Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yobu 20-21

Mawu a Zofari

20 Pamenepo Zofari wa ku Naama anayankha kuti

“Kuvutika kwa mʼmaganizo kwanga kwandifulumiza kuti ndiyankhe
    chifukwa ndasautsidwa kwambiri.
Ndikumva kudzudzula kondinyoza,
    ndipo kumvetsetsa kwanga kwa zinthu kwandifulumiza kuti ndiyankhe.

“Ndithudi iwe ukudziwa momwe zinthu zakhala zikuchitikira kuyambira kale,
    kuchoka nthawi imene munthu analengedwa pa dziko lapansi,
kuti chisangalalo cha woyipa nʼchosachedwa kutha,
    chimwemwe cha wosapembedza Mulungu nʼchakanthawi kochepa.
Ngakhale atamayenda mapewa ake ali mmwamba
    ndipo mutu wake uli nengʼaa,
iye adzatheratu monga momwe imatayikira ndowe yake yomwe;
    iwo amene ankamuona adzati, ‘Kodi uje uja ali kuti?’
Adzazimirira ngati maloto ndipo sadzapezekanso,
    adzachotsedwa ngati masomphenya a usiku.
Diso limene linamuona silidzamuonanso;
    sadzapezekanso pamalo pake.
10 Ana ake adzabwezera zonse
    zimene iyeyo analanda anthu osauka;
11 Mphamvu zaunyamata zimene zili mʼthupi mwake
    zidzagona naye limodzi mʼfumbi.

12 “Ngakhale zoyipa zili zozuna mʼkamwa mwake
    ndipo amazibisa kunsi kwa lilime lake,
13 ngakhale salola kuzilavula,
    ndipo amazisunga mʼkamwa mwake,
14 koma chakudya chake chidzawawasa mʼmimba mwake;
    chidzasanduka ngati ndulu ya njoka mʼkati mwa iyeyo.
15 Adzachisanza chuma chimene anachimeza;
    Mulungu adzachitulutsa mʼmimba mwa munthuyo.
16 Iye adzayamwa ndulu ya njoka ndipo
    ululu wa mphiri udzamupha.
17 Sadzasangalala ndi timitsinje,
    mitsinje yoyenda uchi ndi mafuta.
18 Ayenera kubweza zimene anazigwirira ntchito osazidya;
    sadzasangalala ndi phindu la malonda ake.
19 Pakuti iye anapondereza anthu osauka ndipo anawasiya wopanda thandizo;
    iyeyo analanda nyumba zimene sanamange.

20 “Chifukwa choti umbombo wake sutha,
    sadzatha kusunga chilichonse chimene amakondwera nacho.
21 Palibe chatsala kuti iye adye;
    chuma chake sichidzachedwa kutha.
22 Ngakhale ndi munthu wachuma, mavuto adzamugwera;
    mavuto aakulu adzamugwera.
23 Akadya nʼkukhuta,
    Mulungu adzamugwetsera ukali wamoto
    ngati mvula yosalekeza.
24 Ngakhale athawe mkondo wachitsulo,
    muvi wamkuwa wosongoka udzamulasa.
25 Muviwo adzawutulutsira ku msana,
    songa yake yowala kuchoka mʼmphafa mwake.
Adzagwidwa ndi mantha aakulu;
26     mdima wandiweyani ukudikira chuma chake.
Moto wopanda wowukoleza udzamupsereza
    ndi kuwononga zonse zotsala mʼnyumba yake.
27 Zamumlengalenga zidzawulula kulakwa kwake;
    dziko lapansi lidzamuwukira.
28 Chigumula cha madzi chidzawononga nyumba yake,
    katundu wake adzatengedwa pa tsiku la ukali wa Mulungu.
29 Izi ndi zimene Mulungu amasungira anthu oyipa,
    mphotho imene Mulungu amayikira iwowo.”

Mawu a Yobu

21 Pamenepo Yobu anayankha kuti,

“Mvetserani bwino mawu anga;
    ichi chikhale chitonthozo changa chochokera kwa inu.
Ndiloleni ndiyankhule
    ndipo ndikatha kuyankhula munditonzetonze.

“Kodi ine ndikudandaulira munthu?
    Tsono ndilekerenji kupsa mtima?
Ndipenyeni ndipo mudabwe;
    mugwire dzanja pakamwa.
Ndikamaganiza zimenezi ndimachita mantha kwambiri;
    thupi langa limanjenjemera.
Chifukwa chiyani anthu oyipa amakhalabe ndi moyo,
    amakalamba ndi kusanduka amphamvu?
Amaona ana awo akukhazikika pamodzi nawo,
    zidzukulu zawo zikukula bwino iwo akuona.
Mabanja awo amakhala pa mtendere ndipo sakhala ndi mantha;
    mkwapulo wa Mulungu suwakhudza nʼkomwe.
10 Ngʼombe zawo zazimuna sizilephera kubereketsa;
    ngʼombe zawo zazikazi sizipoloza.
11 Amatulutsa ana awo ngati gulu la nkhosa;
    makanda awo amavinavina pabwalo.
12 Amayimba nyimbo pogwiritsa ntchito matambolini ndi azeze;
    amakondwa pakumva kulira kwa chitoliro.
13 Zaka zawo zimatha ali mu ulemerero
    ndipo amatsikira ku manda mwamtendere.
14 Koma anthuwo amawuza Mulungu kuti, ‘Tichokereni!’
    Ife tilibe chikhumbokhumbo chofuna kudziwa njira zanu.
15 Kodi Wamphamvuzonseyo ndani kuti timutumikire?
    Ife tipindula chiyani tikamapemphera kwa Iyeyo?
16 Komatu ulemerero wawo suli mʼmanja mwawo,
    koma ine ndimakhala patali ndi uphungu wa anthu oyipa.

17 “Koma nʼkangati kamene nyale ya anthu oyipa imazimitsidwa?
    Nʼkangati kamene tsoka limawagwera?
    Nʼkangati kamene Mulungu amawakwiyira ndi kuwalanga?
18 Nʼkangati kamene iwo amakhala ngati phesi lowuluka ndi mphepo,
    ngati mungu wowuluzika ndi kamvuluvulu?
19 Paja amati, ‘Mulungu amalanga ana chifukwa cha machimo abambo awo.’
    Koma Mulungu amabwezera chilango munthuyo, kuti adziwe kuti Mulungu amalangadi.
20 Mulole kuti adzionere yekha chilango chake,
    kuti alawe ukali wa Wamphamvuzonse.
21 Nanga kodi amalabadira chiyani zabanja lake limene walisiya mʼmbuyo,
    pamene chiwerengero cha masiku ake chatha?

22 “Kodi alipo wina amene angaphunzitse Mulungu nzeru,
    poti Iye amaweruza ngakhale anthu apamwamba?
23 Munthu wina amamwalira ali ndi mphamvu zonse,
    ali pa mtendere ndi pa mpumulo,
24 thupi lake lili lonenepa,
    mafupa ake ali odzaza ndi mafuta.
25 Munthu wina amamwalira ali wowawidwa mtima,
    wosalawapo chinthu chabwino chilichonse.
26 Olemera ndi osauka omwe amamwalira ndi kuyikidwa mʼmanda
    ndipo onse amatuluka mphutsi.

27 “Ndikudziwa bwino zimene mukuganiza,
    ziwembu zanu zomwe mukuti mundichitire.
28 Inu mukuti, ‘Kodi nyumba ya mkulu uja ili kuti,
    matenti amene munkakhala anthu oyipa aja ali kuti?’
29 Kodi munawafunsapo anthu amene ali pa ulendo?
    Kodi munaganizirapo zimene iwo amanena?
30 Zakuti munthu woyipa amasungidwa chifukwa cha tsiku la tsoka,
    kuti amapulumutsidwa chifukwa cha tsiku la ukali wa Mulungu?
31 Kodi ndani amadzudzula munthu wochimwayo?
    Ndani amamubwezera zoyipa zimene anachita?
32 Iye amanyamulidwa kupita ku manda
    ndipo anthu amachezera pa manda ake.
33 Dothi la ku chigwa limamukomera;
    anthu onse amatsatira mtembo wake,
    ndipo anthu osawerengeka amakhala patsogolo pa chitanda chakecho.

34 “Nanga inu mudzanditonthoza bwanji ine ndi mawu anu opandapakewo
    palibe chimene chatsala kuti muyankhe koma mabodza basi!”

Machitidwe a Atumwi 10:24-48

Petro ku Nyumba ya Korneliyo

24 Tsiku linalo Petro anafika ku Kaisareya. Korneliyo anawadikirira ndipo anali atawasonkhanitsa pamodzi abale ake ndi abwenzi ake a pamtima. 25 Petro akulowa mʼnyumba, Korneliyo anakumana naye ndipo anadzigwetsa pa mapazi ake namulambira. 26 Koma Petro anamuyimiritsa nati, “Imirira, inenso ndine munthu ngati iwe.”

27 Akuyankhula naye, Petro analowa mʼnyumba ndipo anapeza gulu lalikulu la anthu litasonkhana. 28 Iye anawawuza kuti, “Inu mukudziwa bwino kuti ndi kutsutsana ndi lamulo ngati Myuda ayanjana ndi Mkunja kapena kuyendera wina aliyense wa mtundu wina. Koma Mulungu wandionetsa ine kuti ndisatchule munthu aliyense kuti ndi wosayenera kapena wonyansa. 29 Nʼchifukwa chake ndabwera mosawiringula pamene munandiyitana. Tsopano ndikufunseni,” Mwandiyitanira chiyani?

30 Komeliyo anayankha kuti, “Masiku anayi apitawo, nthawi yonga yomwe ino, 3 koloko masana ndimapemphera mʼnyumba mwanga. Mwadzidzidzi patsogolo panga panayimirira munthu wovala zovala zonyezimira. 31 Ndipo anati, ‘Korneliyo, Mulungu wamva mapemphero ako ndipo wakumbukira mphatso zako kwa osauka. 32 Tuma anthu ku Yopa akayitane Simoni wotchedwa Petro. Iye akukhala mʼnyumba ya Simoni mmisiri wazikopa amene amakhala mʼmbali mwa nyanja.’ 33 Nʼchifukwa chake ndinatumiza anthu nthawi yomweyo ndipo mwachita bwino kuti mwabwera. Tsopano ife tonse tili pano pamaso pa Mulungu kuti timve zonse zimene Ambuye akukulamulani kuti mutiwuze ife.”

34 Ndipo Petro anayamba kuyankhula nati, “Zoonadi, tsopano ndazindikira kuti Mulungu sakondera. 35 Koma amalandira anthu a mtundu uli wonse amene amaopa Iye ndiponso kuchita chilungamo. 36 Uwu ndi uthenga umene Mulungu anatumiza kwa Aisraeli, kulalikira Uthenga Wabwino wamtendere mwa Yesu Khristu amene ndi Ambuye wa onse. 37 Inu mukudziwa zimene zinachitika ku Yudeya konse, kuyambira ku Galileya pambuyo pa ubatizo umene Yohane analalikira, 38 kuti Mulungu, anamudzoza Yesu, wa ku Nazareti ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu ndiponso mmene Iye anapita nachita zabwino ndi kuchiritsa onse amene anali pansi pa mphamvu ya mdierekezi, popeza kuti Mulungu anali naye.

39 “Ife ndife mboni za zonse zimene anachita mʼdziko la Ayuda ndiponso ku Yerusalemu. Anamupha Iye pakumupachika pa mtengo, 40 koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa pa tsiku lachitatu, ndipo analola kuti aonekere poyera. 41 Iye sanaonekere kwa anthu onse koma kwa mboni zimene Mulungu anazisankhiratu, kwa ife amene timadya ndi kumwa naye atauka kwa akufa. 42 Iye anatilamulira ife kuti tilalikire kwa anthu ndi kuchitira umboni kuti Iye ndiye amene Mulungu anamusankha kukhala woweruza wa amoyo ndi akufa. 43 Aneneri onse achitira Iye umboni kuti aliyense amene akhulupirira Iye amakhululukidwa machimo chifukwa cha dzina lake.”

44 Petro akuyankhulabe mawu amenewa, Mzimu Woyera unatsikira pa onse amene amamva uthengawo. 45 Abale a mdulidwe omwe anabwera ndi Petro anadabwa kuona kuti mphatso ya Mzimu Woyera yapatsidwanso kwa anthu a mitundu ina. 46 Pakuti anamva iwo akuyankhula mʼmalilime ndi kuyamika Mulungu. Ndipo Petro anati, 47 “Kodi alipo amene angawaletse anthu awa kubatizidwa mʼmadzi? Iwotu alandira Mzimu Woyera monga ifenso.” 48 Tsono iye analamula kuti abatizidwe mʼdzina la Yesu Khristu. Ndipo anthu aja anamupempha Petro kuti akhale nawo masiku angapo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.