Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yobu 3-4

Mawu a Yobu

Pambuyo pake Yobu anatsekula pakamwa pake nayamba kutemberera tsiku limene iyeyo anabadwa. Ndipo Yobu anati:

“Tsiku limene ine ndinabadwa litembereredwe
    ndi usiku umene ananena kuti, ‘Mwana wamwamuna wabadwa!’
Tsiku limenelo lisanduke mdima;
    Mulungu wa kumwambako asalilabadirenso;
    kuwala kusaonekenso pa tsikulo.
Mdima ndi mthunzi wa imfa zikhale pa tsiku limeneli;
    mtambo uphimbe tsikuli;
    mdima wandiweyani udetse kuwala kwake.
Usiku umenewo ukutidwe ndi mdima wandiweyani;
    usawerengedwenso pamodzi ndi masiku a chaka,
    kapena kukhala pa mwezi wina uliwonse.
Usiku umenewo usabweretse chilichonse chabwino;
    kusamvekenso nthungululu za chikondwerero.
Odziwa kutemberera masiku alitemberere tsikulo,
    iwo amene akonzekera kuwutsa Leviyatani.
Nyenyezi zake za mʼbandakucha zikhale mdima;
    tsikulo liyembekezere kucha pachabe
    ndipo lisaonenso kuwala koyamba kwa mʼbandakucha.
10 Pakuti tsiku limenelo ndiye ndinatuluka mʼmimba ya amayi anga
    ndipo ndi limene linandionetsa zovuta.

11 “Bwanji ine sindinawonongeke pamene ndinkabadwa
    ndi kufa pamene ndimatuluka mʼmimba?
12 Chifukwa chiyani panali mawondo wondilandirirapo
    ndi mawere woti andiyamwitsepo?
13 Pakuti tsopano bwenzi ndili gone mwamtendere;
    ndikanakhala nditagona tulo ndili pa mpumulo
14 pamodzi ndi mafumu ndi aphungu a dziko lapansi,
    amene anadzimangira nyumba zikuluzikulu zimene tsopano ndi mabwinja,
15 pamodzi ndi olamulira amene anali ndi golide,
    amene anadzaza nyumba zawo ndi siliva.
16 Kapena, bwanji sindinakwiriridwe pansi monga mwana wobadwa wakufa kale,
    ngati khanda limene silinaone kuwala kwa dzuwa?
17 Ku mandako anthu oyipa sakhalanso pa mavuto,
    ndipo kumeneko anthu otopa ali pa mpumulo.
18 A mʼndende kumeneko akusangalala ndi mtendere;
    sakumvanso mawu ofuwula a kapitawo wa akapolo.
19 Anthu wamba ndi anthu apamwamba ali kumeneko,
    ndipo kapolo ndi womasuka kwa mbuye wake.

20 “Chifukwa chiyani dzuwa limawalira iwo amene ali pa mavuto,
    ndipo moyo umapatsidwa kwa owawidwa mtima,
21 kwa iwo amene amalakalaka imfa imene sibwera,
    amene amayifunafuna imfayo kupambana chuma chobisika,
22 amene amakondwa ndi kusangalala
    akamalowa mʼmanda?
23 Chifuwa chiyani moyo umaperekedwa kwa munthu
    amene njira yake yabisika,
    amene Mulungu wamuzinga ponseponse?
24 Mʼmalo moti ndidye, ndimalira,
    ndi kubuwula kwanga nʼkosalekeza.
25 Chimene ndinkachiopa chandigwera;
    chimene ndinkachita nacho mantha chandichitikira.
26 Ndilibe mtendere kapena bata,
    ndilibe mpumulo, koma mavuto okhaokha.”

Mawu a Elifazi

Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,

“Ngati wina atakuyankha, kodi ungakhumudwe?
    Koma ndani angakhale chete wosayankhula?
Taganiza momwe iwe walangizira anthu ambiri,
    momwe walimbitsira anthu ofowoka.
Mawu ako analimbitsa anthu ofuna kugwa;
    unachirikiza anthu wotha mphamvu.
Koma tsopano mavuto akufikira ndipo wataya mtima,
    zakukhudza ndipo uli ndi mantha.
Kodi kuopa Mulungu kwako sindiko kulimbika mtima kwako?
    Ndipo moyo wako wosalakwa ndiye chiyembekezo chako?

“Ganiza bwino tsopano: Kodi munthu wosalakwa anawonongekapo nʼkale lonse?
    Nʼkuti kumene munthu wolungama mtima anaphedwa?
Monga ndaonera ine, anthu amene amatipula zoyipa,
    ndi iwo amene amadzala mavuto, amakolola zomwezo.
Iwo amaphedwa ndi mpweya wa Mulungu;
    amawonongeka ndi mpweya waukali wa mkwiyo wake.
10 Mikango imabangula ndi kulira,
    komabe mano a mikango yamphamvu amathyoledwa.
11 Mkango umafa chifukwa chosowa nyama,
    ndipo ana amkango amamwazikana.

12 “Mawu anabwera kwa ine mwamseri,
    makutu anga anamva kunongʼona kwake.
13 Mʼkati mwa maloto ochititsa mantha usiku,
    nthawi imene anthu amagona tulo tofa nato,
14 ndinagwidwa ndi mantha, ndi kuyamba kunjenjemera
    ndipo mafupa anga onse anaweyeseka.
15 Pamenepo mzimu unadutsa pamaso panga,
    ndipo ubweya wa pa thupi langa unayima kuti njoo.
16 Chinthucho chinayimirira
    koma sindinathe kuzindikira kuti chinali chiyani.
Chinthu chinayima patsogolo panga,
    kunali zii ndipo ndinamva mawu akuti,
17 ‘Kodi munthu angathe kukhala wolungama kupambana Mulungu?
    Kodi munthu angathe kukhala wangwiro kupambana Mlengi wake?
18 Ngati Mulungu sakhulupirira atumiki ake omwe,
    ngati Iye amawapeza angelo ake ndi cholakwa,
19 nanga kuli bwanji ndi iwo amene amakhala mʼnyumba zadothi,
    amene maziko awo ndi fumbi,
    amene amathudzuka mosavuta ngati kadziwotche!
20 Mmawa ali moyo, pofika madzulo afa;
    mwakachetechete, amawonongeka kwamuyaya.
21 Kodi zonse zimene ali nazo sizimatheratu,
    kotero kuti amafa osadziwa nʼkanthu komwe?’

Machitidwe a Atumwi 7:44-60

44 “Makolo athu anali ndi tenti ya msonkhano pakati pawo mʼchipululu. Anayipanga monga momwe Mulungu anawuzira Mose, molingana ndi chithunzi chimene Mose anachiona. 45 Makolo athu, atayilandira Tentiyo, anabwera nayo motsogozedwa ndi Yoswa pamene analanda dziko la mitundu imene Mulungu anayipirikitsa pamaso pawo. Tentiyo inakhala mʼdzikomo mpaka nthawi ya Davide, 46 amene anapeza chisomo pamaso pa Mulungu ndipo anapempha kuti amʼmangire nyumba Mulungu wa Yakobo. 47 Koma anali Solomoni amene anamanga nyumbayo.

48 “Komatu, Wammwambamwambayo sakhala mʼnyumba zomangidwa ndi anthu. Monga mneneri akunena kuti,

49 “ ‘Kumwamba ndi mpando wanga waufumu,
    ndipo dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga.
Kodi mudzandimangira nyumba yotani?
            Akutero Ambuye.
    Kapena malo opumuliramo Ine ali kuti?
50 Kodi si dzanja langa linapanga zonsezi?’

51 “Anthu wokanika inu, osachita mdulidwe wa mu mtima ndi a makutu ogontha! Inu ofanana ndi makolo anu. Nthawi zonse mumakana kumvera Mzimu Woyera: 52 Kodi analipo mneneri amene makolo anu sanamuzunze? Iwo anapha ngakhale amene ananeneratu za kubwera kwa Wolungamayo. Ndipo tsopano inu munamupereka ndi kumupha Iye. 53 Inu amene munalandira Malamulo amene anaperekedwa ndi angelo ndipo simunawamvere.”

Kuphedwa kwa Stefano

54 Atamva zimenezi, iwo anakwiya kwambiri ndipo anamukukutira mano. 55 Koma Stefano, wodzaza ndi Mzimu Woyera, anayangʼana kumwamba ndipo anaona ulemerero wa Mulungu ndiponso Yesu atayimirira ku dzanja lamanja la Mulungu. 56 Stefano anati, “Taonani, ndikuona kumwamba kotsekuka ndiponso Mwana wa Munthu atayimirira ku dzanja la manja la Mulungu.”

57 Koma iwo anatseka mʼmakutu mwawo, ndipo anafuwula kolimba, onse anathamangira kwa iye, 58 anamukokera kunja kwa mzinda ndipo anayamba kumugenda miyala. Mboni zinasungitsa zovala zawo kwa mnyamata otchedwa Saulo.

59 Akumugenda miyala, Stefano anapemphera kuti, “Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.” 60 Ndipo anagwada pansi nafuwula mwamphamvu kuti, “Ambuye musawawerengere tchimoli.” Atanena mawu amenewa anamwalira.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.