wamasiye ngati chikole.
4 Amachotsa mʼmisewu anthu osauka,
ndipo amathamangitsa amphawi onse mʼdziko.
5 Amphawiwo amakhala ngati mbidzi mʼchipululu,
amayendayenda kufuna chakudya;
dziko lowuma limapereka chakudya cha ana awo.
6 Iwo amakolola za mʼminda ya eni ake,
ndipo amakunkha mphesa mʼminda ya anthu oyipa.
7 Amagona maliseche usiku wonse kusowa zovala;
pa nthawi yozizira amasowa chofunda.
8 Amavumbwa ndi mvula ya mʼmapiri
ndipo amakangamira ku matanthwe kusowa pobisalapo.
9 Amatsomphola mwana wamasiye wa ku bere;
ndipo amagwira mwana wakhanda wa mʼmphawi kuti akhale chikole.
10 Amphawi amangoyenda maliseche kusowa zovala;
amasenza mitolo ya tirigu, koma nʼkumagonabe ndi njala.
11 Iwo amayenga mafuta a olivi mʼminda ya anthu oyipa;
amapsinya mphesa, koma nʼkumamvabe ludzu.
12 Kubuwula kwa anthu amene akufa kumamveka kuchokera mu mzinda,
anthu ovulala akulirira chithandizo.
Koma Mulungu sakuyimba mlandu wina aliyense.
13 “Pali ena amene amakana kuwala,
amene safuna kuyenda mʼkuwalako
kapena kukhala mʼnjira zake.
14 Dzuwa likalowa, wopha anzake amadzuka
ndipo amakapha osauka ndi amphawi;
nthawi ya usiku iye amasanduka mbala.
15 Munthu wachigololo amadikira chisisira;
iyeyo amaganiza kuti, ‘Palibe amene akundiona,’
ndipo amaphimba nkhope yake.
16 Mbala zimathyola nyumba usiku,
koma masana zimadzitsekera;
izo zimathawa kuwala.
17 Pakuti kwa onsewa mdima wandiweyani ndiye kuti kwawachera.
Iwo amachita ubale ndi zoopsa za mdima.
18 “Komatu iwowo ndi thovu loyandama pa madzi;
minda yawo ndi yotembereredwa pa dzikolo
kotero kuti palibe amene amapita ku minda ya mpesa.
19 Monga momwe kutentha ndi chilala zimasungunulira madzi owundana
ndi momwemonso mmene manda amachotsera omwe achimwa.
20 Mayi wowabereka amawayiwala,
mphutsi zimasangalala powadya;
anthu oyipa sakumbukiridwanso
koma amathyoka ngati mtengo.
21 Amachitira nkhanza mayi wosabala ndi mayi amene alibe mwana,
ndipo sakomera mtima mkazi wamasiye.
22 Koma Mulungu amawononga munthu wamphamvu mwa mphamvu zake;
ngakhale munthuyo atakhazikika, alibe chiyembekezo cha moyo wake.
23 Mulungu atha kuwalola kuti akhale mosatekeseka,
koma amakhala akupenyetsetsa njira zawo.
24 Kwa kanthawi kochepa oyipa amakwezedwa ndipo kenaka saonekanso;
amatsitsidwa ndipo amachotsedwa monga ena onse;
amadulidwa ngati ngala za tirigu.
25 “Ngati zimenezi sizoona, ndani angaonetse kuti ndine wabodza
ndi kusandutsa mawu anga kukhala wopanda pake?”
Petro Afotokozera Mpingo
11 Atumwi ndi abale a ku Yudeya konse anamva kuti anthu a mitundu ina analandiranso Mawu a Mulungu. 2 Tsono Petro atafika ku Yerusalemu, abale amene anali a mdulidwe anamutsutsa iye, 3 ndipo anati, “Iwe unalowa mʼnyumba ya anthu osachita mdulidwe ndi kudya nawo.”
4 Koma Petro anayamba kuwafotokozera zonse mwatsatanetsatane momwe zinachitikira kuti, 5 “Ine ndimapemphera mu mzinda wa Yopa ndipo ndili ngati wokomoka ndinaona masomphenya. Ndinaona chinthu chokhala ngati chinsalu chachikulu chikutsika kuchokera kumwamba chogwiridwa msonga zake zinayi, ndipo chinatsikira pa ine. 6 Ine ndinayangʼana mʼkati mwake ndipo ndinaona nyama za miyendo inayi za mʼdziko lapansi, zirombo, zokwawa, ndi mbalame zamlengalenga. 7 Kenaka ine ndinamva mawu akuti, ‘Petro, Imirira. Ipha, nudye.’
8 “Ine ndinayankha kuti, ‘Ayi, Ambuye! Pakuti chinthu chodetsedwa ndi chonyansa sindinadyepo pakamwa pangapa.’
9 “Mawu ochokera kumwamba ananenanso kachiwiri kuti, ‘Chimene Mulungu wachiyeretsa usanene kuti ndi chodetsedwa.’ 10 Zimenezi zinachitika katatu ndipo kenaka zonse zinatengedwa kupita kumwamba.
11 “Nthawi yomweyo anthu atatu amene anatumidwa kuchokera ku Kaisareya anayima pa nyumba yomwe ndimakhalayo. 12 Mzimu anandiwuza kuti ndisakayike, koma ndipite nawo. Abale asanu ndi mmodzi awa anapitanso nane ndipo tinalowa mʼnyumba ya munthuyo. 13 Iye anatiwuza mmene anaonera mngelo atayimirira mʼnyumba mwake ndi kumuwuza kuti, ‘Tumiza anthu ku Yopa kuti akayitane Simoni wotchedwa Petro. 14 Iye adzakuwuza uthenga umene udzapulumutsa iwe ndi a pa banja ako.’
15 “Nditangoyamba kuyankhula, Mzimu Woyera anafika pa iwo monga momwe anafikira pa ife poyamba paja. 16 Kenaka ndinakumbukira zimene Ambuye ananena kuti, ‘Yohane anabatiza ndi madzi, koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.’ 17 Tsono ngati Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyo imene anatipatsa ife, amene tinakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, ndine yani kuti nditsutsane ndi Mulungu?”
18 Iwo atamva zimenezi analibenso chonena ndipo anayamika Mulungu nati, “Potero Mulungu wapatsa anthu a mitundu ina mwayi wotembenuka mtima ndi kulandira moyo.”
Mpingo wa ku Antiokeya
19 Tsopano amene anabalalika chifukwa cha mazunzo amene anayamba ataphedwa Stefano, anapita mpaka ku Foinike, ku Kupro ndi ku Antiokeya, ndipo ankalalikira kwa Ayuda okha. 20 Komabe, ena pakati pawo ochokera ku Kupro ndi ku Kurene anapita ku Antiokeya ndipo iwo anayamba kuyankhulanso kwa Agriki, nawawuza za Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu. 21 Mphamvu ya Ambuye inali nawo ndipo anthu ambiri anakhulupirira natembenukira kwa Ambuye.
22 Mbiri imeneyi inamveka ku mpingo wa ku Yerusalemu ndipo iwo anatumiza Barnaba ku Antiokeya. 23 Atafika ndi kuona chisomo cha Mulungu pa iwo, anakondwa ndi kuwalimbikitsa anthu onsewo kuti apitirire kukhala woona mu mtima mwa Ambuye. 24 Barnabayo anali munthu wabwino, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro ndipo gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Ambuye.
25 Kenaka Barnaba anapita ku Tarisisi kukafuna Saulo, 26 ndipo pamene anamupeza anabwera naye ku Antiokeya. Barnaba ndi Saulo anasonkhana ndi mpingo kwa chaka chimodzi naphunzitsa anthu ambirimbiri. Okhulupirirawo anayamba kutchedwa Akhristu ku Antiokeya.
27 Masiku amenewo ku Antiokeya kunafika aneneri ena ochokera ku Yerusalemu. 28 Mmodzi wa iwo dzina lake Agabu, anayimirira ndipo Mzimu anamutsogolera kunenera zamʼtsogolo kuti padzakhala njala yayikulu pa dziko lonse lapansi. (Izi zinachitikadi nthawi ya ulamuliro wa Klaudiyo). 29 Ophunzirawo, aliyense monga mwakupata kwake, anatsimikiza kuthandiza abale okhala ku Yudeya. 30 Izi anazichitadi ndipo anatuma Barnaba ndi Saulo kukapereka mphatsozo kwa akulu a mpingo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.