Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Estere 9-10

Chigonjetso cha Ayuda

Pa mwezi wa 12, mwezi wa Adara pa tsiku la 13 la mwezi womwewo, tsiku limene lamulo loyamba lija la mfumu linayembekezereka kuti litsatidwe, pamene adani a Ayuda anati awononge Ayudawo, zinthu zinasintha. Ayuda ndiwo anawononga adani awo. Ayuda anasonkhana mʼmizinda ya zigawo zonse za Mfumu Ahasiwero kuthira nkhondo onse amene anafuna kuwawononga. Palibe amene akanalimbana nawo chifukwa anthu onse a mitundu ina anachita nawo mantha. Ndipo akuluakulu onse a zigawo, akalonga, akazembe ndi ogwira ntchito za mfumu anathandiza Ayuda, chifukwa anachita mantha ndi Mordekai. Pajatu Mordekai anali munthu wamkulu mʼnyumba ya ufumu. Mbiri yake inafalikira zigawo zonse, ndipo mphamvu zake zinakulirakulirabe.

Motero Ayuda anakantha adani awo onse ndi lupanga, kuwapha ndi kuwawononga, ndipo anachita chimene chinawakomera kwa adani awo. Ku likulu la mzinda wa Susa, Ayuda anapha ndi kuwononga anthu 500. Ayuda anaphanso Parisandata, Dalifoni, Asipata, Porata, Adaliya, Aridata, Parimasita, Arisai, Aridai ndi Vaisata, 10 ana khumi a Hamani, mwana wa Hamedata, mdani wa Ayuda. Koma sanalande katundu wawo.

11 Tsiku lomwelo anawuza mfumu chiwerengero cha anthu amene anaphedwa mu likulu la mzinda wa Susa. 12 Mfumu inati kwa mfumukazi Estere, “Ayuda apha ndi kuwononga anthu 500 ndi ana khumi a Hamani mu likulu la mzinda wa Susa. Nanga ku zigawo zina zonse za mfumu achitako chiyani? Kodi tsopano ukupemphanso chiyani? Chimene ukupempha ndidzakupatsa. Kodi ukufuna chiyani? Chimene ukufuna ndidzakupatsa.”

13 Estere anayankha kuti, “Ngati chingakukomereni mfumu, apatseni chilolezo Ayuda okhala mu Susa kuti achitenso zimene achita lerozi mawa, potsata lamulo ndipo mulole kuti ana khumi a Hamani aja mitembo yawo ipachikidwe pa mtanda.”

14 Choncho mfumu inalamula kuti izi zichitike. Anapereka lamulo mu Susa ndipo mitembo ya ana khumi a Hamani anayipachika pa mtanda. 15 Ayuda a mu mzinda wa Susa anasonkhana pamodzi pa tsiku la 14 la mwezi wa Adara ndipo anapha anthu 300 mu Susa, koma sanatenge katundu wawo.

16 Tsono Ayuda ena onse amene anali mu zigawo za mfumu anasonkhananso kudziteteza ndipo sanasautsidwenso ndi adani popeza anapha anthu 75,000 koma sanalande zofunkha zawo. 17 Zonsezi zinachitika pa tsiku la 13 la mwezi wa Adara ndipo pa tsiku la 14 anapumula ndi kupanga tsikuli kuti likhale la madyerero ndi chikondwerero.

Kukondwerera Purimu

18 Koma Ayuda okhala mu Susa anasonkhana pa tsiku la 13 ndi la 14 ndipo anakonza tsiku la 15 kuti likhale tsiku la madyerero ndi chikondwerero.

19 Ichi ndi chifukwa chake Ayuda a ku midzi, amene amakhala mʼzithando amasunga tsiku la 14 la mwezi wa Adara ngati la madyerero ndi chikondwerero, tsiku lopatsana mphatso.

20 Mordekai analemba mawu awa mʼmakalata ndipo anawatumiza kwa Ayuda onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero, a pafupi ndi a kutali: 21 Anati chaka chilichonse, Ayudawo azisunga tsiku la 14 ndi 15 la mwezi wa Adara, 22 ngati masiku amene Ayuda anapulumutsidwa kwa adani awo, ndiponso ngati mwezi umene chisoni chawo chinasandulika chimwemwe ndi kulira kwawo kunasandulika chikondwerero. Anawalembera kuti azisunga masikuwa ngati masiku a madyerero ndi chikondwerero, masiku opatsana mphatso zachakudya kwa wina ndi mnzake komanso opereka mphatso kwa osauka.

23 Choncho Ayuda anavomereza kusunga masikuwa ngati a chikondwerero monga analembera Mordekai. 24 Hamani mwana wa Hamedata, Mwagagi, mdani wa Ayuda onse, anakonza chiwembu chakupha ndi kuwononga Ayuda ndipo anachita maere otchedwa Purimu kuti awaphe ndi kuwawononga. 25 Koma mfumu itazindikira za chiwembuchi, inalamula kuti zilembedwe mʼmakalata kuti chiwembu chimene Hamani anakonzera Ayuda chigwere pa iye mwini, ndi kuti iye pamodzi ndi ana ake apachikidwe pa mtanda. 26 Ndi chifukwa chake masiku amenewa amatchedwa masiku a Purimu potsata dzina lakuti Purimu. Chifukwa cha kalata ya Mordekai ndiponso chifukwa cha zimene anaziona ndi kuwachitikira, 27 Ayuda onse anagwirizana kukhazikitsa lamulo lokhudza iwo, zidzukulu zawo ndi onse amene adzapanga nawo ubale kuti asalephere kusunga masiku awiri amenewa chaka chilichonse monga zinalembedweramo ndiponso potsata nthawi imene anayika. 28 Azisunga ndi kukumbukira masiku amenewa mu mʼbado uliwonse ndi banja lililonse, mʼchigawo chilichonse ndi mu mzinda uliwonse. Ndipo Ayuda asadzasiye kukondwerera masiku a Purimuwa ndiponso zidzukulu zawo zisadzaleke kuwakumbukira.

29 Choncho mfumukazi Estere, mwana wa mkazi wa Abihaili, pamodzi ndi Mordekai Myuda analemba ndi ulamuliro onse kutsimikizira kalata iyi yachiwiri yokhudza Purimu. 30 Ndipo Mordekai anatumiza makalata kwa Ayuda onse ku zigawo 127 za ufumu wa Ahasiwero. Kalatayi inali ya mawu a mtendere ndiponso a kukhulupirika 31 kuti azisunga masiku a Purimu pa nyengo imene inavomerezeka monga mmene Mordekai Myuda ndi mfumukazi Estere anawalamulira ndiponso monga anadziyikira eni okha ndi zidzukulu zawo zonena za nthawi zawo za kusala zakudya ndi kulira. 32 Lamulo la Estere linakhazikitsa mwambo wa Purimuwu ndipo zinalembedwa mʼmabuku.

Ukulu wa Mordekai

10 Mfumu Ahasiwero anakhometsa msonkho mʼdziko lake lonse mpaka ku zilumba zonse. Ndipo ntchito zonse zochitika ndi mphamvu zake komanso ndi zonse zofotokoza za ukulu wa Mordekai, kukwezedwa kwake ndi mfumu, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Mediya ndi Peresiya? Pakuti Mordekai Myuda uja anali wachiwiri wa mfumu Ahasiwero. Kwa Ayuda onse Mordekai anali munthu wamkulu ndipo ankamukonda chifukwa ankachitira zabwino mtundu wake ndi kufunira mtendere abale ake.

Machitidwe a Atumwi 7:1-21

Mawu a Stefano

Kenaka mkulu wa ansembe anafunsa Stefano kuti, “Kodi zimene akukunenerazi ndi zoona?”

Stefano anayankha kuti, “Abale ndi makolo, tamverani! Mulungu waulemerero anaoneka kwa kholo lathu Abrahamu pamene ankakhala ku Mesopotamiya, asanakakhale ku Harani. Mulungu anati, ‘Tuluka mʼdziko lako, siya abale ako, ndipo pita ku dziko limene ndidzakusonyeza.’

“Ndipo iye anatulukadi mʼdziko la Akaldeya ndi kukakhala ku Harani. Atamwalira abambo ake, Mulungu anamuchotsa kumeneko ndi kumubweretsa mʼdziko lino limene inu mukukhalamo tsopano. Mulungu sanamupatse cholowa kuno, ngakhale kadera kakangʼono kadziko. Koma Mulungu anamulonjeza kuti adzapereka dziko lino kwa iye ndi kwa zidzukulu zake, ngakhale kuti pa nthawi imeneyi analibe mwana. Mulungu anayankhula motere kwa iye: ‘Zidzukulu zako zidzakhala alendo mʼdziko lachilendo, ndipo zidzakhala akapolo ndi kuzunzidwa zaka 400.’ Mulungu anati, ‘Ine ndidzalanga dziko limene zidzukulu zako zidzagwireko ukapolo, ndipo pambuyo pake akadzatuluka mʼdzikolo adzandipembedza Ine pamalo pano.’ Kenaka Mulungu anachita pangano la mdulidwe ndi Abrahamu. Ndipo Abrahamu, anabereka Isake, namudula ali ndi masiku asanu ndi atatu. Ndipo Isake anabereka Yakobo, Yakobo anabereka makolo khumi ndi awiri aja.

“Makolo athu anachita nsanje ndi Yosefe ndipo anamugulitsa kuti akakhale kapolo ku Igupto. Koma Mulungu anali naye 10 ndipo anamupulumutsa iye kumasautso ake onse. Mulungu anamupatsa Yosefe nzeru ndi chisomo pamaso pa Farao mfumu ya ku Igupto, kotero mfumuyo inamuyika iye kukhala nduna yayikulu ya dziko la Igupto ndiponso nyumba yake yonse yaufumu.

11 “Kenaka munalowa njala mʼdziko la Kanaani, kotero kuti anthu anavutika kwambiri, ndipo makolo athu sanathe kupeza chakudya. 12 Pamene Yakobo anamva kuti ku Igupto kunali tirigu, iye anatuma makolo athu ulendo woyamba. 13 Pa ulendo wawo wachiwiri, Yosefe anadziwulula kwa abale akewo ndipo Farao anadziwa za banja la Yosefe. 14 Izi zinachitika, Yosefe anayitanitsa abambo ake Yakobo ndi banja lonse, onse pamodzi analipo 75. 15 Motero Yakobo anapita ku Igupto, kumene iye ndiponso makolo athu anamwalira. 16 Mitembo yawo anayinyamula ndi kupita nayo ku Sekemu kumene inayikidwa mʼmanda amene Abrahamu anagula kochokera kwa ana a Hamori ku Sekemuko.

17 “Nthawi itayandikira yakuti Mulungu achite zimene analonjeza kwa Abrahamu, mtundu wathu unakula ndi kuchuluka kwambiri mu Igupto. 18 Pambuyo pake mfumu yatsopano imene sinkamudziwa Yosefe, inayamba kulamulira dziko la Igupto. 19 Mfumuyo inachita mwachinyengo ndi mtundu wathu ndi kuwazunza kuti ataye ana awo akhanda kuti afe.

20 “Pa nthawi imeneyo Mose anabadwa, ndipo anali wokongola kwambiri. Iye analeredwa mʼnyumba ya abambo ake kwa miyezi itatu. 21 Atakamutaya, mwana wamkazi wa Farao anamutola nakamulera ngati mwana wake.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.